Psalms 101 (BOGWICC)
undefined Salimo la Davide. 1 Ndidzayimba za chikondi ndi chiweruzo chanu cholungama;kwa Inu Yehova ndidzayimba matamando. 2 Ndidzatsata njira yolungama;nanga mudzabwera liti kwa ine? Ndidzayenda mʼnyumba mwangandi mtima wosalakwa. 3 Sindidzayika chinthu chilichonse choyipapamaso panga. Ine ndimadana ndi zochita za anthu opanda chikhulupiriro;iwo sadzadziphatika kwa ine. 4 Anthu a mtima wokhota adzakhala kutali ndi ine;ine sindidzalola choyipa chilichonse kulowa mwa ine. 5 Aliyense wosinjirira mnansi wake mseriameneyo ndidzamuletsa;aliyense amene ali ndi maso amwano ndi mtima wodzikuza,ameneyo sindidzamulekerera. 6 Maso anga adzakhala pa okhulupirika mʼdziko,kuti akhale pamodzi ndi ine;iye amene mayendedwe ake ndi wosalakwaadzanditumikira. 7 Aliyense wochita chinyengosadzakhala mʼnyumba mwanga.Aliyense woyankhula mwachinyengosadzayima pamaso panga. 8 Mmawa uliwonse ndidzatontholetsa anthuonse oyipa mʼdziko;ndidzachotsa aliyense wochita zoyipamu mzinda wa Yehova.