Job 36 (BOGWICC)

1 Ndipo Elihu anapitirira kuyankhula nati: 2 “Mundilole pangʼono pokha ndipo ndikuonetsanikuti zilipo zambiri zoti ziyankhulidwe mʼmalo mwa Mulungu. 3 Nzeru zanga ndimazitenga kutali;ndidzaonetsa kulungama kwa Mlengi wanga. 4 Ndithudi mawu anga si abodza;wanzeru zangwiro ali ndi inu. 5 “Mulungu ndi wamphamvu, koma sanyoza anthu;Iye ndi wamphamvu, ndipo ndi wokhazikika pa cholinga chake. 6 Salola oyipa kuti akhalebe ndi moyokoma amapereka ufulu kwa anthu osautsidwa. 7 Iye saleka kuyangʼanira anthu olungama;amawayika kuti alamulire pamodzi ndi mafumundipo amawalemekeza mpaka muyaya. 8 Koma ngati anthu amangidwa ndi unyolo,ndipo akondwa ndi zingwe zamasautso, 9 Iye amawafotokozera zomwe anachita,kuti iwo anachimwa modzikuza. 10 Mulungu amawatsekula makutu kuti amve malangizo akendipo amawalamula kuti alape zoyipa zawo. 11 Ngati iwo amumvera ndi kumutumikira,adzatsiriza masiku a moyo wawo mwamtendere,adzatsiriza zaka zawo mosangalala. 12 Koma ngati samvera,adzaphedwa ndi lupangandipo adzafa osadziwa kanthu. 13 “Anthu osapembedza amasunga mkwiyo mu mtima mwawo;akawalanga, safuwulira kwa Iye kupempha thandizo. 14 Amafa akanali achinyamata,pakati pa amuna achiwerewere a kumalo azipembedzo. 15 Koma ovutika, Iye amawapulumutsa pa mavuto awo;Mulungu amawayankhula mʼmasautso awowo. 16 “Iye akukukopani inu kuti muchoke mʼmasautso,kuti mupite ku malo aakulu kumene kulibe chokutchingani,kumalo a mpumulo kumene kuli chakudya chabwino kwambiri. 17 Koma tsopano inu mwapezeka wopalamula chifukwa cha kuyipa kwanu;chiweruzo ndi chilungamo chakugwerani. 18 Muchenjere kuti wina asakukopeni ndi chuma;musalole kuti chiphuphu chachikulu chikusocheretseni. 19 Kodi chuma chanukapena mphamvu zanu zonsezingakusungeni kotero kuti simungakhale pa masautso? 20 Musalakalake kuti usiku ubwere,pakuti ndiyo nthawi imene anthu adzawonongeka. 21 Muchenjere kuti musatembenukire ku uchimo,chifukwa uchimowo ndiwo unabweretsa kuzunzika kwanu. 22 “Taonani, Mulungu ndi wamkulu ndiponso ndi wamphamvu.Kodi ndi mphunzitsi uti amene angafanane naye? 23 Kodi ndani amene anamuwuzapo Mulungu zoti achite,kapena kumuwuza kuti, ‘Inu mwachita chinthu cholakwa?’ 24 Kumbukirani kutamanda ntchito zakezimene anthu amaziyamika mʼnyimbo. 25 Anthu onse amaziona ntchitozo;anthuwo amaziona ali kutali. 26 Ndithudi, Mulungu ndi wamkulu, sitimudziwa nʼpangʼono pomwe!Chiwerengero cha zaka zake nʼchosadziwika. 27 “Mulungu ndiye amakweza timadontho tamadzi kuthambo,timene timasungunuka nʼkukhala mvula; 28 mitambo imagwetsa mvulayondipo mvulayo imavumbwa pa anthu mokwanira. 29 Kodi ndani amene angadziwe momwe mitambo imayendera,momwe Iye amabangulira kuchokera kumalo ake? 30 Taonani momwe amawalitsira zingʼaningʼani pa malo ake onse,zimafika ngakhale pansi pa nyanja. 31 Umu ndi mmene Iye amalamulira mitundu ya anthundi kuwapatsa chakudya chochuluka. 32 Amadzaza manja ake ndi zingʼaningʼani,ndipo amazilamulira kuti zigwe pamalo pamene Iye akufuna. 33 Mabingu ake amalengeza za kubwera kwa mvula yamkuntho;ngʼombe nazo zimalengeza za kubwera kwake.

In Other Versions

Job 36 in the ANGEFD

Job 36 in the ANTPNG2D

Job 36 in the AS21

Job 36 in the BAGH

Job 36 in the BBPNG

Job 36 in the BBT1E

Job 36 in the BDS

Job 36 in the BEV

Job 36 in the BHAD

Job 36 in the BIB

Job 36 in the BLPT

Job 36 in the BNT

Job 36 in the BNTABOOT

Job 36 in the BNTLV

Job 36 in the BOATCB

Job 36 in the BOATCB2

Job 36 in the BOBCV

Job 36 in the BOCNT

Job 36 in the BOECS

Job 36 in the BOHCB

Job 36 in the BOHCV

Job 36 in the BOHLNT

Job 36 in the BOHNTLTAL

Job 36 in the BOICB

Job 36 in the BOILNTAP

Job 36 in the BOITCV

Job 36 in the BOKCV

Job 36 in the BOKCV2

Job 36 in the BOKHWOG

Job 36 in the BOKSSV

Job 36 in the BOLCB

Job 36 in the BOLCB2

Job 36 in the BOMCV

Job 36 in the BONAV

Job 36 in the BONCB

Job 36 in the BONLT

Job 36 in the BONUT2

Job 36 in the BOPLNT

Job 36 in the BOSCB

Job 36 in the BOSNC

Job 36 in the BOTLNT

Job 36 in the BOVCB

Job 36 in the BOYCB

Job 36 in the BPBB

Job 36 in the BPH

Job 36 in the BSB

Job 36 in the CCB

Job 36 in the CUV

Job 36 in the CUVS

Job 36 in the DBT

Job 36 in the DGDNT

Job 36 in the DHNT

Job 36 in the DNT

Job 36 in the ELBE

Job 36 in the EMTV

Job 36 in the ESV

Job 36 in the FBV

Job 36 in the FEB

Job 36 in the GGMNT

Job 36 in the GNT

Job 36 in the HARY

Job 36 in the HNT

Job 36 in the IRVA

Job 36 in the IRVB

Job 36 in the IRVG

Job 36 in the IRVH

Job 36 in the IRVK

Job 36 in the IRVM

Job 36 in the IRVM2

Job 36 in the IRVO

Job 36 in the IRVP

Job 36 in the IRVT

Job 36 in the IRVT2

Job 36 in the IRVU

Job 36 in the ISVN

Job 36 in the JSNT

Job 36 in the KAPI

Job 36 in the KBT1ETNIK

Job 36 in the KBV

Job 36 in the KJV

Job 36 in the KNFD

Job 36 in the LBA

Job 36 in the LBLA

Job 36 in the LNT

Job 36 in the LSV

Job 36 in the MAAL

Job 36 in the MBV

Job 36 in the MBV2

Job 36 in the MHNT

Job 36 in the MKNFD

Job 36 in the MNG

Job 36 in the MNT

Job 36 in the MNT2

Job 36 in the MRS1T

Job 36 in the NAA

Job 36 in the NASB

Job 36 in the NBLA

Job 36 in the NBS

Job 36 in the NBVTP

Job 36 in the NET2

Job 36 in the NIV11

Job 36 in the NNT

Job 36 in the NNT2

Job 36 in the NNT3

Job 36 in the PDDPT

Job 36 in the PFNT

Job 36 in the RMNT

Job 36 in the SBIAS

Job 36 in the SBIBS

Job 36 in the SBIBS2

Job 36 in the SBICS

Job 36 in the SBIDS

Job 36 in the SBIGS

Job 36 in the SBIHS

Job 36 in the SBIIS

Job 36 in the SBIIS2

Job 36 in the SBIIS3

Job 36 in the SBIKS

Job 36 in the SBIKS2

Job 36 in the SBIMS

Job 36 in the SBIOS

Job 36 in the SBIPS

Job 36 in the SBISS

Job 36 in the SBITS

Job 36 in the SBITS2

Job 36 in the SBITS3

Job 36 in the SBITS4

Job 36 in the SBIUS

Job 36 in the SBIVS

Job 36 in the SBT

Job 36 in the SBT1E

Job 36 in the SCHL

Job 36 in the SNT

Job 36 in the SUSU

Job 36 in the SUSU2

Job 36 in the SYNO

Job 36 in the TBIAOTANT

Job 36 in the TBT1E

Job 36 in the TBT1E2

Job 36 in the TFTIP

Job 36 in the TFTU

Job 36 in the TGNTATF3T

Job 36 in the THAI

Job 36 in the TNFD

Job 36 in the TNT

Job 36 in the TNTIK

Job 36 in the TNTIL

Job 36 in the TNTIN

Job 36 in the TNTIP

Job 36 in the TNTIZ

Job 36 in the TOMA

Job 36 in the TTENT

Job 36 in the UBG

Job 36 in the UGV

Job 36 in the UGV2

Job 36 in the UGV3

Job 36 in the VBL

Job 36 in the VDCC

Job 36 in the YALU

Job 36 in the YAPE

Job 36 in the YBVTP

Job 36 in the ZBP