Romans 12 (BOGWICC)
1 Nʼchifukwa chake ine ndikukupemphani abale, mwa chifundo cha Mulungu, kuti mupereke matupi anu monga nsembe yamoyo, yopatulika ndi yokondweretsa Mulungu. Nsembeyi ndiye kupembedza kwanu kwa uzimu. 2 Musafanizidwenso ndi makhalidwe a dziko lino koma musandulike pokonzanso maganizo anu. Ndipo mudzadziwa ndi kuzindikira chifuniro chabwino cha Mulungu chomwe ndi chokondweretsa ndi changwiro. 3 Chifukwa cha chisomo chopatsidwa kwa ine, ndinena kwa aliyense wa inu kuti musadziyenereze nokha kuposa mmene mulili. Koma mudziganizire nokha modzichepetsa, molingana ndi muyeso wa chikhulupiriro chimene Mulungu wakupatsani. 4 Pakuti monga aliyense wa ife ali ndi thupi limodzi koma ziwalo zambiri, ziwalozi sizili ndi ntchito yofanana. 5 Momwemonso mwa Khristu ife amene tili ambiri tipanga thupi limodzi ndipo chiwalo chilichonse ndi cholumikizika ku chinzake. 6 Ife tili ndi mphatso zosiyana, molingana ndi chisomo chopatsidwa kwa ife. Ngati mphatso ya munthu ndi kunenera, musiyeni ayigwiritse ntchito molingana ndi chikhulupiriro chake. 7 Ngati ndi kutumikira, musiyeni atumikire. Ngati ndi kuphunzitsa, musiyeni aphunzitse. 8 Ngati ndi kulimbikitsa, musiyeni alimbikitse. Ngati ndi kupereka kuthandiza osowa, musiyeni apereke mowolowamanja. Ngati ndi utsogoleri, musiyeni alamulire mosamala. Ngati ndi kuonetsa chifundo, musiyeni achite mosangalala. 9 Chikondi chikhale chopanda chinyengo. Dana nacho choyipa; gwiritsitsa chabwino. 10 Mukondane kwathunthu monga abale. Lemekezanani wina ndi mnzake kuposa inu eni. 11 Musakhale aulesi mʼmachitidwe anu. Khalani achangu mu mzimu ndipo tumikirani Ambuye. 12 Kondwerani mʼchiyembekezo, pirirani mʼmasautso ndiponso khulupirikani mʼpemphero. 13 Gawanani ndi anthu a Mulungu amene ali ndi chosowa. Cherezani alendo. 14 Adalitseni amene akuzunzani. Adalitseni ndipo musawatemberere. 15 Kondwani pamodzi ndi amene akukondwa ndipo lirani ndi amene akulira. 16 Muyanjane wina ndi mnzake. Musakhale onyada, koma lolani kuyanjana ndi anthu wamba. Musaganize kuti mumadziwa zonse. 17 Musabwezere choyipa ndi choyipa kwa aliyense. Samalitsani kuchita chabwino pamaso pa aliyense. 18 Ngati nʼkotheka, khalani mwamtendere ndi aliyense monga momwe mungathere. 19 Okondedwa anga, musabwezere choyipa, koma lekerani Mulungu. Pakuti kwalembedwa, “Kubwezera chilango nʼkwanga. Ndidzawalanga ndine,” akutero Ambuye. 20 Koma,“Ngati mdani wako ali ndi njala, mupatse chakudya.Ngati ali ndi ludzu, mupatse kanthu kakumwa.Pochita ichi, udzamuwunjikira makala amoto pamutu pake.” 21 Musagonjetsedwe ndi choyipa, koma gonjetsani choyipa pochita chabwino.
In Other Versions
Romans 12 in the ANGEFD
Romans 12 in the ANTPNG2D
Romans 12 in the AS21
Romans 12 in the BAGH
Romans 12 in the BBPNG
Romans 12 in the BBT1E
Romans 12 in the BDS
Romans 12 in the BEV
Romans 12 in the BHAD
Romans 12 in the BIB
Romans 12 in the BLPT
Romans 12 in the BNT
Romans 12 in the BNTABOOT
Romans 12 in the BNTLV
Romans 12 in the BOATCB
Romans 12 in the BOATCB2
Romans 12 in the BOBCV
Romans 12 in the BOCNT
Romans 12 in the BOECS
Romans 12 in the BOHCB
Romans 12 in the BOHCV
Romans 12 in the BOHLNT
Romans 12 in the BOHNTLTAL
Romans 12 in the BOICB
Romans 12 in the BOILNTAP
Romans 12 in the BOITCV
Romans 12 in the BOKCV
Romans 12 in the BOKCV2
Romans 12 in the BOKHWOG
Romans 12 in the BOKSSV
Romans 12 in the BOLCB
Romans 12 in the BOLCB2
Romans 12 in the BOMCV
Romans 12 in the BONAV
Romans 12 in the BONCB
Romans 12 in the BONLT
Romans 12 in the BONUT2
Romans 12 in the BOPLNT
Romans 12 in the BOSCB
Romans 12 in the BOSNC
Romans 12 in the BOTLNT
Romans 12 in the BOVCB
Romans 12 in the BOYCB
Romans 12 in the BPBB
Romans 12 in the BPH
Romans 12 in the BSB
Romans 12 in the CCB
Romans 12 in the CUV
Romans 12 in the CUVS
Romans 12 in the DBT
Romans 12 in the DGDNT
Romans 12 in the DHNT
Romans 12 in the DNT
Romans 12 in the ELBE
Romans 12 in the EMTV
Romans 12 in the ESV
Romans 12 in the FBV
Romans 12 in the FEB
Romans 12 in the GGMNT
Romans 12 in the GNT
Romans 12 in the HARY
Romans 12 in the HNT
Romans 12 in the IRVA
Romans 12 in the IRVB
Romans 12 in the IRVG
Romans 12 in the IRVH
Romans 12 in the IRVK
Romans 12 in the IRVM
Romans 12 in the IRVM2
Romans 12 in the IRVO
Romans 12 in the IRVP
Romans 12 in the IRVT
Romans 12 in the IRVT2
Romans 12 in the IRVU
Romans 12 in the ISVN
Romans 12 in the JSNT
Romans 12 in the KAPI
Romans 12 in the KBT1ETNIK
Romans 12 in the KBV
Romans 12 in the KJV
Romans 12 in the KNFD
Romans 12 in the LBA
Romans 12 in the LBLA
Romans 12 in the LNT
Romans 12 in the LSV
Romans 12 in the MAAL
Romans 12 in the MBV
Romans 12 in the MBV2
Romans 12 in the MHNT
Romans 12 in the MKNFD
Romans 12 in the MNG
Romans 12 in the MNT
Romans 12 in the MNT2
Romans 12 in the MRS1T
Romans 12 in the NAA
Romans 12 in the NASB
Romans 12 in the NBLA
Romans 12 in the NBS
Romans 12 in the NBVTP
Romans 12 in the NET2
Romans 12 in the NIV11
Romans 12 in the NNT
Romans 12 in the NNT2
Romans 12 in the NNT3
Romans 12 in the PDDPT
Romans 12 in the PFNT
Romans 12 in the RMNT
Romans 12 in the SBIAS
Romans 12 in the SBIBS
Romans 12 in the SBIBS2
Romans 12 in the SBICS
Romans 12 in the SBIDS
Romans 12 in the SBIGS
Romans 12 in the SBIHS
Romans 12 in the SBIIS
Romans 12 in the SBIIS2
Romans 12 in the SBIIS3
Romans 12 in the SBIKS
Romans 12 in the SBIKS2
Romans 12 in the SBIMS
Romans 12 in the SBIOS
Romans 12 in the SBIPS
Romans 12 in the SBISS
Romans 12 in the SBITS
Romans 12 in the SBITS2
Romans 12 in the SBITS3
Romans 12 in the SBITS4
Romans 12 in the SBIUS
Romans 12 in the SBIVS
Romans 12 in the SBT
Romans 12 in the SBT1E
Romans 12 in the SCHL
Romans 12 in the SNT
Romans 12 in the SUSU
Romans 12 in the SUSU2
Romans 12 in the SYNO
Romans 12 in the TBIAOTANT
Romans 12 in the TBT1E
Romans 12 in the TBT1E2
Romans 12 in the TFTIP
Romans 12 in the TFTU
Romans 12 in the TGNTATF3T
Romans 12 in the THAI
Romans 12 in the TNFD
Romans 12 in the TNT
Romans 12 in the TNTIK
Romans 12 in the TNTIL
Romans 12 in the TNTIN
Romans 12 in the TNTIP
Romans 12 in the TNTIZ
Romans 12 in the TOMA
Romans 12 in the TTENT
Romans 12 in the UBG
Romans 12 in the UGV
Romans 12 in the UGV2
Romans 12 in the UGV3
Romans 12 in the VBL
Romans 12 in the VDCC
Romans 12 in the YALU
Romans 12 in the YAPE
Romans 12 in the YBVTP
Romans 12 in the ZBP