Isaiah 24 (BOGWICC)
1 Taonani, Yehova adzawononga dziko lapansindi kulisandutsa chipululu;Iye adzasakaza maonekedwe akendi kumwaza anthu ake onse. 2 Aliyense zidzamuchitikira mofanana:wansembe chimodzimodzi munthu wamba,antchito aamuna mofanananso ndi ambuye awo aamuna,antchito aakazi chimodzimodzi ambuye awo aakazi,wogula chimodzimodzi wogulitsa,wobwereka chimodzimodzi wobwereketsa,okongola chimodzimodzi okongoza. 3 Dziko lapansi lidzawonongedwa kwathunthundi kusakazikiratu.Yehova wanena mawu awa. 4 Dziko lapansi likulira ndipo likufota,dziko lonse likuvutika ndipo likuwuma,anthu omveka a dziko lapansi akuvutika. 5 Anthu ayipitsa dziko lapansi;posamvera malangizo ake;pophwanya mawu akendi pangano lake lamuyaya. 6 Nʼchifukwa chake matemberero akuwononga dziko lapansi;anthu a mʼdzikomo akuzunzika chifukwa cha kulakwa kwawo,iwo asakazikandipo atsala ochepa okha. 7 Vinyo watsopano watha ndipo mphesa zikufota;onse okonda zosangalatsa ali ndi chisoni. 8 Kulira kokometsera kwa matambolini kwatha,phokoso la anthu osangalala latha,zeze wosangalatsa wati zii. 9 Anthu sadzayimbanso akumwa vinyo;akadzamwa zaukali zidzakhala zowawa mʼkamwa mwawo. 10 Mzinda wachisokonezo uja wawonongeka;nyumba iliyonse yatsekedwa. 11 Anthu akulira mʼmisewu kufuna vinyo;chimwemwe chonse chatheratu,palibenso chisangalalo pa dziko lapansi. 12 Mzinda wasanduka bwinjazipata zake zagumuka. 13 Zimenezi ndizo zidzachitikire mitundu yonse ya dziko lapansindiponso pakati pa mitundu ya anthu.Zidzakhala ngati pamene mitengo ya olivi yayoyoledwa,kapena ngati nthawi ya kunkha la mphesa atatsiriza kukolola. 14 Koma otsala onse akufuwula ndi kuyimba mwachimwemwe;anthu akumadzulo akutamanda ukulu wa Yehova. 15 Nʼchifukwa chake inu akummawa, tamandani Yehova;ndi inu okhala mʼmphepete mwa nyanja kwezani dzina la Yehova, Mulungu wa Israeli. 16 Kuchokera kumalekezero a dziko lapansi tikumva kuyimba kotamanda“Wolungamayo.” Koma ine ndinati, “Ndatheratu, ndatheratu!Tsoka kwa ine!Anthu achinyengo akupitirizabe kuchita zachinyengo,inde chinyengo chawo chikunkerankera mʼtsogolo.” 17 Inu anthu adziko lapansi, zoopsa, dzenjendi msampha zikukudikirani. 18 Aliyense wothawa phokoso la zoopsaadzagwa mʼdzenje;ndipo aliyense wotuluka mʼdzenjemoadzakodwa ndi msampha. Zitseko zakumwamba zatsekulidwa,ndipo maziko a dziko lapansi agwedezeka. 19 Dziko lapansi lathyokathyoka,ndipo lagawika pakati,dziko lapansi lagwedezeka kotheratu. 20 Dziko lapansi likudzandira ngati munthu woledzeralikugwedezeka ndi mphepo ngati chisimba;lalemedwa ndi machimo ake.Lidzagwa ndipo silidzadzukanso. 21 Tsiku limenelo Yehova adzalangaamphamvu a kumwambandiponso mafumu apansi pano. 22 Mulungu adzawasonkhanitsa pamodzingati amʼndende amene ali mʼdzenje.Adzawatsekera mʼndendendipo adzalangidwa patapita nthawi yayitali. 23 Mwezi udzanyazitsidwa, dzuwa lidzachita manyazi;pakuti Yehova Wamphamvuzonse adzakhala mfumu ndipo adzalamulira;pa Phiri la Ziyoni ndi ku Yerusalemu,ndipo adzaonetsa ulemerero wake pamaso pa akuluakulu.
In Other Versions
Isaiah 24 in the ANGEFD
Isaiah 24 in the ANTPNG2D
Isaiah 24 in the AS21
Isaiah 24 in the BAGH
Isaiah 24 in the BBPNG
Isaiah 24 in the BBT1E
Isaiah 24 in the BDS
Isaiah 24 in the BEV
Isaiah 24 in the BHAD
Isaiah 24 in the BIB
Isaiah 24 in the BLPT
Isaiah 24 in the BNT
Isaiah 24 in the BNTABOOT
Isaiah 24 in the BNTLV
Isaiah 24 in the BOATCB
Isaiah 24 in the BOATCB2
Isaiah 24 in the BOBCV
Isaiah 24 in the BOCNT
Isaiah 24 in the BOECS
Isaiah 24 in the BOHCB
Isaiah 24 in the BOHCV
Isaiah 24 in the BOHLNT
Isaiah 24 in the BOHNTLTAL
Isaiah 24 in the BOICB
Isaiah 24 in the BOILNTAP
Isaiah 24 in the BOITCV
Isaiah 24 in the BOKCV
Isaiah 24 in the BOKCV2
Isaiah 24 in the BOKHWOG
Isaiah 24 in the BOKSSV
Isaiah 24 in the BOLCB
Isaiah 24 in the BOLCB2
Isaiah 24 in the BOMCV
Isaiah 24 in the BONAV
Isaiah 24 in the BONCB
Isaiah 24 in the BONLT
Isaiah 24 in the BONUT2
Isaiah 24 in the BOPLNT
Isaiah 24 in the BOSCB
Isaiah 24 in the BOSNC
Isaiah 24 in the BOTLNT
Isaiah 24 in the BOVCB
Isaiah 24 in the BOYCB
Isaiah 24 in the BPBB
Isaiah 24 in the BPH
Isaiah 24 in the BSB
Isaiah 24 in the CCB
Isaiah 24 in the CUV
Isaiah 24 in the CUVS
Isaiah 24 in the DBT
Isaiah 24 in the DGDNT
Isaiah 24 in the DHNT
Isaiah 24 in the DNT
Isaiah 24 in the ELBE
Isaiah 24 in the EMTV
Isaiah 24 in the ESV
Isaiah 24 in the FBV
Isaiah 24 in the FEB
Isaiah 24 in the GGMNT
Isaiah 24 in the GNT
Isaiah 24 in the HARY
Isaiah 24 in the HNT
Isaiah 24 in the IRVA
Isaiah 24 in the IRVB
Isaiah 24 in the IRVG
Isaiah 24 in the IRVH
Isaiah 24 in the IRVK
Isaiah 24 in the IRVM
Isaiah 24 in the IRVM2
Isaiah 24 in the IRVO
Isaiah 24 in the IRVP
Isaiah 24 in the IRVT
Isaiah 24 in the IRVT2
Isaiah 24 in the IRVU
Isaiah 24 in the ISVN
Isaiah 24 in the JSNT
Isaiah 24 in the KAPI
Isaiah 24 in the KBT1ETNIK
Isaiah 24 in the KBV
Isaiah 24 in the KJV
Isaiah 24 in the KNFD
Isaiah 24 in the LBA
Isaiah 24 in the LBLA
Isaiah 24 in the LNT
Isaiah 24 in the LSV
Isaiah 24 in the MAAL
Isaiah 24 in the MBV
Isaiah 24 in the MBV2
Isaiah 24 in the MHNT
Isaiah 24 in the MKNFD
Isaiah 24 in the MNG
Isaiah 24 in the MNT
Isaiah 24 in the MNT2
Isaiah 24 in the MRS1T
Isaiah 24 in the NAA
Isaiah 24 in the NASB
Isaiah 24 in the NBLA
Isaiah 24 in the NBS
Isaiah 24 in the NBVTP
Isaiah 24 in the NET2
Isaiah 24 in the NIV11
Isaiah 24 in the NNT
Isaiah 24 in the NNT2
Isaiah 24 in the NNT3
Isaiah 24 in the PDDPT
Isaiah 24 in the PFNT
Isaiah 24 in the RMNT
Isaiah 24 in the SBIAS
Isaiah 24 in the SBIBS
Isaiah 24 in the SBIBS2
Isaiah 24 in the SBICS
Isaiah 24 in the SBIDS
Isaiah 24 in the SBIGS
Isaiah 24 in the SBIHS
Isaiah 24 in the SBIIS
Isaiah 24 in the SBIIS2
Isaiah 24 in the SBIIS3
Isaiah 24 in the SBIKS
Isaiah 24 in the SBIKS2
Isaiah 24 in the SBIMS
Isaiah 24 in the SBIOS
Isaiah 24 in the SBIPS
Isaiah 24 in the SBISS
Isaiah 24 in the SBITS
Isaiah 24 in the SBITS2
Isaiah 24 in the SBITS3
Isaiah 24 in the SBITS4
Isaiah 24 in the SBIUS
Isaiah 24 in the SBIVS
Isaiah 24 in the SBT
Isaiah 24 in the SBT1E
Isaiah 24 in the SCHL
Isaiah 24 in the SNT
Isaiah 24 in the SUSU
Isaiah 24 in the SUSU2
Isaiah 24 in the SYNO
Isaiah 24 in the TBIAOTANT
Isaiah 24 in the TBT1E
Isaiah 24 in the TBT1E2
Isaiah 24 in the TFTIP
Isaiah 24 in the TFTU
Isaiah 24 in the TGNTATF3T
Isaiah 24 in the THAI
Isaiah 24 in the TNFD
Isaiah 24 in the TNT
Isaiah 24 in the TNTIK
Isaiah 24 in the TNTIL
Isaiah 24 in the TNTIN
Isaiah 24 in the TNTIP
Isaiah 24 in the TNTIZ
Isaiah 24 in the TOMA
Isaiah 24 in the TTENT
Isaiah 24 in the UBG
Isaiah 24 in the UGV
Isaiah 24 in the UGV2
Isaiah 24 in the UGV3
Isaiah 24 in the VBL
Isaiah 24 in the VDCC
Isaiah 24 in the YALU
Isaiah 24 in the YAPE
Isaiah 24 in the YBVTP
Isaiah 24 in the ZBP