2 Chronicles 23 (BOGWICC)

1 Mʼchaka chachisanu ndi chiwiri Yehoyada anaonetsa mphamvu zake. Iye anachita pangano ndi olamulira magulu a anthu 100: Azariya mwana wa Yerohamu, Ismaeli mwana wa Yehohanani, Azariya mwana wa Obedi, Maaseya mwana wa Adaya ndi Elisafati mwana wa Zikiri. 2 Iwo anayendayenda mʼdziko la Yuda ndipo anasonkhanitsa Alevi ndi atsogoleri a mabanja a Aisraeli ochokera mʼmizinda yonse. Atabwera ku Yerusalemu, 3 msonkhano wonse unachita pangano ndi mfumu mu Nyumba ya Mulungu.Yehoyada anawawuza kuti, “Mwana wa mfumu adzalamulira monga ananenera Yehova zokhudza ana a Davide. 4 Tsopano zimene muti muchite ndi izi: Limodzi mwa magawo atatu a ansembe ndi Alevi amene mudzakhale pa ntchito pa Sabata muzikalondera pa khomo, 5 ndi limodzi la magawo atatu likakhale ku nyumba yaufumu ndipo limodzi la magawo atatu likakhale ku chipata cha Maziko ndipo anthu ena onse akakhale mʼmabwalo a Nyumba ya Yehova. 6 Musalole aliyense kulowa mʼNyumba ya Yehova kupatula ansembe ndi Alevi amene akutumikira. Iwo atha kutero chifukwa apatulidwa koma anthu ena onse ayenera kumvera zimene Yehova walamula. 7 Alevi akhale mozungulira mfumu, munthu aliyense ali ndi chida chake mʼmanja. Aliyense amene alowe mʼNyumba ya Mulungu ayenera kuphedwa. Mukhale nayo pafupi mfumu kulikonse kumene izipita.” 8 Alevi ndi anthu onse a ku Yuda anachita monga momwe wansembe Yehoyada anawalamulira. Aliyense anatenga anthu ake amene ankagwira ntchito pa Sabata ndi amene amapita kukapuma, pakuti wansembe Yehoyada sanalole gulu lililonse kuti lipite. 9 Ndipo Yehoyada anapereka kwa atsogoleri a magulu a anthu 100 mikondo ndi zishango zazikulu ndi zazingʼono zimene zinali za Davide ndipo zinali mʼNyumba ya Mulungu. 10 Iye anayika anthu onse, aliyense ali ndi chida mʼdzanja lake mozungulira mfumu pafupi ndi guwa ndi Nyumba ya Mulungu, kuyambira mbali ya kummwera mpaka kumpoto kwa Nyumba ya Mulungu. 11 Yehoyada ndi ana ake anatulutsa mwana wa mfumu ndipo anamumveka chipewa chaufumu ndipo anamupatsa Buku la Chipangano namulonga ufumu. Yehoyada ndi ana ake anamudzoza ndipo anafuwula kuti, “Ikhale ndi moyo wautali mfumu!” 12 Ataliya atamva phokoso la anthu akuthamanga ndi kukondwerera mfumu, anapita ku Nyumba ya Yehova komwe kunali anthuko. 13 Iye anayangʼana, ndipo anaona mfumu itayima pa chipilala chake chapakhomo. Atsogoleri ndi oyimba malipenga anali pafupi ndi mfumuyo, ndipo anthu onse a mʼderali amakondwerera ndi kuyimba malipenga ndiponso oyimba ndi zida amatsogolera matamando. Pamenepo Ataliya anangʼamba mkanjo wake ndipo anafuwula kuti, “Kuwukira! Kuwukira!” 14 Wansembe Yehoyada anatumiza olamulira magulu a anthu 100 aja, amene amayangʼanira asilikali ndipo anawawuza kuti, “Mutulutseni ameneyu pakati pa mizere yanu ndipo muphe aliyense amene adzamutsata.” Pakuti ansembe anati, “Musamuphere mʼNyumba ya Mulungu wa Yehova,” 15 choncho anamugwira pamene amafika pa chipata cha Kavalo pa bwalo la nyumba yaufumu, ndipo anamuphera pamenepo. 16 Tsono Yehoyada anachita pangano, iye mwini ndi anthu onse ndiponso mfumu kuti adzakhala anthu a Yehova. 17 Anthu onse anapita ku kachisi wa Baala ndipo anamugwetsa. Iwo anaphwanya maguwa ndi mafano ndi kupha Matani wansembe wa Baala patsogolo pa maguwawo. 18 Kenaka Yehoyada anayika ansembe, omwe anali Alevi kukhala oyangʼanira Nyumba ya Yehova, amene Davide anawapatsa ntchito yoti azipereka nsembe zopsereza kwa Yehova mʼNyumba ya Mulungu, monga zinalembedwa mʼmalamulo a Mose kuti azitero akukondwera ndi kuyimba monga Davide analamulira. 19 Ndipo anayika alonda a pa khomo pa zipata za Nyumba ya Yehova kuti aliyense amene ndi odetsedwa asalowe. 20 Iye anatenga olamulira magulu a anthu 100, anthu otchuka, olamulira anthu ndi anthu onse a mʼderalo ndipo anabweretsa mfumu kuchokera ku Nyumba ya Mulungu. Iwo anapita ku nyumba yaufumu kudzera ku Chipata Chakumitu ndipo anayikira mfumu mpando wolemekezeka, 21 ndipo anthu onse a mʼderali anakondwera. Tsono mu mzinda munali bata chifukwa Ataliya anaphedwa ndi lupanga.

In Other Versions

2 Chronicles 23 in the ANGEFD

2 Chronicles 23 in the ANTPNG2D

2 Chronicles 23 in the AS21

2 Chronicles 23 in the BAGH

2 Chronicles 23 in the BBPNG

2 Chronicles 23 in the BBT1E

2 Chronicles 23 in the BDS

2 Chronicles 23 in the BEV

2 Chronicles 23 in the BHAD

2 Chronicles 23 in the BIB

2 Chronicles 23 in the BLPT

2 Chronicles 23 in the BNT

2 Chronicles 23 in the BNTABOOT

2 Chronicles 23 in the BNTLV

2 Chronicles 23 in the BOATCB

2 Chronicles 23 in the BOATCB2

2 Chronicles 23 in the BOBCV

2 Chronicles 23 in the BOCNT

2 Chronicles 23 in the BOECS

2 Chronicles 23 in the BOHCB

2 Chronicles 23 in the BOHCV

2 Chronicles 23 in the BOHLNT

2 Chronicles 23 in the BOHNTLTAL

2 Chronicles 23 in the BOICB

2 Chronicles 23 in the BOILNTAP

2 Chronicles 23 in the BOITCV

2 Chronicles 23 in the BOKCV

2 Chronicles 23 in the BOKCV2

2 Chronicles 23 in the BOKHWOG

2 Chronicles 23 in the BOKSSV

2 Chronicles 23 in the BOLCB

2 Chronicles 23 in the BOLCB2

2 Chronicles 23 in the BOMCV

2 Chronicles 23 in the BONAV

2 Chronicles 23 in the BONCB

2 Chronicles 23 in the BONLT

2 Chronicles 23 in the BONUT2

2 Chronicles 23 in the BOPLNT

2 Chronicles 23 in the BOSCB

2 Chronicles 23 in the BOSNC

2 Chronicles 23 in the BOTLNT

2 Chronicles 23 in the BOVCB

2 Chronicles 23 in the BOYCB

2 Chronicles 23 in the BPBB

2 Chronicles 23 in the BPH

2 Chronicles 23 in the BSB

2 Chronicles 23 in the CCB

2 Chronicles 23 in the CUV

2 Chronicles 23 in the CUVS

2 Chronicles 23 in the DBT

2 Chronicles 23 in the DGDNT

2 Chronicles 23 in the DHNT

2 Chronicles 23 in the DNT

2 Chronicles 23 in the ELBE

2 Chronicles 23 in the EMTV

2 Chronicles 23 in the ESV

2 Chronicles 23 in the FBV

2 Chronicles 23 in the FEB

2 Chronicles 23 in the GGMNT

2 Chronicles 23 in the GNT

2 Chronicles 23 in the HARY

2 Chronicles 23 in the HNT

2 Chronicles 23 in the IRVA

2 Chronicles 23 in the IRVB

2 Chronicles 23 in the IRVG

2 Chronicles 23 in the IRVH

2 Chronicles 23 in the IRVK

2 Chronicles 23 in the IRVM

2 Chronicles 23 in the IRVM2

2 Chronicles 23 in the IRVO

2 Chronicles 23 in the IRVP

2 Chronicles 23 in the IRVT

2 Chronicles 23 in the IRVT2

2 Chronicles 23 in the IRVU

2 Chronicles 23 in the ISVN

2 Chronicles 23 in the JSNT

2 Chronicles 23 in the KAPI

2 Chronicles 23 in the KBT1ETNIK

2 Chronicles 23 in the KBV

2 Chronicles 23 in the KJV

2 Chronicles 23 in the KNFD

2 Chronicles 23 in the LBA

2 Chronicles 23 in the LBLA

2 Chronicles 23 in the LNT

2 Chronicles 23 in the LSV

2 Chronicles 23 in the MAAL

2 Chronicles 23 in the MBV

2 Chronicles 23 in the MBV2

2 Chronicles 23 in the MHNT

2 Chronicles 23 in the MKNFD

2 Chronicles 23 in the MNG

2 Chronicles 23 in the MNT

2 Chronicles 23 in the MNT2

2 Chronicles 23 in the MRS1T

2 Chronicles 23 in the NAA

2 Chronicles 23 in the NASB

2 Chronicles 23 in the NBLA

2 Chronicles 23 in the NBS

2 Chronicles 23 in the NBVTP

2 Chronicles 23 in the NET2

2 Chronicles 23 in the NIV11

2 Chronicles 23 in the NNT

2 Chronicles 23 in the NNT2

2 Chronicles 23 in the NNT3

2 Chronicles 23 in the PDDPT

2 Chronicles 23 in the PFNT

2 Chronicles 23 in the RMNT

2 Chronicles 23 in the SBIAS

2 Chronicles 23 in the SBIBS

2 Chronicles 23 in the SBIBS2

2 Chronicles 23 in the SBICS

2 Chronicles 23 in the SBIDS

2 Chronicles 23 in the SBIGS

2 Chronicles 23 in the SBIHS

2 Chronicles 23 in the SBIIS

2 Chronicles 23 in the SBIIS2

2 Chronicles 23 in the SBIIS3

2 Chronicles 23 in the SBIKS

2 Chronicles 23 in the SBIKS2

2 Chronicles 23 in the SBIMS

2 Chronicles 23 in the SBIOS

2 Chronicles 23 in the SBIPS

2 Chronicles 23 in the SBISS

2 Chronicles 23 in the SBITS

2 Chronicles 23 in the SBITS2

2 Chronicles 23 in the SBITS3

2 Chronicles 23 in the SBITS4

2 Chronicles 23 in the SBIUS

2 Chronicles 23 in the SBIVS

2 Chronicles 23 in the SBT

2 Chronicles 23 in the SBT1E

2 Chronicles 23 in the SCHL

2 Chronicles 23 in the SNT

2 Chronicles 23 in the SUSU

2 Chronicles 23 in the SUSU2

2 Chronicles 23 in the SYNO

2 Chronicles 23 in the TBIAOTANT

2 Chronicles 23 in the TBT1E

2 Chronicles 23 in the TBT1E2

2 Chronicles 23 in the TFTIP

2 Chronicles 23 in the TFTU

2 Chronicles 23 in the TGNTATF3T

2 Chronicles 23 in the THAI

2 Chronicles 23 in the TNFD

2 Chronicles 23 in the TNT

2 Chronicles 23 in the TNTIK

2 Chronicles 23 in the TNTIL

2 Chronicles 23 in the TNTIN

2 Chronicles 23 in the TNTIP

2 Chronicles 23 in the TNTIZ

2 Chronicles 23 in the TOMA

2 Chronicles 23 in the TTENT

2 Chronicles 23 in the UBG

2 Chronicles 23 in the UGV

2 Chronicles 23 in the UGV2

2 Chronicles 23 in the UGV3

2 Chronicles 23 in the VBL

2 Chronicles 23 in the VDCC

2 Chronicles 23 in the YALU

2 Chronicles 23 in the YAPE

2 Chronicles 23 in the YBVTP

2 Chronicles 23 in the ZBP