Romans 4 (BOGWICC)

1 Nanga tsono tidzati chiyani za Abrahamu kholo lathu, iyeyu anapezana ndi zotani pa nkhani imeneyi? 2 Kunena zoona, Abrahamu akanalungamitsidwa ndi ntchito zake, akanakhala nako kanthu kodzitamandira, koma osati pamaso pa Mulungu. 3 Kodi Malemba akuti chiyani? “Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo ichi chinamuchititsa kukhala wolungama.” 4 Tsopano munthu amene wagwira ntchito, malipiro ake satengedwa kukhala ngati mphatso koma zimene anayenera kulandira. 5 Koma kwa munthu amene sanagwire ntchito ndipo akhulupirira Mulungu amene amalungamitsa ochimwa, chikhulupiriro chakecho chimatengedwa kukhala chilungamo. 6 Davide ponena zomwezi pamene anayankhula za kudala kwa munthu amene Mulungu amulungamitsa osati chifukwa cha ntchito zake akuti, 7 “Odala ndi amenezoyipa zawo zakhululukidwa;amene machimo awo afafanizidwa. 8 Ngodala munthu amenemachimo ake Ambuye sadzawakumbukiranso.” 9 Kodi madalitso amenewa ali kwa ochita mdulidwe okha kapena kwa amene sanachitepo mdulidwe? Ife takhala tikunena kuti chikhulupiriro cha Abrahamu chinamuchititsa kukhala wolungama. 10 Kodi chinatengedwa bwanji? Kodi nʼkuti iye atachita mdulidwe kapena asanachite? Osati atachita mdulidwe koma asanachite! 11 Ndipo iye anachita mdulidwe ngati chizindikiro ndi chitsimikizo cha kulungama kumene anali nako mwachikhulupiriro pomwe anali asanachite mdulidwe. Choncho, iye ndi kholo la onse amene akhulupirira koma sanachite mdulidwe, ndi cholinga chakuti alungamitsidwe. 12 Ndipo iyenso ndiyenso kholo la ochita mdulidwe osati amene anangochita mdulidwe kokha koma amene amatsata chitsanzo cha chikhulupiriro chimene kholo lathu Abrahamu anali nacho asanachite mdulidwe. 13 Abrahamu ndi zidzukulu zake sanalandire lonjezano lakuti adzalandira dziko lapansi kudzera mu Malamulo, koma kudzera mu chilungamo chimene chimabwera ndi chikhulupiriro. 14 Pakuti ngati amene amadalira Malamulo ndiye olowa mʼmalo, ndiye kuti chikhulupiriro nʼchopanda pake ndipo lonjezano ndi lopanda phindu 15 chifukwa Malamulo anabweretsa chilango. Ndipo kumene kulibe Malamulo kulibenso kuwalakwitsa. 16 Motero, timalandira lonjezo mwachikhulupiriro. Laperekedwa mwachisomo kuti patsimikizidwe kuti lonjezolo liperekedwa kwa ana ndi zidzukulu zonse za Abrahamu, osati kwa iwo okha amene amatsatira Malamulo komanso kwa iwo amene ali ndi chikhulupiriro cha Abrahamu. Iye ndiye kholo la ife tonse. 17 Monga kwalembedwa kuti, “Ine ndakusandutsa kukhala kholo la mitundu yambiri.” Iye ndiye kholo lathu pamaso pa Mulungu, amene anamukhulupirira, Mulungu amene amapereka moyo kwa akufa ndipo amapereka moyo kwa zinthu zopanda moyo. 18 Ngakhale zinali zosayembekezeka, Abrahamu anakhulupirira ndi chiyembekezo kuti adzakhala kholo la mitundu yambiri. Izi ndi monga zinanenedwa kwa iye kuti, “Ndi mmene adzakhalire ana ako ndi zidzukulu zako.” 19 Iye sanafowoke mʼchikhulupiriro. Anadziwa choonadi cha thupi lake kuti linali lakufa popeza anali ndi zaka pafupifupi 100 ndiponso mimba ya Sara inali yowuma. 20 Komabe iye sanagwedezeke chifukwa chosakhulupirira pa zokhudzana ndi lonjezo la Mulungu. Iye analimbikitsidwa mʼchikhulupiriro chake ndi kupereka ulemerero kwa Mulungu. 21 Anatsimikiza mu mtima mwake kuti Mulungu anali ndi mphamvu yochita chomwe analonjeza. 22 Nʼchifukwa chake “chinamuchititsa kukhala wolungama.” 23 Mawu akuti, “chinatengedwa kwa iye” sanalembedwe chifukwa cha iye yekha, 24 komanso chifukwa ife amene Mulungu adzatiyesa olungama, ife amene tikhulupirira mwa Iye amene anamuukitsa kwa akufa, Yesu Ambuye athu. 25 Iye anaperekedwa kuti aphedwe chifukwa cha machimo athu ndipo anaukitsidwa ndi kukhala ndi moyo kuti tilungamitsidwe.

In Other Versions

Romans 4 in the ANGEFD

Romans 4 in the ANTPNG2D

Romans 4 in the AS21

Romans 4 in the BAGH

Romans 4 in the BBPNG

Romans 4 in the BBT1E

Romans 4 in the BDS

Romans 4 in the BEV

Romans 4 in the BHAD

Romans 4 in the BIB

Romans 4 in the BLPT

Romans 4 in the BNT

Romans 4 in the BNTABOOT

Romans 4 in the BNTLV

Romans 4 in the BOATCB

Romans 4 in the BOATCB2

Romans 4 in the BOBCV

Romans 4 in the BOCNT

Romans 4 in the BOECS

Romans 4 in the BOHCB

Romans 4 in the BOHCV

Romans 4 in the BOHLNT

Romans 4 in the BOHNTLTAL

Romans 4 in the BOICB

Romans 4 in the BOILNTAP

Romans 4 in the BOITCV

Romans 4 in the BOKCV

Romans 4 in the BOKCV2

Romans 4 in the BOKHWOG

Romans 4 in the BOKSSV

Romans 4 in the BOLCB

Romans 4 in the BOLCB2

Romans 4 in the BOMCV

Romans 4 in the BONAV

Romans 4 in the BONCB

Romans 4 in the BONLT

Romans 4 in the BONUT2

Romans 4 in the BOPLNT

Romans 4 in the BOSCB

Romans 4 in the BOSNC

Romans 4 in the BOTLNT

Romans 4 in the BOVCB

Romans 4 in the BOYCB

Romans 4 in the BPBB

Romans 4 in the BPH

Romans 4 in the BSB

Romans 4 in the CCB

Romans 4 in the CUV

Romans 4 in the CUVS

Romans 4 in the DBT

Romans 4 in the DGDNT

Romans 4 in the DHNT

Romans 4 in the DNT

Romans 4 in the ELBE

Romans 4 in the EMTV

Romans 4 in the ESV

Romans 4 in the FBV

Romans 4 in the FEB

Romans 4 in the GGMNT

Romans 4 in the GNT

Romans 4 in the HARY

Romans 4 in the HNT

Romans 4 in the IRVA

Romans 4 in the IRVB

Romans 4 in the IRVG

Romans 4 in the IRVH

Romans 4 in the IRVK

Romans 4 in the IRVM

Romans 4 in the IRVM2

Romans 4 in the IRVO

Romans 4 in the IRVP

Romans 4 in the IRVT

Romans 4 in the IRVT2

Romans 4 in the IRVU

Romans 4 in the ISVN

Romans 4 in the JSNT

Romans 4 in the KAPI

Romans 4 in the KBT1ETNIK

Romans 4 in the KBV

Romans 4 in the KJV

Romans 4 in the KNFD

Romans 4 in the LBA

Romans 4 in the LBLA

Romans 4 in the LNT

Romans 4 in the LSV

Romans 4 in the MAAL

Romans 4 in the MBV

Romans 4 in the MBV2

Romans 4 in the MHNT

Romans 4 in the MKNFD

Romans 4 in the MNG

Romans 4 in the MNT

Romans 4 in the MNT2

Romans 4 in the MRS1T

Romans 4 in the NAA

Romans 4 in the NASB

Romans 4 in the NBLA

Romans 4 in the NBS

Romans 4 in the NBVTP

Romans 4 in the NET2

Romans 4 in the NIV11

Romans 4 in the NNT

Romans 4 in the NNT2

Romans 4 in the NNT3

Romans 4 in the PDDPT

Romans 4 in the PFNT

Romans 4 in the RMNT

Romans 4 in the SBIAS

Romans 4 in the SBIBS

Romans 4 in the SBIBS2

Romans 4 in the SBICS

Romans 4 in the SBIDS

Romans 4 in the SBIGS

Romans 4 in the SBIHS

Romans 4 in the SBIIS

Romans 4 in the SBIIS2

Romans 4 in the SBIIS3

Romans 4 in the SBIKS

Romans 4 in the SBIKS2

Romans 4 in the SBIMS

Romans 4 in the SBIOS

Romans 4 in the SBIPS

Romans 4 in the SBISS

Romans 4 in the SBITS

Romans 4 in the SBITS2

Romans 4 in the SBITS3

Romans 4 in the SBITS4

Romans 4 in the SBIUS

Romans 4 in the SBIVS

Romans 4 in the SBT

Romans 4 in the SBT1E

Romans 4 in the SCHL

Romans 4 in the SNT

Romans 4 in the SUSU

Romans 4 in the SUSU2

Romans 4 in the SYNO

Romans 4 in the TBIAOTANT

Romans 4 in the TBT1E

Romans 4 in the TBT1E2

Romans 4 in the TFTIP

Romans 4 in the TFTU

Romans 4 in the TGNTATF3T

Romans 4 in the THAI

Romans 4 in the TNFD

Romans 4 in the TNT

Romans 4 in the TNTIK

Romans 4 in the TNTIL

Romans 4 in the TNTIN

Romans 4 in the TNTIP

Romans 4 in the TNTIZ

Romans 4 in the TOMA

Romans 4 in the TTENT

Romans 4 in the UBG

Romans 4 in the UGV

Romans 4 in the UGV2

Romans 4 in the UGV3

Romans 4 in the VBL

Romans 4 in the VDCC

Romans 4 in the YALU

Romans 4 in the YAPE

Romans 4 in the YBVTP

Romans 4 in the ZBP