2 Chronicles 13 (BOGWICC)

1 Mʼchaka cha 18 cha ulamuliro wa Yeroboamu, Abiya analowa ufumu wa Yuda, 2 ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka zitatu. Dzina la amayi ake linali Maaka mwana wa Urieli wa ku Gibeya.Koma panali nkhondo pakati pa Abiya ndi Yeroboamu. 3 Abiya anapita ku nkhondo ndi asilikali odziwa bwino nkhondo 400,000, ndipo Yeroboamu anandandalitsa ankhondo, asilikali 800,000 odziwa bwino nkhondo, osankhidwa ndi amphamvu, woti amenyane naye. 4 Abiya anayima pa phiri la Zemaraimu, mʼdziko lamapiri la Efereimu, ndipo anati, “Yeroboamu ndi Aisraeli onse, tandimverani! 5 Kodi inu simukudziwa kuti Yehova, Mulungu wa Israeli, wapereka ufumu wa Israeli kwa Davide ndi zidzukulu zake mpaka muyaya ndiponso pangano la mchere? 6 Komabe Yeroboamu mwana wa Nebati, mtumiki wa Solomoni mwana wa Davide, anawukira mbuye wake. 7 Ndipo anthu ena achabechabe anasonkhana kwa iye ndipo anatsutsana ndi Rehobowamu mwana wa Solomoni pamene anali wamngʼono ndi wosalimba mtima ndi wopanda mphamvu kuti athe kulimbana nawo. 8 “Ndipo tsopano inu mwakonzekera kutsutsana ndi ufumu wa Yehova, umene uli mʼmanja mwa zidzukulu za Davide. Inu ndithu mulipo ankhondo ambirimbiri ndipo muli ndi ana angʼombe agolide amene Yeroboamu anapanga kuti akhale milungu yanu. 9 Koma kodi inu simunathamangitse ansembe a Yehova, ana a Aaroni ndiponso Alevi ndi kudzisankhira ansembe anuanu monga anthu ena amachitira? Aliyense amene amabwera kuti adzipatule atatenga mwana wangʼombe wamwamuna ndi nkhosa zazimuna zisanu ndi ziwiri amakhala wansembe wa zinthu zimene sizili milungu. 10 “Koma kunena za ife, Yehova ndiye Mulungu wathu, ndipo sitinamusiye. Ansembe amene amatumikira Yehova ndi ana a Aaroni ndipo amathandizidwa ndi Alevi. 11 Mmawa uliwonse ndi madzulo aliwonse amapereka nsembe zopsereza ndi kufukiza lubani kwa Yehova. Iwo amayika buledi pa tebulo loyeretsedwa monga mwa mwambo ndipo amayatsa nyale pa zoyikapo nyale zagolide madzulo aliwonse. Ife timachita zofuna za Yehova Mulungu wathu. Koma inu mwamusiya. 12 Mulungu ali nafe pakuti ndiye mtsogoleri wathu. Ansembe ake atanyamula malipenga, adzayimba mfuwu wankhondo kulimbana nanu. Inu Aisraeli musalimbane ndi Yehova, Mulungu wa makolo anu, pakuti simungathe kupambana.” 13 Tsono Yeroboamu anali atatumiza asilikali kumbuyo mowazungulira, kotero kuti iye ali kutsogolo kwa anthu a ku Yuda, anthu owabisalira anali kumbuyo kwawo. 14 Asilikali a Yuda anatembenuka ndipo anaona kuti nkhondo imachitikira kutsogolo ndi kumbuyo. Ndipo iwo anafuwulira Yehova. Ansembe anayimba malipenga awo 15 ndipo asilikali a Yuda anafuwula mawu ankhondo. Atafuwula mawu ankhondowo, Mulungu anagonjetsa Yeroboamu pamodzi ndi Aisraeli onse pamaso pa Abiya ndi Yuda. 16 Aisraeli anathawa Ayuda. Ndipo Mulungu anawapereka mʼmanja mwawo. 17 Abiya pamodzi ndi anthu ake anapha anthu ambiri, kotero kuti Aisraeli 500,000 odziwa bwino nkhondo anaphedwa. 18 Ankhondo a Israeli anagonjetsedwa pa nthawi imeneyi, ndipo ankhondo a Yuda anapambana chifukwa anadalira Yehova, Mulungu wa makolo awo. 19 Abiya anathamangitsa Yeroboamu ndipo anamulanda mizinda ya Beteli, Yesana, ndi Efroni pamodzi ndi midzi yawo yozungulira. 20 Yeroboamu sanapezenso mphamvu nthawi ya Abiya. Ndipo Yehova anamukantha nafa. 21 Koma Abiya mphamvu zake zinakula. Iye anakwatira akazi 14 ndipo anali ndi ana aamuna 22 ndi ana aakazi 16. 22 Zina ndi zina zokhudza Abiya, zimene anachita ndi zimene anayankhula, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mneneri Ido.

In Other Versions

2 Chronicles 13 in the ANGEFD

2 Chronicles 13 in the ANTPNG2D

2 Chronicles 13 in the AS21

2 Chronicles 13 in the BAGH

2 Chronicles 13 in the BBPNG

2 Chronicles 13 in the BBT1E

2 Chronicles 13 in the BDS

2 Chronicles 13 in the BEV

2 Chronicles 13 in the BHAD

2 Chronicles 13 in the BIB

2 Chronicles 13 in the BLPT

2 Chronicles 13 in the BNT

2 Chronicles 13 in the BNTABOOT

2 Chronicles 13 in the BNTLV

2 Chronicles 13 in the BOATCB

2 Chronicles 13 in the BOATCB2

2 Chronicles 13 in the BOBCV

2 Chronicles 13 in the BOCNT

2 Chronicles 13 in the BOECS

2 Chronicles 13 in the BOHCB

2 Chronicles 13 in the BOHCV

2 Chronicles 13 in the BOHLNT

2 Chronicles 13 in the BOHNTLTAL

2 Chronicles 13 in the BOICB

2 Chronicles 13 in the BOILNTAP

2 Chronicles 13 in the BOITCV

2 Chronicles 13 in the BOKCV

2 Chronicles 13 in the BOKCV2

2 Chronicles 13 in the BOKHWOG

2 Chronicles 13 in the BOKSSV

2 Chronicles 13 in the BOLCB

2 Chronicles 13 in the BOLCB2

2 Chronicles 13 in the BOMCV

2 Chronicles 13 in the BONAV

2 Chronicles 13 in the BONCB

2 Chronicles 13 in the BONLT

2 Chronicles 13 in the BONUT2

2 Chronicles 13 in the BOPLNT

2 Chronicles 13 in the BOSCB

2 Chronicles 13 in the BOSNC

2 Chronicles 13 in the BOTLNT

2 Chronicles 13 in the BOVCB

2 Chronicles 13 in the BOYCB

2 Chronicles 13 in the BPBB

2 Chronicles 13 in the BPH

2 Chronicles 13 in the BSB

2 Chronicles 13 in the CCB

2 Chronicles 13 in the CUV

2 Chronicles 13 in the CUVS

2 Chronicles 13 in the DBT

2 Chronicles 13 in the DGDNT

2 Chronicles 13 in the DHNT

2 Chronicles 13 in the DNT

2 Chronicles 13 in the ELBE

2 Chronicles 13 in the EMTV

2 Chronicles 13 in the ESV

2 Chronicles 13 in the FBV

2 Chronicles 13 in the FEB

2 Chronicles 13 in the GGMNT

2 Chronicles 13 in the GNT

2 Chronicles 13 in the HARY

2 Chronicles 13 in the HNT

2 Chronicles 13 in the IRVA

2 Chronicles 13 in the IRVB

2 Chronicles 13 in the IRVG

2 Chronicles 13 in the IRVH

2 Chronicles 13 in the IRVK

2 Chronicles 13 in the IRVM

2 Chronicles 13 in the IRVM2

2 Chronicles 13 in the IRVO

2 Chronicles 13 in the IRVP

2 Chronicles 13 in the IRVT

2 Chronicles 13 in the IRVT2

2 Chronicles 13 in the IRVU

2 Chronicles 13 in the ISVN

2 Chronicles 13 in the JSNT

2 Chronicles 13 in the KAPI

2 Chronicles 13 in the KBT1ETNIK

2 Chronicles 13 in the KBV

2 Chronicles 13 in the KJV

2 Chronicles 13 in the KNFD

2 Chronicles 13 in the LBA

2 Chronicles 13 in the LBLA

2 Chronicles 13 in the LNT

2 Chronicles 13 in the LSV

2 Chronicles 13 in the MAAL

2 Chronicles 13 in the MBV

2 Chronicles 13 in the MBV2

2 Chronicles 13 in the MHNT

2 Chronicles 13 in the MKNFD

2 Chronicles 13 in the MNG

2 Chronicles 13 in the MNT

2 Chronicles 13 in the MNT2

2 Chronicles 13 in the MRS1T

2 Chronicles 13 in the NAA

2 Chronicles 13 in the NASB

2 Chronicles 13 in the NBLA

2 Chronicles 13 in the NBS

2 Chronicles 13 in the NBVTP

2 Chronicles 13 in the NET2

2 Chronicles 13 in the NIV11

2 Chronicles 13 in the NNT

2 Chronicles 13 in the NNT2

2 Chronicles 13 in the NNT3

2 Chronicles 13 in the PDDPT

2 Chronicles 13 in the PFNT

2 Chronicles 13 in the RMNT

2 Chronicles 13 in the SBIAS

2 Chronicles 13 in the SBIBS

2 Chronicles 13 in the SBIBS2

2 Chronicles 13 in the SBICS

2 Chronicles 13 in the SBIDS

2 Chronicles 13 in the SBIGS

2 Chronicles 13 in the SBIHS

2 Chronicles 13 in the SBIIS

2 Chronicles 13 in the SBIIS2

2 Chronicles 13 in the SBIIS3

2 Chronicles 13 in the SBIKS

2 Chronicles 13 in the SBIKS2

2 Chronicles 13 in the SBIMS

2 Chronicles 13 in the SBIOS

2 Chronicles 13 in the SBIPS

2 Chronicles 13 in the SBISS

2 Chronicles 13 in the SBITS

2 Chronicles 13 in the SBITS2

2 Chronicles 13 in the SBITS3

2 Chronicles 13 in the SBITS4

2 Chronicles 13 in the SBIUS

2 Chronicles 13 in the SBIVS

2 Chronicles 13 in the SBT

2 Chronicles 13 in the SBT1E

2 Chronicles 13 in the SCHL

2 Chronicles 13 in the SNT

2 Chronicles 13 in the SUSU

2 Chronicles 13 in the SUSU2

2 Chronicles 13 in the SYNO

2 Chronicles 13 in the TBIAOTANT

2 Chronicles 13 in the TBT1E

2 Chronicles 13 in the TBT1E2

2 Chronicles 13 in the TFTIP

2 Chronicles 13 in the TFTU

2 Chronicles 13 in the TGNTATF3T

2 Chronicles 13 in the THAI

2 Chronicles 13 in the TNFD

2 Chronicles 13 in the TNT

2 Chronicles 13 in the TNTIK

2 Chronicles 13 in the TNTIL

2 Chronicles 13 in the TNTIN

2 Chronicles 13 in the TNTIP

2 Chronicles 13 in the TNTIZ

2 Chronicles 13 in the TOMA

2 Chronicles 13 in the TTENT

2 Chronicles 13 in the UBG

2 Chronicles 13 in the UGV

2 Chronicles 13 in the UGV2

2 Chronicles 13 in the UGV3

2 Chronicles 13 in the VBL

2 Chronicles 13 in the VDCC

2 Chronicles 13 in the YALU

2 Chronicles 13 in the YAPE

2 Chronicles 13 in the YBVTP

2 Chronicles 13 in the ZBP