Revelation 16 (BOGWICC)
1 Kenaka ndinamva mawu ofuwula kuchokera ku Nyumba ya Mulungu ija kuwuza angelo asanu ndi awiri kuti, “Pitani, katsanulireni pa dziko lapansi ukali wa Mulungu umene uli mʼmbale zisanu ndi ziwirizi!” 2 Mngelo woyamba anapita natsanula mbale yake pa dziko lapansi ndipo zilonda zoyipa ndi zowawa zinabuka pa anthu amene anali ndi chizindikiro cha chirombo chija, napembedza fano lake. 3 Mngelo wachiwiri anapita natsanula mbale yake pa nyanja ndipo madzi ake anasanduka magazi, magazi ake ngati a munthu wakufa. Chamoyo chilichonse cha mʼnyanjamo chinafa. 4 Mngelo wachitatu anapita natsanula mbale yake pa mitsinje ndi akasupe amadzi ndipo zinasanduka magazi. 5 Kenaka ndinamva mngelo wolamulira madzi uja akuti,“Inu mwachita chilungamo, Inu Woyerayo,amene mulipo ndipo munalipo; 6 pakuti iwo anakhetsa magazi a oyera anu ndi aneneri anu,nʼchifukwa chake mwawapatsa magazi kuti amwe, zomwe zikuwayenera.” 7 Kenaka ndinamva mawu ochokera ku guwa lansembe akuti,“Inde, Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse,chiweruzo chanu ndi choona ndi cholungama.” 8 Mngelo wachinayi anapita natsanula mbale yake pa dzuwa ndipo dzuwa linapatsidwa mphamvu yopsereza anthu ndi moto. 9 Anapserera nako kutentha kwakukuluko ndipo anatukwana Mulungu, amene anali ndi ulamuliro pa miliri imeneyi, koma anakana kulapa ndi kumulemekeza. 10 Mngelo wachisanu anapita natsanula mbale yake pa mpando waufumu wa chirombo chija ndipo mdima unagwa ponse pamene panali ufumu wake. Anthu analuma malilime awo chifukwa cha ululu. 11 Ndipo anatukwana Mulungu wakumwamba chifukwa cha maululu awo ndi zilonda zawo koma anakana kulapa pa zimene anachita. 12 Mngelo wachisanu ndi chimodzi anapita natsanula mbale yake pa mtsinje waukulu wa Yufurate, ndipo madzi ake anaphwa kuti pakhale njira yodzera mafumu ochokera kummawa. 13 Kenaka ndinaona mizimu yoyipa itatu imene inkaoneka ngati achule; inatuluka mʼkamwa mwa chinjoka chija, mʼkamwa mwa chirombo chija ndi mʼkamwa mwa mneneri wonyenga uja. 14 Imeneyi ndiyo mizimu ya ziwanda imene imachita zizindikiro zodabwitsa ndipo imatuluka kupita kwa mafumu a dziko lonse, kukawasonkhanitsa ku nkhondo ya pa tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuzonse. 15 “Taonani, ndikubwera ngati mbala! Wodala munthu amene ali maso, nasunga zovala zake, kuti asayende maliseche kuti angaonetse maliseche ake.” 16 Kenaka mizimu ija inasonkhanitsa pamodzi mafumu ku malo amene mʼChihebri amatchedwa Armagedo. 17 Mngelo wachisanu ndi chiwiri anatsanulira mbale yake mu mlengalenga ndipo ku Nyumba ya Mulungu kunamveka mawu ofuwula kuchokera ku mpando waufumu kuti, “Kwatha!” 18 Kenaka kunachitika mphenzi, phokoso, mabingu ndi chivomerezi choopsa. Chivomerezi ngati ichi sichinachitikepo chikhalire cha munthu pa dziko lapansi. Chinali chivomerezi choopsa kwambiri. 19 Mzinda waukuluwo unagawika magawo atatu ndipo mizinda ya mitundu ya anthu inagwa. Mulungu anakumbukira Babuloni Wamkulu namupatsa chikho chake chodzaza ndi vinyo wa ukali wa mkwiyo wake. 20 Chilumba chilichonse chinathawa ndipo mapiri sanaonekenso. 21 Matalala akuluakulu olemera pafupifupi makilogalamu makumi asanu anagwa kuchokera kumwamba kugwera pa anthu. Ndipo anthu anatukwana Mulungu chifukwa cha mliri wa matalala popeza unali mliri woopsa kwambiri.
In Other Versions
Revelation 16 in the ANGEFD
Revelation 16 in the ANTPNG2D
Revelation 16 in the AS21
Revelation 16 in the BAGH
Revelation 16 in the BBPNG
Revelation 16 in the BBT1E
Revelation 16 in the BDS
Revelation 16 in the BEV
Revelation 16 in the BHAD
Revelation 16 in the BIB
Revelation 16 in the BLPT
Revelation 16 in the BNT
Revelation 16 in the BNTABOOT
Revelation 16 in the BNTLV
Revelation 16 in the BOATCB
Revelation 16 in the BOATCB2
Revelation 16 in the BOBCV
Revelation 16 in the BOCNT
Revelation 16 in the BOECS
Revelation 16 in the BOHCB
Revelation 16 in the BOHCV
Revelation 16 in the BOHLNT
Revelation 16 in the BOHNTLTAL
Revelation 16 in the BOICB
Revelation 16 in the BOILNTAP
Revelation 16 in the BOITCV
Revelation 16 in the BOKCV
Revelation 16 in the BOKCV2
Revelation 16 in the BOKHWOG
Revelation 16 in the BOKSSV
Revelation 16 in the BOLCB
Revelation 16 in the BOLCB2
Revelation 16 in the BOMCV
Revelation 16 in the BONAV
Revelation 16 in the BONCB
Revelation 16 in the BONLT
Revelation 16 in the BONUT2
Revelation 16 in the BOPLNT
Revelation 16 in the BOSCB
Revelation 16 in the BOSNC
Revelation 16 in the BOTLNT
Revelation 16 in the BOVCB
Revelation 16 in the BOYCB
Revelation 16 in the BPBB
Revelation 16 in the BPH
Revelation 16 in the BSB
Revelation 16 in the CCB
Revelation 16 in the CUV
Revelation 16 in the CUVS
Revelation 16 in the DBT
Revelation 16 in the DGDNT
Revelation 16 in the DHNT
Revelation 16 in the DNT
Revelation 16 in the ELBE
Revelation 16 in the EMTV
Revelation 16 in the ESV
Revelation 16 in the FBV
Revelation 16 in the FEB
Revelation 16 in the GGMNT
Revelation 16 in the GNT
Revelation 16 in the HARY
Revelation 16 in the HNT
Revelation 16 in the IRVA
Revelation 16 in the IRVB
Revelation 16 in the IRVG
Revelation 16 in the IRVH
Revelation 16 in the IRVK
Revelation 16 in the IRVM
Revelation 16 in the IRVM2
Revelation 16 in the IRVO
Revelation 16 in the IRVP
Revelation 16 in the IRVT
Revelation 16 in the IRVT2
Revelation 16 in the IRVU
Revelation 16 in the ISVN
Revelation 16 in the JSNT
Revelation 16 in the KAPI
Revelation 16 in the KBT1ETNIK
Revelation 16 in the KBV
Revelation 16 in the KJV
Revelation 16 in the KNFD
Revelation 16 in the LBA
Revelation 16 in the LBLA
Revelation 16 in the LNT
Revelation 16 in the LSV
Revelation 16 in the MAAL
Revelation 16 in the MBV
Revelation 16 in the MBV2
Revelation 16 in the MHNT
Revelation 16 in the MKNFD
Revelation 16 in the MNG
Revelation 16 in the MNT
Revelation 16 in the MNT2
Revelation 16 in the MRS1T
Revelation 16 in the NAA
Revelation 16 in the NASB
Revelation 16 in the NBLA
Revelation 16 in the NBS
Revelation 16 in the NBVTP
Revelation 16 in the NET2
Revelation 16 in the NIV11
Revelation 16 in the NNT
Revelation 16 in the NNT2
Revelation 16 in the NNT3
Revelation 16 in the PDDPT
Revelation 16 in the PFNT
Revelation 16 in the RMNT
Revelation 16 in the SBIAS
Revelation 16 in the SBIBS
Revelation 16 in the SBIBS2
Revelation 16 in the SBICS
Revelation 16 in the SBIDS
Revelation 16 in the SBIGS
Revelation 16 in the SBIHS
Revelation 16 in the SBIIS
Revelation 16 in the SBIIS2
Revelation 16 in the SBIIS3
Revelation 16 in the SBIKS
Revelation 16 in the SBIKS2
Revelation 16 in the SBIMS
Revelation 16 in the SBIOS
Revelation 16 in the SBIPS
Revelation 16 in the SBISS
Revelation 16 in the SBITS
Revelation 16 in the SBITS2
Revelation 16 in the SBITS3
Revelation 16 in the SBITS4
Revelation 16 in the SBIUS
Revelation 16 in the SBIVS
Revelation 16 in the SBT
Revelation 16 in the SBT1E
Revelation 16 in the SCHL
Revelation 16 in the SNT
Revelation 16 in the SUSU
Revelation 16 in the SUSU2
Revelation 16 in the SYNO
Revelation 16 in the TBIAOTANT
Revelation 16 in the TBT1E
Revelation 16 in the TBT1E2
Revelation 16 in the TFTIP
Revelation 16 in the TFTU
Revelation 16 in the TGNTATF3T
Revelation 16 in the THAI
Revelation 16 in the TNFD
Revelation 16 in the TNT
Revelation 16 in the TNTIK
Revelation 16 in the TNTIL
Revelation 16 in the TNTIN
Revelation 16 in the TNTIP
Revelation 16 in the TNTIZ
Revelation 16 in the TOMA
Revelation 16 in the TTENT
Revelation 16 in the UBG
Revelation 16 in the UGV
Revelation 16 in the UGV2
Revelation 16 in the UGV3
Revelation 16 in the VBL
Revelation 16 in the VDCC
Revelation 16 in the YALU
Revelation 16 in the YAPE
Revelation 16 in the YBVTP
Revelation 16 in the ZBP