Ezekiel 12 (BOGWICC)

1 Yehova anayankhula nane kuti, 2 “Iwe mwana wa munthu, ukukhala pakati pa anthu owukira, iwowo maso openyera ali nawo, koma sakuona ndipo makutu omvera ali nawo, koma sakumva chifukwa choti ndi anthu owukira. 3 “Choncho, iwe mwana wa munthu, longedza katundu wako wopita naye ku ukapolo. Unyamuke nthawi yamasana iwo akuona. Uchite ngati wanyamuka kuchoka kumene ukukhala kupita ku dziko lachilendo iwowo akuona. Mwina adzamvetsetsa, paja ndi anthu aupandu. 4 Utulutse katundu wako wopita naye ku ukapolo nthawi ya masana iwo akuona. Ndipo nthawi ya madzulo, iwo akuona, uchoke monga ngati ukupita ku ukapolo. 5 Iwo akuona, ubowole pa khoma ndipo utulutsirepo katundu wako. 6 Usenze katundu wako pa phewa iwo akuona, ndipo upite kunja ku mdima. Uphimbe nkhope yako kuti usaone pansi, pakuti ndakusandutsa iwe chizindikiro chochenjeza Aisraeli.” 7 Choncho ine ndinachita monga momwe anandilamulira. Nthawi yamasana ndinatulutsa zinthu zanga nditazimanga ngati ndikupita ku ukapolo. Ndipo nthawi yamadzulo ndinabowola khoma ndi manja anga. Pamene chisisira chinkayamba, ndinasenza katundu wanga pa phewa kutuluka naye iwo akuona. 8 Mmawa mwake Yehova anandiyankhula nati: 9 “Iwe mwana wa munthu, kodi anthu aupandu a Israeli sanakufunse kuti ukuchita chiyani? 10 “Uwawuze kuti, ‘zimene ndikunena Ine Ambuye Wamphamvuzonse ndi izi: Uthengawu ndi wonena za kalonga wa ku Yerusalemu pamodzi ndi banja lonse la Israeli amene akukhala kumeneko.’ 11 Uwawuze kuti, ‘Ndiwe chizindikiro chowachenjeza.’“Zidzakuchitikirani monga momwe zakuchitikira iwemu. Iwo adzatengedwa kupita ku ukapolo.” 12 “Kalonga wawo adzatenga katundu wake nʼchisisira nʼkunyamuka. Adzatulukira pa bowo limene anthu anabowola pa khoma. Adzaphimba nkhope yake kuti asaone kumene akupita. 13 Ndidzayala ukonde wanga pa iye ndi kumukola mu msampha wanga. Ndidzabwera naye ku Babuloni, dziko la Akaldeya, koma sadzaliona dzikolo, ndipo adzafera kumeneko. 14 Ine ndidzabalalitsa kumbali zonse zinayi onse okhala naye pafupi, ndiwo omuthandiza ake pamodzi ndi ankhondo ake. Ndidzawalondola ndi lupanga losolola. 15 “Iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndikadzawamwaza pakati pa anthu a mitundu ina ndi kuwabalalitsira ku mayiko ena. 16 Koma ndidzasiyako ena pangʼono amene adzapulumuke ku lupanga, njala ndi mliri, kuti akafotokoze ntchito zawo zonse zonyansa pakati pa anthu achilendo kumene akupitako. Pamenepo adzadziwa kuti ndine Yehova.” 17 Pambuyo pake Yehova anandiyankhulanso nati, 18 “Iwe mwana wa munthu, uzinjenjemera ukamadya chakudya chako, ndipo uzinthunthumira ndi mantha ukamamwa madzi ako. 19 Uwawuze anthu a mʼdzikomo kuti izi ndi zimene Ambuye Wamphamvuzonse akunena za anthu okhala mu Yerusalemu ndi dziko la Israeli: Iwo adzadya chakudya chawo ndi mantha ndi kumwa madzi awo ndi nkhawa. Zonse za mʼdziko lawo zidzalandidwa chifukwa cha ziwawa za anthu onse okhala mʼmenemo. 20 Mizinda imene ili ndi anthu idzasakazika ndipo dziko lidzasanduka chipululu. Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.” 21 Yehova anayankhulanso nane kuti, 22 “Iwe mwana wa munthu, kodi mwambi umene ukunenedwa mu Israeli ndi wotani: ‘Masiku akupita koma masomphenya onse sakukwaniritsidwa?’ 23 Choncho uwawuze anthuwo kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndidzawuthetsa mwambi umenewu ndipo sadzawunenanso mu Israeli.’ Uwawuze kuti, ‘masiku ayandikira oti zonse zimene ndinanena mʼmasomphenya zichitikedi. 24 Pakuti masiku amenewo sikudzakhalanso masomphenya abodza kapena kuwombeza kwa chinyengo pakati pa anthu a Israeli. 25 Koma Ine Ambuye ndidzayankhula chimene ndikufuna, ndipo chidzachitikadi, osachedwa ayi. Pakuti mʼmasiku anu omwe ano, inu anthu opanduka, ndidzakwaniritsa chilichonse chimene ndidzanena. Ndikutero Ine Yehova.’ ” 26 Yehova anandiyankhula nati: 27 “Iwe mwana wa munthu, Aisraeli akunena kuti, ‘masomphenya amene ukuona sadzachitika kwa zaka zambiri. Iwo akuti ukulosa za zinthu zimene zidzachitika ku tsogolo kwambiri.’ 28 “Choncho uwawuze kuti, ‘zimene Ine Ambuye Yehova ndikunena ndi izi: Zonena zanga sizidzachedwanso; chilichonse chimene ndikunena chidzachitikadi. Ndikutero Ine Yehova.’ ”

In Other Versions

Ezekiel 12 in the ANGEFD

Ezekiel 12 in the ANTPNG2D

Ezekiel 12 in the AS21

Ezekiel 12 in the BAGH

Ezekiel 12 in the BBPNG

Ezekiel 12 in the BBT1E

Ezekiel 12 in the BDS

Ezekiel 12 in the BEV

Ezekiel 12 in the BHAD

Ezekiel 12 in the BIB

Ezekiel 12 in the BLPT

Ezekiel 12 in the BNT

Ezekiel 12 in the BNTABOOT

Ezekiel 12 in the BNTLV

Ezekiel 12 in the BOATCB

Ezekiel 12 in the BOATCB2

Ezekiel 12 in the BOBCV

Ezekiel 12 in the BOCNT

Ezekiel 12 in the BOECS

Ezekiel 12 in the BOHCB

Ezekiel 12 in the BOHCV

Ezekiel 12 in the BOHLNT

Ezekiel 12 in the BOHNTLTAL

Ezekiel 12 in the BOICB

Ezekiel 12 in the BOILNTAP

Ezekiel 12 in the BOITCV

Ezekiel 12 in the BOKCV

Ezekiel 12 in the BOKCV2

Ezekiel 12 in the BOKHWOG

Ezekiel 12 in the BOKSSV

Ezekiel 12 in the BOLCB

Ezekiel 12 in the BOLCB2

Ezekiel 12 in the BOMCV

Ezekiel 12 in the BONAV

Ezekiel 12 in the BONCB

Ezekiel 12 in the BONLT

Ezekiel 12 in the BONUT2

Ezekiel 12 in the BOPLNT

Ezekiel 12 in the BOSCB

Ezekiel 12 in the BOSNC

Ezekiel 12 in the BOTLNT

Ezekiel 12 in the BOVCB

Ezekiel 12 in the BOYCB

Ezekiel 12 in the BPBB

Ezekiel 12 in the BPH

Ezekiel 12 in the BSB

Ezekiel 12 in the CCB

Ezekiel 12 in the CUV

Ezekiel 12 in the CUVS

Ezekiel 12 in the DBT

Ezekiel 12 in the DGDNT

Ezekiel 12 in the DHNT

Ezekiel 12 in the DNT

Ezekiel 12 in the ELBE

Ezekiel 12 in the EMTV

Ezekiel 12 in the ESV

Ezekiel 12 in the FBV

Ezekiel 12 in the FEB

Ezekiel 12 in the GGMNT

Ezekiel 12 in the GNT

Ezekiel 12 in the HARY

Ezekiel 12 in the HNT

Ezekiel 12 in the IRVA

Ezekiel 12 in the IRVB

Ezekiel 12 in the IRVG

Ezekiel 12 in the IRVH

Ezekiel 12 in the IRVK

Ezekiel 12 in the IRVM

Ezekiel 12 in the IRVM2

Ezekiel 12 in the IRVO

Ezekiel 12 in the IRVP

Ezekiel 12 in the IRVT

Ezekiel 12 in the IRVT2

Ezekiel 12 in the IRVU

Ezekiel 12 in the ISVN

Ezekiel 12 in the JSNT

Ezekiel 12 in the KAPI

Ezekiel 12 in the KBT1ETNIK

Ezekiel 12 in the KBV

Ezekiel 12 in the KJV

Ezekiel 12 in the KNFD

Ezekiel 12 in the LBA

Ezekiel 12 in the LBLA

Ezekiel 12 in the LNT

Ezekiel 12 in the LSV

Ezekiel 12 in the MAAL

Ezekiel 12 in the MBV

Ezekiel 12 in the MBV2

Ezekiel 12 in the MHNT

Ezekiel 12 in the MKNFD

Ezekiel 12 in the MNG

Ezekiel 12 in the MNT

Ezekiel 12 in the MNT2

Ezekiel 12 in the MRS1T

Ezekiel 12 in the NAA

Ezekiel 12 in the NASB

Ezekiel 12 in the NBLA

Ezekiel 12 in the NBS

Ezekiel 12 in the NBVTP

Ezekiel 12 in the NET2

Ezekiel 12 in the NIV11

Ezekiel 12 in the NNT

Ezekiel 12 in the NNT2

Ezekiel 12 in the NNT3

Ezekiel 12 in the PDDPT

Ezekiel 12 in the PFNT

Ezekiel 12 in the RMNT

Ezekiel 12 in the SBIAS

Ezekiel 12 in the SBIBS

Ezekiel 12 in the SBIBS2

Ezekiel 12 in the SBICS

Ezekiel 12 in the SBIDS

Ezekiel 12 in the SBIGS

Ezekiel 12 in the SBIHS

Ezekiel 12 in the SBIIS

Ezekiel 12 in the SBIIS2

Ezekiel 12 in the SBIIS3

Ezekiel 12 in the SBIKS

Ezekiel 12 in the SBIKS2

Ezekiel 12 in the SBIMS

Ezekiel 12 in the SBIOS

Ezekiel 12 in the SBIPS

Ezekiel 12 in the SBISS

Ezekiel 12 in the SBITS

Ezekiel 12 in the SBITS2

Ezekiel 12 in the SBITS3

Ezekiel 12 in the SBITS4

Ezekiel 12 in the SBIUS

Ezekiel 12 in the SBIVS

Ezekiel 12 in the SBT

Ezekiel 12 in the SBT1E

Ezekiel 12 in the SCHL

Ezekiel 12 in the SNT

Ezekiel 12 in the SUSU

Ezekiel 12 in the SUSU2

Ezekiel 12 in the SYNO

Ezekiel 12 in the TBIAOTANT

Ezekiel 12 in the TBT1E

Ezekiel 12 in the TBT1E2

Ezekiel 12 in the TFTIP

Ezekiel 12 in the TFTU

Ezekiel 12 in the TGNTATF3T

Ezekiel 12 in the THAI

Ezekiel 12 in the TNFD

Ezekiel 12 in the TNT

Ezekiel 12 in the TNTIK

Ezekiel 12 in the TNTIL

Ezekiel 12 in the TNTIN

Ezekiel 12 in the TNTIP

Ezekiel 12 in the TNTIZ

Ezekiel 12 in the TOMA

Ezekiel 12 in the TTENT

Ezekiel 12 in the UBG

Ezekiel 12 in the UGV

Ezekiel 12 in the UGV2

Ezekiel 12 in the UGV3

Ezekiel 12 in the VBL

Ezekiel 12 in the VDCC

Ezekiel 12 in the YALU

Ezekiel 12 in the YAPE

Ezekiel 12 in the YBVTP

Ezekiel 12 in the ZBP