Job 30 (BOGWICC)
1 “Koma tsopano akundinyoza,ana angʼonoangʼono kwa ine,anthu amene makolo awo sindikanawalolakuti azithandizana ndi agalu anga kuweta nkhosa zanga. 2 Kodi mphamvu zawo ndi za phindu lanji kwa ine,pakuti mphamvu zawo zinatha kale? 3 Anali atatheratu kuwonda ndi njala,ankayendayenda mʼdziko lopanda madzi,mʼchipululu usiku. 4 Ankathyola therere ndi masamba owawa,ndipo chakudya chawo chinali mizu ya mitengo ya masache. 5 Anapirikitsidwa pakati pa anthu anzawo,akuwakuwiza ngati kuti anali akuba. 6 Anawumirizidwa kukhala ku zigwembe za mitsinje yowuma,pakati pa matanthwe ndi mʼmaenje a mʼnthaka. 7 Ankalira ngati nyama kuthengondipo ankawunjikana pamodzi pa ziyangoyango. 8 Anali anthu achabechabe ndi wopanda dzina,anathamangitsidwa mʼdziko. 9 “Ndipo tsopano ana awo akundiyimba nyimbo zachipongwe;ineyo ndasanduka chisudzo chawo. 10 Iwo amanyansidwa nane ndipo amandithawa;akandiona salephera kundilavulira mʼmaso mwangamu. 11 Tsopano pakuti Mulungu wakhwefula uta wanga ndipo wandisautsa,iwowo analekeratu kundiopa. 12 Ku dzanja langa lamanja anthu akulimbana nane;andikumbira dzenje loti ndigweremo ndikamayenda,andipangira mitumbira ya nkhondo kuti alimbane nane. 13 Iwo anditsekera njira;akufuna kundichititsa ngozi,popanda wina aliyense wowaletsa. 14 Akundithamangitsa ngati madzi olowera pa mpanda wobowoka,iwo akubwererabwerera pakati pa chipasupasu. 15 Zoopsa zandithetsa mphamvu;ulemu wanga wachita ngati wauluzika ndi mphepo,chuma changa chija chazimirira ngati mtambo. 16 “Ndipo tsopano mtima wanga wachokamo;ndili mʼmasiku amasautso. 17 Mafupa anga akuphwanya usiku pakutizowawa zanga sizikuleka. 18 Mʼmphamvu zake Mulungu wakhala ngati chovala changa;Iye wandigwira ngati chovala chondithina pa khosi. 19 Wandiponya mʼmatope,ndipo ndasanduka ngati fumbi ndi phulusa. 20 “Inu Mulungu, ine ndikulirira kwa Inu, koma simukundiyankha;ndikayimirira, Inu simundiyangʼana nʼkomwe. 21 Inuyo mumandichitira zankhanza;mumandizunza ndi dzanja lanu lamphamvu. 22 Mwandinyamulira ku mphepo ndipo mwandiwulutsa ndi mphepoyo;mwandiponya mʼmphepo ya mkuntho. 23 Ndikudziwa kuti Inu mudzandifikitsa ku imfa,kumalo kumene amoyo onse adzapitako. 24 “Ndithudi palibe munthu amene amalanga munthu wosweka mtima,amene akupempha thandizo mʼmasautso ake. 25 Kodi ine sindinalire nawo iwo amene anali pamavuto?Kodi mtima wanga sunamvere chisoni anthu osauka? 26 Koma pamene ndinkayembekezera zabwino, zoyipa ndiye zinandigwera;pamene ndinkafunafuna kuwala, mdima ndiye unandigwera. 27 Kuwawa kwa mʼkati mwanga sikukuleka;ndili mʼmasiku amasautso. 28 Ndikuyenda wothimbirira, komatu osati ndi dzuwa;ndimayimirira pa msonkhano ndi kupempha chithandizo molira. 29 Ndasanduka mʼbale wa nkhandwe,mnzawo wa akadzidzi. 30 Khungu langa layamba kuda ndipo likufunduka;thupi langa likutentha chifukwa cha kuphwanya kwa thupi. 31 Pangwe wanga wasanduka woyimbira maliro,ndipo chitoliro changa chikuyimbira anthu olira.
In Other Versions
Job 30 in the ANGEFD
Job 30 in the ANTPNG2D
Job 30 in the AS21
Job 30 in the BAGH
Job 30 in the BBPNG
Job 30 in the BBT1E
Job 30 in the BDS
Job 30 in the BEV
Job 30 in the BHAD
Job 30 in the BIB
Job 30 in the BLPT
Job 30 in the BNT
Job 30 in the BNTABOOT
Job 30 in the BNTLV
Job 30 in the BOATCB
Job 30 in the BOATCB2
Job 30 in the BOBCV
Job 30 in the BOCNT
Job 30 in the BOECS
Job 30 in the BOHCB
Job 30 in the BOHCV
Job 30 in the BOHLNT
Job 30 in the BOHNTLTAL
Job 30 in the BOICB
Job 30 in the BOILNTAP
Job 30 in the BOITCV
Job 30 in the BOKCV
Job 30 in the BOKCV2
Job 30 in the BOKHWOG
Job 30 in the BOKSSV
Job 30 in the BOLCB
Job 30 in the BOLCB2
Job 30 in the BOMCV
Job 30 in the BONAV
Job 30 in the BONCB
Job 30 in the BONLT
Job 30 in the BONUT2
Job 30 in the BOPLNT
Job 30 in the BOSCB
Job 30 in the BOSNC
Job 30 in the BOTLNT
Job 30 in the BOVCB
Job 30 in the BOYCB
Job 30 in the BPBB
Job 30 in the BPH
Job 30 in the BSB
Job 30 in the CCB
Job 30 in the CUV
Job 30 in the CUVS
Job 30 in the DBT
Job 30 in the DGDNT
Job 30 in the DHNT
Job 30 in the DNT
Job 30 in the ELBE
Job 30 in the EMTV
Job 30 in the ESV
Job 30 in the FBV
Job 30 in the FEB
Job 30 in the GGMNT
Job 30 in the GNT
Job 30 in the HARY
Job 30 in the HNT
Job 30 in the IRVA
Job 30 in the IRVB
Job 30 in the IRVG
Job 30 in the IRVH
Job 30 in the IRVK
Job 30 in the IRVM
Job 30 in the IRVM2
Job 30 in the IRVO
Job 30 in the IRVP
Job 30 in the IRVT
Job 30 in the IRVT2
Job 30 in the IRVU
Job 30 in the ISVN
Job 30 in the JSNT
Job 30 in the KAPI
Job 30 in the KBT1ETNIK
Job 30 in the KBV
Job 30 in the KJV
Job 30 in the KNFD
Job 30 in the LBA
Job 30 in the LBLA
Job 30 in the LNT
Job 30 in the LSV
Job 30 in the MAAL
Job 30 in the MBV
Job 30 in the MBV2
Job 30 in the MHNT
Job 30 in the MKNFD
Job 30 in the MNG
Job 30 in the MNT
Job 30 in the MNT2
Job 30 in the MRS1T
Job 30 in the NAA
Job 30 in the NASB
Job 30 in the NBLA
Job 30 in the NBS
Job 30 in the NBVTP
Job 30 in the NET2
Job 30 in the NIV11
Job 30 in the NNT
Job 30 in the NNT2
Job 30 in the NNT3
Job 30 in the PDDPT
Job 30 in the PFNT
Job 30 in the RMNT
Job 30 in the SBIAS
Job 30 in the SBIBS
Job 30 in the SBIBS2
Job 30 in the SBICS
Job 30 in the SBIDS
Job 30 in the SBIGS
Job 30 in the SBIHS
Job 30 in the SBIIS
Job 30 in the SBIIS2
Job 30 in the SBIIS3
Job 30 in the SBIKS
Job 30 in the SBIKS2
Job 30 in the SBIMS
Job 30 in the SBIOS
Job 30 in the SBIPS
Job 30 in the SBISS
Job 30 in the SBITS
Job 30 in the SBITS2
Job 30 in the SBITS3
Job 30 in the SBITS4
Job 30 in the SBIUS
Job 30 in the SBIVS
Job 30 in the SBT
Job 30 in the SBT1E
Job 30 in the SCHL
Job 30 in the SNT
Job 30 in the SUSU
Job 30 in the SUSU2
Job 30 in the SYNO
Job 30 in the TBIAOTANT
Job 30 in the TBT1E
Job 30 in the TBT1E2
Job 30 in the TFTIP
Job 30 in the TFTU
Job 30 in the TGNTATF3T
Job 30 in the THAI
Job 30 in the TNFD
Job 30 in the TNT
Job 30 in the TNTIK
Job 30 in the TNTIL
Job 30 in the TNTIN
Job 30 in the TNTIP
Job 30 in the TNTIZ
Job 30 in the TOMA
Job 30 in the TTENT
Job 30 in the UBG
Job 30 in the UGV
Job 30 in the UGV2
Job 30 in the UGV3
Job 30 in the VBL
Job 30 in the VDCC
Job 30 in the YALU
Job 30 in the YAPE
Job 30 in the YBVTP
Job 30 in the ZBP