1 Peter 3 (BOGWICC)
1 Momwemonso, akazi inu gonjerani amuna anu kuti ngati ena a iwo sakhulupirira Mawu a Mulungu, akopeke ndi makhalidwe a akazi awo ndipo sipadzafunikanso mawu 2 pamene aona moyo wanu wachiyero ndi moyo woopa Mulungu. 3 Kudzikongoletsa kwanu kusakhale kwa maonekedwe akunja, monga kuluka tsitsi ndi kuvala zokometsera zagolide ndi zovala zamberewere. 4 Mʼmalo mwake kudzikongoletsa kwanu kukhale kwa munthu wa mʼkatimo, kukongola kosatha kwa mtima ofatsa ndi mzimu wachete, zimene ndi za mtengowapatali pamaso pa Mulungu. 5 Pakuti umo ndi mmene akazi oyera mtima akale amene anali ndi chiyembekezo pa Mulungu anadzikongoletsera. Iwo ankagonjera amuna awo, 6 monga Sara, amene anamvera Abrahamu namutcha iye mbuye wake. Akazi inu ndinu ana ake ngati muchita zoyenera, ndipo musaope choopsa chilichonse. 7 Momwemonso amuna inu, khalani mwanzeru ndi akazi anu, ndipo muwachitire ulemu monga anzanu ofowoka ndiponso olandira nanu pamodzi mphatso ya moyo wosatha, kuti pasakhale kanthu kotsekereza mapemphero anu. 8 Potsiriza, nonse khalani a mtima umodzi, omverana chisoni. Kondanani monga abale, muchitirane chifundo ndi kudzichepetsa. 9 Wina akakuchitirani choyipa musabwezere pochitanso choyipa, kapena kubwezera chipongwe akakuchitirani chipongwe, koma muwadalitse. Munayitanidwa kuti mulandire mdalitso. 10 Pakuti,“Iye amene angakonde moyondi kuona masiku abwino,aletse lilime lake kuyankhula zoyipa,ndiponso milomo yake kunena mabodza. 11 Apewe zoyipa, ndipo azichita zabwino.Afunefune mtendere ndi kuyesetsa kuwupeza. 12 Pakuti Ambuye amayangʼanira bwino anthu olungamandipo amatchera khutu ku mapemphero awo.Koma Ambuye sawayangʼana bwino amene amachita zoyipa.” 13 Ndani angakuchitireni zoyipa ngati muchita changu kuchita zabwino? 14 Koma ngakhale mumve zowawa chifukwa cha chilungamo, ndinu odala. “Musaope anthu, musachite mantha.” 15 Koma lemekezani Khristu mʼmitima mwanu ngati Ambuye wanu. Khalani okonzeka nthawi zonse kuyankha aliyense amene akufunsani za chiyembekezo chimene muli nacho. 16 Koma chitani zimenezi mofatsa ndi mwaulemu, mukhale ndi chikumbumtima chosakutsutsani, kuti anthu ena akanena zoyipa za makhalidwe anu abwino mwa Khristu, achite okha manyazi ndi chipongwe chawocho. 17 Nʼkwabwino ngati ndi chifuniro cha Mulungu kumva zowawa chifukwa chochita zabwino kusiyana ndi kumva zowawa chifukwa chochita zoyipa. 18 Pakuti Khristu anafa chifukwa cha machimo kamodzi kokha kufera onse, wolungama kufera osalungama, kuti akufikitseni kwa Mulungu. Anaphedwa ku thupi koma anapatsidwa moyo mu mzimu. 19 Ndipo ali ngati mzimu chomwecho anapita ndi kukalalikira mizimu imene inali mʼndende, 20 ya anthu amene sanamvere Mulungu atadikira moleza mtima pa nthawi imene Nowa ankapanga chombo. Mʼchombo chija anthu owerengeka okha, asanu ndi atatu, ndiwo anapulumutsidwa ku madzi. 21 Madziwo akufanizira ubatizo umene lero ukukupulumutsaninso, osati chifukwa chochotsa litsiro la mʼthupi koma chifukwa cha chikumbumtima choona pamaso pa Mulungu. Umakupulumutsani chifukwa cha kuuka kwa Yesu Khristu, 22 amene anapita kumwamba ndipo ali kudzanja lamanja la Mulungu komwe angelo ndi maulamuliro ndi amphamvu amamvera Iye.
In Other Versions
1 Peter 3 in the ANGEFD
1 Peter 3 in the ANTPNG2D
1 Peter 3 in the AS21
1 Peter 3 in the BAGH
1 Peter 3 in the BBPNG
1 Peter 3 in the BBT1E
1 Peter 3 in the BDS
1 Peter 3 in the BEV
1 Peter 3 in the BHAD
1 Peter 3 in the BIB
1 Peter 3 in the BLPT
1 Peter 3 in the BNT
1 Peter 3 in the BNTABOOT
1 Peter 3 in the BNTLV
1 Peter 3 in the BOATCB
1 Peter 3 in the BOATCB2
1 Peter 3 in the BOBCV
1 Peter 3 in the BOCNT
1 Peter 3 in the BOECS
1 Peter 3 in the BOHCB
1 Peter 3 in the BOHCV
1 Peter 3 in the BOHLNT
1 Peter 3 in the BOHNTLTAL
1 Peter 3 in the BOICB
1 Peter 3 in the BOILNTAP
1 Peter 3 in the BOITCV
1 Peter 3 in the BOKCV
1 Peter 3 in the BOKCV2
1 Peter 3 in the BOKHWOG
1 Peter 3 in the BOKSSV
1 Peter 3 in the BOLCB
1 Peter 3 in the BOLCB2
1 Peter 3 in the BOMCV
1 Peter 3 in the BONAV
1 Peter 3 in the BONCB
1 Peter 3 in the BONLT
1 Peter 3 in the BONUT2
1 Peter 3 in the BOPLNT
1 Peter 3 in the BOSCB
1 Peter 3 in the BOSNC
1 Peter 3 in the BOTLNT
1 Peter 3 in the BOVCB
1 Peter 3 in the BOYCB
1 Peter 3 in the BPBB
1 Peter 3 in the BPH
1 Peter 3 in the BSB
1 Peter 3 in the CCB
1 Peter 3 in the CUV
1 Peter 3 in the CUVS
1 Peter 3 in the DBT
1 Peter 3 in the DGDNT
1 Peter 3 in the DHNT
1 Peter 3 in the DNT
1 Peter 3 in the ELBE
1 Peter 3 in the EMTV
1 Peter 3 in the ESV
1 Peter 3 in the FBV
1 Peter 3 in the FEB
1 Peter 3 in the GGMNT
1 Peter 3 in the GNT
1 Peter 3 in the HARY
1 Peter 3 in the HNT
1 Peter 3 in the IRVA
1 Peter 3 in the IRVB
1 Peter 3 in the IRVG
1 Peter 3 in the IRVH
1 Peter 3 in the IRVK
1 Peter 3 in the IRVM
1 Peter 3 in the IRVM2
1 Peter 3 in the IRVO
1 Peter 3 in the IRVP
1 Peter 3 in the IRVT
1 Peter 3 in the IRVT2
1 Peter 3 in the IRVU
1 Peter 3 in the ISVN
1 Peter 3 in the JSNT
1 Peter 3 in the KAPI
1 Peter 3 in the KBT1ETNIK
1 Peter 3 in the KBV
1 Peter 3 in the KJV
1 Peter 3 in the KNFD
1 Peter 3 in the LBA
1 Peter 3 in the LBLA
1 Peter 3 in the LNT
1 Peter 3 in the LSV
1 Peter 3 in the MAAL
1 Peter 3 in the MBV
1 Peter 3 in the MBV2
1 Peter 3 in the MHNT
1 Peter 3 in the MKNFD
1 Peter 3 in the MNG
1 Peter 3 in the MNT
1 Peter 3 in the MNT2
1 Peter 3 in the MRS1T
1 Peter 3 in the NAA
1 Peter 3 in the NASB
1 Peter 3 in the NBLA
1 Peter 3 in the NBS
1 Peter 3 in the NBVTP
1 Peter 3 in the NET2
1 Peter 3 in the NIV11
1 Peter 3 in the NNT
1 Peter 3 in the NNT2
1 Peter 3 in the NNT3
1 Peter 3 in the PDDPT
1 Peter 3 in the PFNT
1 Peter 3 in the RMNT
1 Peter 3 in the SBIAS
1 Peter 3 in the SBIBS
1 Peter 3 in the SBIBS2
1 Peter 3 in the SBICS
1 Peter 3 in the SBIDS
1 Peter 3 in the SBIGS
1 Peter 3 in the SBIHS
1 Peter 3 in the SBIIS
1 Peter 3 in the SBIIS2
1 Peter 3 in the SBIIS3
1 Peter 3 in the SBIKS
1 Peter 3 in the SBIKS2
1 Peter 3 in the SBIMS
1 Peter 3 in the SBIOS
1 Peter 3 in the SBIPS
1 Peter 3 in the SBISS
1 Peter 3 in the SBITS
1 Peter 3 in the SBITS2
1 Peter 3 in the SBITS3
1 Peter 3 in the SBITS4
1 Peter 3 in the SBIUS
1 Peter 3 in the SBIVS
1 Peter 3 in the SBT
1 Peter 3 in the SBT1E
1 Peter 3 in the SCHL
1 Peter 3 in the SNT
1 Peter 3 in the SUSU
1 Peter 3 in the SUSU2
1 Peter 3 in the SYNO
1 Peter 3 in the TBIAOTANT
1 Peter 3 in the TBT1E
1 Peter 3 in the TBT1E2
1 Peter 3 in the TFTIP
1 Peter 3 in the TFTU
1 Peter 3 in the TGNTATF3T
1 Peter 3 in the THAI
1 Peter 3 in the TNFD
1 Peter 3 in the TNT
1 Peter 3 in the TNTIK
1 Peter 3 in the TNTIL
1 Peter 3 in the TNTIN
1 Peter 3 in the TNTIP
1 Peter 3 in the TNTIZ
1 Peter 3 in the TOMA
1 Peter 3 in the TTENT
1 Peter 3 in the UBG
1 Peter 3 in the UGV
1 Peter 3 in the UGV2
1 Peter 3 in the UGV3
1 Peter 3 in the VBL
1 Peter 3 in the VDCC
1 Peter 3 in the YALU
1 Peter 3 in the YAPE
1 Peter 3 in the YBVTP
1 Peter 3 in the ZBP