Revelation 11 (BOGWICC)
1 Ndinapatsidwa bango longa ndodo yoyezera ndipo ndinawuzidwa kuti, “Pita, kayeze Nyumba ya Mulungu ndi guwa lansembe, ndipo ukawerenge anthu opembedza mʼNyumbamo. 2 Koma bwalo lakunja ulisiye, usaliyeze chifukwa linaperekedwa kwa a mitundu ina. Iwo adzawupondereza mzinda woyerawo kwa miyezi 42. 3 Ndipo ndidzapereka mphamvu kwa mboni zanga ziwiri, zitavala ziguduli, ndipo kwa masiku 1,260 zidzakhala zikulalikira.” 4 Mboni ziwirizo ndi mitengo iwiri ya olivi ndi zoyikapo nyale ziwiri zija zimene zili pamaso pa Ambuye wa dziko lapansi. 5 Ngati wina atafuna kuzipweteka mbonizo, moto umatuluka mʼkamwa mwawo ndikuwononga adani awo. 6 Mbonizo zili ndi mphamvu yomanga mvula kuti isagwe pa nthawi imene akulalikirayo; ndipo zili ndi mphamvu yosanduliza madzi kukhala magazi ndi yokantha dziko lapansi ndi miliri ya mitundumitundu nthawi iliyonse imene zingafune. 7 Tsono zikadzatsiriza umboni wawowo, chirombo chotuluka mʼChidzenje chakuya chija chidzachita nawo nkhondo nʼkuzigonjetsa mpaka kuzipha. 8 Mitembo yawo idzakhala ili gone pabwalo la mu mzinda waukulu umene mozimbayitsa umatchedwa Sodomu ndi Igupto, kumenenso Ambuye wawo anapachikidwako. 9 Kwa masiku atatu ndi theka, anthu ochokera ku mtundu uliwonse, fuko lililonse, chiyankhulo chilichonse ndi dziko lililonse, azidzayangʼanitsitsa mitembo yawoyo koma adzakana kuyikwirira. 10 Anthu okhala pa dziko lapansi adzasangalala nazo zimenezi. Adzachita chikondwerero ndi kutumizirana mphatso, chifukwa aneneri awiri amenewa ankasautsa anthu okhala pa dziko lapansi. 11 Koma patapita masiku atatu ndi theka aja, mpweya wopatsa moyo wochoka kwa Mulungu unalowa mwa aneneriwo, ndipo anayimirira, ndipo amene anawaona anachita mantha aakulu. 12 Kenaka aneneri aja anamva mawu ofuwula ochokera kumwamba owawuza kuti, “Bwerani kuno.” Ndipo anapitadi kumwamba mu mtambo adani awo aja akuwaona. 13 Nthawi yomweyo panachitika chivomerezi choopsa mwakuti chigawo chimodzi cha magawo khumi a mzinda chinagwa. Anthu 7,000 anaphedwa ndi chivomerezicho, ndipo opulumukawo anachita mantha kwambiri nayamba kutamanda Mulungu wakumwamba. 14 Tsoka lachiwiri lapita; koma tsoka lachitatu likubwera posachedwapa. 15 Mngelo wachisanu ndi chiwiri anawomba lipenga lake, ndipo kumwamba kunamveka mawu ofuwula amene anati,“Ufumu wa dziko lapansi ulimʼmanja mwa Ambuye athu ndi Khristu wake uja,ndipo adzalamulira mpaka muyaya.” 16 Ndipo akuluakulu 24 aja okhala pa mipando yawo yaufumu pamaso pa Mulungu, anadzigwetsa chafufumimba napembedza Mulungu 17 Iwo anati,“Ife tikuyamika Inu Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse,amene mulipo ndipo munalipo,chifukwa mwaonetsa mphamvu yanu yayikulu,ndipo mwayamba kulamulira. 18 A mitundu ina anapsa mtima;koma yafika nthawi yoonetsa mkwiyo.Nthawi yakwana yoweruza anthu akufa,yopereka mphotho kwa atumiki anu, aneneri,anthu oyera mtima anu ndi amene amaopa dzina lanu,wamngʼono pamodzi ndi wamkulu yemwe.Yafika nthawi yowononga amene awononga dziko lapansi.” 19 Pamenepo anatsekula Nyumba ya Mulungu kumwamba ndipo mʼkati mwake munaoneka Bokosi la Chipangano. Kenaka kunachita mphenzi, phokoso, mabingu, chivomerezi ndipo kunachita mkuntho wamatalala akuluakulu.
In Other Versions
Revelation 11 in the ANGEFD
Revelation 11 in the ANTPNG2D
Revelation 11 in the AS21
Revelation 11 in the BAGH
Revelation 11 in the BBPNG
Revelation 11 in the BBT1E
Revelation 11 in the BDS
Revelation 11 in the BEV
Revelation 11 in the BHAD
Revelation 11 in the BIB
Revelation 11 in the BLPT
Revelation 11 in the BNT
Revelation 11 in the BNTABOOT
Revelation 11 in the BNTLV
Revelation 11 in the BOATCB
Revelation 11 in the BOATCB2
Revelation 11 in the BOBCV
Revelation 11 in the BOCNT
Revelation 11 in the BOECS
Revelation 11 in the BOHCB
Revelation 11 in the BOHCV
Revelation 11 in the BOHLNT
Revelation 11 in the BOHNTLTAL
Revelation 11 in the BOICB
Revelation 11 in the BOILNTAP
Revelation 11 in the BOITCV
Revelation 11 in the BOKCV
Revelation 11 in the BOKCV2
Revelation 11 in the BOKHWOG
Revelation 11 in the BOKSSV
Revelation 11 in the BOLCB
Revelation 11 in the BOLCB2
Revelation 11 in the BOMCV
Revelation 11 in the BONAV
Revelation 11 in the BONCB
Revelation 11 in the BONLT
Revelation 11 in the BONUT2
Revelation 11 in the BOPLNT
Revelation 11 in the BOSCB
Revelation 11 in the BOSNC
Revelation 11 in the BOTLNT
Revelation 11 in the BOVCB
Revelation 11 in the BOYCB
Revelation 11 in the BPBB
Revelation 11 in the BPH
Revelation 11 in the BSB
Revelation 11 in the CCB
Revelation 11 in the CUV
Revelation 11 in the CUVS
Revelation 11 in the DBT
Revelation 11 in the DGDNT
Revelation 11 in the DHNT
Revelation 11 in the DNT
Revelation 11 in the ELBE
Revelation 11 in the EMTV
Revelation 11 in the ESV
Revelation 11 in the FBV
Revelation 11 in the FEB
Revelation 11 in the GGMNT
Revelation 11 in the GNT
Revelation 11 in the HARY
Revelation 11 in the HNT
Revelation 11 in the IRVA
Revelation 11 in the IRVB
Revelation 11 in the IRVG
Revelation 11 in the IRVH
Revelation 11 in the IRVK
Revelation 11 in the IRVM
Revelation 11 in the IRVM2
Revelation 11 in the IRVO
Revelation 11 in the IRVP
Revelation 11 in the IRVT
Revelation 11 in the IRVT2
Revelation 11 in the IRVU
Revelation 11 in the ISVN
Revelation 11 in the JSNT
Revelation 11 in the KAPI
Revelation 11 in the KBT1ETNIK
Revelation 11 in the KBV
Revelation 11 in the KJV
Revelation 11 in the KNFD
Revelation 11 in the LBA
Revelation 11 in the LBLA
Revelation 11 in the LNT
Revelation 11 in the LSV
Revelation 11 in the MAAL
Revelation 11 in the MBV
Revelation 11 in the MBV2
Revelation 11 in the MHNT
Revelation 11 in the MKNFD
Revelation 11 in the MNG
Revelation 11 in the MNT
Revelation 11 in the MNT2
Revelation 11 in the MRS1T
Revelation 11 in the NAA
Revelation 11 in the NASB
Revelation 11 in the NBLA
Revelation 11 in the NBS
Revelation 11 in the NBVTP
Revelation 11 in the NET2
Revelation 11 in the NIV11
Revelation 11 in the NNT
Revelation 11 in the NNT2
Revelation 11 in the NNT3
Revelation 11 in the PDDPT
Revelation 11 in the PFNT
Revelation 11 in the RMNT
Revelation 11 in the SBIAS
Revelation 11 in the SBIBS
Revelation 11 in the SBIBS2
Revelation 11 in the SBICS
Revelation 11 in the SBIDS
Revelation 11 in the SBIGS
Revelation 11 in the SBIHS
Revelation 11 in the SBIIS
Revelation 11 in the SBIIS2
Revelation 11 in the SBIIS3
Revelation 11 in the SBIKS
Revelation 11 in the SBIKS2
Revelation 11 in the SBIMS
Revelation 11 in the SBIOS
Revelation 11 in the SBIPS
Revelation 11 in the SBISS
Revelation 11 in the SBITS
Revelation 11 in the SBITS2
Revelation 11 in the SBITS3
Revelation 11 in the SBITS4
Revelation 11 in the SBIUS
Revelation 11 in the SBIVS
Revelation 11 in the SBT
Revelation 11 in the SBT1E
Revelation 11 in the SCHL
Revelation 11 in the SNT
Revelation 11 in the SUSU
Revelation 11 in the SUSU2
Revelation 11 in the SYNO
Revelation 11 in the TBIAOTANT
Revelation 11 in the TBT1E
Revelation 11 in the TBT1E2
Revelation 11 in the TFTIP
Revelation 11 in the TFTU
Revelation 11 in the TGNTATF3T
Revelation 11 in the THAI
Revelation 11 in the TNFD
Revelation 11 in the TNT
Revelation 11 in the TNTIK
Revelation 11 in the TNTIL
Revelation 11 in the TNTIN
Revelation 11 in the TNTIP
Revelation 11 in the TNTIZ
Revelation 11 in the TOMA
Revelation 11 in the TTENT
Revelation 11 in the UBG
Revelation 11 in the UGV
Revelation 11 in the UGV2
Revelation 11 in the UGV3
Revelation 11 in the VBL
Revelation 11 in the VDCC
Revelation 11 in the YALU
Revelation 11 in the YAPE
Revelation 11 in the YBVTP
Revelation 11 in the ZBP