Psalms 121 (BOGWICC)
undefined Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. 1 Ndikweza maso anga ku mapiri;kodi thandizo langa limachokera kuti? 2 Thandizo langa limachokera kwa Yehova,wolenga kumwamba ndi dziko lapansi. 3 Sadzalola kuti phazi lako literereke;Iye amene amakusunga sadzawodzera. 4 Taonani, Iye amene amasunga Israelisadzawodzera kapena kugona. 5 Yehova ndiye amene amakusunga;Yehova ndiye mthunzi wako ku dzanja lako lamanja. 6 Dzuwa silidzakupweteka nthawi ya masana,kapena mwezi nthawi ya usiku. 7 Yehova adzakuteteza ku zoyipa zonse;adzasunga moyo wako. 8 Yehova adzayangʼanira kutuluka kwako ndi kulowa kwako;kuyambira tsopano mpaka muyaya.