Psalms 104 (BOGWICC)
1 Tamanda Yehova, iwe moyo wanga. Inu Yehova Mulungu wanga, ndinu wamkulu kwambiri;mwavala ulemerero ndi ufumu. 2 Iye wadzifunditsa kuwala ngati chovala;watambasula miyamba ngati tenti 3 ndipo wayika pa madzi mitanda ya chipinda chake.Iye amasandutsa mitambo kukhala galeta lake,ndi kuwuluka pa mapiko a mphepo. 4 Amapanga mphepo kukhala amithenga ake,malawi amoto kukhala atumiki ake. 5 Anakhazikitsa dziko lapansi pa maziko ake;silingasunthike. 6 Munaliphimba ndi nyanja yozama ngati chovala;madzi anayimirira pamwamba pa mapiri. 7 Koma pakudzudzula kwanu madzi anathawa,pa mkokomo wa bingu lanu iwo anamwazika; 8 Inu munamiza mapiri,iwo anatsikira ku zigwakumalo kumene munawakonzera. 9 Inu munayika malire ndipo sangathe kudutsa,iwo sadzamizanso dziko lapansi. 10 Iye achititsa akasupe kutulutsa madzi kupita ku zigwa;madziwo amayenda pakati pa mapiri. 11 Iwo amapereka madzi kwa zirombo zonse zakuthengo;abulu akuthengo amapha ludzu lawo. 12 Mbalame zamlengalenga zimayika zisa mʼmbali mwa madzi;zimayimba pakati pa thambo. 13 Iye amathirira mapiri kuchokera ku zipinda zake zapamwamba;dziko lapansi limakhutitsidwa ndi chipatso cha ntchito yake. 14 Amameretsa udzu kuti ngʼombe zidye,ndi zomera, kuti munthu azilimakubweretsa chakudya kuchokera mʼdziko lapansi: 15 vinyo amene amasangalatsa mtima wa munthu,mafuta amene amachititsa nkhope yake kuwala,ndi buledi amene amapereka mphamvu. 16 Mitengo ya Yehova ndi yothiriridwa bwino,mikungudza ya ku Lebanoni imene Iye anadzala. 17 Mbalame zimamanga zisa zawo;kakowa ali ndi malo ake mʼmikungudzamo. 18 Mapiri ataliatali ndi a mbalale;mʼmingʼalu ya miyala ndi mobisalamo mbira. 19 Mwezi umasiyanitsa nyengondipo dzuwa limadziwa nthawi yake yolowera. 20 Inu mumabweretsa mdima nukhala usiku,ndipo zirombo zonse za ku nkhalango zimatuluka. 21 Mikango imabangula kufuna nyama,ndi kufunafuna chakudya chawo kuchokera kwa Mulungu. 22 Dzuwa limatuluka ndipo iyo imapita kukabisala;imabwerera kukagona pansi mʼmapanga awo. 23 Pamenepo munthu amapita ku ntchito yake,kukagwira ntchito yake mpaka madzulo. 24 Ntchito zanu ndi zochulukadi Inu Yehova!Munazipanga zonse mwanzeru,dziko lapansi ladzaza ndi zolengedwa zanu. 25 Kuli nyanja yayikulu ndi yotambalala,yodzaza ndi zolengedwa zosawerengeka,zamoyo zanu zazikulu ndi zazingʼono zomwe. 26 Kumeneko sitima zapamadzi zimayenda uku ndi uku,ndiponso Leviyatani amene munamulenga kuti asewere kumeneko. 27 Zonsezi zimayangʼana kwa Inukuti muzipatse chakudya chawo pa nthawi yake yoyenera. 28 Mukazipatsa,zimachisonkhanitsa pamodzi;mukatsekula dzanja lanu,izo zimakhutitsidwa ndi zinthu zabwino. 29 Mukabisa nkhope yanu,izo zimachita mantha aakulu;mukachotsa mpweya wawo,zimafa ndi kubwerera ku fumbi. 30 Mukatumiza mzimu wanu,izo zimalengedwandipo mumakozanso maonekedwe a dziko lapansi. 31 Ulemerero wa Yehova ukhalebe mpaka muyaya;Yehova akondwere ndi ntchito ya manja ake; 32 Iye amene amayangʼana dziko lapansi ndipo limanjenjemera,amene amakhudza mapiri ndipo amatuluka utsi. 33 Ine ndidzayimbira Yehova moyo wanga wonse;ndidzayimbira matamando Mulungu wanga nthawi yonse imene ndili ndi moyo. 34 Zolingalira zanga zikhale zomukomera Iye,pamene ndikusangalala mwa Yehova. 35 Koma anthu ochimwa awonongeke pa dziko lapansindipo anthu oyipa asapezekenso. Tamanda Yehova, Iwe moyo wanga. Tamandani Yehova.
In Other Versions
Psalms 104 in the ANGEFD
Psalms 104 in the ANTPNG2D
Psalms 104 in the AS21
Psalms 104 in the BAGH
Psalms 104 in the BBPNG
Psalms 104 in the BBT1E
Psalms 104 in the BDS
Psalms 104 in the BEV
Psalms 104 in the BHAD
Psalms 104 in the BIB
Psalms 104 in the BLPT
Psalms 104 in the BNT
Psalms 104 in the BNTABOOT
Psalms 104 in the BNTLV
Psalms 104 in the BOATCB
Psalms 104 in the BOATCB2
Psalms 104 in the BOBCV
Psalms 104 in the BOCNT
Psalms 104 in the BOECS
Psalms 104 in the BOHCB
Psalms 104 in the BOHCV
Psalms 104 in the BOHLNT
Psalms 104 in the BOHNTLTAL
Psalms 104 in the BOICB
Psalms 104 in the BOILNTAP
Psalms 104 in the BOITCV
Psalms 104 in the BOKCV
Psalms 104 in the BOKCV2
Psalms 104 in the BOKHWOG
Psalms 104 in the BOKSSV
Psalms 104 in the BOLCB
Psalms 104 in the BOLCB2
Psalms 104 in the BOMCV
Psalms 104 in the BONAV
Psalms 104 in the BONCB
Psalms 104 in the BONLT
Psalms 104 in the BONUT2
Psalms 104 in the BOPLNT
Psalms 104 in the BOSCB
Psalms 104 in the BOSNC
Psalms 104 in the BOTLNT
Psalms 104 in the BOVCB
Psalms 104 in the BOYCB
Psalms 104 in the BPBB
Psalms 104 in the BPH
Psalms 104 in the BSB
Psalms 104 in the CCB
Psalms 104 in the CUV
Psalms 104 in the CUVS
Psalms 104 in the DBT
Psalms 104 in the DGDNT
Psalms 104 in the DHNT
Psalms 104 in the DNT
Psalms 104 in the ELBE
Psalms 104 in the EMTV
Psalms 104 in the ESV
Psalms 104 in the FBV
Psalms 104 in the FEB
Psalms 104 in the GGMNT
Psalms 104 in the GNT
Psalms 104 in the HARY
Psalms 104 in the HNT
Psalms 104 in the IRVA
Psalms 104 in the IRVB
Psalms 104 in the IRVG
Psalms 104 in the IRVH
Psalms 104 in the IRVK
Psalms 104 in the IRVM
Psalms 104 in the IRVM2
Psalms 104 in the IRVO
Psalms 104 in the IRVP
Psalms 104 in the IRVT
Psalms 104 in the IRVT2
Psalms 104 in the IRVU
Psalms 104 in the ISVN
Psalms 104 in the JSNT
Psalms 104 in the KAPI
Psalms 104 in the KBT1ETNIK
Psalms 104 in the KBV
Psalms 104 in the KJV
Psalms 104 in the KNFD
Psalms 104 in the LBA
Psalms 104 in the LBLA
Psalms 104 in the LNT
Psalms 104 in the LSV
Psalms 104 in the MAAL
Psalms 104 in the MBV
Psalms 104 in the MBV2
Psalms 104 in the MHNT
Psalms 104 in the MKNFD
Psalms 104 in the MNG
Psalms 104 in the MNT
Psalms 104 in the MNT2
Psalms 104 in the MRS1T
Psalms 104 in the NAA
Psalms 104 in the NASB
Psalms 104 in the NBLA
Psalms 104 in the NBS
Psalms 104 in the NBVTP
Psalms 104 in the NET2
Psalms 104 in the NIV11
Psalms 104 in the NNT
Psalms 104 in the NNT2
Psalms 104 in the NNT3
Psalms 104 in the PDDPT
Psalms 104 in the PFNT
Psalms 104 in the RMNT
Psalms 104 in the SBIAS
Psalms 104 in the SBIBS
Psalms 104 in the SBIBS2
Psalms 104 in the SBICS
Psalms 104 in the SBIDS
Psalms 104 in the SBIGS
Psalms 104 in the SBIHS
Psalms 104 in the SBIIS
Psalms 104 in the SBIIS2
Psalms 104 in the SBIIS3
Psalms 104 in the SBIKS
Psalms 104 in the SBIKS2
Psalms 104 in the SBIMS
Psalms 104 in the SBIOS
Psalms 104 in the SBIPS
Psalms 104 in the SBISS
Psalms 104 in the SBITS
Psalms 104 in the SBITS2
Psalms 104 in the SBITS3
Psalms 104 in the SBITS4
Psalms 104 in the SBIUS
Psalms 104 in the SBIVS
Psalms 104 in the SBT
Psalms 104 in the SBT1E
Psalms 104 in the SCHL
Psalms 104 in the SNT
Psalms 104 in the SUSU
Psalms 104 in the SUSU2
Psalms 104 in the SYNO
Psalms 104 in the TBIAOTANT
Psalms 104 in the TBT1E
Psalms 104 in the TBT1E2
Psalms 104 in the TFTIP
Psalms 104 in the TFTU
Psalms 104 in the TGNTATF3T
Psalms 104 in the THAI
Psalms 104 in the TNFD
Psalms 104 in the TNT
Psalms 104 in the TNTIK
Psalms 104 in the TNTIL
Psalms 104 in the TNTIN
Psalms 104 in the TNTIP
Psalms 104 in the TNTIZ
Psalms 104 in the TOMA
Psalms 104 in the TTENT
Psalms 104 in the UBG
Psalms 104 in the UGV
Psalms 104 in the UGV2
Psalms 104 in the UGV3
Psalms 104 in the VBL
Psalms 104 in the VDCC
Psalms 104 in the YALU
Psalms 104 in the YAPE
Psalms 104 in the YBVTP
Psalms 104 in the ZBP