Mark 1 (BOGWICC)

1 Chiyambi cha Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu, 2 monga zalembedwera mʼbuku la mneneri Yesaya:“Ine ndidzatuma mthenga wanga patsogolo panu,amene adzakonza njira yanu,” 3 “Mawu a wofuwula mʼchipululu,‘Konzani njira ya Ambuye,wongolani njira zake.’ ” 4 Ndipo Yohane anabwera mʼmadera a mʼchipululu nabatiza, ndi kulalikira za ubatizo wa kutembenuka mtima ndi wa chikhululukiro cha machimo. 5 Madera onse a ku Yudeya ndi anthu onse a ku Yerusalemu anatuluka napita kwa iye. Akavomereza machimo awo, amawabatiza mu mtsinje wa Yorodani. 6 Yohane amavala zovala zopangidwa ndi ubweya wangamira, ndi lamba wachikopa mʼchiwuno mwake, ndipo amadya dzombe ndi uchi wamthengo. 7 Ndipo uthenga wake unali uwu: “Pambuyo panga pakubwera wina wondiposa ine mphamvu. Ine si woyenera kuwerama ndi kumasula zingwe za nsapato zake. 8 Ine ndikubatizani ndi madzi, koma Iye adzakubatizani ndi Mzimu Woyera.” 9 Pa nthawi imeneyo Yesu anabwera kuchokera ku Nazareti wa ku Galileya ndipo anabatizidwa ndi Yohane mu mtsinje wa Yorodani. 10 Pamene Yesu ankatuluka mʼmadzi, anaona kumwamba kukutsekuka ndipo Mzimu Woyera akutsikira pa Iye ngati nkhunda. 11 Ndipo Mawu anamveka kuchokera kumwamba: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa; ndipo ndikondwera nawe.” 12 Nthawi yomweyo Mzimu Woyera anamutumiza Iye ku chipululu, 13 ndipo anali mʼchipululumo masiku makumi anayi, akuyesedwa ndi Satana. Anali pakati pa nyama zakuthengo; ndipo angelo anamutumikira. 14 Yohane atamutsekera mʼndende, Yesu anapita ku Galileya nalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu nati, 15 “Nthawi yafika, ufumu wa Mulungu wayandikira. Tembenukani mtima ndi kukhulupirira Uthenga Wabwino!” 16 Pamene Yesu ankayenda mʼmbali mwa nyanja ya Galileya, anaona Simoni ndi mʼbale wake Andreya akuponya khoka mʼnyanja, popeza anali asodzi. 17 Yesu anati, “Bwerani, tsateni Ine, ndipo ndidzakusandutsani asodzi a anthu.” 18 Nthawi yomweyo anasiya makoka awo namutsata Iye. 19 Atapita patsogolo pangʼono, anaona Yakobo ndi mʼbale wake Yohane ana a Zebedayo, ali mʼbwato akukonza makoka awo. 20 Mosataya nthawi anawayitana, ndipo anasiya abambo awo Zebedayo ndi anyamata aganyu ali mʼbwatomo, namutsata Iye. 21 Iwo anapita ku Kaperenawo, ndipo tsiku la Sabata litafika, Yesu analowa mʼsunagoge nayamba kuphunzitsa. 22 Anthu anadabwa ndi chiphunzitso chake, chifukwa anawaphunzitsa ngati munthu amene anali ndi ulamuliro, osati ngati aphunzitsi amalamulo. 23 Pomwepo munthu wina mʼsunagogemo amene anali wogwidwa ndi mzimu woyipa anafuwula kuti, 24 “Mukufuna chiyani kwa ife, Yesu wa ku Nazareti? Kodi mwabwera kudzatiwononga? Ndikudziwa kuti ndinu ndani, ndinu Woyerayo wa Mulungu!” 25 Yesu anadzudzula chiwandacho mwamphamvu nati, “Khala chete! Tuluka mwa iye!” 26 Mzimu woyipawo unamugwedeza mwamphamvu ndipo unatuluka mwa iye ukufuwula. 27 Anthu anadabwa kwambiri kotero kuti anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Ichi nʼchiyani? Chiphunzitso chatsopano ndi ulamuliro! Iye akulamula, ngakhale mizimu yoyipa ikumumvera.” 28 Mbiri yake inafalikira kudera lonse la Galileya mofulumira. 29 Atangochoka mu sunagoge, Yesu pamodzi ndi Yakobo ndi Yohane anakalowa mʼnyumba ya Simoni ndi Andreya. 30 Mpongozi wa Simoni anali chigonere akudwala malungo, ndipo anamuwuza Yesu za iye. 31 Ndipo Yesu anapita kwa iye, namugwira dzanja namuthandiza kudzuka. Malungo anachoka ndipo anayamba kuwatumikira. 32 Madzulo omwewo dzuwa litalowa anthu anabweretsa kwa Yesu anthu onse odwala ndi ogwidwa ndi ziwanda. 33 Anthu onse a mʼmudzimo anasonkhana pa khomo, 34 Yesu anachiritsa ambiri amene anali ndi matenda osiyanasiyana, komanso anatulutsa ziwanda zambiri, ndipo sanalole kuti ziwandazo ziyankhule chifukwa zinkamudziwa Iye. 35 Mmamawa, kukanali kamdima, Yesu anadzuka, nachoka pa nyumbapo kupita kumalo kwa yekha, kumene anakapemphera. 36 Simoni ndi anzake anapita kokamufunafuna Iye, 37 ndipo atamupeza, anamuwuza kuti, “Aliyense akukufunani!” 38 Yesu anayakha kuti, “Tiyeni tipite kwina ku midzi ya pafupi kuti ndikalalikirenso kumeneko. Ichi ndi chifukwa chimene ndinabwerera.” 39 Potero anayendayenda mu Galileya, kulalikira mʼmasunagoge awo ndi kutulutsa ziwanda. 40 Munthu wakhate anabwera kwa Iye, nagwada, namupempha kuti, “Ngati mukufuna, mukhoza kundiyeretsa.” 41 Yesu pomva naye chifundo, anatambasula dzanja lake namukhudza munthuyo nati, “Ndikufuna, yeretsedwa!” 42 Nthawi yomweyo khate linachoka ndipo anachiritsidwa. 43 Nthawi yomweyo Yesu anamuwuza kuti apite koma anamuchenjeza kuti, 44 “Wonetsetsa kuti usawuze aliyense za zimenezi. Koma pita, kadzionetse wekha kwa wansembe ndi kukapereka nsembe zimene Mose analamulira zotsimikizira kuyeretsedwa kwanu, ngati umboni kwa iwo.” 45 Mʼmalo mwake anapita nayamba kuyankhula momasuka, nafalitsa mbiriyo. Zotsatira zake, Yesu sanathe kulowa mʼmudzi moonekera, koma anakhala kunja kumalo kopanda anthu. Komabe anthu amabwera kwa Iye kuchokera kulikonse.

In Other Versions

Mark 1 in the ANGEFD

Mark 1 in the ANTPNG2D

Mark 1 in the AS21

Mark 1 in the BAGH

Mark 1 in the BBPNG

Mark 1 in the BBT1E

Mark 1 in the BDS

Mark 1 in the BEV

Mark 1 in the BHAD

Mark 1 in the BIB

Mark 1 in the BLPT

Mark 1 in the BNT

Mark 1 in the BNTABOOT

Mark 1 in the BNTLV

Mark 1 in the BOATCB

Mark 1 in the BOATCB2

Mark 1 in the BOBCV

Mark 1 in the BOCNT

Mark 1 in the BOECS

Mark 1 in the BOHCB

Mark 1 in the BOHCV

Mark 1 in the BOHLNT

Mark 1 in the BOHNTLTAL

Mark 1 in the BOICB

Mark 1 in the BOILNTAP

Mark 1 in the BOITCV

Mark 1 in the BOKCV

Mark 1 in the BOKCV2

Mark 1 in the BOKHWOG

Mark 1 in the BOKSSV

Mark 1 in the BOLCB

Mark 1 in the BOLCB2

Mark 1 in the BOMCV

Mark 1 in the BONAV

Mark 1 in the BONCB

Mark 1 in the BONLT

Mark 1 in the BONUT2

Mark 1 in the BOPLNT

Mark 1 in the BOSCB

Mark 1 in the BOSNC

Mark 1 in the BOTLNT

Mark 1 in the BOVCB

Mark 1 in the BOYCB

Mark 1 in the BPBB

Mark 1 in the BPH

Mark 1 in the BSB

Mark 1 in the CCB

Mark 1 in the CUV

Mark 1 in the CUVS

Mark 1 in the DBT

Mark 1 in the DGDNT

Mark 1 in the DHNT

Mark 1 in the DNT

Mark 1 in the ELBE

Mark 1 in the EMTV

Mark 1 in the ESV

Mark 1 in the FBV

Mark 1 in the FEB

Mark 1 in the GGMNT

Mark 1 in the GNT

Mark 1 in the HARY

Mark 1 in the HNT

Mark 1 in the IRVA

Mark 1 in the IRVB

Mark 1 in the IRVG

Mark 1 in the IRVH

Mark 1 in the IRVK

Mark 1 in the IRVM

Mark 1 in the IRVM2

Mark 1 in the IRVO

Mark 1 in the IRVP

Mark 1 in the IRVT

Mark 1 in the IRVT2

Mark 1 in the IRVU

Mark 1 in the ISVN

Mark 1 in the JSNT

Mark 1 in the KAPI

Mark 1 in the KBT1ETNIK

Mark 1 in the KBV

Mark 1 in the KJV

Mark 1 in the KNFD

Mark 1 in the LBA

Mark 1 in the LBLA

Mark 1 in the LNT

Mark 1 in the LSV

Mark 1 in the MAAL

Mark 1 in the MBV

Mark 1 in the MBV2

Mark 1 in the MHNT

Mark 1 in the MKNFD

Mark 1 in the MNG

Mark 1 in the MNT

Mark 1 in the MNT2

Mark 1 in the MRS1T

Mark 1 in the NAA

Mark 1 in the NASB

Mark 1 in the NBLA

Mark 1 in the NBS

Mark 1 in the NBVTP

Mark 1 in the NET2

Mark 1 in the NIV11

Mark 1 in the NNT

Mark 1 in the NNT2

Mark 1 in the NNT3

Mark 1 in the PDDPT

Mark 1 in the PFNT

Mark 1 in the RMNT

Mark 1 in the SBIAS

Mark 1 in the SBIBS

Mark 1 in the SBIBS2

Mark 1 in the SBICS

Mark 1 in the SBIDS

Mark 1 in the SBIGS

Mark 1 in the SBIHS

Mark 1 in the SBIIS

Mark 1 in the SBIIS2

Mark 1 in the SBIIS3

Mark 1 in the SBIKS

Mark 1 in the SBIKS2

Mark 1 in the SBIMS

Mark 1 in the SBIOS

Mark 1 in the SBIPS

Mark 1 in the SBISS

Mark 1 in the SBITS

Mark 1 in the SBITS2

Mark 1 in the SBITS3

Mark 1 in the SBITS4

Mark 1 in the SBIUS

Mark 1 in the SBIVS

Mark 1 in the SBT

Mark 1 in the SBT1E

Mark 1 in the SCHL

Mark 1 in the SNT

Mark 1 in the SUSU

Mark 1 in the SUSU2

Mark 1 in the SYNO

Mark 1 in the TBIAOTANT

Mark 1 in the TBT1E

Mark 1 in the TBT1E2

Mark 1 in the TFTIP

Mark 1 in the TFTU

Mark 1 in the TGNTATF3T

Mark 1 in the THAI

Mark 1 in the TNFD

Mark 1 in the TNT

Mark 1 in the TNTIK

Mark 1 in the TNTIL

Mark 1 in the TNTIN

Mark 1 in the TNTIP

Mark 1 in the TNTIZ

Mark 1 in the TOMA

Mark 1 in the TTENT

Mark 1 in the UBG

Mark 1 in the UGV

Mark 1 in the UGV2

Mark 1 in the UGV3

Mark 1 in the VBL

Mark 1 in the VDCC

Mark 1 in the YALU

Mark 1 in the YAPE

Mark 1 in the YBVTP

Mark 1 in the ZBP