Exodus 35 (BOGWICC)

1 Mose anasonkhanitsa gulu lonse la Aisraeli ndipo anawawuza kuti, “Zinthu zimene Yehova wakulamulirani kuti muzichite ndi izi: 2 Muzigwira ntchito zanu pa masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku la chisanu ndi chiwiri likhale la Sabata, tsiku lanu lopuma, lopatulika kwa Yehova. Aliyense amene adzagwira ntchito iliyonse pa tsikuli ayenera kuphedwa. 3 Pa tsiku la Sabata musakoleze moto paliponse pamene mukhala.” 4 Mose ananena kwa gulu lonse la Aisraeli kuti, “Zimene Yehova wakulamulirani ndi izi: 5 Kuchokera pa zomwe muli nazo, mutenge chopereka cha Yehova. Aliyense amene ali ndi mtima wofuna kupereka abweretse kwa Yehova zopereka izi: Golide, siliva ndi mkuwa; 6 nsalu zobiriwira, zapepo, zofiira, nsalu zofewa; ubweya wambuzi; 7 zikopa za nkhosa zazimuna za utoto wofiira ndi zikopa za akatumbu; matabwa amtengo wa mkesha, 8 mafuta anyale a olivi, zonunkhiritsa mafuta odzozera ndi zopangira lubani wonunkhira; 9 miyala yokongola ya mtundu wa onikisi ndi ina yabwino yoyika pa Efodi ndi pa chovala cha pachifuwa. 10 “Anthu onse aluso pakati panu abwere ndi kupanga zonse zimene Yehova walamula: 11 Chihema ndi tenti yake ndiponso chophimba chake, ngowe zake, maferemu ake, mitanda yake, mizati yake ndi matsinde ake; 12 Bokosi la Chipangano pamodzi ndi mitengo yake yonyamulira ndiponso chovundikira chake cha bokosilo ndi nsalu zophimba bokosilo; 13 tebulo pamodzi ndi mitengo yake yonyamulira pamodzi ndi zipangizo zake zonse ndiponso buledi wokhala pamaso pa Yehova; 14 choyikapo nyale yowunikira pamodzi ndi zipangizo zake, nyale ndi mafuta anyalezo; 15 guwa lofukizira lubani pamodzi ndi mitengo yake yonyamulira, mafuta odzozera ndi lubani onunkhira; nsalu yotchinga pa khomo lolowera mʼchihema; 16 guwa lansembe yopsereza pamodzi ndi sefa yamkuwa, mitengo yake yonyamulira ndi zipangizo zake zonse, beseni losambira lamkuwa ndi miyendo yake; 17 nsalu yotchingira bwalo pamodzi ndi mizati yake ndi matsinde ake, ndiponso nsalu yotchingira pa khomo lolowera ku bwalo; 18 zikhomo za tenti ya chihema ndiponso za bwalo, ndi zingwe zake; 19 zovala zolukidwa zovala potumikira kumalo opatulika, zovala zopatulika za wansembe, Aaroni pamodzi ndi za ana ake aamuna pamene akutumikira monga ansembe.” 20 Kenaka gulu lonse la Aisraeli linachoka pamaso pa Mose, 21 ndipo aliyense amene anakhudzidwa mu mtima mwake nafuna kupereka, anabwera kudzapereka chopereka kwa Yehova cha ntchito yokonza tenti ya msonkhano, cha ntchito zonse za mʼtentimo ndi cha zovala zopatulika. 22 Onse amene anali ndi mtima wofuna, amuna ndi amayi omwe anabwera kudzapereka zodzikometsera zagolide za mtundu uliwonse: zomangira zovala, ndolo, mphete ndi zokometsera. Onse anapereka golide wawo monga nsembe yoweyula pamaso pa Yehova. 23 Aliyense amene anali ndi nsalu ya mtundu wa mtambo, yapepo kapena yofiira kapena yofewa, yosalala, kapena ubweya wambuzi, zikopa za nkhosa zonyika mu utoto wofiira kapena zikopa anazibweretsa. 24 Onse amene anapereka chopereka cha siliva kapena mkuwa anabweretsa monga chopereka kwa Yehova. Ndipo aliyense amene anali ndi matabwa a mtengo wa mkesha kuti awagwiritse ntchito mbali ina iliyonse ya ntchitoyo, anabweretsa. 25 Mayi aliyense waluso analuka ndi manja ake ndi kubweretsa chomwe analuka cha mtundu wa mtambo, chapepo kapena chofiira kapena chofewa, chosalala. 26 Ndipo amayi onse amene anali ndi mtima wofuna ndipo anali ndi luso analuka ubweya wa mbuzi. 27 Atsogoleri anabweretsa miyala ya onikisi ndi miyala yokongola yoyika pa efodi ndi chovala chapachifuwa. 28 Anabweretsanso zonunkhiritsa ndiponso mafuta owunikira a olivi ndi odzozera ndi zofukizira zonunkhira. 29 Aisraeli onse aamuna ndi aakazi amene anali ndi mtima wofuna, anabweretsa kwa Yehova chopereka chaufulu ku ntchito yonse ya Yehova imene analamulira kudzera mwa Mose kuti achite. 30 Kenaka Mose anati kwa Aisraeli, “Taonani, Yehova wasankha Bezaleli mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa fuko la Yuda, 31 ndipo wamudzaza ndi Mzimu wa Mulungu kotero kuti ali ndi luso ndi nzeru zomvetsa zinthu, ndipo akudziwa bwino ntchito zonse zamanja monga izi: 32 Kulemba ndondomeko ya ntchito zaluso ndi kupanga zinthu zagolide, zasiliva ndi zamkuwa, 33 kusema ndi kuyika miyala yokongola, kukonza zinthu zamatabwa ndiponso kugwira ntchito ina iliyonse yamanja. 34 Ndipo Iye wapereka kwa Bezaleli pamodzi ndi Oholiabu mwana wa Ahisamaki, wa fuko la Dani luso lophunzitsa ena. 35 Mulungu wawapatsa maluso osiyanasiyana, maluso ogoba, olemba ndondomeko, opeta zokometsera pa nsalu zamtundu wamtambo, zapepo ndi zofiira ndiponso zofewa zosalala ndi zoluka. Onsewa ndi amisiri a ntchito zamanja ndi zokonza ndondomeko.

In Other Versions

Exodus 35 in the ANGEFD

Exodus 35 in the ANTPNG2D

Exodus 35 in the AS21

Exodus 35 in the BAGH

Exodus 35 in the BBPNG

Exodus 35 in the BBT1E

Exodus 35 in the BDS

Exodus 35 in the BEV

Exodus 35 in the BHAD

Exodus 35 in the BIB

Exodus 35 in the BLPT

Exodus 35 in the BNT

Exodus 35 in the BNTABOOT

Exodus 35 in the BNTLV

Exodus 35 in the BOATCB

Exodus 35 in the BOATCB2

Exodus 35 in the BOBCV

Exodus 35 in the BOCNT

Exodus 35 in the BOECS

Exodus 35 in the BOHCB

Exodus 35 in the BOHCV

Exodus 35 in the BOHLNT

Exodus 35 in the BOHNTLTAL

Exodus 35 in the BOICB

Exodus 35 in the BOILNTAP

Exodus 35 in the BOITCV

Exodus 35 in the BOKCV

Exodus 35 in the BOKCV2

Exodus 35 in the BOKHWOG

Exodus 35 in the BOKSSV

Exodus 35 in the BOLCB

Exodus 35 in the BOLCB2

Exodus 35 in the BOMCV

Exodus 35 in the BONAV

Exodus 35 in the BONCB

Exodus 35 in the BONLT

Exodus 35 in the BONUT2

Exodus 35 in the BOPLNT

Exodus 35 in the BOSCB

Exodus 35 in the BOSNC

Exodus 35 in the BOTLNT

Exodus 35 in the BOVCB

Exodus 35 in the BOYCB

Exodus 35 in the BPBB

Exodus 35 in the BPH

Exodus 35 in the BSB

Exodus 35 in the CCB

Exodus 35 in the CUV

Exodus 35 in the CUVS

Exodus 35 in the DBT

Exodus 35 in the DGDNT

Exodus 35 in the DHNT

Exodus 35 in the DNT

Exodus 35 in the ELBE

Exodus 35 in the EMTV

Exodus 35 in the ESV

Exodus 35 in the FBV

Exodus 35 in the FEB

Exodus 35 in the GGMNT

Exodus 35 in the GNT

Exodus 35 in the HARY

Exodus 35 in the HNT

Exodus 35 in the IRVA

Exodus 35 in the IRVB

Exodus 35 in the IRVG

Exodus 35 in the IRVH

Exodus 35 in the IRVK

Exodus 35 in the IRVM

Exodus 35 in the IRVM2

Exodus 35 in the IRVO

Exodus 35 in the IRVP

Exodus 35 in the IRVT

Exodus 35 in the IRVT2

Exodus 35 in the IRVU

Exodus 35 in the ISVN

Exodus 35 in the JSNT

Exodus 35 in the KAPI

Exodus 35 in the KBT1ETNIK

Exodus 35 in the KBV

Exodus 35 in the KJV

Exodus 35 in the KNFD

Exodus 35 in the LBA

Exodus 35 in the LBLA

Exodus 35 in the LNT

Exodus 35 in the LSV

Exodus 35 in the MAAL

Exodus 35 in the MBV

Exodus 35 in the MBV2

Exodus 35 in the MHNT

Exodus 35 in the MKNFD

Exodus 35 in the MNG

Exodus 35 in the MNT

Exodus 35 in the MNT2

Exodus 35 in the MRS1T

Exodus 35 in the NAA

Exodus 35 in the NASB

Exodus 35 in the NBLA

Exodus 35 in the NBS

Exodus 35 in the NBVTP

Exodus 35 in the NET2

Exodus 35 in the NIV11

Exodus 35 in the NNT

Exodus 35 in the NNT2

Exodus 35 in the NNT3

Exodus 35 in the PDDPT

Exodus 35 in the PFNT

Exodus 35 in the RMNT

Exodus 35 in the SBIAS

Exodus 35 in the SBIBS

Exodus 35 in the SBIBS2

Exodus 35 in the SBICS

Exodus 35 in the SBIDS

Exodus 35 in the SBIGS

Exodus 35 in the SBIHS

Exodus 35 in the SBIIS

Exodus 35 in the SBIIS2

Exodus 35 in the SBIIS3

Exodus 35 in the SBIKS

Exodus 35 in the SBIKS2

Exodus 35 in the SBIMS

Exodus 35 in the SBIOS

Exodus 35 in the SBIPS

Exodus 35 in the SBISS

Exodus 35 in the SBITS

Exodus 35 in the SBITS2

Exodus 35 in the SBITS3

Exodus 35 in the SBITS4

Exodus 35 in the SBIUS

Exodus 35 in the SBIVS

Exodus 35 in the SBT

Exodus 35 in the SBT1E

Exodus 35 in the SCHL

Exodus 35 in the SNT

Exodus 35 in the SUSU

Exodus 35 in the SUSU2

Exodus 35 in the SYNO

Exodus 35 in the TBIAOTANT

Exodus 35 in the TBT1E

Exodus 35 in the TBT1E2

Exodus 35 in the TFTIP

Exodus 35 in the TFTU

Exodus 35 in the TGNTATF3T

Exodus 35 in the THAI

Exodus 35 in the TNFD

Exodus 35 in the TNT

Exodus 35 in the TNTIK

Exodus 35 in the TNTIL

Exodus 35 in the TNTIN

Exodus 35 in the TNTIP

Exodus 35 in the TNTIZ

Exodus 35 in the TOMA

Exodus 35 in the TTENT

Exodus 35 in the UBG

Exodus 35 in the UGV

Exodus 35 in the UGV2

Exodus 35 in the UGV3

Exodus 35 in the VBL

Exodus 35 in the VDCC

Exodus 35 in the YALU

Exodus 35 in the YAPE

Exodus 35 in the YBVTP

Exodus 35 in the ZBP