Psalms 82 (BOGWICC)
undefined Salimo la Asafu. 1 Mulungu akutsogolera msonkhano waukulu;Iye akuweruza pakati pa “milungu.” 2 “Mudzateteza osalungama mpaka liti,ndi kukondera anthu oyipa? 3 Tetezani anthu ofowoka ndi amasiye;mukhazikitse ufulu wa anthu osauka ndi ozunzika. 4 Landitsani anthu ofowoka ndi osowa;apulumutseni mʼdzanja la anthu oyipa. 5 “Iwo sadziwa kanthu, sazindikira kalikonse.Amayendayenda mu mdima;maziko onse a dziko lapansi agwedezeka. 6 “Ndinati, ‘Inu ndinu Mulungu,nonsenu ndinu ana a Wammwambamwamba.’ 7 Koma mudzafa ngati anthu wamba;mudzagwa ngati wolamula wina aliyense.” 8 Dzukani Inu Mulungu, weruzani dziko lapansi,pakuti mayiko onse ndi cholowa chanu.