Obadiah 1 (BOGWICC)
1 Masomphenya a Obadiya. Ambuye Yehova akunena kwa Edomu kuti,Tamva uthenga wochokera kwa Yehova:Nthumwi yatumidwa kupita kwa anthu a mitundu kukanena kuti,“Konzekani, tiyeni tikachite nkhondo ndi Edomu.” 2 “Taona, ndidzakuchepetsani pakati pa anthu a mitundu ina;udzanyozedwa kwambiri. 3 Kudzikuza kwa mtima wako kwakusocheretsa,iwe amene umakhala mʼmapanga a mʼmatanthwendipo umamanga nyumba zako pa mapiri ataliatali,iwe amene umanena mu mtima mwako kuti,‘Ndani anganditsitse pansi?’ 4 Koma ngakhale umawuluka ngati chiwombankhangandi kumanga chisa chako pakati pa nyenyezi,ndidzakutsitsa pansi kuchokera kumeneko,”akutero Yehova. 5 “Anthu akuba akanabwera kwa iwe,kapena anthu olanda zinthu akanafika usiku,aa, tsoka lanji limene likukudikira iwe!Kodi akanangotengako zimene akuzifuna zokha?Ngati anthu othyola mphesa akanafika,kodi akanakusiyiraniko mphesa pangʼono pokha? 6 Koma Esau adzalandidwa zinthu zonse,chuma chake chobisika chidzabedwa! 7 Anthu onse ogwirizana nawo adzakupirikitsira kumalire;abwenzi ako adzakunyenga ndi kukugonjetsa;amene amadya chakudya chako adzakutchera msampha,koma iwe sudzazindikira zimenezi.” 8 Yehova akunena kuti, “Tsiku limenelo,kodi sindidzawononga anthu onse anzeru a ku Edomu,anthu odziwa zinthu mʼmapiri a Esau? 9 Ankhondo ako, iwe Temani, adzachita mantha,ndipo aliyense amene ali mʼphiri la Esauadzaphedwa pa nkhondo. 10 Chifukwa cha nkhanza zimene unachitira mʼbale wako Yakobo,udzakhala wamanyazi;adzakuwononga mpaka muyaya. 11 Pamene adaniankamulanda chuma chakepamene alendo analowa pa zipata zakendi kuchita maere pa Yerusalemu,pa tsikulo iwe unali ngati mmodzi wa iwo. 12 Iwe sunayenera kunyoza mʼbale wakopa nthawi ya tsoka lake,kapena kunyogodola Ayudachifukwa cha chiwonongeko chawo,kapena kuwaseka pa nthawi yamavuto awo. 13 Iwe sunayenera kudutsa pa zipata za anthu angapa nthawi ya masautso awo,kapena kuwanyogodolapa tsiku la tsoka lawo,kapena kulanda chuma chawopa nthawi ya masautso awo. 14 Sunayenera kudikirira pamphambano ya misewukuti uphe Ayuda othawa,kapena kuwapereka kwa adani awo Ayuda opulumukapa nthawi ya mavuto awo.” 15 “Tsiku la Yehova layandikiralimene adzaweruza mitundu yonse ya anthu.Adzakuchitira zomwe unawachitira ena;zochita zako zidzakubwerera wekha. 16 Iwe unamwa pa phiri langa loyera,koteronso mitundu ina yonse idzamwa kosalekeza;iwo adzamwa ndi kudzandirandipo adzayiwalika pa mbiri ya dziko lapansi. 17 Koma pa Phiri la Ziyoni padzakhala chipulumutso;phirilo lidzakhala lopatulika,ndipo nyumba ya Yakoboidzalandira cholowa chake. 18 Nyumba ya Yakobo idzasanduka motondipo nyumba ya Yosefe idzasanduka lawi la moto;nyumba ya Esau idzasanduka chiputu,ndipo adzayitenthe pa moto ndi kuyipsereza.Sipadzakhala anthu opulumukakuchokera mʼnyumba ya Esau.”Yehova wayankhula. 19 Anthu ochokera ku Negevi adzakhalaku mapiri a Esau,ndipo anthu ochokera mʼmbali mwa mapiriadzatenga dziko la Afilisti.Adzakhala mʼminda ya Efereimu ndi Samariya,ndipo Benjamini adzatenga Giliyadi. 20 Aisraeli amene ali ku ukapoloadzalandira dziko la Kanaani mpaka ku Zarefati;a ku Yerusalemu amene ali ku ukapolo ku Sefaradiadzalandira mizinda ya ku Negevi. 21 Opulumukawo adzapita ku Phiri la Ziyonindipo adzalamulira mapiri a Esau.Koma ufumuwo udzakhala wa Yehova.
In Other Versions
Obadiah 1 in the ANGEFD
Obadiah 1 in the ANTPNG2D
Obadiah 1 in the AS21
Obadiah 1 in the BAGH
Obadiah 1 in the BBPNG
Obadiah 1 in the BBT1E
Obadiah 1 in the BDS
Obadiah 1 in the BEV
Obadiah 1 in the BHAD
Obadiah 1 in the BIB
Obadiah 1 in the BLPT
Obadiah 1 in the BNT
Obadiah 1 in the BNTABOOT
Obadiah 1 in the BNTLV
Obadiah 1 in the BOATCB
Obadiah 1 in the BOATCB2
Obadiah 1 in the BOBCV
Obadiah 1 in the BOCNT
Obadiah 1 in the BOECS
Obadiah 1 in the BOHCB
Obadiah 1 in the BOHCV
Obadiah 1 in the BOHLNT
Obadiah 1 in the BOHNTLTAL
Obadiah 1 in the BOICB
Obadiah 1 in the BOILNTAP
Obadiah 1 in the BOITCV
Obadiah 1 in the BOKCV
Obadiah 1 in the BOKCV2
Obadiah 1 in the BOKHWOG
Obadiah 1 in the BOKSSV
Obadiah 1 in the BOLCB
Obadiah 1 in the BOLCB2
Obadiah 1 in the BOMCV
Obadiah 1 in the BONAV
Obadiah 1 in the BONCB
Obadiah 1 in the BONLT
Obadiah 1 in the BONUT2
Obadiah 1 in the BOPLNT
Obadiah 1 in the BOSCB
Obadiah 1 in the BOSNC
Obadiah 1 in the BOTLNT
Obadiah 1 in the BOVCB
Obadiah 1 in the BOYCB
Obadiah 1 in the BPBB
Obadiah 1 in the BPH
Obadiah 1 in the BSB
Obadiah 1 in the CCB
Obadiah 1 in the CUV
Obadiah 1 in the CUVS
Obadiah 1 in the DBT
Obadiah 1 in the DGDNT
Obadiah 1 in the DHNT
Obadiah 1 in the DNT
Obadiah 1 in the ELBE
Obadiah 1 in the EMTV
Obadiah 1 in the ESV
Obadiah 1 in the FBV
Obadiah 1 in the FEB
Obadiah 1 in the GGMNT
Obadiah 1 in the GNT
Obadiah 1 in the HARY
Obadiah 1 in the HNT
Obadiah 1 in the IRVA
Obadiah 1 in the IRVB
Obadiah 1 in the IRVG
Obadiah 1 in the IRVH
Obadiah 1 in the IRVK
Obadiah 1 in the IRVM
Obadiah 1 in the IRVM2
Obadiah 1 in the IRVO
Obadiah 1 in the IRVP
Obadiah 1 in the IRVT
Obadiah 1 in the IRVT2
Obadiah 1 in the IRVU
Obadiah 1 in the ISVN
Obadiah 1 in the JSNT
Obadiah 1 in the KAPI
Obadiah 1 in the KBT1ETNIK
Obadiah 1 in the KBV
Obadiah 1 in the KJV
Obadiah 1 in the KNFD
Obadiah 1 in the LBA
Obadiah 1 in the LBLA
Obadiah 1 in the LNT
Obadiah 1 in the LSV
Obadiah 1 in the MAAL
Obadiah 1 in the MBV
Obadiah 1 in the MBV2
Obadiah 1 in the MHNT
Obadiah 1 in the MKNFD
Obadiah 1 in the MNG
Obadiah 1 in the MNT
Obadiah 1 in the MNT2
Obadiah 1 in the MRS1T
Obadiah 1 in the NAA
Obadiah 1 in the NASB
Obadiah 1 in the NBLA
Obadiah 1 in the NBS
Obadiah 1 in the NBVTP
Obadiah 1 in the NET2
Obadiah 1 in the NIV11
Obadiah 1 in the NNT
Obadiah 1 in the NNT2
Obadiah 1 in the NNT3
Obadiah 1 in the PDDPT
Obadiah 1 in the PFNT
Obadiah 1 in the RMNT
Obadiah 1 in the SBIAS
Obadiah 1 in the SBIBS
Obadiah 1 in the SBIBS2
Obadiah 1 in the SBICS
Obadiah 1 in the SBIDS
Obadiah 1 in the SBIGS
Obadiah 1 in the SBIHS
Obadiah 1 in the SBIIS
Obadiah 1 in the SBIIS2
Obadiah 1 in the SBIIS3
Obadiah 1 in the SBIKS
Obadiah 1 in the SBIKS2
Obadiah 1 in the SBIMS
Obadiah 1 in the SBIOS
Obadiah 1 in the SBIPS
Obadiah 1 in the SBISS
Obadiah 1 in the SBITS
Obadiah 1 in the SBITS2
Obadiah 1 in the SBITS3
Obadiah 1 in the SBITS4
Obadiah 1 in the SBIUS
Obadiah 1 in the SBIVS
Obadiah 1 in the SBT
Obadiah 1 in the SBT1E
Obadiah 1 in the SCHL
Obadiah 1 in the SNT
Obadiah 1 in the SUSU
Obadiah 1 in the SUSU2
Obadiah 1 in the SYNO
Obadiah 1 in the TBIAOTANT
Obadiah 1 in the TBT1E
Obadiah 1 in the TBT1E2
Obadiah 1 in the TFTIP
Obadiah 1 in the TFTU
Obadiah 1 in the TGNTATF3T
Obadiah 1 in the THAI
Obadiah 1 in the TNFD
Obadiah 1 in the TNT
Obadiah 1 in the TNTIK
Obadiah 1 in the TNTIL
Obadiah 1 in the TNTIN
Obadiah 1 in the TNTIP
Obadiah 1 in the TNTIZ
Obadiah 1 in the TOMA
Obadiah 1 in the TTENT
Obadiah 1 in the UBG
Obadiah 1 in the UGV
Obadiah 1 in the UGV2
Obadiah 1 in the UGV3
Obadiah 1 in the VBL
Obadiah 1 in the VDCC
Obadiah 1 in the YALU
Obadiah 1 in the YAPE
Obadiah 1 in the YBVTP
Obadiah 1 in the ZBP