Psalms 133 (BOGWICC)
undefined Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. 1 Onani, nʼkokoma ndi kokondweretsa ndithupamene abale akhala pamodzi mwachiyanjano! 2 Zili ngati mafuta amtengowapatali othiridwa pa mutu,otsikira ku ndevu,ku ndevu za Aaroni,oyenderera mpaka mʼkhosi mwa mkanjo wake. 3 Zili ngati mame a ku Heremoniotsikira pa Phiri la Ziyoni.Pakuti pamenepo Yehova amaperekapo dalitso,ndiwo moyo wamuyaya.