Acts 13 (BOGWICC)

1 Mu mpingo wa ku Antiokeya munali aneneri ndi aphunzitsi awa: Barnaba, Simeoni, Lukia wa ku Kurene, Manayeni (amene analeredwa pamodzi ndi mfumu Herode), ndiponso Saulo. 2 Iwo pamene ankapembedza Ambuye ndi kusala kudya, Mzimu Woyera anati, “Mundipatulire Barnaba ndi Saulo kuti akagwire ntchito imene ndinawayitanira.” 3 Ndipo atasala kudya ndi kupemphera anasanjika manja awo pa iwo nawatumiza. 4 Barnaba ndi Saulo motumidwa ndi Mzimu Woyera, anapita ku Selukeya ndipo kuchokera kumeneko anakwera sitima ya pamadzi kupita ku Kupro. 5 Pamene anafika ku Salamisi, analalikira Mawu a Mulungu mʼMasunagoge a Ayuda. Iwo anali ndi Yohane monga wowatumikira. 6 Iwo anayenda pa chilumba chonse mpaka anafika ku Pafo, kumeneko anapezanako ndi Myuda, wamatsenga amene analinso mneneri wonama dzina lake Barayesu. 7 Iyeyu, amathandiza mkulu wa boma, Sergio Paulo. Mkulu wa bomayu, munthu wanzeru, anayitana Barnaba ndi Saulo chifukwa anafuna kumva Mawu a Mulungu. 8 Koma Elima wamatsengayo, (Elima tanthauzo lake ndi wamatsenga), anatsutsana nawo ndipo anafuna kumuletsa mkulu wa bomayo kuti asakhulupirire. 9 Koma Saulo, amenenso amatchedwa Paulo, wodzazidwa ndi Mzimu Woyera anamuyangʼanitsitsa Elima ndipo anati, 10 “Iwe ndiwe mwana wa mdierekezi ndiponso mdani wa chilungamo! Ndiwe wodzaza ndi chinyengo cha mtundu uliwonse ndi kuchenjera konse. Kodi sudzaleka kupotoza njira zolungama za Ambuye? 11 Tsopano dzanja la Ambuye likukutsutsa iwe. Udzakhala wosaona ndipo kwa kanthawi sudzatha kuona kuwala kwa dzuwa.”Nthawi yomweyo khungu ndi mdima zinamugwera ndipo anafunafuna munthu woti amugwire dzanja kuti amutsogolere. 12 Pamene mkulu wa bomayo anaona zimene zinachitika anakhulupirira pakuti anadabwa ndi chiphunzitso cha Ambuye. 13 Kuchokera ku Pafo, Paulo ndi anzake anayenda pa sitima ya pamadzi kupita ku Perga wa ku Pamfiliya, kumeneko Yohane anawasiya nabwerera ku Yerusalemu. 14 Kuchokera ku Perga anapita ku Pisidiya wa ku Antiokeya. Pa tsiku la Sabata analowa mʼsunagoge, nakhala pansi. 15 Atawerenga mawu a mʼMalamulo ndi Aneneri, akulu a sunagoge anawatumizira mawu ndi kuti, “Abale ngati muli ndi mawu olimbikitsa nawo anthuwa, nenani.” 16 Atayimirira, Paulo anakweza dzanja lake ndi kuti, “Inu Aisraeli ndiponso inu a mitundu ina amene mumapembedza Mulungu, tandimverani! 17 Mulungu wa Aisraeli anasankha makolo athu ndipo anawapatsa chuma chambiri pamene amakhala ku Igupto. Anawatulutsa mʼdzikomo ndi dzanja lake lamphamvu. 18 Ndipo Iye anapirira khalidwe lawo mʼchipululu kwa zaka makumi anayi. 19 Mulungu anawagonjetsera mitundu isanu ndi iwiri ya ku Kanaani ndipo anapereka dzikolo kwa Israeli kuti likhale lawo. 20 Izi zonse zinatenga zaka 450.“Zitatha izi, Mulungu anawapatsa oweruza mpaka nthawi ya mneneri Samueli. 21 Kenaka anthu anapempha kuti awapatse mfumu, ndipo anawapatsa Sauli mwana wa Kisi, wa fuko la Benjamini amene analamulira zaka makumi anayi. 22 Mulungu atamuchotsa Sauli, anayika Davide kukhala mfumu yawo. Mulungu anamuchitira umboni kuti, ‘Ndapeza Davide mwana wa Yese munthu wa pamtima panga; iye adzachita zonse zimene ine ndikufuna kuti iye achite.’ 23 “Kuchokera mwa zidzukulu za munthu ameneyu, Mulungu anawutsa Yesu kukhala Mpulumutsi wa Aisraeli, monga analonjezera. 24 Yesu asanabwere, Yohane analalikira kwa anthu onse Aisraeli za kutembenuka mtima ndi ubatizo. 25 Pamene Yohane amatsiriza ntchito yake anati: ‘Mukuganiza kuti ine ndine yani? Ine sindine ameneyo ayi, koma Iye akubwera pambuyo panga, amene ine sindine woyenera kumasula zingwe za nsapato zake.’ 26 “Abale, ana a Abrahamu, ndiponso inu a mitundu ina amene mumaopa Mulungu, Iye watumiza uthenga wachipulumutsowo kwa ife. 27 Anthu a ku Yerusalemu ndi atsogoleri awo sanazindikire Yesu, komabe pomuweruza Yesu anakwaniritsa mawu a Aneneri amene amawerengedwa Sabata lililonse. 28 Ngakhale sanapeze chifukwa choti afe, anapempha Pilato kuti amuphe. 29 Atachita zonse zimene zinalembedwa za Iye, iwo anamuchotsa pa mtengo ndipo anamuyika mʼmanda. 30 Koma Mulungu anamuukitsa, 31 ndipo kwa masiku ambiri anaonekera kwa amene anayenda naye kuchokera ku Galileya mpaka ku Yerusalemu. Iwowa tsopano ndi mboni zake kwa anthu a Israeli. 32 “Ife tikukuwuzani Uthenga Wabwino; umene Mulungu analonjeza makolo athu. 33 Iye wakwaniritsa zimenezi kwa ife ana awo, poukitsa Yesu kuchokera kwa akufa. Monga zinalembedwa mu Salimo lachiwiri kuti,“Iwe ndiwe mwana wanga;lero ine ndakhala Atate ako.” 34 Zakuti Mulungu anamuukitsa kuti asawole konse, zinanenedwa mʼmawu awa:“ ‘Ine, ndidzakupatsa madalitso opatulika ndi odalirika amene ndinalonjeza Davide.’ 35 Nʼchifukwa chakenso zinalembedwa mu Salimo lina kuti,“ ‘Simudzalekerera woyera wanu kuti awole.’ 36 “Pakuti pamene Davide anatsiriza kutumikira Mulungu mu mʼbado wake, anamwalira, iye anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake ndipo thupi lake linawola. 37 Koma amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa sanawole ayi. 38 “Nʼchifukwa chake, abale anga, dziwani kuti mwa Yesu chikhululukiro cha machimo chikulalikidwa. 39 Kudzera mwa Iye aliyense amene akhulupirira, alungamitsidwa kuchoka ku tchimo lililonse limene silingachoke ndi Malamulo a Mose. 40 Samalani kuti zimene aneneri akunena zisakuchitikireni inu: 41 “ ‘Onani, inu anthu onyoza,dabwani ndipo wonongekani,chifukwa ine ndidzachita china chake mʼmasiku anu,inu simudzazikhulupirirangakhale wina atakufotokozerani!’ ” 42 Pamene Paulo ndi Barnaba amatuluka mʼSunagoge, anthu anawapempha kuti adzapitirize kuyankhula zinthu zimenezi Sabata linalo. 43 Atatha mapemphero, Ayuda ambiri ndi anthu odzipereka otembenukira ku Chiyuda anatsatira Paulo ndi Barnaba, iwo anayankhula ndi anthuwo ndipo anawapempha kuti apitirire mʼchisomo cha Mulungu. 44 Pa Sabata linalo pafupifupi anthu onse a mu mzindawo anasonkhana kudzamva Mawu a Ambuye. 45 Pamene Ayuda anaona gulu la anthu, anachita nsanje ndipo anayankhula zamwano kutsutsana ndi zimene Paulo amanena. 46 Ndipo Paulo ndi Barnaba anawayankha molimba mtima kuti, “Ife tinayenera kuyankhula Mawu a Mulungu kwa inu poyamba. Popeza inu mwawakana ndi kudziyesa nokha osayenera moyo wosatha, ife tsopano tikupita kwa anthu a mitundu ina. 47 Pakuti izi ndi zimene Ambuye anatilamula ife:“ ‘Ine ndakuyika iwe ukhale kuwunika kwa anthu a mitundu ina,kuti ukafikitse chipulumutso ku malekezero a dziko lapansi!’ ” 48 Anthu a mitundu ina atamva izi, anakondwa ndipo analemekeza Mawu Ambuye; ndipo onse amene anawasankha kuti alandire moyo osatha anakhulupirira. 49 Mawu a Ambuye anafalikira mʼchigawo chonse. 50 Koma Ayuda anawutsa mitima ya akazi otchuka opembedza Mulungu ndi akulu a mu mzindamo. Iwo anabweretsa mazunzo kwa Paulo ndi Barnaba ndipo anawathamangitsa mʼchigawo chawo. 51 Tsono iwo anasasa fumbi la ku mapazi awo powatsutsa, ndipo anapita ku Ikoniya. 52 Ndipo ophunzira anadzazidwa ndi chimwemwe ndiponso ndi Mzimu Woyera.

In Other Versions

Acts 13 in the ANGEFD

Acts 13 in the ANTPNG2D

Acts 13 in the AS21

Acts 13 in the BAGH

Acts 13 in the BBPNG

Acts 13 in the BBT1E

Acts 13 in the BDS

Acts 13 in the BEV

Acts 13 in the BHAD

Acts 13 in the BIB

Acts 13 in the BLPT

Acts 13 in the BNT

Acts 13 in the BNTABOOT

Acts 13 in the BNTLV

Acts 13 in the BOATCB

Acts 13 in the BOATCB2

Acts 13 in the BOBCV

Acts 13 in the BOCNT

Acts 13 in the BOECS

Acts 13 in the BOHCB

Acts 13 in the BOHCV

Acts 13 in the BOHLNT

Acts 13 in the BOHNTLTAL

Acts 13 in the BOICB

Acts 13 in the BOILNTAP

Acts 13 in the BOITCV

Acts 13 in the BOKCV

Acts 13 in the BOKCV2

Acts 13 in the BOKHWOG

Acts 13 in the BOKSSV

Acts 13 in the BOLCB

Acts 13 in the BOLCB2

Acts 13 in the BOMCV

Acts 13 in the BONAV

Acts 13 in the BONCB

Acts 13 in the BONLT

Acts 13 in the BONUT2

Acts 13 in the BOPLNT

Acts 13 in the BOSCB

Acts 13 in the BOSNC

Acts 13 in the BOTLNT

Acts 13 in the BOVCB

Acts 13 in the BOYCB

Acts 13 in the BPBB

Acts 13 in the BPH

Acts 13 in the BSB

Acts 13 in the CCB

Acts 13 in the CUV

Acts 13 in the CUVS

Acts 13 in the DBT

Acts 13 in the DGDNT

Acts 13 in the DHNT

Acts 13 in the DNT

Acts 13 in the ELBE

Acts 13 in the EMTV

Acts 13 in the ESV

Acts 13 in the FBV

Acts 13 in the FEB

Acts 13 in the GGMNT

Acts 13 in the GNT

Acts 13 in the HARY

Acts 13 in the HNT

Acts 13 in the IRVA

Acts 13 in the IRVB

Acts 13 in the IRVG

Acts 13 in the IRVH

Acts 13 in the IRVK

Acts 13 in the IRVM

Acts 13 in the IRVM2

Acts 13 in the IRVO

Acts 13 in the IRVP

Acts 13 in the IRVT

Acts 13 in the IRVT2

Acts 13 in the IRVU

Acts 13 in the ISVN

Acts 13 in the JSNT

Acts 13 in the KAPI

Acts 13 in the KBT1ETNIK

Acts 13 in the KBV

Acts 13 in the KJV

Acts 13 in the KNFD

Acts 13 in the LBA

Acts 13 in the LBLA

Acts 13 in the LNT

Acts 13 in the LSV

Acts 13 in the MAAL

Acts 13 in the MBV

Acts 13 in the MBV2

Acts 13 in the MHNT

Acts 13 in the MKNFD

Acts 13 in the MNG

Acts 13 in the MNT

Acts 13 in the MNT2

Acts 13 in the MRS1T

Acts 13 in the NAA

Acts 13 in the NASB

Acts 13 in the NBLA

Acts 13 in the NBS

Acts 13 in the NBVTP

Acts 13 in the NET2

Acts 13 in the NIV11

Acts 13 in the NNT

Acts 13 in the NNT2

Acts 13 in the NNT3

Acts 13 in the PDDPT

Acts 13 in the PFNT

Acts 13 in the RMNT

Acts 13 in the SBIAS

Acts 13 in the SBIBS

Acts 13 in the SBIBS2

Acts 13 in the SBICS

Acts 13 in the SBIDS

Acts 13 in the SBIGS

Acts 13 in the SBIHS

Acts 13 in the SBIIS

Acts 13 in the SBIIS2

Acts 13 in the SBIIS3

Acts 13 in the SBIKS

Acts 13 in the SBIKS2

Acts 13 in the SBIMS

Acts 13 in the SBIOS

Acts 13 in the SBIPS

Acts 13 in the SBISS

Acts 13 in the SBITS

Acts 13 in the SBITS2

Acts 13 in the SBITS3

Acts 13 in the SBITS4

Acts 13 in the SBIUS

Acts 13 in the SBIVS

Acts 13 in the SBT

Acts 13 in the SBT1E

Acts 13 in the SCHL

Acts 13 in the SNT

Acts 13 in the SUSU

Acts 13 in the SUSU2

Acts 13 in the SYNO

Acts 13 in the TBIAOTANT

Acts 13 in the TBT1E

Acts 13 in the TBT1E2

Acts 13 in the TFTIP

Acts 13 in the TFTU

Acts 13 in the TGNTATF3T

Acts 13 in the THAI

Acts 13 in the TNFD

Acts 13 in the TNT

Acts 13 in the TNTIK

Acts 13 in the TNTIL

Acts 13 in the TNTIN

Acts 13 in the TNTIP

Acts 13 in the TNTIZ

Acts 13 in the TOMA

Acts 13 in the TTENT

Acts 13 in the UBG

Acts 13 in the UGV

Acts 13 in the UGV2

Acts 13 in the UGV3

Acts 13 in the VBL

Acts 13 in the VDCC

Acts 13 in the YALU

Acts 13 in the YAPE

Acts 13 in the YBVTP

Acts 13 in the ZBP