Mark 6 (BOGWICC)

1 Yesu anachoka kumeneko napita ku mudzi kwawo, pamodzi ndi ophunzira ake. 2 Tsiku la Sabata litafika, anayamba kuphunzitsa mʼsunagoge, ndipo ambiri amene anamumva anadabwa.Iwo anafunsa kuti, “Kodi munthu uyu anazitenga kuti zimenezi? Kodi ndi nzeru yotani imene munthu ameneyu wapatsidwa, kuti Iye akuchitanso zodabwitsa! 3 Kodi uyu si mpalamatabwa uja? Kodi uyu si mwana wa Mariya ndi mʼbale wa Yakobo, Yose, Yudasi ndi Simoni? Kodi alongo ake si ali ndi ife?” Ndipo anakhumudwa naye. 4 Yesu anawawuza kuti, “Mneneri amalemekezedwa kulikonse kupatula kwawo, ndi pakati pa abale ake ndi a mʼbanja mwake.” 5 Sanachite zodabwitsa kumeneko, koma anangosanjika manja pa odwala ochepa ndi kuwachiritsa. 6 Ndipo Iye anadabwa chifukwa chakusowa chikhulupiriro kwawo.Pamenepo Yesu anayenda mudzi ndi mudzi kuphunzitsa. 7 Atayitana khumi ndi awiriwo, Iye anawatuma awiriawiri ndipo anawapatsa ulamuliro pa mizimu yoyipa. 8 Zomwe anawalangiza ndi izi: “Musatenge kanthu ka paulendo koma ndodo yokha; osatenga buledi, thumba, kapena ndalama. 9 Muvale nsapato koma osatenga malaya apadera. 10 Pamene mulowa mʼnyumba mukakhale momwemo kufikira mutachoka mʼmudzimo. 11 Ndipo ngati pa malo ena sakakulandirani kapena kukumverani, sasani fumbi la kumapazi anu pamene mukuchoka, kuti ukhale umboni wowatsutsa.” 12 Anatuluka kupita kukalalikira kuti anthu atembenuke mtima. 13 Anatulutsa ziwanda zambiri ndi kudzoza mafuta odwala ambiri ndi kuwachiritsa. 14 Mfumu Herode anamva zimenezi, pakuti dzina la Yesu linali litadziwika kwambiri. Ena amati, “Yohane Mʼbatizi waukitsidwa kwa akufa, ndipo nʼchifukwa chake mphamvu zochita zodabwitsa zinkagwira ntchito mwa Iye.” 15 Ena anati, “Iye ndi Eliya.”Enanso anati, “Ndi mneneri, ofanana ndi mmodzi wa aneneri akale.” 16 Koma Herode atamva zimenezi anati, “Yohane, munthu amene ndinamudula mutu, waukitsidwa kuchokera kwa akufa.” 17 Pakuti Herode iye mwini analamula kuti amumange Yohane ndi kumuyika mʼndende. Anachita izi chifukwa cha Herodia, mkazi wa mʼbale wake Filipo, amene iye anamukwatira. 18 Pakuti Yohane ankanena kwa Herode kuti, “Sikololedwa kwa inu kuti mukwatire mkazi wa mʼbale wanu.” 19 Ndipo Herodia anamusungira Yohane chidani ndipo anafuna kumupha, koma sanathe kutero, 20 chifukwa Herode anaopa Yohane ndipo anamuteteza, podziwa kuti iye anali munthu wolungama ndi woyera mtima. Herode akamamva Yohane, ankathedwa nzeru; komabe amakonda kumumvetsera. 21 Pomaliza mpata unapezeka. Pa tsiku lokumbukira kubadwa kwake, Herode anakonzera phwando akuluakulu ake, akulu a ankhondo ndi anthu odziwika a mu Galileya. 22 Mwana wamkazi wa Herodia atabwera ndi kudzavina, anakondweretsa Herode ndi alendo ake a pa mphwandopo.Mfumu inati kwa mtsikanayo, “Undipemphe chilichonse chimene ukuchifuna, ndipo ndidzakupatsa.” 23 Ndipo analonjeza ndi lumbiriro kuti, “Chilichonse chimene upempha ndidzakupatsa, ngakhale theka la ufumu wanga.” 24 Iye anatuluka nati kwa amayi ake, “Kodi ndikapemphe chiyani?”Iye anamuyankha kuti, “Mutu wa Yohane Mʼbatizi.” 25 Nthawi yomweyo mtsikana uja anafulumira kupita komwe kunali mfumu ndi pempho lake: “Ndikufuna kuti mundipatse pomwe pano mutu wa Yohane Mʼbatizi mʼmbale.” 26 Mfumu inamva chisoni chachikulu, koma chifukwa cha lumbiro lake ndi alendo ake a pa mphwandolo, sanafune kumukaniza. 27 Nthawi yomweyo iye anatumiza yemwe anali ndi ulamuliro wonyonga anthu kuti abweretse mutu wa Yohane. Munthuyo anapita, nakadula mutu wa Yohane mʼndende, 28 nabweretsa mutuwo mʼmbale. Anawupereka kwa mtsikanayo, ndipo iye anakapereka kwa amayi ake. 29 Atamva izi, ophunzira a Yohane anabwera nadzatenga mtembo ndi kukawuyika mʼmanda. 30 Atumwi anasonkhana mozungulira Yesu namufotokozera zonse zomwe anachita ndi kuphunzitsa. 31 Popeza kuti panali anthu ambiri amene amabwera ndi kumapita, analibe mpata wakuti adye, ndipo Iye anawawuza kuti, “Tiyeni kuno kumalo achete kuti tikapume.” 32 Ndipo anachoka okha pa bwato napita kumalo a okhaokha. 33 Koma ambiri amene anawaona akuchoka anawazindikira ndipo anathamanga wapansi kuchokera mʼmidzi yonse nakayambirira kufika. 34 Yesu atafika ku mtunda ndi kuona gulu lalikulu la anthu, anamva nawo chisoni chifukwa anali ngati nkhosa zopanda mʼbusa. Ndipo anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri. 35 Pa nthawi iyi nʼkuti dzuwa litapendeka, ndipo ophunzira ake anabwera kwa Iye nati, “Kuno ndi kuthengo, ndipo ano ndi madzulo. 36 Awuzeni anthuwa azipita ku midzi ndi madera ozungulira, kuti akadzigulire kanthu kakuti adye.” 37 Koma Iye anayankha kuti, “Apatseni kanthu koti adye.”Iwo anati kwa Iye, “Apa pafunika ndalama za miyezi isanu ndi itatu zomwe munthu amalandira! Kodi tipite kukagwiritsa ntchito ndalama zotere kugulira buledi kuti tiwapatse adye?” 38 Iye anawafunsa kuti, “Muli ndi malofu a buledi angati? Pitani mukaone.”Ataona anati kwa Iye, “Asanu ndi nsomba ziwiri.” 39 Pamenepo Yesu anawalamulira kuti awakhazike anthu pansi mʼmagulu pa msipu obiriwira. 40 Ndipo anakhala pansi mʼmagulu a anthu 100 ndi gulu la anthu makumi asanu. 41 Atatenga malofu a buledi asanu ndi nsomba ziwiri, nayangʼana kumwamba, Iye anayamika nagawa malofu a bulediwo. Kenaka anawapatsa ophunzira ake kuti awapatse anthu. Ndipo anagawanso nsomba ziwirizo kwa onse. 42 Onse anadya ndipo anakhuta, 43 ndipo ophunzira ake anatola buledi ndi nsomba zotsalira zokwanira madengu khumi ndi awiri. 44 Chiwerengero cha amuna amene anadya chinali 5,000. 45 Nthawi yomweyo Yesu anawuza ophunzira ake kuti alowe mʼbwato ndi kuti atsogole kupita ku Betisaida, pamene Iye ankawuza anthu kuti azipita. 46 Atawasiya, Iye anakwera ku phiri kukapemphera. 47 Pofika madzulo, bwato linali pakati pa nyanja, ndipo Iye anali yekha pa mtunda. 48 Iye anaona ophunzira ake akuvutika popalasa bwato, chifukwa mphepo imawomba mokumana nawo. Pa nthawi ya mʼbandakucha Iye anafika kwa iwo akuyenda pa nyanja. Anali pafupi kuwapitirira, 49 koma atamuona Iye akuyenda pa nyanja, anaganiza kuti anali mzukwa. Iwo anafuwula, 50 pakuti onse anamuona ndipo anachita mantha.Nthawi yomweyo Iye anawayankhula nati, “Limbani mtima! Ndine. Musachite mantha.” 51 Ndipo Iye anakwera mʼbwato pamodzi nawo, ndipo mphepo inaleka. Iwo anadabwa kwambiri, 52 popeza sanazindikire zimene zinachitika pa malofu a buledi; pakuti mitima yawo inali yowuma. 53 Atawoloka, anafika ku Genesareti nayima pa dooko. 54 Atangotuluka mʼbwato, anthu anamuzindikira Yesu. 55 Anathamanga uku ndi uko mʼdera lonse nakanyamula odwala pa machira kupita nawo kulikonse kumene anamva kuti kuli Iye. 56 Ndipo kulikonse kumene anapita, ku midzi, mʼmizinda ndi madera a ku midzi, iwo anayika odwala mʼmalo a mʼmisika. Iwo anamupempha kuti awalole kuti akhudze ngakhale mphonje za mkanjo wake, ndipo onse amene anamukhudza anachira.

In Other Versions

Mark 6 in the ANGEFD

Mark 6 in the ANTPNG2D

Mark 6 in the AS21

Mark 6 in the BAGH

Mark 6 in the BBPNG

Mark 6 in the BBT1E

Mark 6 in the BDS

Mark 6 in the BEV

Mark 6 in the BHAD

Mark 6 in the BIB

Mark 6 in the BLPT

Mark 6 in the BNT

Mark 6 in the BNTABOOT

Mark 6 in the BNTLV

Mark 6 in the BOATCB

Mark 6 in the BOATCB2

Mark 6 in the BOBCV

Mark 6 in the BOCNT

Mark 6 in the BOECS

Mark 6 in the BOHCB

Mark 6 in the BOHCV

Mark 6 in the BOHLNT

Mark 6 in the BOHNTLTAL

Mark 6 in the BOICB

Mark 6 in the BOILNTAP

Mark 6 in the BOITCV

Mark 6 in the BOKCV

Mark 6 in the BOKCV2

Mark 6 in the BOKHWOG

Mark 6 in the BOKSSV

Mark 6 in the BOLCB

Mark 6 in the BOLCB2

Mark 6 in the BOMCV

Mark 6 in the BONAV

Mark 6 in the BONCB

Mark 6 in the BONLT

Mark 6 in the BONUT2

Mark 6 in the BOPLNT

Mark 6 in the BOSCB

Mark 6 in the BOSNC

Mark 6 in the BOTLNT

Mark 6 in the BOVCB

Mark 6 in the BOYCB

Mark 6 in the BPBB

Mark 6 in the BPH

Mark 6 in the BSB

Mark 6 in the CCB

Mark 6 in the CUV

Mark 6 in the CUVS

Mark 6 in the DBT

Mark 6 in the DGDNT

Mark 6 in the DHNT

Mark 6 in the DNT

Mark 6 in the ELBE

Mark 6 in the EMTV

Mark 6 in the ESV

Mark 6 in the FBV

Mark 6 in the FEB

Mark 6 in the GGMNT

Mark 6 in the GNT

Mark 6 in the HARY

Mark 6 in the HNT

Mark 6 in the IRVA

Mark 6 in the IRVB

Mark 6 in the IRVG

Mark 6 in the IRVH

Mark 6 in the IRVK

Mark 6 in the IRVM

Mark 6 in the IRVM2

Mark 6 in the IRVO

Mark 6 in the IRVP

Mark 6 in the IRVT

Mark 6 in the IRVT2

Mark 6 in the IRVU

Mark 6 in the ISVN

Mark 6 in the JSNT

Mark 6 in the KAPI

Mark 6 in the KBT1ETNIK

Mark 6 in the KBV

Mark 6 in the KJV

Mark 6 in the KNFD

Mark 6 in the LBA

Mark 6 in the LBLA

Mark 6 in the LNT

Mark 6 in the LSV

Mark 6 in the MAAL

Mark 6 in the MBV

Mark 6 in the MBV2

Mark 6 in the MHNT

Mark 6 in the MKNFD

Mark 6 in the MNG

Mark 6 in the MNT

Mark 6 in the MNT2

Mark 6 in the MRS1T

Mark 6 in the NAA

Mark 6 in the NASB

Mark 6 in the NBLA

Mark 6 in the NBS

Mark 6 in the NBVTP

Mark 6 in the NET2

Mark 6 in the NIV11

Mark 6 in the NNT

Mark 6 in the NNT2

Mark 6 in the NNT3

Mark 6 in the PDDPT

Mark 6 in the PFNT

Mark 6 in the RMNT

Mark 6 in the SBIAS

Mark 6 in the SBIBS

Mark 6 in the SBIBS2

Mark 6 in the SBICS

Mark 6 in the SBIDS

Mark 6 in the SBIGS

Mark 6 in the SBIHS

Mark 6 in the SBIIS

Mark 6 in the SBIIS2

Mark 6 in the SBIIS3

Mark 6 in the SBIKS

Mark 6 in the SBIKS2

Mark 6 in the SBIMS

Mark 6 in the SBIOS

Mark 6 in the SBIPS

Mark 6 in the SBISS

Mark 6 in the SBITS

Mark 6 in the SBITS2

Mark 6 in the SBITS3

Mark 6 in the SBITS4

Mark 6 in the SBIUS

Mark 6 in the SBIVS

Mark 6 in the SBT

Mark 6 in the SBT1E

Mark 6 in the SCHL

Mark 6 in the SNT

Mark 6 in the SUSU

Mark 6 in the SUSU2

Mark 6 in the SYNO

Mark 6 in the TBIAOTANT

Mark 6 in the TBT1E

Mark 6 in the TBT1E2

Mark 6 in the TFTIP

Mark 6 in the TFTU

Mark 6 in the TGNTATF3T

Mark 6 in the THAI

Mark 6 in the TNFD

Mark 6 in the TNT

Mark 6 in the TNTIK

Mark 6 in the TNTIL

Mark 6 in the TNTIN

Mark 6 in the TNTIP

Mark 6 in the TNTIZ

Mark 6 in the TOMA

Mark 6 in the TTENT

Mark 6 in the UBG

Mark 6 in the UGV

Mark 6 in the UGV2

Mark 6 in the UGV3

Mark 6 in the VBL

Mark 6 in the VDCC

Mark 6 in the YALU

Mark 6 in the YAPE

Mark 6 in the YBVTP

Mark 6 in the ZBP