Isaiah 42 (BOGWICC)
1 “Nayu mtumiki wanga, amene ndimamuchirikiza,amene ndamusankha, amenenso ndimakondwera naye.Ndayika Mzimu wanga mwa Iyeyo,ndipo adzaweruza anthu a mitundu yonse mwachilungamo. 2 Iye sadzafuwula, sadzamveka mawu,kapena mawu ake kumveka mʼmisewu. 3 Bango lophwanyika sadzalithyola,ndipo moto wozilala sadzawuzimitsa.Motero adzaonetsa kuti chilungamo ndicho choonadi; 4 sadzafowoka kapena kukhumudwampaka atakhazikitsa chilungamo pa dziko lapansi,ndi mpaka mayiko a mʼmbali mwa nyanja atafika poyembekezera malangizo ake.” 5 Yehova Mulunguamene analenga zamlengalenga ndi kuziyalika,amene analenga dziko lapansi ndi zonse zimene zimabereka,amenenso amapereka mpweya kwa anthu ake okhala mʼdzikomo,ndi moyo kwa onse oyendamo, akuti, 6 “Ine Yehova, ndakuyitana chifukwa Ine ndine wolungama;ndikugwira dzanja ndipondidzakuteteza.Ndakupereka kukhala pangano langa kwa anthundi kuwunika kwa anthu a mitundu ina. 7 Udzatsekula maso a anthu osaona,udzamasula anthu a mʼndendendi kutulutsa mʼndende anthu okhala mu mdima. 8 “Ine ndine Yehova: dzina langa ndi limenelo!Sindidzapereka ulemerero wanga kwa wina aliyensekapena matamando anga kwa mafano. 9 Taonani, zinthu zimene ndinalosera kale zachitikadi,ndipo ndikuwuzani zinthu zatsopano;zinthuzo zisanaonekereIne ndakudziwitsani.” 10 Imbirani Yehova nyimbo yatsopano,mutamandeni inu okhala mʼdziko lonse lapansi,inu amene mumayenda pa nyanja, nyanja ikokome ndi zonse zili mʼmenemo.Inu okhala pa zilumba tamandani Yehova. 11 Chipululu ndi mizinda yake zikweze mawu awo;midzi ya Akedara ikondwere.Anthu a ku Sela ayimbe mwachimwemwe;afuwule kuchokera pamwamba pa mapiri. 12 Atamande Yehovandipo alalike matamando ake kwa anthu apazilumba zonse. 13 Yehova adzapita ku nkhondo ngati munthu wamphamvu,adzawutsa ukali wake ngati munthu wankhondo;akukuwa ndiponso akufuwula mfuwu wankhondondipo adzagonjetsa adani ake. 14 Yehova akuti, “Ndakhala ndili chete kwa nthawi yayitali,ndakhala ndili phee osachita kanthu.Koma tsopano, ngati mayi pa nthawi yochira,ndi kubuwula ndi kupuma modukizadukiza ndipo ndili wefuwefu. 15 Ndidzawononga mapiri ndi zitundandipo ndidzawumitsa zomera zawo zonse;ndidzasandutsa mitsinje kukhala zilumbandipo ndidzawumitsa maiwe. 16 Ndidzatsogolera anthu osaona mʼmisewu imene sanayidziwe,ndidzawatsogolera mʼnjira zimene sanayendepo;ndidzasandutsa mdima wa kutsogolo kwawo kuti ukhale kuwalandipo ndidzasalaza malo osalala.Zimenezi ndizo ndidzachite;sindidzawataya. 17 Koma onse amene amadalira mafanoamene amanena kwa mafanowo kuti, ‘ndinu milungu yathu,’ndidzawachititsa manyazi kotheratu. 18 “Imvani, agonthi inu;yangʼanani osaona inu, kuti muone! 19 Ali wosaona ndani, si mtumiki wanga kodi?Ndipo ndani ali wosamva ngati mthenga amene ndamutuma?Kodi ndani ali wosaona ngati uja ndinachita naye pangano,kapena wosaona ndani ngati mtumiki wa Yehova? 20 Iwe waona zinthu zambiri, koma sunazisamale;makutu ako ndi otsekuka koma sumva kanthu.” 21 Chinamukomera Yehovachifukwa cha chilungamo chake,kapena lamulo lake kukhala lalikulu ndi lopambana. 22 Koma awa ndi anthu amene afunkhidwa ndi kuwalanda zinthu zawo,onsewa anawakola mʼmaenjekapena akuwabisa mʼndende.Tsono asanduka chofunkhapopanda wina wowapulumutsakapena kunena kuti,“Abwezeni kwawo.” 23 Kodi ndani wa inu amene adzamvetsera zimenezikapena kutchera khutu ndi kumva za mʼtsogolomo? 24 Ndani anapereka Yakobo kwa ofunkha,ndi Israeli kwa anthu akuba?Kodi si Yehova,amene ife tamuchimwirayu?Pakuti sanathe kutsatira njira zake;ndipo sanamvere malangizo ake. 25 Motero anawakwiyira kwambiri,nawavutitsa ndi nkhondo.Anayatsa moto ponseponse mowazungulira komabe iwo sanamvetse;motowo unawapsereza, koma iwo sanatengepo phunziro ayi.