Matthew 19 (BOGWICC)

1 Yesu atatsiriza kunena zinthu zimenezi, anachoka ku Galileya ndi kupita ku chigawo cha Yudeya mbali ina ya mtsinje wa Yorodani. 2 Magulu akulu a anthu anamutsatira Iye, ndipo iwo anachiritsidwa pomwepo. 3 Afarisi ena anabwera kwa Iye kudzamuyesa. Anamufunsa Iye nati, “Kodi ndikololedwa kuti mwamuna amuleke mkazi wake pa chifukwa china chilichonse?” 4 Iye anayankha kuti, “Kodi simunawerenge kuti pachiyambi Mulungu analenga iwo, ‘mwamuna ndi mkazi?’ 5 Ndipo anati, ‘Pa chifukwa ichi mwamuna adzasiya abambo ake ndi amayi ake nakaphatikana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi.’ 6 Motero salinso awiri ayi koma mmodzi. Nʼchifukwa chake chimene Mulungu wachimanga pamodzi munthu wina asachilekanitse.” 7 Ndipo iwo anamufunsa nati, “Nanga nʼchifukwa chiyani Mose analamula kuti mwamuna azipatsa mkazi wake kalata ya chisudzulo ndi kumuchotsa?” 8 Yesu anayankha kuti, “Mose anakulolezani kuti muzisudzula akazi anu chifukwa cha kuwuma mitima kwanu. Koma sizinali chotere kuyambira pachiyambi. 9 Ine ndikuwuzani kuti aliyense amene asudzula mkazi wake, osati chifukwa cha chiwerewere nakakwatira mkazi wina, achita chigololo.” 10 Ophunzira ake anati kwa Iye, “Ngati umu ndi mmene zilili pa mwamuna ndi mkazi, kuli bwino kusakwatira.” 11 Yesu anayankha kuti, “Si aliyense amene angavomere chiphunzitso ichi, koma kwa okhawo amene achimvetsetsa. 12 Pakuti ena ndi akuti sangakwatire chifukwa anabadwa motero, ena ali motero chifukwa chofulidwa ndi anthu ndipo ena anawukana ukwati chifukwa cha ufumu wakumwamba. Iye amene angalandire ichi alandire.” 13 Pamenepo anabwera nawo ana kwa Yesu kuti awasanjike manja ndi kuwapempherera. Koma ophunzira ake anadzudzula amene anabweretsa anawo. 14 Yesu anati, “Lolani ana abwere kwa Ine, ndipo musawaletse pakuti ufumu wakumwamba ndi wa iwo onga anawa.” 15 Atasanjika manja ake pa anawo, anachokapo. 16 Taonani mnyamata wina anabwera kwa Yesu namufunsa kuti, “Aphunzitsi, ndi chinthu chiti chabwino chimene ndiyenera kuchita kuti ndipeze moyo wosatha?” 17 Yesu anayankha kuti, “Ukundifunsiranji Ine za chinthu chimene ndi chabwino? Pali mmodzi yekha amene ndi wabwino. Ngati ukufuna kulowa mʼmoyo wosatha mvera malamulo.” 18 Mnyamatayo anamufunsa kuti, “Ndi ati?”Yesu anayankha kuti, “Usaphe, usachite chigololo, usabe, usapereke umboni onama, 19 lemekeza abambo ako ndi amayi ako ndipo konda mnansi wako monga iwe mwini.” 20 Mnyamatayo anati, “Zonsezi ndimazisunga, nanga chatsala ndi chiyani?” 21 Yesu anayankha kuti, “Ngati ukufuna kukhala wangwiro, pita kagulitse katundu wako ndi kupereka kwa osauka, ndipo udzakhala ndi chuma kumwamba. Ukakachita zimenezi, ukabwere udzanditsate Ine.” 22 Mnyamatayo atamva zimenezi, anachoka mokhumudwa, chifukwa anali ndi chuma chambiri. 23 Pamenepo Yesu anati kwa ophunzira ake, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti nʼkovuta kuti olemera akalowe mu ufumu wakumwamba. 24 Komanso ndikuwuzani kuti, nʼkwapafupi kuti ngamira idzere pa kabowo ka zingano kusiyana ndi kuti wolemera akalowe mu ufumu wa Mulungu.” 25 Ophunzira atamva zimenezi, anadabwa kwambiri ndipo anamufunsa kuti, “Nanga angapulumuke ndani?” 26 Yesu anawayangʼana iwo nati, “Ndi anthu, izi nʼzosatheka, koma ndi Mulungu zinthu zonse zimatheka.” 27 Petro anamuyankha Iye kuti, “Ife tinasiya zonse ndi kukutsatirani Inu! Nanga tsono ife tidzalandira chiyani?” 28 Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti pa nthawi yokonzanso zinthu zonse, pamene Mwana wa Munthu adzakhala pa mpando wake waufumu mu ulemerero wake kumwamba, inu amene mwanditsata Ine mudzakhalanso pa mipando khumi ndi iwiri yaufumu, kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israeli. 29 Ndipo aliyense amene wasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena bambo kapena mayi kapena mkazi, kapena ana, kapena minda chifukwa cha Ine adzalandira madalitso ochuluka ndi kulandiranso moyo wosatha. 30 Koma ambiri amene ali oyambirira adzakhala omalizira, ndipo ambiri amene ndi omalizira adzakhala oyambirira.”

In Other Versions

Matthew 19 in the ANGEFD

Matthew 19 in the ANTPNG2D

Matthew 19 in the AS21

Matthew 19 in the BAGH

Matthew 19 in the BBPNG

Matthew 19 in the BBT1E

Matthew 19 in the BDS

Matthew 19 in the BEV

Matthew 19 in the BHAD

Matthew 19 in the BIB

Matthew 19 in the BLPT

Matthew 19 in the BNT

Matthew 19 in the BNTABOOT

Matthew 19 in the BNTLV

Matthew 19 in the BOATCB

Matthew 19 in the BOATCB2

Matthew 19 in the BOBCV

Matthew 19 in the BOCNT

Matthew 19 in the BOECS

Matthew 19 in the BOHCB

Matthew 19 in the BOHCV

Matthew 19 in the BOHLNT

Matthew 19 in the BOHNTLTAL

Matthew 19 in the BOICB

Matthew 19 in the BOILNTAP

Matthew 19 in the BOITCV

Matthew 19 in the BOKCV

Matthew 19 in the BOKCV2

Matthew 19 in the BOKHWOG

Matthew 19 in the BOKSSV

Matthew 19 in the BOLCB

Matthew 19 in the BOLCB2

Matthew 19 in the BOMCV

Matthew 19 in the BONAV

Matthew 19 in the BONCB

Matthew 19 in the BONLT

Matthew 19 in the BONUT2

Matthew 19 in the BOPLNT

Matthew 19 in the BOSCB

Matthew 19 in the BOSNC

Matthew 19 in the BOTLNT

Matthew 19 in the BOVCB

Matthew 19 in the BOYCB

Matthew 19 in the BPBB

Matthew 19 in the BPH

Matthew 19 in the BSB

Matthew 19 in the CCB

Matthew 19 in the CUV

Matthew 19 in the CUVS

Matthew 19 in the DBT

Matthew 19 in the DGDNT

Matthew 19 in the DHNT

Matthew 19 in the DNT

Matthew 19 in the ELBE

Matthew 19 in the EMTV

Matthew 19 in the ESV

Matthew 19 in the FBV

Matthew 19 in the FEB

Matthew 19 in the GGMNT

Matthew 19 in the GNT

Matthew 19 in the HARY

Matthew 19 in the HNT

Matthew 19 in the IRVA

Matthew 19 in the IRVB

Matthew 19 in the IRVG

Matthew 19 in the IRVH

Matthew 19 in the IRVK

Matthew 19 in the IRVM

Matthew 19 in the IRVM2

Matthew 19 in the IRVO

Matthew 19 in the IRVP

Matthew 19 in the IRVT

Matthew 19 in the IRVT2

Matthew 19 in the IRVU

Matthew 19 in the ISVN

Matthew 19 in the JSNT

Matthew 19 in the KAPI

Matthew 19 in the KBT1ETNIK

Matthew 19 in the KBV

Matthew 19 in the KJV

Matthew 19 in the KNFD

Matthew 19 in the LBA

Matthew 19 in the LBLA

Matthew 19 in the LNT

Matthew 19 in the LSV

Matthew 19 in the MAAL

Matthew 19 in the MBV

Matthew 19 in the MBV2

Matthew 19 in the MHNT

Matthew 19 in the MKNFD

Matthew 19 in the MNG

Matthew 19 in the MNT

Matthew 19 in the MNT2

Matthew 19 in the MRS1T

Matthew 19 in the NAA

Matthew 19 in the NASB

Matthew 19 in the NBLA

Matthew 19 in the NBS

Matthew 19 in the NBVTP

Matthew 19 in the NET2

Matthew 19 in the NIV11

Matthew 19 in the NNT

Matthew 19 in the NNT2

Matthew 19 in the NNT3

Matthew 19 in the PDDPT

Matthew 19 in the PFNT

Matthew 19 in the RMNT

Matthew 19 in the SBIAS

Matthew 19 in the SBIBS

Matthew 19 in the SBIBS2

Matthew 19 in the SBICS

Matthew 19 in the SBIDS

Matthew 19 in the SBIGS

Matthew 19 in the SBIHS

Matthew 19 in the SBIIS

Matthew 19 in the SBIIS2

Matthew 19 in the SBIIS3

Matthew 19 in the SBIKS

Matthew 19 in the SBIKS2

Matthew 19 in the SBIMS

Matthew 19 in the SBIOS

Matthew 19 in the SBIPS

Matthew 19 in the SBISS

Matthew 19 in the SBITS

Matthew 19 in the SBITS2

Matthew 19 in the SBITS3

Matthew 19 in the SBITS4

Matthew 19 in the SBIUS

Matthew 19 in the SBIVS

Matthew 19 in the SBT

Matthew 19 in the SBT1E

Matthew 19 in the SCHL

Matthew 19 in the SNT

Matthew 19 in the SUSU

Matthew 19 in the SUSU2

Matthew 19 in the SYNO

Matthew 19 in the TBIAOTANT

Matthew 19 in the TBT1E

Matthew 19 in the TBT1E2

Matthew 19 in the TFTIP

Matthew 19 in the TFTU

Matthew 19 in the TGNTATF3T

Matthew 19 in the THAI

Matthew 19 in the TNFD

Matthew 19 in the TNT

Matthew 19 in the TNTIK

Matthew 19 in the TNTIL

Matthew 19 in the TNTIN

Matthew 19 in the TNTIP

Matthew 19 in the TNTIZ

Matthew 19 in the TOMA

Matthew 19 in the TTENT

Matthew 19 in the UBG

Matthew 19 in the UGV

Matthew 19 in the UGV2

Matthew 19 in the UGV3

Matthew 19 in the VBL

Matthew 19 in the VDCC

Matthew 19 in the YALU

Matthew 19 in the YAPE

Matthew 19 in the YBVTP

Matthew 19 in the ZBP