Job 38 (BOGWICC)

1 Apo Yehova anamuyankha Yobu mʼkamvuluvulu. Ndipo anati: 2 “Kodi uyu ndani amene akusokoneza uphungu wangapoyankhula mawu opanda nzeru? 3 Onetsa chamuna;ndikufunsandipo undiyankhe. 4 “Kodi unali kuti pamene ndinkayika maziko a dziko lapansi?Ndiwuze ngati ukudziwa. 5 Ndani amene analemba malire ake? Ndithudi iwe ukudziwa!Ndani amene anayeza ndi chingwe dzikoli? 6 Kodi maziko ake anawakumba potani,kapena ndani anayika mwala wake wapangodya, 7 pamene nyenyezi za kummawa zinkayimba pamodzindipo angelo onse a Mulungu ankafuwula mokondwa? 8 “Kodi ndani amene anatsekera nyanja pamene inkalengedwa,pamene inkachita ngati kutumphuka pansi pa dziko, 9 pamene ndinasandutsa mitambo kukhala chovala chakendi kuyikulunga mu mdima wandiweyani, 10 pamene ndinayilembera malire akendikuyikira zitseko ndi mipiringidzo yake. 11 Pamene ndinati, ‘Ufike mpaka apa ndipo usapitirireapa ndiye pamene mafunde ako amphamvuwo azilekezera?’ 12 “Kodi chibadwire chako unalamulapo dzuwa kuti lituluke mmawa,kapena kuti mʼbandakucha ukhalepo pa nthawi yake, 13 kuti kuwalako kuwunikire dziko lonse lapansindi kuthamangitsa anthu oyipa? 14 Chifukwa cha kuwala kwa usana mapiri ndi zigwa zimaonekera bwino ngati zilembo za chidindo pa mtapo;zimaonekera bwino ngati makwinya a chovala. 15 Kuwala kwa dzuwako sikuwafikira anthu oyipa,ndipo dzanja lawo silingathe kuchita kanthu. 16 “Kodi unayendapo pansi penipeni pa nyanjakapena pa magwero ake ozama? 17 Kodi anakuonetsapo zipata za imfa?Kodi unaonako ku dziko la anthu akufa kumene kuli mdima wandiweyani? 18 Kodi kukula kwa dziko lapansi umakudziwa?Undiwuze ngati ukuzidziwa zonsezi. 19 “Kodi njira yopita kumene kumakhala kuwala ili kuti?Nanga mdima umakhala kuti? 20 Kodi iwe ungathe kuziperekeza kwawoko zimenezi?Kodi ukuyidziwa njira yopita kwawoko? 21 Ndithu, iwe ukuyidziwa, poti paja nthawi imeneyo nʼkuti utabadwa kale!Wakhala ndi moyo zaka zambiridi! 22 “Kodi unalowamo mʼnyumba zosungira chisanu chowundanakapena unayionapo nyumba yosungira matalala, 23 zimene ndazisungira nthawi ya mavutondi nthawi yomenyana ndi ya nkhondo? 24 Kodi umadziwa njira ya kumene kumachokera chingʼaningʼanikapena njira ya kumene kumachokera mphepo ya kummawa imene ili pa dziko lonse lapansi? 25 Kodi ndani amene amakonza ngalande za mvula,nanga ndani anakonza njira yoyendamo mphenzi, 26 kuthirira madzi dziko limene sikukhala munthu,chipululu chopandamo munthu, 27 kukhutitsa nthaka yowuma yagwaandi kumeretsamo udzu? 28 Kodi mvula ili ndi abambo ake?Nanga madzi a mame anawabereka ndani? 29 Kodi madzi owundana anawabereka ndani?Ndani amene anabereka chisanu chochokera kumwamba 30 pamene madzi amawuma gwaa ngati mwala,pamene madzi a pa nyanja amazizira, nalimba kuti gwaa? 31 “Kodi iwe ungayimitse kuyenda kwa nyenyezi?Kodi ungathe kuletsa kuyenda kwa nsangwe ndi akamwiniatsatana? 32 Kodi ungathe kuwongolera nyenyezi pa nyengo yakekapena kutsogolera nyenyezi yayikulu ya chimbalangondo pamodzi ndi ana ake? 33 Kodi malamulo a mlengalenga umawadziwa?Kodi ungathe kukhazikitsa ulamuliro wa Mulungu pa dziko lapansi? 34 “Kodi iwe ungathe kulamula mitambokuti igwetse mvula ya chigumula? 35 Kodi ungathe kutumiza zingʼaningʼani kuti zingʼanime?Kodi zimabwera pamaso pako ndi kuti, ‘Tili pano?’ 36 Kodi ndani anayika nzeru mu mtima,ndani analonga mʼmaganizo nzeru zomvetsa zinthu? 37 Wanzeru ndani amene angathe kuwerenga mitambo?Ndani angathe kupendeketsa mitsuko ya madzi akuthambo 38 pamene fumbi limasanduka matope,ndipo matopewo amawumbika? 39 “Kodi ndani amawusakira chakudya mkango waukazindi kukhutitsa misona ya mikango 40 pamene ili khale mʼmapanga mwawokapena pamene ikubisala pa tchire? 41 Kodi amamupatsa khwangwala chakudya chake ndanipamene ana ake akulirira kwa Mulungundi kumayendayenda chifukwa chosowa zakudya?

In Other Versions

Job 38 in the ANGEFD

Job 38 in the ANTPNG2D

Job 38 in the AS21

Job 38 in the BAGH

Job 38 in the BBPNG

Job 38 in the BBT1E

Job 38 in the BDS

Job 38 in the BEV

Job 38 in the BHAD

Job 38 in the BIB

Job 38 in the BLPT

Job 38 in the BNT

Job 38 in the BNTABOOT

Job 38 in the BNTLV

Job 38 in the BOATCB

Job 38 in the BOATCB2

Job 38 in the BOBCV

Job 38 in the BOCNT

Job 38 in the BOECS

Job 38 in the BOHCB

Job 38 in the BOHCV

Job 38 in the BOHLNT

Job 38 in the BOHNTLTAL

Job 38 in the BOICB

Job 38 in the BOILNTAP

Job 38 in the BOITCV

Job 38 in the BOKCV

Job 38 in the BOKCV2

Job 38 in the BOKHWOG

Job 38 in the BOKSSV

Job 38 in the BOLCB

Job 38 in the BOLCB2

Job 38 in the BOMCV

Job 38 in the BONAV

Job 38 in the BONCB

Job 38 in the BONLT

Job 38 in the BONUT2

Job 38 in the BOPLNT

Job 38 in the BOSCB

Job 38 in the BOSNC

Job 38 in the BOTLNT

Job 38 in the BOVCB

Job 38 in the BOYCB

Job 38 in the BPBB

Job 38 in the BPH

Job 38 in the BSB

Job 38 in the CCB

Job 38 in the CUV

Job 38 in the CUVS

Job 38 in the DBT

Job 38 in the DGDNT

Job 38 in the DHNT

Job 38 in the DNT

Job 38 in the ELBE

Job 38 in the EMTV

Job 38 in the ESV

Job 38 in the FBV

Job 38 in the FEB

Job 38 in the GGMNT

Job 38 in the GNT

Job 38 in the HARY

Job 38 in the HNT

Job 38 in the IRVA

Job 38 in the IRVB

Job 38 in the IRVG

Job 38 in the IRVH

Job 38 in the IRVK

Job 38 in the IRVM

Job 38 in the IRVM2

Job 38 in the IRVO

Job 38 in the IRVP

Job 38 in the IRVT

Job 38 in the IRVT2

Job 38 in the IRVU

Job 38 in the ISVN

Job 38 in the JSNT

Job 38 in the KAPI

Job 38 in the KBT1ETNIK

Job 38 in the KBV

Job 38 in the KJV

Job 38 in the KNFD

Job 38 in the LBA

Job 38 in the LBLA

Job 38 in the LNT

Job 38 in the LSV

Job 38 in the MAAL

Job 38 in the MBV

Job 38 in the MBV2

Job 38 in the MHNT

Job 38 in the MKNFD

Job 38 in the MNG

Job 38 in the MNT

Job 38 in the MNT2

Job 38 in the MRS1T

Job 38 in the NAA

Job 38 in the NASB

Job 38 in the NBLA

Job 38 in the NBS

Job 38 in the NBVTP

Job 38 in the NET2

Job 38 in the NIV11

Job 38 in the NNT

Job 38 in the NNT2

Job 38 in the NNT3

Job 38 in the PDDPT

Job 38 in the PFNT

Job 38 in the RMNT

Job 38 in the SBIAS

Job 38 in the SBIBS

Job 38 in the SBIBS2

Job 38 in the SBICS

Job 38 in the SBIDS

Job 38 in the SBIGS

Job 38 in the SBIHS

Job 38 in the SBIIS

Job 38 in the SBIIS2

Job 38 in the SBIIS3

Job 38 in the SBIKS

Job 38 in the SBIKS2

Job 38 in the SBIMS

Job 38 in the SBIOS

Job 38 in the SBIPS

Job 38 in the SBISS

Job 38 in the SBITS

Job 38 in the SBITS2

Job 38 in the SBITS3

Job 38 in the SBITS4

Job 38 in the SBIUS

Job 38 in the SBIVS

Job 38 in the SBT

Job 38 in the SBT1E

Job 38 in the SCHL

Job 38 in the SNT

Job 38 in the SUSU

Job 38 in the SUSU2

Job 38 in the SYNO

Job 38 in the TBIAOTANT

Job 38 in the TBT1E

Job 38 in the TBT1E2

Job 38 in the TFTIP

Job 38 in the TFTU

Job 38 in the TGNTATF3T

Job 38 in the THAI

Job 38 in the TNFD

Job 38 in the TNT

Job 38 in the TNTIK

Job 38 in the TNTIL

Job 38 in the TNTIN

Job 38 in the TNTIP

Job 38 in the TNTIZ

Job 38 in the TOMA

Job 38 in the TTENT

Job 38 in the UBG

Job 38 in the UGV

Job 38 in the UGV2

Job 38 in the UGV3

Job 38 in the VBL

Job 38 in the VDCC

Job 38 in the YALU

Job 38 in the YAPE

Job 38 in the YBVTP

Job 38 in the ZBP