John 12 (BOGWICC)

1 Masiku asanu ndi limodzi Paska asanafike, Yesu anafika ku Betaniya, kumene kumakhala Lazaro, amene Yesu anamuukitsa kwa akufa. 2 Kumeneko anamukonzera Yesu chakudya cha madzulo. Marita anatumikira pamene Lazaro anali mmodzi wa iwo amene anakhala nawo pa chakudyacho. 3 Kenaka Mariya anatenga botolo la mafuta a nadi, onunkhira bwino kwambiri, amtengowapatali; Iye anadzoza mapazi a Yesu napukuta ndi tsitsi lake. Ndipo nyumba yonse inadzaza ndi fungo lonunkhira bwino la mafutawo. 4 Koma mmodzi wa ophunzira ake, Yudasi Isikarioti, amene pambuyo pake adzamupereka anati, 5 “Nʼchifukwa chiyani mafuta awa sanagulitsidwe ndipo ndalama zake nʼkuzipereka kwa osauka?” Mafutawo anali a mtengo wa malipiro a chaka chimodzi. 6 Iye sananene izi chifukwa cha kuganizira osauka koma chifukwa anali mbava; ngati wosunga thumba la ndalama, amabamo zomwe ankayikamo. 7 Yesu anayankha kuti, “Mulekeni. Mafutawa anayenera kusungidwa mpaka tsiku loyika maliro anga. 8 Inu mudzakhala ndi osauka nthawi zonse, koma simudzakhala nane nthawi zonse.” 9 Pa nthawi imeneyi gulu lalikulu la Ayuda linadziwa kuti Yesu anali kumeneko, ndipo linabwera, sichifukwa cha Iye yekha koma kudzaonanso Lazaro, amene anamuukitsa kwa akufa. 10 Choncho akulu a ansembe anakonza njira yoti aphenso Lazaro, 11 pakuti chifukwa cha iye Ayuda ambiri amapita kwa Yesu ndi kumukhulupirira. 12 Tsiku lotsatira, gulu lalikulu la anthu lomwe linabwera kuphwando linamva kuti Yesu anali mʼnjira kupita ku Yerusalemu. 13 Iwo anatenga nthambi za kanjedza ndi kupita kukakumana naye, akufuwula kuti,“Hosana! “Wodala Iye amene akubwera mʼdzina la Ambuye! “Yodala Mfumu ya Israeli!” 14 Yesu anapeza bulu wamngʼono ndi kukwerapo, monga kunalembedwa kuti: 15 “Usachite mantha mwana wamkazi wa Ziyoni;taona mfumu yako ikubwera,itakhala pa mwana wabulu.” 16 Poyamba ophunzira ake sanamvetsetse zonsezi. Koma pomwe Yesu analemekezedwa ndi pamene anazindikira kuti zinthu izi zinalembedwa ndipo kuti anamuchitira Iye. 17 Tsopano gulu la anthu lomwe linali naye pa nthawi imene amaukitsidwa Lazaro ku manda linapitiriza kuchitira umboni. 18 Anthu ambiri, anapita kukakumana naye, chifukwa iwo anamva kuti Iye anachita chizindikiro chodabwitsachi. 19 Choncho Afarisi anati kwa wina ndi mnzake, “Taonani, palibe chimene mwachitapo. Anthu onse akumutsatira Iye!” 20 Tsopano panali Agriki ena pakati pa amene anapita kukapembedza ku phwando. 21 Iwo anabwera kwa Filipo, wochokera ku Betisaida wa ku Galileya, ndi pempho, nati, “Akulu, ife tikufuna kuona Yesu.” 22 Filipo anapita kukawuza Andreya; Andreya ndi Filipo pamodzi anakawuza Yesu. 23 Yesu anayankha kuti, “Nthawi yafika yakuti Mwana wa Munthu alemekezedwe. 24 Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti, ‘Mbewu ya tirigu imakhala imodzi yokha ngati sikugwa mʼnthaka ndi kufa. Koma ngati imfa, imabereka mbewu zambiri.’ 25 Munthu amene amakonda moyo wake adzawutaya, pamene munthu amene amadana ndi moyo wake mʼdziko lino lapansi adzawusungira ku moyo wosatha. 26 Aliyense amene atumikira Ine ayenera kunditsata; ndipo kumene Ine ndili, wotumikira wanga adzakhalanso komweko. Atate anga adzalemekeza amene atumikira Ine. 27 “Moyo wanga ukuvutika tsopano, kodi ndidzanena chiyani? Ndinene kuti Atate pulumutseni ku nthawi ino? Ayi. Chifukwa chimene Ine ndinabwera pa nthawi iyi ndi chimenechi. 28 Atate, lemekezani dzina lanu!”Kenaka mawu anabwera kuchokera kumwamba, “Ine ndalilemekeza, ndipo ndidzalilemekezanso.” 29 Gulu la anthu lomwe linali pamenepo litamva linati, “Kwagunda bingu,” ena anati, “Mngelo wayankhula kwa Iye.” 30 Yesu anati, “Mawu awa abwera chifukwa cha inu osati chifukwa cha Ine. 31 Ino tsopano ndi nthawi yachiweruzo pa dziko lapansi; tsopano olamulira wa dziko lapansi adzathamangitsidwa. 32 Koma Ine, akadzandipachika pa dziko lapansi, ndidzakokera anthu onse kwa Ine.” 33 Iye ananena izi kuti aonetse mmene adzafere. 34 Gulu la anthu linayankha kuti, “Ife tinamva kuchokera mʼmalamulo kuti Khristu adzakhala kwamuyaya, nanga bwanji Inu mukunena kuti, ‘Mwana wa Munthu ayenera kukwezedwa?’ Kodi Mwana wa Munthuyu ndani?” 35 Kenaka Yesu anawawuza kuti, “Inu mukhala ndi kuwunika kwa nthawi pangʼono. Yendani pamene mukanali ndi kuwunika, kuti mdima usakupitirireni. Munthu amene amayenda mu mdima sadziwa kumene akupita. 36 Khulupirirani kuwunika, pamene mukanali ndi kuwunika, kuti mukhale ana a kuwunika.” Yesu atamaliza kuyankhula izi, Iye anachoka nabisala kuti asamuone. 37 Ngakhale Yesu anachita zizindikiro zodabwitsa zonsezi pamaso pawo, sanamukhulupirirebe. 38 Izi zinakwaniritsa mawu a mneneri Yesaya kuti:“Ambuye, wakhulupirira uthenga wathu ndani,ndipo ndi kwa yani komwe mkono wa Ambuye wavumbulutsidwa?” 39 Pa chifukwa cha ichi iwo sanakhulupirire, chifukwa Yesaya ananenanso kuti: 40 “Iye wachititsa khungu maso awondi kuwumitsa mitima yawo,kotero kuti iwo sangathe kuona ndi maso awo,kapena kuzindikira ndi mitima yawo,kapena kutembenuka kuti Ine ndikanawachiza.” 41 Yesaya ananena izi chifukwa anaona ulemerero wa Yesu ndi kuyankhula za Iye. 42 Komabe pa nthawi yomweyi ambiri ngakhale atsogoleri anakhulupirira Iye. Koma chifukwa cha Afarisi iwo sanavomereze chikhulupiriro chawo chifukwa amaopa kuti angawatulutse mʼsunagoge; 43 pakuti iwo amakonda kuyamikiridwa ndi anthu kuposa kuyamikiridwa ndi Mulungu. 44 Kenaka Yesu anafuwula nati, “Munthu aliyense amene akhulupirira Ine, sakhulupirira Ine ndekha, komanso Iye amene anandituma Ine. 45 Iye amene waona Ine, waonanso Iye amene anandituma Ine. 46 Ine ndabwera mʼdziko lapansi monga kuwunika, kotero palibe amene amakhulupirira Ine nʼkumakhalabe mu mdima. 47 “Ndipo munthu amene amva mawu anga koma osawasunga, Ine sindimuweruza. Pakuti Ine sindinabwere kudzaweruza dziko lapansi, koma kudzapulumutsa. 48 Iye amene akana Ine ndipo salandira mawu anga ali ndi womuweruza. Tsiku lomaliza mawu amene ndiyankhulawa adzamutsutsa. 49 Pakuti Ine sindiyankhula mwa Ine ndekha, koma Atate amene anandituma amandilamulira choti ndinene ndi momwe ndinenere. 50 Ine ndikudziwa kuti lamulo lake ndi moyo wosatha. Choncho chilichonse chimene Ine ndinena ndi chimene Atate andiwuza.”

In Other Versions

John 12 in the ANGEFD

John 12 in the ANTPNG2D

John 12 in the AS21

John 12 in the BAGH

John 12 in the BBPNG

John 12 in the BBT1E

John 12 in the BDS

John 12 in the BEV

John 12 in the BHAD

John 12 in the BIB

John 12 in the BLPT

John 12 in the BNT

John 12 in the BNTABOOT

John 12 in the BNTLV

John 12 in the BOATCB

John 12 in the BOATCB2

John 12 in the BOBCV

John 12 in the BOCNT

John 12 in the BOECS

John 12 in the BOHCB

John 12 in the BOHCV

John 12 in the BOHLNT

John 12 in the BOHNTLTAL

John 12 in the BOICB

John 12 in the BOILNTAP

John 12 in the BOITCV

John 12 in the BOKCV

John 12 in the BOKCV2

John 12 in the BOKHWOG

John 12 in the BOKSSV

John 12 in the BOLCB

John 12 in the BOLCB2

John 12 in the BOMCV

John 12 in the BONAV

John 12 in the BONCB

John 12 in the BONLT

John 12 in the BONUT2

John 12 in the BOPLNT

John 12 in the BOSCB

John 12 in the BOSNC

John 12 in the BOTLNT

John 12 in the BOVCB

John 12 in the BOYCB

John 12 in the BPBB

John 12 in the BPH

John 12 in the BSB

John 12 in the CCB

John 12 in the CUV

John 12 in the CUVS

John 12 in the DBT

John 12 in the DGDNT

John 12 in the DHNT

John 12 in the DNT

John 12 in the ELBE

John 12 in the EMTV

John 12 in the ESV

John 12 in the FBV

John 12 in the FEB

John 12 in the GGMNT

John 12 in the GNT

John 12 in the HARY

John 12 in the HNT

John 12 in the IRVA

John 12 in the IRVB

John 12 in the IRVG

John 12 in the IRVH

John 12 in the IRVK

John 12 in the IRVM

John 12 in the IRVM2

John 12 in the IRVO

John 12 in the IRVP

John 12 in the IRVT

John 12 in the IRVT2

John 12 in the IRVU

John 12 in the ISVN

John 12 in the JSNT

John 12 in the KAPI

John 12 in the KBT1ETNIK

John 12 in the KBV

John 12 in the KJV

John 12 in the KNFD

John 12 in the LBA

John 12 in the LBLA

John 12 in the LNT

John 12 in the LSV

John 12 in the MAAL

John 12 in the MBV

John 12 in the MBV2

John 12 in the MHNT

John 12 in the MKNFD

John 12 in the MNG

John 12 in the MNT

John 12 in the MNT2

John 12 in the MRS1T

John 12 in the NAA

John 12 in the NASB

John 12 in the NBLA

John 12 in the NBS

John 12 in the NBVTP

John 12 in the NET2

John 12 in the NIV11

John 12 in the NNT

John 12 in the NNT2

John 12 in the NNT3

John 12 in the PDDPT

John 12 in the PFNT

John 12 in the RMNT

John 12 in the SBIAS

John 12 in the SBIBS

John 12 in the SBIBS2

John 12 in the SBICS

John 12 in the SBIDS

John 12 in the SBIGS

John 12 in the SBIHS

John 12 in the SBIIS

John 12 in the SBIIS2

John 12 in the SBIIS3

John 12 in the SBIKS

John 12 in the SBIKS2

John 12 in the SBIMS

John 12 in the SBIOS

John 12 in the SBIPS

John 12 in the SBISS

John 12 in the SBITS

John 12 in the SBITS2

John 12 in the SBITS3

John 12 in the SBITS4

John 12 in the SBIUS

John 12 in the SBIVS

John 12 in the SBT

John 12 in the SBT1E

John 12 in the SCHL

John 12 in the SNT

John 12 in the SUSU

John 12 in the SUSU2

John 12 in the SYNO

John 12 in the TBIAOTANT

John 12 in the TBT1E

John 12 in the TBT1E2

John 12 in the TFTIP

John 12 in the TFTU

John 12 in the TGNTATF3T

John 12 in the THAI

John 12 in the TNFD

John 12 in the TNT

John 12 in the TNTIK

John 12 in the TNTIL

John 12 in the TNTIN

John 12 in the TNTIP

John 12 in the TNTIZ

John 12 in the TOMA

John 12 in the TTENT

John 12 in the UBG

John 12 in the UGV

John 12 in the UGV2

John 12 in the UGV3

John 12 in the VBL

John 12 in the VDCC

John 12 in the YALU

John 12 in the YAPE

John 12 in the YBVTP

John 12 in the ZBP