Psalms 131 (BOGWICC)
undefined Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Salimo la Davide. 1 Inu Yehova, mtima wanga siwodzikuza,maso anga siwonyada;sinditengeteka mtimandi zinthu zapamwamba ndi zodabwitsa. 2 Koma moyo wanga ndawutontholetsandi kuwukhalitsa chete ngati mwana amene amayi ake amuletsa kuyamwa,moyo wanga mʼkati mwanga uli ngati mwana amene amuletsa kuyamwa. 3 Yembekeza Yehova, iwe Israeli,kuyambira tsopano mpaka muyaya.