1 Thessalonians 1 (BOGWICC)
1 Paulo, Silivano ndi Timoteyo.Tikulembera mpingo wa ku Tesalonika, umene uli mwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu.Chisomo ndi mtendere kwa inu. 2 Ife timayamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu. Timakutchulani mʼmapemphero athu. 3 Nthawi zonse timakumbukira ntchito yanu yachikhulupiriro, yachikondi ndi kupirira kwanu kwa chiyembekezo mwa Ambuye athu Yesu Khristu, pamaso pa Mulungu wathu ndi Atate. 4 Abale okondedwa ndi Mulungu, tikudziwa kuti Mulungu anakusankhani, 5 chifukwa uthenga wathu wabwino sunafike kwa inu ndi mawu okha, koma ndi mphamvu za Mzimu Woyera ndi chitsimikizo chachikulu. Mukudziwa mmene tinkakhalira pakati panu kuti tikuthandizeni. 6 Inu mwakhala otitsatira athu ndi a Ambuye; ngakhale kuti panali masautso akulu, munalandira uthenga mwachimwemwe chochokera kwa Mzimu Woyera. 7 Ndipo potero munakhala chitsanzo kwa abale onse a ku Makedoniya ndi Akaya. 8 Kuchokera kwa inu, uthenga wa Ambuye unamveka ku Makedoniya ndi ku Akaya ndipo mbiri ya chikhulupiriro chanu mwa Mulungu yamveka ponseponse. Choncho sikofunikanso kuti tinene kanthu, 9 pakuti iwo amafotokoza za momwe munatilandirira. Iwo amatiwuza za momwe munatembenukira kwa Mulungu kusiya mafano ndi kutumikira Mulungu wamoyo ndi woona. 10 Ndipo mukudikira Mwana wake kuchokera kumwamba, Yesu, amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa. Iyeyo amatipulumutsa ku mkwiyo umene ukubwera.
In Other Versions
1 Thessalonians 1 in the ANGEFD
1 Thessalonians 1 in the ANTPNG2D
1 Thessalonians 1 in the BBPNG
1 Thessalonians 1 in the BBT1E
1 Thessalonians 1 in the BNTABOOT
1 Thessalonians 1 in the BNTLV
1 Thessalonians 1 in the BOATCB
1 Thessalonians 1 in the BOATCB2
1 Thessalonians 1 in the BOBCV
1 Thessalonians 1 in the BOCNT
1 Thessalonians 1 in the BOECS
1 Thessalonians 1 in the BOHCB
1 Thessalonians 1 in the BOHCV
1 Thessalonians 1 in the BOHLNT
1 Thessalonians 1 in the BOHNTLTAL
1 Thessalonians 1 in the BOICB
1 Thessalonians 1 in the BOILNTAP
1 Thessalonians 1 in the BOITCV
1 Thessalonians 1 in the BOKCV
1 Thessalonians 1 in the BOKCV2
1 Thessalonians 1 in the BOKHWOG
1 Thessalonians 1 in the BOKSSV
1 Thessalonians 1 in the BOLCB
1 Thessalonians 1 in the BOLCB2
1 Thessalonians 1 in the BOMCV
1 Thessalonians 1 in the BONAV
1 Thessalonians 1 in the BONCB
1 Thessalonians 1 in the BONLT
1 Thessalonians 1 in the BONUT2
1 Thessalonians 1 in the BOPLNT
1 Thessalonians 1 in the BOSCB
1 Thessalonians 1 in the BOSNC
1 Thessalonians 1 in the BOTLNT
1 Thessalonians 1 in the BOVCB
1 Thessalonians 1 in the BOYCB
1 Thessalonians 1 in the DGDNT
1 Thessalonians 1 in the GGMNT
1 Thessalonians 1 in the IRVM2
1 Thessalonians 1 in the IRVT2
1 Thessalonians 1 in the KBT1ETNIK
1 Thessalonians 1 in the MKNFD
1 Thessalonians 1 in the MRS1T
1 Thessalonians 1 in the NBVTP
1 Thessalonians 1 in the NIV11
1 Thessalonians 1 in the PDDPT
1 Thessalonians 1 in the SBIAS
1 Thessalonians 1 in the SBIBS
1 Thessalonians 1 in the SBIBS2
1 Thessalonians 1 in the SBICS
1 Thessalonians 1 in the SBIDS
1 Thessalonians 1 in the SBIGS
1 Thessalonians 1 in the SBIHS
1 Thessalonians 1 in the SBIIS
1 Thessalonians 1 in the SBIIS2
1 Thessalonians 1 in the SBIIS3
1 Thessalonians 1 in the SBIKS
1 Thessalonians 1 in the SBIKS2
1 Thessalonians 1 in the SBIMS
1 Thessalonians 1 in the SBIOS
1 Thessalonians 1 in the SBIPS
1 Thessalonians 1 in the SBISS
1 Thessalonians 1 in the SBITS
1 Thessalonians 1 in the SBITS2
1 Thessalonians 1 in the SBITS3
1 Thessalonians 1 in the SBITS4
1 Thessalonians 1 in the SBIUS
1 Thessalonians 1 in the SBIVS
1 Thessalonians 1 in the SBT1E
1 Thessalonians 1 in the SUSU2
1 Thessalonians 1 in the TBIAOTANT
1 Thessalonians 1 in the TBT1E
1 Thessalonians 1 in the TBT1E2
1 Thessalonians 1 in the TFTIP
1 Thessalonians 1 in the TGNTATF3T
1 Thessalonians 1 in the TNTIK
1 Thessalonians 1 in the TNTIL
1 Thessalonians 1 in the TNTIN
1 Thessalonians 1 in the TNTIP
1 Thessalonians 1 in the TNTIZ
1 Thessalonians 1 in the TTENT