Revelation 1 (BOGWICC)

1 Vumbulutso lochokera kwa Yesu Khristu, limene Mulungu anamupatsa kuti aonetse atumiki ake zimene zinayenera kuchitika posachedwa. Iye anatuma mngelo wake kuti adziwitse mtumiki wake Yohane, 2 amene akuchitira umboni chilichonse chimene anachiona. Awa ndi Mawu a Mulungu ndi umboni wa Yesu Khristu. 3 Ngodala munthu amene awerenga mawu oneneratu zamʼtsogolo ndi iwo amene amamva ndi kusunga zolembedwa mʼbukuli pakuti nthawi yayandikira. 4 Ndine Yohane,Kupita ku mipingo isanu ndi iwiri ya mʼchigawo cha Asiya.Chisomo ndi mtendere kwa inu, kuchokera kwa Iye amene ali, amene analipo ndi amene akubwera ndi kwa mizimu isanu ndi iwiri yokhala patsogolo pa mpando wake waufumu, 5 ndiponso kuchokera kwa Yesu Khristu mboni yokhulupirika, woyamba kuukitsidwa, ndi wolamulira mafumu a dziko lapansi. Kwa Iye amene amatikonda ndipo watimasula ku machimo athu ndi magazi ake, 6 ndipo watisandutsa mafumu ndi ansembe kuti tizitumikira Mulungu ndi Atate ake. Kwa Iye kukhale ulemerero ndi mphamvu ku nthawi zosatha, Ameni. 7 “Onani akubwera ndi mitambo,”ndipo “Aliyense adzamuona,ndi amene anamubaya omwe.”Ndipo anthu a mitundu yonse ya pa dziko lapansi “adzalira chingʼangʼadza chifukwa cha Iye.”Zidzakhaladi momwemo, Ameni. 8 “Ine ndine Alefa ndi Omega,” akutero Ambuye Mulungu Wamphamvuzonseyo “amene muli, amene munalipo, ndi amene mudzakhalapo.” 9 Ine Yohane mʼbale wanu ndi mnzanu mʼmasautso ndi mu ufumu ndi mukupirira kwambiri, zomwe ndi zathu mwa Yesu, ndinali pa chilumba cha Patimo chifukwa cha Mawu a Mulungu ndi umboni wa Yesu. 10 Pa tsiku la Ambuye ndinanyamulidwa ndi Mzimu ndipo ndinamva kumbuyo kwanga mawu ofuwula ngati lipenga, 11 amene anati, “Lemba mʼbuku zimene ukuziona ndipo uzitumize ku mipingo isanu ndi iwiri ya ku Efeso, Simurna, Pergamo, Tiyatira, Sarde, Filadefiya ndi ku Laodikaya.” 12 Nditatembenuka kuti ndione amene amandiyankhulayo, ndinaona zoyikapo nyale zisanu ndi ziwiri zagolide. 13 Pakati pa zoyikapo nyalezo ndinaona wina wooneka ngati Mwana wa Munthu atavala mkanjo wofika kumapazi ake ndipo anamangirira lamba wagolide pa chifuwa pake. 14 Tsitsi lake linali loyera ngati thonje, kuyera ngati matalala, ndipo maso ake amawala ngati malawi amoto. 15 Mapazi ake anali ngati chitsulo choti chili mʼngʼanjo yamoto, ndipo mawu ake anali ngati mkokomo wamadzi othamanga. 16 Mʼdzanja lake lamanja ananyamula nyenyezi zisanu ndi ziwiri, ndipo mʼkamwa mwake munali lupanga lakuthwa konsekonse. Nkhope yake imawala ngati dzuwa lowala kwambiri. 17 Nditamuona ndinagwa pa mapazi ake ngati wakufa. Kenaka Iye anasanjika dzanja lake lamanja pa ine nati, “Usachite mantha. Ndine Woyamba ndi Wotsiriza. 18 Ine ndine Wamoyo; ndinali wakufa ndipo taona ndine wamoyo mpaka muyaya! Ndipo ndili ndi makiyi a imfa ndi Hade. 19 “Chomwecho, lemba zimene waona, zimene zilipo panopa ndi zimene zidzachitike mʼtsogolo. 20 Tanthauzo la nyenyezi zisanu ndi ziwiri zimene waziona mʼdzanja langa lamanja ndi la zoyikapo nyale zagolide zisanu ndi ziwiri ndi ili: Nyenyezi zisanu ndi ziwiri ndi angelo a mipingo isanu ndi iwiri ija, ndipo zoyikapo nyale zisanu ndi ziwiri zija ndi mipingo isanu ndi iwiri ija.”

In Other Versions

Revelation 1 in the ANGEFD

Revelation 1 in the ANTPNG2D

Revelation 1 in the AS21

Revelation 1 in the BAGH

Revelation 1 in the BBPNG

Revelation 1 in the BBT1E

Revelation 1 in the BDS

Revelation 1 in the BEV

Revelation 1 in the BHAD

Revelation 1 in the BIB

Revelation 1 in the BLPT

Revelation 1 in the BNT

Revelation 1 in the BNTABOOT

Revelation 1 in the BNTLV

Revelation 1 in the BOATCB

Revelation 1 in the BOATCB2

Revelation 1 in the BOBCV

Revelation 1 in the BOCNT

Revelation 1 in the BOECS

Revelation 1 in the BOHCB

Revelation 1 in the BOHCV

Revelation 1 in the BOHLNT

Revelation 1 in the BOHNTLTAL

Revelation 1 in the BOICB

Revelation 1 in the BOILNTAP

Revelation 1 in the BOITCV

Revelation 1 in the BOKCV

Revelation 1 in the BOKCV2

Revelation 1 in the BOKHWOG

Revelation 1 in the BOKSSV

Revelation 1 in the BOLCB

Revelation 1 in the BOLCB2

Revelation 1 in the BOMCV

Revelation 1 in the BONAV

Revelation 1 in the BONCB

Revelation 1 in the BONLT

Revelation 1 in the BONUT2

Revelation 1 in the BOPLNT

Revelation 1 in the BOSCB

Revelation 1 in the BOSNC

Revelation 1 in the BOTLNT

Revelation 1 in the BOVCB

Revelation 1 in the BOYCB

Revelation 1 in the BPBB

Revelation 1 in the BPH

Revelation 1 in the BSB

Revelation 1 in the CCB

Revelation 1 in the CUV

Revelation 1 in the CUVS

Revelation 1 in the DBT

Revelation 1 in the DGDNT

Revelation 1 in the DHNT

Revelation 1 in the DNT

Revelation 1 in the ELBE

Revelation 1 in the EMTV

Revelation 1 in the ESV

Revelation 1 in the FBV

Revelation 1 in the FEB

Revelation 1 in the GGMNT

Revelation 1 in the GNT

Revelation 1 in the HARY

Revelation 1 in the HNT

Revelation 1 in the IRVA

Revelation 1 in the IRVB

Revelation 1 in the IRVG

Revelation 1 in the IRVH

Revelation 1 in the IRVK

Revelation 1 in the IRVM

Revelation 1 in the IRVM2

Revelation 1 in the IRVO

Revelation 1 in the IRVP

Revelation 1 in the IRVT

Revelation 1 in the IRVT2

Revelation 1 in the IRVU

Revelation 1 in the ISVN

Revelation 1 in the JSNT

Revelation 1 in the KAPI

Revelation 1 in the KBT1ETNIK

Revelation 1 in the KBV

Revelation 1 in the KJV

Revelation 1 in the KNFD

Revelation 1 in the LBA

Revelation 1 in the LBLA

Revelation 1 in the LNT

Revelation 1 in the LSV

Revelation 1 in the MAAL

Revelation 1 in the MBV

Revelation 1 in the MBV2

Revelation 1 in the MHNT

Revelation 1 in the MKNFD

Revelation 1 in the MNG

Revelation 1 in the MNT

Revelation 1 in the MNT2

Revelation 1 in the MRS1T

Revelation 1 in the NAA

Revelation 1 in the NASB

Revelation 1 in the NBLA

Revelation 1 in the NBS

Revelation 1 in the NBVTP

Revelation 1 in the NET2

Revelation 1 in the NIV11

Revelation 1 in the NNT

Revelation 1 in the NNT2

Revelation 1 in the NNT3

Revelation 1 in the PDDPT

Revelation 1 in the PFNT

Revelation 1 in the RMNT

Revelation 1 in the SBIAS

Revelation 1 in the SBIBS

Revelation 1 in the SBIBS2

Revelation 1 in the SBICS

Revelation 1 in the SBIDS

Revelation 1 in the SBIGS

Revelation 1 in the SBIHS

Revelation 1 in the SBIIS

Revelation 1 in the SBIIS2

Revelation 1 in the SBIIS3

Revelation 1 in the SBIKS

Revelation 1 in the SBIKS2

Revelation 1 in the SBIMS

Revelation 1 in the SBIOS

Revelation 1 in the SBIPS

Revelation 1 in the SBISS

Revelation 1 in the SBITS

Revelation 1 in the SBITS2

Revelation 1 in the SBITS3

Revelation 1 in the SBITS4

Revelation 1 in the SBIUS

Revelation 1 in the SBIVS

Revelation 1 in the SBT

Revelation 1 in the SBT1E

Revelation 1 in the SCHL

Revelation 1 in the SNT

Revelation 1 in the SUSU

Revelation 1 in the SUSU2

Revelation 1 in the SYNO

Revelation 1 in the TBIAOTANT

Revelation 1 in the TBT1E

Revelation 1 in the TBT1E2

Revelation 1 in the TFTIP

Revelation 1 in the TFTU

Revelation 1 in the TGNTATF3T

Revelation 1 in the THAI

Revelation 1 in the TNFD

Revelation 1 in the TNT

Revelation 1 in the TNTIK

Revelation 1 in the TNTIL

Revelation 1 in the TNTIN

Revelation 1 in the TNTIP

Revelation 1 in the TNTIZ

Revelation 1 in the TOMA

Revelation 1 in the TTENT

Revelation 1 in the UBG

Revelation 1 in the UGV

Revelation 1 in the UGV2

Revelation 1 in the UGV3

Revelation 1 in the VBL

Revelation 1 in the VDCC

Revelation 1 in the YALU

Revelation 1 in the YAPE

Revelation 1 in the YBVTP

Revelation 1 in the ZBP