Ezekiel 30 (BOGWICC)
1 Yehova anandiyankhula kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, nenera ndipo ulengeze zimene Ine Ambuye Yehova ndikunena.“ ‘Ufuwule mawu awa akuti,‘Kalanga, tsiku lafika!’ 3 Pakuti tsiku layandikira,tsiku la Yehova lili pafupi,tsiku la mitambo yakuda,tsiku lachiwonongeko cha mitundu ya anthu. 4 Lupanga lidzabwera kudzalimbana ndi Iguptondipo mavuto adzafika pa Kusi.Pamene anthu ambiri adzaphedwa mu Igupto,chuma chake chidzatengedwandipo maziko ake adzagumuka. 5 Kusi, Puti, Ludi ndi Arabiya yense, Libiya ndiponso anthu a mʼdziko logwirizana naye adzaphedwa ndi lupanga pamodzi ndi Igupto. 6 “ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti:“ ‘Onse othandiza Igupto adzaphedwandipo kunyadira mphamvu zake kudzatheratu.Adzaphedwa ndi lupangakuyambira ku Migidoli mpaka ku mzinda wa Asiwani,’ ”ndikutero Ine Ambuye Yehova. 7 “ ‘Dziko la Igupto lidzasanduka bwinjakupambana mabwinja ena onse opasuka,ndipo mizinda yake idzakhala yopasukakupambana mizinda ina yonse. 8 Nditatha kutentha Iguptondi kupha onse omuthandiza,pamenepo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova. 9 “ ‘Nthawi imeneyo ikadzafika, amithenga adzapita mofulumira kuchokera kwa Ine kukaopseza Kusi, iwowo osadziwako kanthu. Ndipo adzada nkhawa pa tsiku limene Igupto adzawonongedwa, chifukwa tsikulo lidzafika ndithu. 10 “ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti,“ ‘Ndidzagwiritsa ntchito Nebukadinezara, mfumu ya ku Babulonikuti ndithetse gulu lankhondo la Igupto. 11 Iye ndi gulu lake lankhondo, mtundu wa anthu ankhanza kwambiri ajaadzabwera kudzawononga dzikolo.Adzasolola malupanga awo kulimbana ndi Iguptondipo dziko lidzadzaza ndi mitembo. 12 Ndidzawumitsa mtsinje wa Nailondi kugulitsa dziko la Igupto kwa anthu oyipa.Ndidzagwiritsa ntchito anthu achilendo kuti ndiwononge dzikolopamodzi ndi zonse zili mʼmenemo.Ine Yehova ndayankhula. 13 “ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti,“ ‘Ndidzawononga mafanondi kuthetsa milungu yosema ya ku Mefisi.Simudzakhalanso mfumu mu Igupto,ndipo ndidzaopseza dziko lonse. 14 Ndidzasandutsa chipululu mzinda wa Patirosi,ndi kutentha mzinda wa Zowani.Ndidzalanga mzinda wa Thebesi. 15 Ndidzakhuthulira ukali wanga pa mzinda wa Peluziumu,linga lolimba la Igupto,ndi kuwononga gulu lankhondo la Thebesi. 16 Ndidzatentha ndi moto dziko la Igupto;Peluziumu adzazunzika ndi ululu.Malinga a Thebesi adzagumuka,ndipo mzindawo udzasefukira ndi madzi. 17 Anyamata a ku Oni ndi ku Pibesetiadzaphedwa ndi lupangandipo okhala mʼmizinda yake adzatengedwa ukapolo. 18 Ku Tehafinehezi kudzakhala mdimapamene ndidzathyola goli la Igupto;motero kunyada kwake kudzatha.Iye adzaphimbidwa ndi mitambo yakuda,ndipo okhala mʼmizinda yake adzapita ku ukapolo. 19 Kotero ndidzalanga dziko la Igupto,ndipo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’ ” 20 Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri la mwezi woyamba wa chaka chakhumi ndi chimodzi, Yehova anandiyankhula kuti: 21 “Iwe mwana wa munthu, ndathyola dzanja la Farao mfumu ya Igupto. Taona, silinamangidwe kuti lipole, ngakhale kulilimbitsa ndi nsalu kuti lithe kugwiranso lupanga. 22 Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti, Ine ndikudana ndi Farao mfumu ya Igupto. Ndidzathyola manja ake onse; dzanja labwino pamodzi ndi lothyokalo, ndipo lupanga lidzagwa mʼmanja mwake. 23 Ndidzamwaza Aigupto pakati pa mitundu ya anthu ndikuwabalalitsira ku mayiko ambiri. 24 Ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babuloni, ndipo mʼmanja mwake ndidzayikamo lupanga langa. Koma ndidzathyola manja a Farao, ndipo adzabuwula ngati wolasidwa koopsa pamaso pa mfumu ya ku Babuloniyo. 25 Ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babuloni, koma manja a Farao adzafowoka. Motero anthu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndikadzayika lupanga langa mʼmanja mwa mfumu ya ku Babuloni. Ndipo adzaligwiritsa ntchito pothira nkhondo dziko la Igupto. 26 Ndidzamwaza Aigupto pakati pa mitundu ya anthu, ndikuwabalalitsira ku mayiko ambiri. Motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”
In Other Versions
Ezekiel 30 in the ANGEFD
Ezekiel 30 in the ANTPNG2D
Ezekiel 30 in the AS21
Ezekiel 30 in the BAGH
Ezekiel 30 in the BBPNG
Ezekiel 30 in the BBT1E
Ezekiel 30 in the BDS
Ezekiel 30 in the BEV
Ezekiel 30 in the BHAD
Ezekiel 30 in the BIB
Ezekiel 30 in the BLPT
Ezekiel 30 in the BNT
Ezekiel 30 in the BNTABOOT
Ezekiel 30 in the BNTLV
Ezekiel 30 in the BOATCB
Ezekiel 30 in the BOATCB2
Ezekiel 30 in the BOBCV
Ezekiel 30 in the BOCNT
Ezekiel 30 in the BOECS
Ezekiel 30 in the BOHCB
Ezekiel 30 in the BOHCV
Ezekiel 30 in the BOHLNT
Ezekiel 30 in the BOHNTLTAL
Ezekiel 30 in the BOICB
Ezekiel 30 in the BOILNTAP
Ezekiel 30 in the BOITCV
Ezekiel 30 in the BOKCV
Ezekiel 30 in the BOKCV2
Ezekiel 30 in the BOKHWOG
Ezekiel 30 in the BOKSSV
Ezekiel 30 in the BOLCB
Ezekiel 30 in the BOLCB2
Ezekiel 30 in the BOMCV
Ezekiel 30 in the BONAV
Ezekiel 30 in the BONCB
Ezekiel 30 in the BONLT
Ezekiel 30 in the BONUT2
Ezekiel 30 in the BOPLNT
Ezekiel 30 in the BOSCB
Ezekiel 30 in the BOSNC
Ezekiel 30 in the BOTLNT
Ezekiel 30 in the BOVCB
Ezekiel 30 in the BOYCB
Ezekiel 30 in the BPBB
Ezekiel 30 in the BPH
Ezekiel 30 in the BSB
Ezekiel 30 in the CCB
Ezekiel 30 in the CUV
Ezekiel 30 in the CUVS
Ezekiel 30 in the DBT
Ezekiel 30 in the DGDNT
Ezekiel 30 in the DHNT
Ezekiel 30 in the DNT
Ezekiel 30 in the ELBE
Ezekiel 30 in the EMTV
Ezekiel 30 in the ESV
Ezekiel 30 in the FBV
Ezekiel 30 in the FEB
Ezekiel 30 in the GGMNT
Ezekiel 30 in the GNT
Ezekiel 30 in the HARY
Ezekiel 30 in the HNT
Ezekiel 30 in the IRVA
Ezekiel 30 in the IRVB
Ezekiel 30 in the IRVG
Ezekiel 30 in the IRVH
Ezekiel 30 in the IRVK
Ezekiel 30 in the IRVM
Ezekiel 30 in the IRVM2
Ezekiel 30 in the IRVO
Ezekiel 30 in the IRVP
Ezekiel 30 in the IRVT
Ezekiel 30 in the IRVT2
Ezekiel 30 in the IRVU
Ezekiel 30 in the ISVN
Ezekiel 30 in the JSNT
Ezekiel 30 in the KAPI
Ezekiel 30 in the KBT1ETNIK
Ezekiel 30 in the KBV
Ezekiel 30 in the KJV
Ezekiel 30 in the KNFD
Ezekiel 30 in the LBA
Ezekiel 30 in the LBLA
Ezekiel 30 in the LNT
Ezekiel 30 in the LSV
Ezekiel 30 in the MAAL
Ezekiel 30 in the MBV
Ezekiel 30 in the MBV2
Ezekiel 30 in the MHNT
Ezekiel 30 in the MKNFD
Ezekiel 30 in the MNG
Ezekiel 30 in the MNT
Ezekiel 30 in the MNT2
Ezekiel 30 in the MRS1T
Ezekiel 30 in the NAA
Ezekiel 30 in the NASB
Ezekiel 30 in the NBLA
Ezekiel 30 in the NBS
Ezekiel 30 in the NBVTP
Ezekiel 30 in the NET2
Ezekiel 30 in the NIV11
Ezekiel 30 in the NNT
Ezekiel 30 in the NNT2
Ezekiel 30 in the NNT3
Ezekiel 30 in the PDDPT
Ezekiel 30 in the PFNT
Ezekiel 30 in the RMNT
Ezekiel 30 in the SBIAS
Ezekiel 30 in the SBIBS
Ezekiel 30 in the SBIBS2
Ezekiel 30 in the SBICS
Ezekiel 30 in the SBIDS
Ezekiel 30 in the SBIGS
Ezekiel 30 in the SBIHS
Ezekiel 30 in the SBIIS
Ezekiel 30 in the SBIIS2
Ezekiel 30 in the SBIIS3
Ezekiel 30 in the SBIKS
Ezekiel 30 in the SBIKS2
Ezekiel 30 in the SBIMS
Ezekiel 30 in the SBIOS
Ezekiel 30 in the SBIPS
Ezekiel 30 in the SBISS
Ezekiel 30 in the SBITS
Ezekiel 30 in the SBITS2
Ezekiel 30 in the SBITS3
Ezekiel 30 in the SBITS4
Ezekiel 30 in the SBIUS
Ezekiel 30 in the SBIVS
Ezekiel 30 in the SBT
Ezekiel 30 in the SBT1E
Ezekiel 30 in the SCHL
Ezekiel 30 in the SNT
Ezekiel 30 in the SUSU
Ezekiel 30 in the SUSU2
Ezekiel 30 in the SYNO
Ezekiel 30 in the TBIAOTANT
Ezekiel 30 in the TBT1E
Ezekiel 30 in the TBT1E2
Ezekiel 30 in the TFTIP
Ezekiel 30 in the TFTU
Ezekiel 30 in the TGNTATF3T
Ezekiel 30 in the THAI
Ezekiel 30 in the TNFD
Ezekiel 30 in the TNT
Ezekiel 30 in the TNTIK
Ezekiel 30 in the TNTIL
Ezekiel 30 in the TNTIN
Ezekiel 30 in the TNTIP
Ezekiel 30 in the TNTIZ
Ezekiel 30 in the TOMA
Ezekiel 30 in the TTENT
Ezekiel 30 in the UBG
Ezekiel 30 in the UGV
Ezekiel 30 in the UGV2
Ezekiel 30 in the UGV3
Ezekiel 30 in the VBL
Ezekiel 30 in the VDCC
Ezekiel 30 in the YALU
Ezekiel 30 in the YAPE
Ezekiel 30 in the YBVTP
Ezekiel 30 in the ZBP