Job 25 (BOGWICC)
1 Apo Bilidadi wa ku Suki anayankha kuti, 2 “Ulamuliro ndi kuopsa ndi za Mulungu,Iye amakhazikitsa bata mu ufumu wake kumwambako. 3 Kodi magulu ake ankhondo nʼkuwerengeka?Kodi kuwala kwake sikuwalira ndani? 4 Kodi munthu angakhale bwanji wolungama pamaso pa Mulungu?Kodi munthu wobadwa mwa mayi angakhale wangwiro? 5 Ngati mwezi sutha kuwala kwenikweni,ndipo nyenyezi sizitha kuwala pamaso pake, 6 nanji tsono munthu amene ali ngati mphutsi,mwana wa munthu amene ali ngati nyongolotsi!”