Jeremiah 20 (BOGWICC)
1 Wansembe Pasuri mwana wa Imeri, woyangʼanira wamkulu wa Nyumba ya Yehova, anamva Yeremiya akulosera zinthu zimenezi. 2 Tsono iye analamula kuti mneneri Yeremiyayo amenyedwe ndi kuyikidwa mʼndende pa Chipata chakumtunda kwa Benjamini ku Nyumba ya Yehova. 3 Mmawa mwake, Pasuri anatulutsa Yeremiya mʼndende, ndipo Yeremiyayo anamuwuza kuti, “Pasuri, Yehova sadzakutchulanso dzina lako kuti Pasuri koma Zoopsa pa Mbali Zonse. 4 Pakuti Yehova akuti, ‘Ndidzakusandutsa choopsa kwa mwiniwakewe ndi kwa abwenzi ako onse; iweyo ukuona. Anthu a ku Yuda ndidzawapereka onse mʼmanja mwa mfumu ya ku Babuloni. Ena adzatengedwa ukapolo ku Babuloni ndipo ena adzaphedwa pa nkhondo. 5 Ndidzapereka kwa adani awo chuma chonse cha mu mzinda uno, phindu lonse la ntchito yake, zinthu zake zonse za mtengowapatali ndiponso katundu yense wa mafumu a ku Yuda. Iwo adzazitenga monga zinthu zolanda ku nkhondo ndi kupita nazo ku Babuloni. 6 Ndipo iwe, Pasuri, pamodzi ndi onse a pa banja pako mudzapita ku ukapolo ku Babuloni. Mudzafera kumeneko ndi kuyikidwa mʼmanda, iweyo pamodzi ndi abwenzi ako amene unawalosera zabodza.’ ” 7 Inu Yehova, mwandinamiza, ndipo ndinapusadi;Inu ndi wamphamvu kuposa ine ndipo munandipambana.Anthu akundinyoza tsiku lonse.Aliyense akundiseka kosalekeza. 8 Nthawi iliyonse ndikamayankhula,ndimafuwula kunena kuti, ziwawa kuno! Tikuwonongeka!Mawu anu Yehova andisandutsa chinthu chonyozekandipo ndimachitidwa chipongwe tsiku lonse. 9 Koma ndikanena kuti, “Sindidzalalikiranso za Iyekapena kuyankhulanso mʼdzina lake,”mawu anu amayaka ngati moto mu mtima mwanga,amakhaladi ngati moto wotsekeredwa mʼmafupa anga.Ndapirira kusunga mawu anu mu mtima mwanga osawatulutsa,koma sindingathe kupirirabe. 10 Ndimamva anthu ambiri akunongʼona kuti,“Zoopsa ku mbali zonse!Kamunenezeni! Tiyeni tikamuneneze!”Onse amene anali abwenzi angaakuyembekezera kuti ndigwa pansi, akumanena kuti,“Mwina mwake adzanyengedwa;tidzamugwirandi kulipsira pa iye.” 11 Koma Yehova ali nane, ndiye wankhondo wamphamvu.Nʼchifukwa chake ondizunza adzalephera ndipo sadzandipambana.Adzachita manyazi kwambiri chifukwa sadzapambana.Manyazi awo sadzayiwalika konse. 12 Inu Yehova Wamphamvuzonse, Inu amene mumayesa anthu molungamandipo mupenya za mu mtima mwa munthu.Ndiloleni kuti ndione kuti mwalipsira adani angapopeza ndapereka mlandu wanga kwa Inu. 13 Imbirani Yehova!Mutamandeni Yehova!Iye amapulumutsa wosaukamʼmanja mwa anthu oyipa. 14 Litembereredwe tsiku limene ndinabadwa!Tsiku limene amayi anga anandibereka lisatamandidwe! 15 Wotembereredwa munthu amene anapita kukasangalatsa abambo angandi uthenga woti:“Kwabadwa mwana wamwamuna!” 16 Munthu ameneyo akhale ngati mizinda imeneYehova anayiwononga mopanda chisoni.Amve mfuwu mmawa,phokoso la nkhondo masana. 17 Chifukwa sanandiphere mʼmimba,kuti amayi anga asanduke manda anga,mimba yawo ikhale yayikulu mpaka kalekale. 18 Kodi ndinabadwira mavuto ndi chisonikuti moyo wangaukhale wamanyazi wokhawokha?
In Other Versions
Jeremiah 20 in the ANGEFD
Jeremiah 20 in the ANTPNG2D
Jeremiah 20 in the AS21
Jeremiah 20 in the BAGH
Jeremiah 20 in the BBPNG
Jeremiah 20 in the BBT1E
Jeremiah 20 in the BDS
Jeremiah 20 in the BEV
Jeremiah 20 in the BHAD
Jeremiah 20 in the BIB
Jeremiah 20 in the BLPT
Jeremiah 20 in the BNT
Jeremiah 20 in the BNTABOOT
Jeremiah 20 in the BNTLV
Jeremiah 20 in the BOATCB
Jeremiah 20 in the BOATCB2
Jeremiah 20 in the BOBCV
Jeremiah 20 in the BOCNT
Jeremiah 20 in the BOECS
Jeremiah 20 in the BOHCB
Jeremiah 20 in the BOHCV
Jeremiah 20 in the BOHLNT
Jeremiah 20 in the BOHNTLTAL
Jeremiah 20 in the BOICB
Jeremiah 20 in the BOILNTAP
Jeremiah 20 in the BOITCV
Jeremiah 20 in the BOKCV
Jeremiah 20 in the BOKCV2
Jeremiah 20 in the BOKHWOG
Jeremiah 20 in the BOKSSV
Jeremiah 20 in the BOLCB
Jeremiah 20 in the BOLCB2
Jeremiah 20 in the BOMCV
Jeremiah 20 in the BONAV
Jeremiah 20 in the BONCB
Jeremiah 20 in the BONLT
Jeremiah 20 in the BONUT2
Jeremiah 20 in the BOPLNT
Jeremiah 20 in the BOSCB
Jeremiah 20 in the BOSNC
Jeremiah 20 in the BOTLNT
Jeremiah 20 in the BOVCB
Jeremiah 20 in the BOYCB
Jeremiah 20 in the BPBB
Jeremiah 20 in the BPH
Jeremiah 20 in the BSB
Jeremiah 20 in the CCB
Jeremiah 20 in the CUV
Jeremiah 20 in the CUVS
Jeremiah 20 in the DBT
Jeremiah 20 in the DGDNT
Jeremiah 20 in the DHNT
Jeremiah 20 in the DNT
Jeremiah 20 in the ELBE
Jeremiah 20 in the EMTV
Jeremiah 20 in the ESV
Jeremiah 20 in the FBV
Jeremiah 20 in the FEB
Jeremiah 20 in the GGMNT
Jeremiah 20 in the GNT
Jeremiah 20 in the HARY
Jeremiah 20 in the HNT
Jeremiah 20 in the IRVA
Jeremiah 20 in the IRVB
Jeremiah 20 in the IRVG
Jeremiah 20 in the IRVH
Jeremiah 20 in the IRVK
Jeremiah 20 in the IRVM
Jeremiah 20 in the IRVM2
Jeremiah 20 in the IRVO
Jeremiah 20 in the IRVP
Jeremiah 20 in the IRVT
Jeremiah 20 in the IRVT2
Jeremiah 20 in the IRVU
Jeremiah 20 in the ISVN
Jeremiah 20 in the JSNT
Jeremiah 20 in the KAPI
Jeremiah 20 in the KBT1ETNIK
Jeremiah 20 in the KBV
Jeremiah 20 in the KJV
Jeremiah 20 in the KNFD
Jeremiah 20 in the LBA
Jeremiah 20 in the LBLA
Jeremiah 20 in the LNT
Jeremiah 20 in the LSV
Jeremiah 20 in the MAAL
Jeremiah 20 in the MBV
Jeremiah 20 in the MBV2
Jeremiah 20 in the MHNT
Jeremiah 20 in the MKNFD
Jeremiah 20 in the MNG
Jeremiah 20 in the MNT
Jeremiah 20 in the MNT2
Jeremiah 20 in the MRS1T
Jeremiah 20 in the NAA
Jeremiah 20 in the NASB
Jeremiah 20 in the NBLA
Jeremiah 20 in the NBS
Jeremiah 20 in the NBVTP
Jeremiah 20 in the NET2
Jeremiah 20 in the NIV11
Jeremiah 20 in the NNT
Jeremiah 20 in the NNT2
Jeremiah 20 in the NNT3
Jeremiah 20 in the PDDPT
Jeremiah 20 in the PFNT
Jeremiah 20 in the RMNT
Jeremiah 20 in the SBIAS
Jeremiah 20 in the SBIBS
Jeremiah 20 in the SBIBS2
Jeremiah 20 in the SBICS
Jeremiah 20 in the SBIDS
Jeremiah 20 in the SBIGS
Jeremiah 20 in the SBIHS
Jeremiah 20 in the SBIIS
Jeremiah 20 in the SBIIS2
Jeremiah 20 in the SBIIS3
Jeremiah 20 in the SBIKS
Jeremiah 20 in the SBIKS2
Jeremiah 20 in the SBIMS
Jeremiah 20 in the SBIOS
Jeremiah 20 in the SBIPS
Jeremiah 20 in the SBISS
Jeremiah 20 in the SBITS
Jeremiah 20 in the SBITS2
Jeremiah 20 in the SBITS3
Jeremiah 20 in the SBITS4
Jeremiah 20 in the SBIUS
Jeremiah 20 in the SBIVS
Jeremiah 20 in the SBT
Jeremiah 20 in the SBT1E
Jeremiah 20 in the SCHL
Jeremiah 20 in the SNT
Jeremiah 20 in the SUSU
Jeremiah 20 in the SUSU2
Jeremiah 20 in the SYNO
Jeremiah 20 in the TBIAOTANT
Jeremiah 20 in the TBT1E
Jeremiah 20 in the TBT1E2
Jeremiah 20 in the TFTIP
Jeremiah 20 in the TFTU
Jeremiah 20 in the TGNTATF3T
Jeremiah 20 in the THAI
Jeremiah 20 in the TNFD
Jeremiah 20 in the TNT
Jeremiah 20 in the TNTIK
Jeremiah 20 in the TNTIL
Jeremiah 20 in the TNTIN
Jeremiah 20 in the TNTIP
Jeremiah 20 in the TNTIZ
Jeremiah 20 in the TOMA
Jeremiah 20 in the TTENT
Jeremiah 20 in the UBG
Jeremiah 20 in the UGV
Jeremiah 20 in the UGV2
Jeremiah 20 in the UGV3
Jeremiah 20 in the VBL
Jeremiah 20 in the VDCC
Jeremiah 20 in the YALU
Jeremiah 20 in the YAPE
Jeremiah 20 in the YBVTP
Jeremiah 20 in the ZBP