Psalms 120 (BOGWICC)
undefined Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. 1 Ndimafuwulira kwa Yehova mʼmasautso anga,ndipo Iye amandiyankha. 2 Pulumutseni Yehova ku milomo yabodza,ndi kwa anthu achinyengo. 3 Kodi adzakuchitani chiyani,ndipo adzawonjezerapo zotani, inu anthu achinyengo? 4 Adzakulangani ndi mivi yakuthwa ya munthu wankhondo,ndi makala oyaka a mtengo wa tsanya. 5 Tsoka ine kuti ndimakhala ku Mesaki,kuti ndimakhala pakati pa matenti a ku Kedara! 6 Kwa nthawi yayitali ndakhala pakatipa iwo amene amadana ndi mtendere. 7 Ine ndine munthu wamtendere;koma ndikamayankhula, iwo amafuna nkhondo.