Psalms 142 (BOGWICC)
undefined Ndakatulo ya Davide, pamene iyeyo anali mʼphanga. Pemphero. 1 Ndikulirira Yehova mofuwula;ndikukweza mawu anga kwa Yehova kupempha chifundo. 2 Ndikukhuthula madandawulo anga pamaso pake;ndikufotokoza za masautso anga pamaso pake. 3 Pamene mzimu wanga walefuka mʼkati mwanga,ndinu amene mudziwa njira yanga.Mʼnjira imene ndimayendamoanthu anditchera msampha mobisa. 4 Yangʼanani kumanja kwanga ndipo onani;palibe amene akukhudzika nane.Ndilibe pothawira;palibe amene amasamala za moyo wanga. 5 Ndilirira Inu Yehova;ndikuti, “Ndinu pothawirapo panga,gawo langa mʼdziko la anthu amoyo.” 6 Mverani kulira kwangapakuti ndathedwa nzeru;pulumutseni kwa amene akundithamangitsapakuti ndi amphamvu kuposa ine. 7 Tulutseni mʼndende yangakuti nditamande dzina lanu. Ndipo anthu olungama adzandizungulirachifukwa cha zabwino zanu pa ine.