Luke 6 (BOGWICC)

1 Tsiku lina la Sabata Yesu ankadutsa mʼminda yatirigu, ndipo ophunzira ake anayamba kubudula ngala zatirigu, namazifikisa mʼmanja mwawo ndi kumadya. 2 Ena mwa Afarisi anafunsa kuti, “Kodi nʼchifukwa chiyani mukuchita zosaloledwa pa tsiku la Sabata?” 3 Yesu anawayankha iwo kuti, “Kodi simunawerenge zimene Davide anachita pamene iye ndi anzake anali ndi njala? 4 Iye analowa mʼnyumba ya Mulungu ndipo atatenga buledi wopatulika anadya amene ndi ololedwa kudya ansembe okha. Ndipo anaperekanso wina kwa anzake.” 5 Kenaka Yesu anawawuza kuti, “Mwana wa Munthu ndi Ambuye wa Sabata.” 6 La Sabata lina Iye analowa mʼsunagoge kukaphunzitsa ndipo mʼmenemo anapeza munthu wadzanja lolumala. 7 Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo ankamuyangʼana kuti apeze chifukwa Yesu, choncho anamuyangʼanitsitsa kuti aone ngati Iye akanamuchiritsa pa Sabata. 8 Koma Yesu anadziwa zimene ankaganiza ndipo anati kwa munthu wadzanja lolumalayo, “Tanyamuka ndipo uyime patsogolo pa onsewa.” Choncho iye ananyamuka nayima pamenepo. 9 Kenaka Yesu anawawuza kuti, “Ndikufunseni, kodi chololedwa pa Sabata ndi chiti: kuchita chabwino kapena kuchita choyipa, kupulumutsa moyo kapena kuwononga?” 10 Iye atawayangʼana onsewo, anati kwa munthuyo, “Wongola dzanja lako.” Iye anaterodi, ndipo dzanja lake linachiritsidwa. 11 Koma iwo anapsa mtima nayamba kukambirana wina ndi mnzake chomwe akanamuchitira Yesu. 12 Tsiku lina, masiku amenewo, Yesu anapita ku phiri kukapemphera ndipo anakhala usiku wonse akupemphera kwa Mulungu. 13 Kutacha, anayitana ophunzira ake ndipo anasankha khumi ndi awiri a iwo amene anawayika kukhala atumwi: 14 Simoni (amene anamutcha Petro), mʼbale wake wa Andreya, Yakobo, Yohane, Filipo, Bartumeyu, 15 Mateyu, Tomasi, Yakobo mwana wa Alufeyo, Simoni amene amatchedwa Zaleti, 16 Yudasi mwana wa Yakobo ndi Yudasi Isikarioti amene anamupereka. 17 Iye anatsika pamodzi ndi atumwiwo ndipo anayima pamalo athyathyathya. Gulu lalikulu la ophunzira ake, gulu lalikulu la anthu ochokera ku Yudeya konse, ku Yerusalemu ndi ochokera mʼmphepete mwa nyanja ya Turo ndi Sidoni anali pomwepo. 18 Iwo anabwera kudzamvetsera ndi kuchiritsidwa ku matenda awo. Osautsidwa ndi mizimu yoyipa anachiritsidwa, 19 ndipo anthu ankayesetsa kuti amukhudze chifukwa mphamvu imatuluka mwa Iye ndi kuchiritsa onse. 20 Akuyangʼana ophunzira ake, Iye anati, “Odala ndinu amene ndi osauka, chifukwa ufumu wa Mulungu ndi wanu. 21 Inu amene mukumva njala tsopano, ndinu odala chifukwa mudzakhutitsidwa. Inu amene mukulira tsopano, ndinu odala chifukwa mudzasekerera. 22 Ndinu odala, anthu akamakudani, kukusalani ndi kukunyozani ndi kumayipitsa dzina lanu chifukwa cha Mwana wa Munthu. 23 “Nthawi imeneyo sangalalani ndipo lumphani ndi chimwemwe chifukwa mphotho yanu ndi yayikulu kumwamba. Pakuti ndi zomwezonso zimene makolo awo anachitira aneneri. 24 “Ndinu atsoka, anthu olemera, popeza mwalandiriratu zokusangalatsani. 25 Tsoka inu amene mukudya bwino tsopano, chifukwa mudzakhala ndi njala. Ndinu atsoka, amene mukusekerera tsopano, chifukwa mudzabuma ndi kulira. 26 Ndinu atsoka, anthu akamakuyamikirani, popeza makolo anu anawachitira aneneri onama zomwezi.” 27 “Koma Ine ndikuwuza inu amene mukundimva: Kondani adani anu, chitirani zabwino amene amakudani. 28 Dalitsani amene amakutembererani, apempherereni amene amakusautsani. 29 Ngati wina akumenyani patsaya limodzi mupatseninso tsaya linalo. Ngati wina akulanda mwinjiro wako, umulole atenge ndi mkanjo omwe. 30 Mupatseni aliyense amene akupemphani kanthu ndipo ngati wina atenga chinthu chanu, musamulamule kuti akubwezereni. 31 Inu muwachitire anthu ena, zomwe mukanafuna kuti iwo akuchitireni. 32 “Ngati mukonda okhawo amene amakukondani, mwapindula chiyani? Ngakhale ‘ochimwa’ amakonda amene amawakondanso. 33 Ndipo ngati muchita zabwino kwa amene ndi abwino kwa inu, mwapindula chiyani? Ngakhale ‘ochimwa’ amachita izi. 34 Ndipo ngati mukongoza amene mukuyembekeza kuti abweza, mwapindula chiyani? Ngakhale ‘ochimwa’ amabwereketsa kwa ochimwa anzawo, ndipo amayembekezera kubwezeredwa zonse. 35 Koma kondani adani anu, achitireni zabwino, akongozeni koma osayembekezera kulandira kanthu. Pamenepo mphotho yanu idzakhala yayikulu ndipo inu mudzakhala ana a Wammwambamwamba, chifukwa ndi wokoma mtima kwa anthu osayamika ndi oyipa. 36 Khalani achifundo, monga momwe Atate anu ali achifundo.” 37 “Musaweruze, ndipo inu simudzaweruzidwa. Musatsutse ndipo inu simudzatsutsidwa. Khululukirani ena ndipo mudzakhululukidwa. 38 Perekani ndipo mudzapatsidwa. Adzakupatsani mʼthumba mwanu muyeso wabwino, wotsenderezeka, wokhutchumuka ndi wosefukira. Pakuti muyeso umene mumagwiritsa ntchito, ndi omwewo adzakuyeserani.” 39 Iye anawawuzanso fanizo ili, “Kodi munthu wakhungu angatsogolere munthu wakhungu mnzake? Kodi onse sadzagwera mʼdzenje? 40 Wophunzira sangapose mphunzitsi wake, koma yense amene waphunzitsidwa bwinobwino adzakhala ngati mphunzitsi wake. 41 “Kodi ndi chifukwa chiyani mumaona kachitsotso mʼdiso la mʼbale wanu ndi kusasamala mtengo uli mʼdiso mwanu? 42 Kodi munganene bwanji kwa mʼbale wanu kuti, ‘Mʼbale nʼtakuchotsa kachitsotso mʼdiso mwako,’ pamene inu eni ake mukulephera kuona mtengo uli mʼdiso mwanu? Inu achiphamaso, yambani mwachotsa mtengo uli mʼdiso mwanu, ndipo kenaka mudzaona bwinobwino ndi kuchotsa kachitsotso mʼdiso la mʼbale wanu.” 43 Palibe mtengo wabwino umene umabala chipatso choyipa, kapena mtengo oyipa umene umabala chipatso chabwino. 44 Mtengo uliwonse umadziwika ndi chipatso chake. Anthu sathyola nkhuyu pa mtengo waminga, kapena mphesa pa nthungwi. 45 Munthu wabwino amatulutsa zinthu zabwino zosungidwa mu mtima mwake, koma munthu oyipa amatulutsa zinthu zoyipa zosungidwa mu mtima mwake. Pakamwa pake pamayankhula zimene zadzaza mu mtima mwake. 46 “Kodi nʼchifukwa chiyani munditchula kuti, ‘Ambuye, Ambuye’ koma simuchita zimene Ine ndinena? 47 Ine ndidzakuonetsani mmene alili munthu amene amabwera kwa Ine ndi kumva mawu anga ndi kuwachita. 48 Iye ali ngati munthu womanga nyumba, amene anakumba mozama nayika maziko ake pa mwala. Madzi osefukira atabwera ndi mphamvu, nawomba nyumbayo koma sinagwedezeka, chifukwa anayimanga bwino. 49 Koma amene amamva mawu anga koma osawachita, akufanana ndi munthu amene anamanga nyumba yake koma yopanda maziko. Nthawi yomwe madziwo anawomba nyumbayo, inagwa ndipo inawonongekeratu.”

In Other Versions

Luke 6 in the ANGEFD

Luke 6 in the ANTPNG2D

Luke 6 in the AS21

Luke 6 in the BAGH

Luke 6 in the BBPNG

Luke 6 in the BBT1E

Luke 6 in the BDS

Luke 6 in the BEV

Luke 6 in the BHAD

Luke 6 in the BIB

Luke 6 in the BLPT

Luke 6 in the BNT

Luke 6 in the BNTABOOT

Luke 6 in the BNTLV

Luke 6 in the BOATCB

Luke 6 in the BOATCB2

Luke 6 in the BOBCV

Luke 6 in the BOCNT

Luke 6 in the BOECS

Luke 6 in the BOHCB

Luke 6 in the BOHCV

Luke 6 in the BOHLNT

Luke 6 in the BOHNTLTAL

Luke 6 in the BOICB

Luke 6 in the BOILNTAP

Luke 6 in the BOITCV

Luke 6 in the BOKCV

Luke 6 in the BOKCV2

Luke 6 in the BOKHWOG

Luke 6 in the BOKSSV

Luke 6 in the BOLCB

Luke 6 in the BOLCB2

Luke 6 in the BOMCV

Luke 6 in the BONAV

Luke 6 in the BONCB

Luke 6 in the BONLT

Luke 6 in the BONUT2

Luke 6 in the BOPLNT

Luke 6 in the BOSCB

Luke 6 in the BOSNC

Luke 6 in the BOTLNT

Luke 6 in the BOVCB

Luke 6 in the BOYCB

Luke 6 in the BPBB

Luke 6 in the BPH

Luke 6 in the BSB

Luke 6 in the CCB

Luke 6 in the CUV

Luke 6 in the CUVS

Luke 6 in the DBT

Luke 6 in the DGDNT

Luke 6 in the DHNT

Luke 6 in the DNT

Luke 6 in the ELBE

Luke 6 in the EMTV

Luke 6 in the ESV

Luke 6 in the FBV

Luke 6 in the FEB

Luke 6 in the GGMNT

Luke 6 in the GNT

Luke 6 in the HARY

Luke 6 in the HNT

Luke 6 in the IRVA

Luke 6 in the IRVB

Luke 6 in the IRVG

Luke 6 in the IRVH

Luke 6 in the IRVK

Luke 6 in the IRVM

Luke 6 in the IRVM2

Luke 6 in the IRVO

Luke 6 in the IRVP

Luke 6 in the IRVT

Luke 6 in the IRVT2

Luke 6 in the IRVU

Luke 6 in the ISVN

Luke 6 in the JSNT

Luke 6 in the KAPI

Luke 6 in the KBT1ETNIK

Luke 6 in the KBV

Luke 6 in the KJV

Luke 6 in the KNFD

Luke 6 in the LBA

Luke 6 in the LBLA

Luke 6 in the LNT

Luke 6 in the LSV

Luke 6 in the MAAL

Luke 6 in the MBV

Luke 6 in the MBV2

Luke 6 in the MHNT

Luke 6 in the MKNFD

Luke 6 in the MNG

Luke 6 in the MNT

Luke 6 in the MNT2

Luke 6 in the MRS1T

Luke 6 in the NAA

Luke 6 in the NASB

Luke 6 in the NBLA

Luke 6 in the NBS

Luke 6 in the NBVTP

Luke 6 in the NET2

Luke 6 in the NIV11

Luke 6 in the NNT

Luke 6 in the NNT2

Luke 6 in the NNT3

Luke 6 in the PDDPT

Luke 6 in the PFNT

Luke 6 in the RMNT

Luke 6 in the SBIAS

Luke 6 in the SBIBS

Luke 6 in the SBIBS2

Luke 6 in the SBICS

Luke 6 in the SBIDS

Luke 6 in the SBIGS

Luke 6 in the SBIHS

Luke 6 in the SBIIS

Luke 6 in the SBIIS2

Luke 6 in the SBIIS3

Luke 6 in the SBIKS

Luke 6 in the SBIKS2

Luke 6 in the SBIMS

Luke 6 in the SBIOS

Luke 6 in the SBIPS

Luke 6 in the SBISS

Luke 6 in the SBITS

Luke 6 in the SBITS2

Luke 6 in the SBITS3

Luke 6 in the SBITS4

Luke 6 in the SBIUS

Luke 6 in the SBIVS

Luke 6 in the SBT

Luke 6 in the SBT1E

Luke 6 in the SCHL

Luke 6 in the SNT

Luke 6 in the SUSU

Luke 6 in the SUSU2

Luke 6 in the SYNO

Luke 6 in the TBIAOTANT

Luke 6 in the TBT1E

Luke 6 in the TBT1E2

Luke 6 in the TFTIP

Luke 6 in the TFTU

Luke 6 in the TGNTATF3T

Luke 6 in the THAI

Luke 6 in the TNFD

Luke 6 in the TNT

Luke 6 in the TNTIK

Luke 6 in the TNTIL

Luke 6 in the TNTIN

Luke 6 in the TNTIP

Luke 6 in the TNTIZ

Luke 6 in the TOMA

Luke 6 in the TTENT

Luke 6 in the UBG

Luke 6 in the UGV

Luke 6 in the UGV2

Luke 6 in the UGV3

Luke 6 in the VBL

Luke 6 in the VDCC

Luke 6 in the YALU

Luke 6 in the YAPE

Luke 6 in the YBVTP

Luke 6 in the ZBP