Isaiah 13 (BOGWICC)

1 Uthenga onena za Babuloni umene Yesaya mwana wa Amozi anawulandira: 2 Kwezani mbendera yankhondo pa phiri loti see,muwafuwulire ankhondo;muwakodole kuti adzalowe pa zipataza anthu olemekezeka. 3 Ine Yehova, ndalamulira ankhondo anga;ndasonkhanitsa ankhondo anga kuti akhale zida zanga zolangiraamene amadzikuza ndi chipambano changa. 4 Tamvani phokoso ku mapiri,likumveka ngati phokoso la gulu lalikulu la anthu!Tamvani phokoso pakati pa maufumu,ngati kuti mitundu ya anthu ikusonkhana pamodzi!Yehova Wamphamvuzonse akukhazika asilikali ake mokonzekerakuchita nkhondo. 5 Iwo akuchokera ku mayiko akutali,kuchokera kumalekezero a dzikoYehova ali ndi zida zake za nkhondokuti adzawononge dziko la Babuloni. 6 Lirani mofuwula, pakuti tsiku la Yehova layandikira;lidzabwera ngati chiwonongeko chochokera kwa Wamphamvuzonse. 7 Zimenezi zinafowoketsa manja onse,mtima wa munthu aliyense udzachokamo. 8 Anthu adzagwidwa ndi mantha aakulu,zowawa ndi masautso zidzawagwera;adzamva zowawa zonga amamva mayi pobereka.Adzayangʼanana mwamantha,nkhope zawo zikufiira ngati malawi amoto. 9 Taonani, tsiku la Yehova likubwera,tsiku lopanda chisoni, lawukali ndi lamkwiyo;kudzasandutsa dziko kuti likhale chipululundi kuwononga anthu ochimwa a mʼmenemo. 10 Nyenyezi zakumwamba ndiponso zonse zamlengalengasizidzaonetsa kuwala kwawo.Dzuwa lidzada potuluka,ndipo mwezi sudzawala konse. 11 Ndidzalanga dziko lonse chifukwa cha zolakwa zake,anthu oyipa ndidzawalanga chifukwa cha machimo awo.Ndidzathetsa kunyada kwa odzikuza,ndipo ndidzatsitsa kudzitukumula kwa anthu ankhanza. 12 Ndidzasandutsa anthu kukhala ovuta kupeza kuposa mmene amasowera golide wabwino.Iwo sazidzapezekapezeka kuposa mmene amasowera golide wa ku Ofiri. 13 Tsono ndidzagwedeza miyambandipo dziko lapansi lidzachoka pa maziko ake.Izi zidzachitika chifukwa cha ukali wa Wamphamvuzonsepa tsiku la mkwiyo wake woopsa. 14 Ngati mbawala zosakidwa,ngati nkhosa zopanda wozikusa,munthu aliyense adzabwerera kwa anthu akwawo,aliyense adzathawira ku dziko lake. 15 Aliyense amene atadzapezeke ndi kugwidwaadzaphedwa momubaya ndi lupanga. 16 Ana awo akhanda adzaphwanyidwa iwo akuona;nyumba zawo zidzafunkhidwa ndipo akazi awo adzagwiriridwa. 17 Taona, Ine ndidzadzutsa Amedi amene safuna silivandipo sasangalatsidwa ndi golide,kuti amenyane ndi Ababuloni. 18 Adzapha anyamata ndi mauta awo;sadzachitira chifundo anangakhale kumvera chisoni ana akhanda. 19 Babuloni, ufumu wake ndi waulemerero kuposa mafumu onse.Anthu ake amawunyadira.Koma Yehova adzawuwonongangati mmene anawonongera Sodomu ndi Gomora. 20 Anthu sadzakhalamonsokapena kukhazikikamo pa mibado yonse;palibe Mwarabu amene adzayimike tenti yake,palibe mʼbusa amene adzawetamo ziweto zake. 21 Koma nyama zakuthengo ndizo zidzakhale kumeneko,nyumba zake zidzadzaza ndi nkhandwe;mu mzindamo muzidzakhala akadzidzi,ndipo atonde akuthengo azidzalumphalumphamo. 22 Mu nsanja zake muzidzalira afisi,mʼnyumba zake zokongola muzidzalira nkhandwe.Nthawi yake yayandikirandipo masiku ake ali pafupi kutha.

In Other Versions

Isaiah 13 in the ANGEFD

Isaiah 13 in the ANTPNG2D

Isaiah 13 in the AS21

Isaiah 13 in the BAGH

Isaiah 13 in the BBPNG

Isaiah 13 in the BBT1E

Isaiah 13 in the BDS

Isaiah 13 in the BEV

Isaiah 13 in the BHAD

Isaiah 13 in the BIB

Isaiah 13 in the BLPT

Isaiah 13 in the BNT

Isaiah 13 in the BNTABOOT

Isaiah 13 in the BNTLV

Isaiah 13 in the BOATCB

Isaiah 13 in the BOATCB2

Isaiah 13 in the BOBCV

Isaiah 13 in the BOCNT

Isaiah 13 in the BOECS

Isaiah 13 in the BOHCB

Isaiah 13 in the BOHCV

Isaiah 13 in the BOHLNT

Isaiah 13 in the BOHNTLTAL

Isaiah 13 in the BOICB

Isaiah 13 in the BOILNTAP

Isaiah 13 in the BOITCV

Isaiah 13 in the BOKCV

Isaiah 13 in the BOKCV2

Isaiah 13 in the BOKHWOG

Isaiah 13 in the BOKSSV

Isaiah 13 in the BOLCB

Isaiah 13 in the BOLCB2

Isaiah 13 in the BOMCV

Isaiah 13 in the BONAV

Isaiah 13 in the BONCB

Isaiah 13 in the BONLT

Isaiah 13 in the BONUT2

Isaiah 13 in the BOPLNT

Isaiah 13 in the BOSCB

Isaiah 13 in the BOSNC

Isaiah 13 in the BOTLNT

Isaiah 13 in the BOVCB

Isaiah 13 in the BOYCB

Isaiah 13 in the BPBB

Isaiah 13 in the BPH

Isaiah 13 in the BSB

Isaiah 13 in the CCB

Isaiah 13 in the CUV

Isaiah 13 in the CUVS

Isaiah 13 in the DBT

Isaiah 13 in the DGDNT

Isaiah 13 in the DHNT

Isaiah 13 in the DNT

Isaiah 13 in the ELBE

Isaiah 13 in the EMTV

Isaiah 13 in the ESV

Isaiah 13 in the FBV

Isaiah 13 in the FEB

Isaiah 13 in the GGMNT

Isaiah 13 in the GNT

Isaiah 13 in the HARY

Isaiah 13 in the HNT

Isaiah 13 in the IRVA

Isaiah 13 in the IRVB

Isaiah 13 in the IRVG

Isaiah 13 in the IRVH

Isaiah 13 in the IRVK

Isaiah 13 in the IRVM

Isaiah 13 in the IRVM2

Isaiah 13 in the IRVO

Isaiah 13 in the IRVP

Isaiah 13 in the IRVT

Isaiah 13 in the IRVT2

Isaiah 13 in the IRVU

Isaiah 13 in the ISVN

Isaiah 13 in the JSNT

Isaiah 13 in the KAPI

Isaiah 13 in the KBT1ETNIK

Isaiah 13 in the KBV

Isaiah 13 in the KJV

Isaiah 13 in the KNFD

Isaiah 13 in the LBA

Isaiah 13 in the LBLA

Isaiah 13 in the LNT

Isaiah 13 in the LSV

Isaiah 13 in the MAAL

Isaiah 13 in the MBV

Isaiah 13 in the MBV2

Isaiah 13 in the MHNT

Isaiah 13 in the MKNFD

Isaiah 13 in the MNG

Isaiah 13 in the MNT

Isaiah 13 in the MNT2

Isaiah 13 in the MRS1T

Isaiah 13 in the NAA

Isaiah 13 in the NASB

Isaiah 13 in the NBLA

Isaiah 13 in the NBS

Isaiah 13 in the NBVTP

Isaiah 13 in the NET2

Isaiah 13 in the NIV11

Isaiah 13 in the NNT

Isaiah 13 in the NNT2

Isaiah 13 in the NNT3

Isaiah 13 in the PDDPT

Isaiah 13 in the PFNT

Isaiah 13 in the RMNT

Isaiah 13 in the SBIAS

Isaiah 13 in the SBIBS

Isaiah 13 in the SBIBS2

Isaiah 13 in the SBICS

Isaiah 13 in the SBIDS

Isaiah 13 in the SBIGS

Isaiah 13 in the SBIHS

Isaiah 13 in the SBIIS

Isaiah 13 in the SBIIS2

Isaiah 13 in the SBIIS3

Isaiah 13 in the SBIKS

Isaiah 13 in the SBIKS2

Isaiah 13 in the SBIMS

Isaiah 13 in the SBIOS

Isaiah 13 in the SBIPS

Isaiah 13 in the SBISS

Isaiah 13 in the SBITS

Isaiah 13 in the SBITS2

Isaiah 13 in the SBITS3

Isaiah 13 in the SBITS4

Isaiah 13 in the SBIUS

Isaiah 13 in the SBIVS

Isaiah 13 in the SBT

Isaiah 13 in the SBT1E

Isaiah 13 in the SCHL

Isaiah 13 in the SNT

Isaiah 13 in the SUSU

Isaiah 13 in the SUSU2

Isaiah 13 in the SYNO

Isaiah 13 in the TBIAOTANT

Isaiah 13 in the TBT1E

Isaiah 13 in the TBT1E2

Isaiah 13 in the TFTIP

Isaiah 13 in the TFTU

Isaiah 13 in the TGNTATF3T

Isaiah 13 in the THAI

Isaiah 13 in the TNFD

Isaiah 13 in the TNT

Isaiah 13 in the TNTIK

Isaiah 13 in the TNTIL

Isaiah 13 in the TNTIN

Isaiah 13 in the TNTIP

Isaiah 13 in the TNTIZ

Isaiah 13 in the TOMA

Isaiah 13 in the TTENT

Isaiah 13 in the UBG

Isaiah 13 in the UGV

Isaiah 13 in the UGV2

Isaiah 13 in the UGV3

Isaiah 13 in the VBL

Isaiah 13 in the VDCC

Isaiah 13 in the YALU

Isaiah 13 in the YAPE

Isaiah 13 in the YBVTP

Isaiah 13 in the ZBP