John 2 (BOGWICC)

1 Pa tsiku lachitatu munali ukwati mu Kana wa ku Galileya. Amayi ake a Yesu anali komweko, 2 ndipo Yesu ndi ophunzira ake anayitanidwanso ku ukwatiwo. 3 Vinyo atatha, amayi a Yesu anati kwa Iye, “Wawathera vinyo.” 4 Yesu anayankha kuti, “Amayi, chifukwa chiyani mukundiwuza Ine? Nthawi yanga sinakwane.” 5 Amayi ake anati kwa antchito, “Inu muchite chilichonse chimene akuwuzeni.” 6 Pamenepo panali mitsuko yamiyala yothiramo madzi isanu ndi umodzi, imene Ayuda amagwiritsa ntchito pa mwambo wodziyeretsa. Uliwonse unali ndi malita 100 kapena kupitirirapo. 7 Yesu anati kwa antchitowo, “Dzazani madzi mʼmitsukoyi,” ndipo iwo anadzaza ndendende. 8 Ndipo Iye anatinso kwa iwo, “Tsopano tungani ndipo kaperekeni kwa mkulu waphwando.”Iwo anachita momwemo. 9 Mkulu waphwando analawa madziwo amene anasandulika vinyo, ndipo sanazindikire kumene vinyoyo anachokera, ngakhale kuti antchito amene anatunga madziwo amadziwa. Kenaka anayitanira mkwati pambali 10 ndipo anati, “Aliyense amatulutsa vinyo wokoma kwambiri poyambirira ndipo kenaka vinyo wosakoma pamene oyitanidwa atamwa kale wambiri; koma iwe wasunga wokoma mpaka tsopano.” 11 Ichi chinali chizindikiro chodabwitsa choyamba chimene Yesu anachita ku Kana wa ku Galileya. Potero Iye anawulula ulemerero wake, ndipo ophunzira ake anamukhulupirira Iye. 12 Zitatha izi Iye anatsikira ku Kaperenawo pamodzi ndi amayi ake, abale ake ndi ophunzira ake. Iwo anakhala kumeneko masiku owerengeka. 13 Nthawi ya Paska ya Ayuda itayandikira, Yesu anapita ku Yerusalemu. 14 Mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu Iye anapeza anthu akugulitsa ngʼombe, nkhosa ndi nkhunda ndipo ena akusintha ndalama pa matebulo. 15 Chifukwa cha zimenezi Iye anapanga chikwapu cha zingwe ndipo anatulutsa onse mʼbwalo la Nyumbayo, pamodzi ndi nkhosa ndi ngʼombe; Iye anamwaza ndalama zawo ndi kugudubuza matebulo. 16 Kwa amene amagulitsa nkhunda, Iye anati, “Tulutsani izi muno! Osasandutsa Nyumba ya Atate anga msika!” 17 Ophunzira ake anakumbukira kuti zinalembedwa kuti, “Kudzipereka kwanga ku nyumba yanu kudzandiphetsa.” 18 Kenaka Ayuda anamufunsa Yesu kuti, “Kodi mungationetse chizindikiro chodabwitsa chotani chotsimikizira ulamuliro wanu wochitira izi?” 19 Yesu anawayankha kuti, “Gwetsani Nyumba ya Mulunguyi ndipo Ine ndidzayimanganso mʼmasiku atatu.” 20 Ayuda anayankha kuti, “Zinatenga zaka makumi anayi kumanga Nyumbayi, kodi Inu mungayimange masiku atatu?” 21 Koma Nyumba ya Mulungu imene amanena linali thupi lake. 22 Iye ataukitsidwa kwa akufa, ophunzira ake anakumbukira zimene Iye ananena ndipo anakhulupirira Malemba ndi mawu amene Yesu anayankhula. 23 Tsopano Iye ali mu Yerusalemu pa phwando la Paska, anthu ambiri anaona zizindikiro zodabwitsa zimene amachita ndipo anakhulupirira dzina lake. 24 Koma Yesu sanawakhulupirire iwo, pakuti amadziwa anthu onse. 25 Iye sanafune umboni wa wina aliyense popeza amadziwa zomwe zinali mʼmitima mwa anthu.

In Other Versions

John 2 in the ANGEFD

John 2 in the ANTPNG2D

John 2 in the AS21

John 2 in the BAGH

John 2 in the BBPNG

John 2 in the BBT1E

John 2 in the BDS

John 2 in the BEV

John 2 in the BHAD

John 2 in the BIB

John 2 in the BLPT

John 2 in the BNT

John 2 in the BNTABOOT

John 2 in the BNTLV

John 2 in the BOATCB

John 2 in the BOATCB2

John 2 in the BOBCV

John 2 in the BOCNT

John 2 in the BOECS

John 2 in the BOHCB

John 2 in the BOHCV

John 2 in the BOHLNT

John 2 in the BOHNTLTAL

John 2 in the BOICB

John 2 in the BOILNTAP

John 2 in the BOITCV

John 2 in the BOKCV

John 2 in the BOKCV2

John 2 in the BOKHWOG

John 2 in the BOKSSV

John 2 in the BOLCB

John 2 in the BOLCB2

John 2 in the BOMCV

John 2 in the BONAV

John 2 in the BONCB

John 2 in the BONLT

John 2 in the BONUT2

John 2 in the BOPLNT

John 2 in the BOSCB

John 2 in the BOSNC

John 2 in the BOTLNT

John 2 in the BOVCB

John 2 in the BOYCB

John 2 in the BPBB

John 2 in the BPH

John 2 in the BSB

John 2 in the CCB

John 2 in the CUV

John 2 in the CUVS

John 2 in the DBT

John 2 in the DGDNT

John 2 in the DHNT

John 2 in the DNT

John 2 in the ELBE

John 2 in the EMTV

John 2 in the ESV

John 2 in the FBV

John 2 in the FEB

John 2 in the GGMNT

John 2 in the GNT

John 2 in the HARY

John 2 in the HNT

John 2 in the IRVA

John 2 in the IRVB

John 2 in the IRVG

John 2 in the IRVH

John 2 in the IRVK

John 2 in the IRVM

John 2 in the IRVM2

John 2 in the IRVO

John 2 in the IRVP

John 2 in the IRVT

John 2 in the IRVT2

John 2 in the IRVU

John 2 in the ISVN

John 2 in the JSNT

John 2 in the KAPI

John 2 in the KBT1ETNIK

John 2 in the KBV

John 2 in the KJV

John 2 in the KNFD

John 2 in the LBA

John 2 in the LBLA

John 2 in the LNT

John 2 in the LSV

John 2 in the MAAL

John 2 in the MBV

John 2 in the MBV2

John 2 in the MHNT

John 2 in the MKNFD

John 2 in the MNG

John 2 in the MNT

John 2 in the MNT2

John 2 in the MRS1T

John 2 in the NAA

John 2 in the NASB

John 2 in the NBLA

John 2 in the NBS

John 2 in the NBVTP

John 2 in the NET2

John 2 in the NIV11

John 2 in the NNT

John 2 in the NNT2

John 2 in the NNT3

John 2 in the PDDPT

John 2 in the PFNT

John 2 in the RMNT

John 2 in the SBIAS

John 2 in the SBIBS

John 2 in the SBIBS2

John 2 in the SBICS

John 2 in the SBIDS

John 2 in the SBIGS

John 2 in the SBIHS

John 2 in the SBIIS

John 2 in the SBIIS2

John 2 in the SBIIS3

John 2 in the SBIKS

John 2 in the SBIKS2

John 2 in the SBIMS

John 2 in the SBIOS

John 2 in the SBIPS

John 2 in the SBISS

John 2 in the SBITS

John 2 in the SBITS2

John 2 in the SBITS3

John 2 in the SBITS4

John 2 in the SBIUS

John 2 in the SBIVS

John 2 in the SBT

John 2 in the SBT1E

John 2 in the SCHL

John 2 in the SNT

John 2 in the SUSU

John 2 in the SUSU2

John 2 in the SYNO

John 2 in the TBIAOTANT

John 2 in the TBT1E

John 2 in the TBT1E2

John 2 in the TFTIP

John 2 in the TFTU

John 2 in the TGNTATF3T

John 2 in the THAI

John 2 in the TNFD

John 2 in the TNT

John 2 in the TNTIK

John 2 in the TNTIL

John 2 in the TNTIN

John 2 in the TNTIP

John 2 in the TNTIZ

John 2 in the TOMA

John 2 in the TTENT

John 2 in the UBG

John 2 in the UGV

John 2 in the UGV2

John 2 in the UGV3

John 2 in the VBL

John 2 in the VDCC

John 2 in the YALU

John 2 in the YAPE

John 2 in the YBVTP

John 2 in the ZBP