Ezekiel 26 (BOGWICC)

1 Pa chaka cha khumi ndi chimodzi, tsiku loyamba la mwezi, Yehova anandiyankhula kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, anthu a ku Turo ananyogodola Yerusalemu kuti ‘Hii! Uja amene anali chipata choloweramo anthu a mitundu ina wawonongeka. Zitseko zake zatsekukira ife. Tidzalemera popeza wasanduka bwinja.’ 3 Nʼchifukwa chake, Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzakulangani, inu anthu a ku Turo. Ndidzakuyitanirani anthu a mitundu ina kuti adzakulangeni monga momwe mafunde amawombera pa Nyanja. 4 Anthuwo adzawononga makoma a Turo ndi kugwetsa nsanja zake. Ndidzapala dothi lake ndipo ndidzamusandutsa thanthwe losalala. 5 Udzakhala poyanikapo makoka pakati pa nyanja. Ine Ambuye Yehova ndayankhula zimenezo. Udzasanduka chofunkha cha anthu a mitundu ina. 6 Anthu okhala ku mtunda adzasakazidwa ndi lupanga. Pamenepo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova. 7 “Ine Ambuye Yehova ndikuti: Iwe Turo, ndidzakubweretsera Nebukadinezara, mfumu ya ku Babuloni mfumu ya mafumu, kuchokera kumpoto pamodzi ndi akavalo ndiponso magaleta, anthu okwera pa akavalo ndi gulu lalikulu la ankhondo. 8 Anthu okhala ku mtunda adzawapha ndi lupanga. Adzapanga mitumbira yankhondo ndi kukukwezera zishango kuti alimbane nawe. 9 Adzagwetsa makoma ako ndi zida zogumulira khoma ndi kugwetsa nsanja zako ndi nkhwangwa zake. 10 Akavalo ake adzakhala ochuluka kwambiri kotero kuti adzakukwirira ndi fumbi lawo. Makoma ako adzagwedezeka ndi mdidi wa akavalo, ngolo ndi magaleta pamene iye adzalowa pa zipata monga mmene amalowera mu mzinda umene makoma ake agwetsedwa. 11 Akavalo ake adzapondaponda mʼmisewu yako yonse ndi ziboda zawo. Adzapha anthu ako ndi lupanga. Mizati yako yolimba idzagwetsedwa. 12 Iwo adzafunkha chuma chako ndipo adzalanda zinthu zako za malonda. Adzagwetsa makoma ako ndi kuwononga nyumba zako zabwino. Adzaponya miyala yako, matabwa ako ndi dothi lako mʼnyanja. 13 Choncho ndidzathetsa phokoso la nyimbo zanu, ndipo kulira kwa apangwe ako sikudzamvekanso. 14 Ndidzakusandutsa thanthwe losalala, ndipo udzakhala malo woyanikapo makoka a nsomba. Sudzamangidwanso, pakuti Ine Yehova ndayankhula, akutero Ambuye Yehova. 15 “Ine Ambuye Yehova ndikukuwuza, iwe mzinda wa Turo, kuti zilumba zidzagwedezeka pakumva za kugwa kwako ndiponso poona anthu opweteka akubuwula ndipo anthu akuphedwa pakati pako. 16 Pamenepo mafumu a mʼmbali mwa nyanja adzatsika pa mipando yawo yaufumu. Adzayika pambali mikanjo yawo ndi kuvala zovala zawo zamakaka. Adzachita mantha ndipo adzakhala pansi akunjenjemera kosalekeza. Adzathedwa nzeru poona zimene zakugwera. 17 Pamenepo adzayimba nyimbo yokudandaula ndipo adzati kwa iwe:“ ‘Nʼkuchita kuwonongeka chotere, iwe mzinda wotchuka,wodzaza ndi anthu a ku nyanja!Unali wamphamvu pa nyanja,iwe ndi nzika zako;unkaopseza anthu onse ameneankakhala kumeneko. 18 Tsopano mayiko a mʼmbali mwa nyanja akunjenjemerachifukwa cha kugwa kwako;okhala pa zilumba nawonso agwidwa ndi mantha aakuluchifukwa cha kugwa kwako.’ 19 “Mawu a Ine Ambuye Yehova ndi awa: Ndidzakusandutsa bwinja, ngati mizinda imene anthu sangathe kukhalamo. Ndidzakuphimba ndi madzi ozama a mʼnyanja, madzi amphamvu woti akumize. 20 Ndidzakugwetsa pansi kuti ukhale pamodzi ndi anthu amvulazakale amene akutsikira ku manda. Ine ndidzakusunga ku dzenjeko ngati ku bwinja losiyidwa kalekale, pamodzi ndi anthu amene anafa kale motero sudzabwererako kukhala pakati pa anthu amoyo. 21 Ine ndidzakuthetsa mochititsa mantha, ndipo sudzakhalaponso. Anthu adzakufunafuna, koma sudzapezekanso, akutero Ambuye Yehova.”

In Other Versions

Ezekiel 26 in the ANGEFD

Ezekiel 26 in the ANTPNG2D

Ezekiel 26 in the AS21

Ezekiel 26 in the BAGH

Ezekiel 26 in the BBPNG

Ezekiel 26 in the BBT1E

Ezekiel 26 in the BDS

Ezekiel 26 in the BEV

Ezekiel 26 in the BHAD

Ezekiel 26 in the BIB

Ezekiel 26 in the BLPT

Ezekiel 26 in the BNT

Ezekiel 26 in the BNTABOOT

Ezekiel 26 in the BNTLV

Ezekiel 26 in the BOATCB

Ezekiel 26 in the BOATCB2

Ezekiel 26 in the BOBCV

Ezekiel 26 in the BOCNT

Ezekiel 26 in the BOECS

Ezekiel 26 in the BOHCB

Ezekiel 26 in the BOHCV

Ezekiel 26 in the BOHLNT

Ezekiel 26 in the BOHNTLTAL

Ezekiel 26 in the BOICB

Ezekiel 26 in the BOILNTAP

Ezekiel 26 in the BOITCV

Ezekiel 26 in the BOKCV

Ezekiel 26 in the BOKCV2

Ezekiel 26 in the BOKHWOG

Ezekiel 26 in the BOKSSV

Ezekiel 26 in the BOLCB

Ezekiel 26 in the BOLCB2

Ezekiel 26 in the BOMCV

Ezekiel 26 in the BONAV

Ezekiel 26 in the BONCB

Ezekiel 26 in the BONLT

Ezekiel 26 in the BONUT2

Ezekiel 26 in the BOPLNT

Ezekiel 26 in the BOSCB

Ezekiel 26 in the BOSNC

Ezekiel 26 in the BOTLNT

Ezekiel 26 in the BOVCB

Ezekiel 26 in the BOYCB

Ezekiel 26 in the BPBB

Ezekiel 26 in the BPH

Ezekiel 26 in the BSB

Ezekiel 26 in the CCB

Ezekiel 26 in the CUV

Ezekiel 26 in the CUVS

Ezekiel 26 in the DBT

Ezekiel 26 in the DGDNT

Ezekiel 26 in the DHNT

Ezekiel 26 in the DNT

Ezekiel 26 in the ELBE

Ezekiel 26 in the EMTV

Ezekiel 26 in the ESV

Ezekiel 26 in the FBV

Ezekiel 26 in the FEB

Ezekiel 26 in the GGMNT

Ezekiel 26 in the GNT

Ezekiel 26 in the HARY

Ezekiel 26 in the HNT

Ezekiel 26 in the IRVA

Ezekiel 26 in the IRVB

Ezekiel 26 in the IRVG

Ezekiel 26 in the IRVH

Ezekiel 26 in the IRVK

Ezekiel 26 in the IRVM

Ezekiel 26 in the IRVM2

Ezekiel 26 in the IRVO

Ezekiel 26 in the IRVP

Ezekiel 26 in the IRVT

Ezekiel 26 in the IRVT2

Ezekiel 26 in the IRVU

Ezekiel 26 in the ISVN

Ezekiel 26 in the JSNT

Ezekiel 26 in the KAPI

Ezekiel 26 in the KBT1ETNIK

Ezekiel 26 in the KBV

Ezekiel 26 in the KJV

Ezekiel 26 in the KNFD

Ezekiel 26 in the LBA

Ezekiel 26 in the LBLA

Ezekiel 26 in the LNT

Ezekiel 26 in the LSV

Ezekiel 26 in the MAAL

Ezekiel 26 in the MBV

Ezekiel 26 in the MBV2

Ezekiel 26 in the MHNT

Ezekiel 26 in the MKNFD

Ezekiel 26 in the MNG

Ezekiel 26 in the MNT

Ezekiel 26 in the MNT2

Ezekiel 26 in the MRS1T

Ezekiel 26 in the NAA

Ezekiel 26 in the NASB

Ezekiel 26 in the NBLA

Ezekiel 26 in the NBS

Ezekiel 26 in the NBVTP

Ezekiel 26 in the NET2

Ezekiel 26 in the NIV11

Ezekiel 26 in the NNT

Ezekiel 26 in the NNT2

Ezekiel 26 in the NNT3

Ezekiel 26 in the PDDPT

Ezekiel 26 in the PFNT

Ezekiel 26 in the RMNT

Ezekiel 26 in the SBIAS

Ezekiel 26 in the SBIBS

Ezekiel 26 in the SBIBS2

Ezekiel 26 in the SBICS

Ezekiel 26 in the SBIDS

Ezekiel 26 in the SBIGS

Ezekiel 26 in the SBIHS

Ezekiel 26 in the SBIIS

Ezekiel 26 in the SBIIS2

Ezekiel 26 in the SBIIS3

Ezekiel 26 in the SBIKS

Ezekiel 26 in the SBIKS2

Ezekiel 26 in the SBIMS

Ezekiel 26 in the SBIOS

Ezekiel 26 in the SBIPS

Ezekiel 26 in the SBISS

Ezekiel 26 in the SBITS

Ezekiel 26 in the SBITS2

Ezekiel 26 in the SBITS3

Ezekiel 26 in the SBITS4

Ezekiel 26 in the SBIUS

Ezekiel 26 in the SBIVS

Ezekiel 26 in the SBT

Ezekiel 26 in the SBT1E

Ezekiel 26 in the SCHL

Ezekiel 26 in the SNT

Ezekiel 26 in the SUSU

Ezekiel 26 in the SUSU2

Ezekiel 26 in the SYNO

Ezekiel 26 in the TBIAOTANT

Ezekiel 26 in the TBT1E

Ezekiel 26 in the TBT1E2

Ezekiel 26 in the TFTIP

Ezekiel 26 in the TFTU

Ezekiel 26 in the TGNTATF3T

Ezekiel 26 in the THAI

Ezekiel 26 in the TNFD

Ezekiel 26 in the TNT

Ezekiel 26 in the TNTIK

Ezekiel 26 in the TNTIL

Ezekiel 26 in the TNTIN

Ezekiel 26 in the TNTIP

Ezekiel 26 in the TNTIZ

Ezekiel 26 in the TOMA

Ezekiel 26 in the TTENT

Ezekiel 26 in the UBG

Ezekiel 26 in the UGV

Ezekiel 26 in the UGV2

Ezekiel 26 in the UGV3

Ezekiel 26 in the VBL

Ezekiel 26 in the VDCC

Ezekiel 26 in the YALU

Ezekiel 26 in the YAPE

Ezekiel 26 in the YBVTP

Ezekiel 26 in the ZBP