Job 22 (BOGWICC)

1 Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha kuti, 2 “Kodi munthu nʼkukhala waphindu kwa Mulungu?Kodi munthu wanzeru angamupindulire Iye? 3 Kodi Wamphamvuzonse akanapeza chabwino chotani iweyo ukanakhala wolungama?Kodi iyeyo akanapeza phindu lanji makhalidwe ako akanakhala angwiro? 4 “Kodi nʼchifukwa choti umamuopa, kuti azikudzudzula,kuti azifuna kukukokera ku mlandu? 5 Kodi osati nʼchifukwa chakuti kuyipa kwako nʼkwakukulu?Kodi machimo ako si opanda malire? 6 Iwe unkawumiriza abale ako kuti akupatse chikole popanda chifukwa;umalanda anthu zovala zawo ndi kuwasiya amaliseche. 7 Sunawapatse madzi anthu otopa,ndipo unawamana chakudya anthu anjala, 8 ngakhale unali munthu wamphamvu, wokhala ndi malo akeake,munthu waulemu wake, wokhala mʼdzikomo. 9 Ndipo akazi amasiye unawachotsa wopanda kanthu,ndipo unapondereza ana amasiye. 10 Nʼchifukwa chake misampha yakuzungulira,nʼchifukwa chake tsoka ladzidzidzi lakuchititsa mantha, 11 nʼchifukwa chake kuli mdima kuti sungathe kuona kanthu,nʼchifukwa chakenso madzi achigumula akumiza. 12 “Kodi Mulungu sali kutalitali kumwamba?Ndipo ona nyenyezi zili mmwamba kwambirizo, ona kutalika kwake pamene zililipo! 13 Komabe iweyo ukunena kuti, ‘Kodi Mulungu amadziwa chiyani?Kodi Iye amaweruza mu mdima woterewu? 14 Mitambo yakuda yamuphimba, kotero kuti Iye sakutionapamene akuyendayenda pamwamba pa thambopo.’ 15 Kodi iwe udzayendabe mʼnjira yakaleimene anthu oyipa ankayendamo? 16 Iwo anachotsedwa nthawi yawo isanakwane,maziko awo anakokoloka ndi madzi achigumula. 17 Anthuwo anati kwa Mulungu, ‘Tichokereni!Kodi Wamphamvuzonse angatichitire chiyani?’ 18 Chonsecho ndi Iye amene anadzaza nyumba zawo ndi zinthu zabwino,choncho ine sindigwirizana ndi uphungu wa anthu oyipa. 19 “Anthu olungama amaona kuwonongeka kwawo ndipo amakondwera;anthu osalakwa amangoseka, akamuona woyipa akulangidwa. 20 Amanena kuti, ‘Ndithudi adani athu awonongekandipo moto wawononga chuma chawo!’ 21 “Gonjera Mulungu kuti ukhale naye pamtendere;ukatero udzaona zabwino. 22 Landira malangizo a pakamwa pakendipo usunge mawu ake mu mtima mwako. 23 Ukabwerera kwa Wamphamvuzonse udzabwezeretsedwa;ukachotsa zoyipa zonse zimene zimachitika mʼnyumba mwako, 24 ndipo chuma chamtengowapatali nuchiona ngati fumbi,golide wa ku Ofiri numutaya ku miyala ya ku zigwa. 25 Pamenepo Wamphamvuzonseyo adzakhala golide wako,siliva wako wamtengowapatali. 26 Pamenepo udzakondwera naye Wamphamvuzonsendipo udzakweza nkhope yako kwa Mulungu. 27 Udzamupempha ndipo adzakumvera,ndipo udzapereka zimene unalonjeza. 28 Chimene watsimikiza kuti uchite, chidzachitikadi,kuwala kudzakuwunikira pa njira yako. 29 Pamene anthu agwetsedwa pansi, iwe nʼkunena kuti, ‘Akwezeni!’Pamenepo Iye adzapulumutsa anthu oponderezedwa. 30 Iye adzapulumutsa ngakhale munthu amene ndi wolakwa,ameneyo adzapulumutsidwa kudzera mʼkulungama kwako.”

In Other Versions

Job 22 in the ANGEFD

Job 22 in the ANTPNG2D

Job 22 in the AS21

Job 22 in the BAGH

Job 22 in the BBPNG

Job 22 in the BBT1E

Job 22 in the BDS

Job 22 in the BEV

Job 22 in the BHAD

Job 22 in the BIB

Job 22 in the BLPT

Job 22 in the BNT

Job 22 in the BNTABOOT

Job 22 in the BNTLV

Job 22 in the BOATCB

Job 22 in the BOATCB2

Job 22 in the BOBCV

Job 22 in the BOCNT

Job 22 in the BOECS

Job 22 in the BOHCB

Job 22 in the BOHCV

Job 22 in the BOHLNT

Job 22 in the BOHNTLTAL

Job 22 in the BOICB

Job 22 in the BOILNTAP

Job 22 in the BOITCV

Job 22 in the BOKCV

Job 22 in the BOKCV2

Job 22 in the BOKHWOG

Job 22 in the BOKSSV

Job 22 in the BOLCB

Job 22 in the BOLCB2

Job 22 in the BOMCV

Job 22 in the BONAV

Job 22 in the BONCB

Job 22 in the BONLT

Job 22 in the BONUT2

Job 22 in the BOPLNT

Job 22 in the BOSCB

Job 22 in the BOSNC

Job 22 in the BOTLNT

Job 22 in the BOVCB

Job 22 in the BOYCB

Job 22 in the BPBB

Job 22 in the BPH

Job 22 in the BSB

Job 22 in the CCB

Job 22 in the CUV

Job 22 in the CUVS

Job 22 in the DBT

Job 22 in the DGDNT

Job 22 in the DHNT

Job 22 in the DNT

Job 22 in the ELBE

Job 22 in the EMTV

Job 22 in the ESV

Job 22 in the FBV

Job 22 in the FEB

Job 22 in the GGMNT

Job 22 in the GNT

Job 22 in the HARY

Job 22 in the HNT

Job 22 in the IRVA

Job 22 in the IRVB

Job 22 in the IRVG

Job 22 in the IRVH

Job 22 in the IRVK

Job 22 in the IRVM

Job 22 in the IRVM2

Job 22 in the IRVO

Job 22 in the IRVP

Job 22 in the IRVT

Job 22 in the IRVT2

Job 22 in the IRVU

Job 22 in the ISVN

Job 22 in the JSNT

Job 22 in the KAPI

Job 22 in the KBT1ETNIK

Job 22 in the KBV

Job 22 in the KJV

Job 22 in the KNFD

Job 22 in the LBA

Job 22 in the LBLA

Job 22 in the LNT

Job 22 in the LSV

Job 22 in the MAAL

Job 22 in the MBV

Job 22 in the MBV2

Job 22 in the MHNT

Job 22 in the MKNFD

Job 22 in the MNG

Job 22 in the MNT

Job 22 in the MNT2

Job 22 in the MRS1T

Job 22 in the NAA

Job 22 in the NASB

Job 22 in the NBLA

Job 22 in the NBS

Job 22 in the NBVTP

Job 22 in the NET2

Job 22 in the NIV11

Job 22 in the NNT

Job 22 in the NNT2

Job 22 in the NNT3

Job 22 in the PDDPT

Job 22 in the PFNT

Job 22 in the RMNT

Job 22 in the SBIAS

Job 22 in the SBIBS

Job 22 in the SBIBS2

Job 22 in the SBICS

Job 22 in the SBIDS

Job 22 in the SBIGS

Job 22 in the SBIHS

Job 22 in the SBIIS

Job 22 in the SBIIS2

Job 22 in the SBIIS3

Job 22 in the SBIKS

Job 22 in the SBIKS2

Job 22 in the SBIMS

Job 22 in the SBIOS

Job 22 in the SBIPS

Job 22 in the SBISS

Job 22 in the SBITS

Job 22 in the SBITS2

Job 22 in the SBITS3

Job 22 in the SBITS4

Job 22 in the SBIUS

Job 22 in the SBIVS

Job 22 in the SBT

Job 22 in the SBT1E

Job 22 in the SCHL

Job 22 in the SNT

Job 22 in the SUSU

Job 22 in the SUSU2

Job 22 in the SYNO

Job 22 in the TBIAOTANT

Job 22 in the TBT1E

Job 22 in the TBT1E2

Job 22 in the TFTIP

Job 22 in the TFTU

Job 22 in the TGNTATF3T

Job 22 in the THAI

Job 22 in the TNFD

Job 22 in the TNT

Job 22 in the TNTIK

Job 22 in the TNTIL

Job 22 in the TNTIN

Job 22 in the TNTIP

Job 22 in the TNTIZ

Job 22 in the TOMA

Job 22 in the TTENT

Job 22 in the UBG

Job 22 in the UGV

Job 22 in the UGV2

Job 22 in the UGV3

Job 22 in the VBL

Job 22 in the VDCC

Job 22 in the YALU

Job 22 in the YAPE

Job 22 in the YBVTP

Job 22 in the ZBP