Romans 14 (BOGWICC)
1 Mulandire amene ndi ofowoka mʼchikhulupiriro, osatsutsana naye pa maganizo ake. 2 Chikhulupiriro cha munthu wina chimamulola kudya china chilichonse koma munthu wina, amene chikhulupiriro chake ndi chofowoka, amangodya zamasamba zokha. 3 Munthu amene amadya chilichonse sayenera kunyoza amene satero, ndipo munthu amene samadya chilichonse asaweruze munthu amene amatero, pakuti Mulungu anamulandira. 4 Kodi ndiwe ndani kuti uweruze wantchito wamwini? Mbuye wake yekha ndiye aweruze ngati iye wakhoza kapena walephera pa ntchito yake. Ndipo adzakhoza popeza kuti Mbuye wake angathe kumukhozetsa. 5 Munthu wina amayesa tsiku limodzi lopatulika kuposa lina. Munthu wina amayesa masiku onse ofanana. Aliyense akhale otsimikiza mʼmaganizo ake. 6 Iye amene amaganiza kuti tsiku limodzi ndi lopambana, amatero kwa Ambuye. Iye amene amadya nyama, amadya mwa Ambuye pakuti amayamika Mulungu. Ndipo iye amene sadya, amatero kwa Ambuye ndi kuyamika Mulungu. 7 Pakuti palibe wina wa ife amene amakhala moyo pa yekha ndiponso palibe wina wa ife amene amafa pa yekha. 8 Ngati ife tikhala ndi moyo, ife tikhala ndi moyo kwa Ambuye. Ndipo ngati ife tifa, tifa kwa Ambuye. Choncho, ngati tikhala ndi moyo kapena kufa, ndife ake a Ambuye. 9 Pa chifukwa ichi, Khristu anafa ndi kuukanso kotero kuti Iye akhale ndi Ambuye wa akufa ndi amoyo. 10 Tsono nʼchifukwa chiyani iwe ukuweruza mʼbale wako? Kapena nʼchifukwa chiyani ukumunyoza mʼbale wako? Pakuti ife tonse tidzayima pa mpando wakuweruza wa Mulungu. 11 Kwalembedwa, akutero Ambuye,“Pamene Ine ndili ndi moyo,aliyense adzandigwadirandipo lilime lililonse lidzavomereza Mulungu.” 12 Choncho tsopano, aliyense wa ife adzafotokoza yekha kwa Mulungu. 13 Motero, tiyeni tisiye kuweruzana wina ndi mnzake. Mʼmalo mwake, tsimikizani mʼmaganizo anu kuti musayike chokhumudwitsa kapena chotchinga mʼnjira ya mʼbale wanu. 14 Monga mmodzi amene ndili mwa Ambuye Yesu, ndine wotsimikiza mtima kuti palibe chakudya chimene pachokha ndi chodetsedwa. Koma ngati wina atenga china chake kukhala chodetsedwa, kwa iyeyo ndi chodetsedwa. 15 Ngati mʼbale wako akuvutika chifukwa cha chimene umadya, iwe sukuchitanso mwachikondi. Usamuwononge mʼbale wako amene Khristu anamufera chifukwa cha chakudya chakocho. 16 Musalole kuti chimene muchiyesa chabwino achinene ngati choyipa. 17 Pakuti Ufumu wa Mulungu si nkhani yakudya ndi kumwa, koma chilungamo, mtendere ndi chimwemwe mwa Mzimu Woyera. 18 Nʼchifukwa chake aliyense amene atumikira Khristu mʼnjira iyi akondweretsa Mulungu ndi kuvomerezedwa ndi anthu. 19 Tsono tiyeni tiyesetse kuchita zimene zidzabweretsa mtendere ndi kulimbikitsana mwachikondi. 20 Musawononge ntchito ya Mulungu chifukwa cha chakudya. Chakudya chonse ndi choyera, koma munthu amalakwa ngati adya chilichonse chimene chimakhumudwitsa wina. 21 Nʼkwabwino kusadya kapena kumwa vinyo kapena kuchita chilichonse chimene chidzachititsa mʼbale wako kugwa. 22 Tsono zimene ukukhulupirira pa zinthu izi zikhale pakati pa iwe ndi Mulungu. Wodala munthu amene sadzitsutsa yekha pa zimene amazivomereza. 23 Koma munthu amene akukayika atsutsidwa ngati adya, chifukwa kudya kwake si kwa chikhulupiriro; ndipo chilichonse chosachokera mʼchikhulupiriro ndi tchimo.
In Other Versions
Romans 14 in the ANGEFD
Romans 14 in the ANTPNG2D
Romans 14 in the AS21
Romans 14 in the BAGH
Romans 14 in the BBPNG
Romans 14 in the BBT1E
Romans 14 in the BDS
Romans 14 in the BEV
Romans 14 in the BHAD
Romans 14 in the BIB
Romans 14 in the BLPT
Romans 14 in the BNT
Romans 14 in the BNTABOOT
Romans 14 in the BNTLV
Romans 14 in the BOATCB
Romans 14 in the BOATCB2
Romans 14 in the BOBCV
Romans 14 in the BOCNT
Romans 14 in the BOECS
Romans 14 in the BOHCB
Romans 14 in the BOHCV
Romans 14 in the BOHLNT
Romans 14 in the BOHNTLTAL
Romans 14 in the BOICB
Romans 14 in the BOILNTAP
Romans 14 in the BOITCV
Romans 14 in the BOKCV
Romans 14 in the BOKCV2
Romans 14 in the BOKHWOG
Romans 14 in the BOKSSV
Romans 14 in the BOLCB
Romans 14 in the BOLCB2
Romans 14 in the BOMCV
Romans 14 in the BONAV
Romans 14 in the BONCB
Romans 14 in the BONLT
Romans 14 in the BONUT2
Romans 14 in the BOPLNT
Romans 14 in the BOSCB
Romans 14 in the BOSNC
Romans 14 in the BOTLNT
Romans 14 in the BOVCB
Romans 14 in the BOYCB
Romans 14 in the BPBB
Romans 14 in the BPH
Romans 14 in the BSB
Romans 14 in the CCB
Romans 14 in the CUV
Romans 14 in the CUVS
Romans 14 in the DBT
Romans 14 in the DGDNT
Romans 14 in the DHNT
Romans 14 in the DNT
Romans 14 in the ELBE
Romans 14 in the EMTV
Romans 14 in the ESV
Romans 14 in the FBV
Romans 14 in the FEB
Romans 14 in the GGMNT
Romans 14 in the GNT
Romans 14 in the HARY
Romans 14 in the HNT
Romans 14 in the IRVA
Romans 14 in the IRVB
Romans 14 in the IRVG
Romans 14 in the IRVH
Romans 14 in the IRVK
Romans 14 in the IRVM
Romans 14 in the IRVM2
Romans 14 in the IRVO
Romans 14 in the IRVP
Romans 14 in the IRVT
Romans 14 in the IRVT2
Romans 14 in the IRVU
Romans 14 in the ISVN
Romans 14 in the JSNT
Romans 14 in the KAPI
Romans 14 in the KBT1ETNIK
Romans 14 in the KBV
Romans 14 in the KJV
Romans 14 in the KNFD
Romans 14 in the LBA
Romans 14 in the LBLA
Romans 14 in the LNT
Romans 14 in the LSV
Romans 14 in the MAAL
Romans 14 in the MBV
Romans 14 in the MBV2
Romans 14 in the MHNT
Romans 14 in the MKNFD
Romans 14 in the MNG
Romans 14 in the MNT
Romans 14 in the MNT2
Romans 14 in the MRS1T
Romans 14 in the NAA
Romans 14 in the NASB
Romans 14 in the NBLA
Romans 14 in the NBS
Romans 14 in the NBVTP
Romans 14 in the NET2
Romans 14 in the NIV11
Romans 14 in the NNT
Romans 14 in the NNT2
Romans 14 in the NNT3
Romans 14 in the PDDPT
Romans 14 in the PFNT
Romans 14 in the RMNT
Romans 14 in the SBIAS
Romans 14 in the SBIBS
Romans 14 in the SBIBS2
Romans 14 in the SBICS
Romans 14 in the SBIDS
Romans 14 in the SBIGS
Romans 14 in the SBIHS
Romans 14 in the SBIIS
Romans 14 in the SBIIS2
Romans 14 in the SBIIS3
Romans 14 in the SBIKS
Romans 14 in the SBIKS2
Romans 14 in the SBIMS
Romans 14 in the SBIOS
Romans 14 in the SBIPS
Romans 14 in the SBISS
Romans 14 in the SBITS
Romans 14 in the SBITS2
Romans 14 in the SBITS3
Romans 14 in the SBITS4
Romans 14 in the SBIUS
Romans 14 in the SBIVS
Romans 14 in the SBT
Romans 14 in the SBT1E
Romans 14 in the SCHL
Romans 14 in the SNT
Romans 14 in the SUSU
Romans 14 in the SUSU2
Romans 14 in the SYNO
Romans 14 in the TBIAOTANT
Romans 14 in the TBT1E
Romans 14 in the TBT1E2
Romans 14 in the TFTIP
Romans 14 in the TFTU
Romans 14 in the TGNTATF3T
Romans 14 in the THAI
Romans 14 in the TNFD
Romans 14 in the TNT
Romans 14 in the TNTIK
Romans 14 in the TNTIL
Romans 14 in the TNTIN
Romans 14 in the TNTIP
Romans 14 in the TNTIZ
Romans 14 in the TOMA
Romans 14 in the TTENT
Romans 14 in the UBG
Romans 14 in the UGV
Romans 14 in the UGV2
Romans 14 in the UGV3
Romans 14 in the VBL
Romans 14 in the VDCC
Romans 14 in the YALU
Romans 14 in the YAPE
Romans 14 in the YBVTP
Romans 14 in the ZBP