Galatians 3 (BOGWICC)

1 Agalatiya opusa inu, anakulodzani ndani? Tinamuonetsa poyera pamaso panu Yesu Khristu monga wopachikidwa pa mtanda. 2 Ine ndikufuna ndiphunzire kuchokera kwa inu chinthu chimodzi ichi: Kodi munalandira Mzimu pochita ntchito za lamulo, kapena pokhulupirira zimene munamva? 3 Kani ndinu opusa chotere? Inu mutayamba ndi Mzimu, kodi mukufuna kutsiriza ndi ntchito zathupi? 4 Kodi munavutika kwambiri pachabe, ngati kunali kwachabedi? 5 Kodi Mulungu amene anakupatsani Mzimu wake ndi kuchita zodabwitsa pakati panu, amachita zimenezi chifukwa mumachita ntchito za lamulo kapena chifukwa mumakhulupirira zimene munamva? 6 Nʼchimodzimodzinso Abrahamu, “Iye anakhulupirira Mulungu, ndipo Mulungu anamutenga kukhala wolungama.” 7 Tsono zindikirani kuti amene akhulupirira, ndi ana a Abrahamu. 8 Malemba anaonetseratu kuti Mulungu adzalungamitsa anthu a mitundu ina mwachikhulupiriro, ndipo ananeneratu Uthenga Wabwino kwa Abrahamu kuti, “Mitundu yonse ya anthu idzadalitsika kudzera mwa iwe.” 9 Choncho iwo amene ali ndi chikhulupiriro ndi odalitsidwa pamodzi ndi Abrahamu, munthu wachikhulupiriro. 10 Onse amene amadalira ntchito za lamulo ndi otembereredwa, pakuti zalembedwa mʼBuku la Malamulo kuti, “Ndi wotembereredwa aliyense amene sachita zonse zimene zalembedwa mʼBuku la Malamulo.” 11 Chodziwikiratu nʼchakuti palibe amene amalungamitsidwa pamaso pa Mulungu ndi lamulo, chifukwa, “Wolungama adzakhala ndi moyo mwachikhulupiriro.” 12 Koma chikhulupiriro si Malamulo, chifukwa Malemba akuti, “Munthu amene achita zinthu izi adzakhala ndi moyo pozichita.” 13 Khristu anatiwombola ku temberero la lamulo pokhala temberero mʼmalo mwathu, pakuti analemba kuti, “Aliyense wopachikidwa pamtengo ndi wotembereredwa.” 14 Iye anatiwombola ife ndi cholinga chakuti madalitso woperekedwa kwa Abrahamu abwere kwa anthu a mitundu ina kudzera mwa Khristu Yesu, kuti ndi chikhulupiriro tilandire lonjezo la Mzimu. 15 Abale, ndiloleni ndipereke chitsanzo cha zochitika mʼmoyo wa tsiku ndi tsiku. Pangano likakhazikitsidwa palibe amene angachotsepo kapena kuwonjezerapo, choncho ndi chimodzimodzi pa nkhani iyi. 16 Malonjezo awa anaperekedwa kwa Abrahamu ndi kwa mbewu yake. Malemba sakunena kuti, “kwa mbewu zake,” kutanthauza anthu ambiri, koma, “kwa mbewu yako,” kutanthauza munthu mmodzi, amene ndi Khristu. 17 Chimene ndikutanthauza ine ndi ichi: Malamulo amene anabwera patatha zaka 430, sangathetse pangano limene linakhazikitsidwa kale ndi Mulungu ndi kuliwononga lonjezolo. 18 Ngati madalitso athu akudalira ntchito za lamulo ndiye kuti madalitsowo sakupatsidwa chifukwa cha lonjezo. Koma Mulungu mwachisomo chake anadalitsa Abrahamu kudzera mu lonjezo. 19 Nanga tsono cholinga cha lamulo chinali chiyani? Linaperekedwa chifukwa cha zolakwa mpaka itafika mbewu imene lonjezo limanena. Malamulowo anaperekedwa ndi angelo kudzera mwa mʼkhalapakati. 20 Ngakhale zili chomwecho, mʼkhalapakati sayimira mbali imodzi yokha, koma Mulungu ndi mmodzi. 21 Kodi ndiye kuti lamulo limatsutsana ndi malonjezo a Mulungu? Ayi. Nʼkosatheka! Pakuti ngati tikanapatsidwa malamulo opatsa moyo ndiye kuti mwa lamulo tikanakhala olungama. 22 Koma Malemba akunenetsa kuti dziko lonse lili mu ulamuliro wauchimo, kuti mwachikhulupiriro mwa Yesu Khristu, chimene chinalonjezedwa chiperekedwe kwa amene akhulupirira. 23 Chikhulupiriro ichi chisanabwere, ife tinali mʼndende ya lamulo, otsekeredwa mpaka pamene chikhulupiriro chikanavumbulutsidwa. 24 Choncho lamulo linayikidwa kukhala lotiyangʼanira kuti lititsogolere kwa Khristu kuti tilungamitsidwe mwachikhulupiriro. 25 Tsopano pakuti chikhulupiriro chabwera, ife sitilinso mu ulamuliro wa lamulo. 26 Nonse ndinu ana a Mulungu kudzera mʼchikhulupiriro mwa Khristu Yesu, 27 pakuti nonse amene munalumikizana ndi Khristu mu ubatizo munavala Khristu. 28 Palibe Myuda kapena Mgriki, kapolo kapena mfulu, mwamuna kapena mkazi, pakuti nonse ndinu amodzi mwa Khristu Yesu. 29 Ngati inu muli ake a Khristu, ndiye kuti ndinu mbewu ya Abrahamu, ndi olowamʼmalo molingana ndi lonjezo.

In Other Versions

Galatians 3 in the ANGEFD

Galatians 3 in the ANTPNG2D

Galatians 3 in the AS21

Galatians 3 in the BAGH

Galatians 3 in the BBPNG

Galatians 3 in the BBT1E

Galatians 3 in the BDS

Galatians 3 in the BEV

Galatians 3 in the BHAD

Galatians 3 in the BIB

Galatians 3 in the BLPT

Galatians 3 in the BNT

Galatians 3 in the BNTABOOT

Galatians 3 in the BNTLV

Galatians 3 in the BOATCB

Galatians 3 in the BOATCB2

Galatians 3 in the BOBCV

Galatians 3 in the BOCNT

Galatians 3 in the BOECS

Galatians 3 in the BOHCB

Galatians 3 in the BOHCV

Galatians 3 in the BOHLNT

Galatians 3 in the BOHNTLTAL

Galatians 3 in the BOICB

Galatians 3 in the BOILNTAP

Galatians 3 in the BOITCV

Galatians 3 in the BOKCV

Galatians 3 in the BOKCV2

Galatians 3 in the BOKHWOG

Galatians 3 in the BOKSSV

Galatians 3 in the BOLCB

Galatians 3 in the BOLCB2

Galatians 3 in the BOMCV

Galatians 3 in the BONAV

Galatians 3 in the BONCB

Galatians 3 in the BONLT

Galatians 3 in the BONUT2

Galatians 3 in the BOPLNT

Galatians 3 in the BOSCB

Galatians 3 in the BOSNC

Galatians 3 in the BOTLNT

Galatians 3 in the BOVCB

Galatians 3 in the BOYCB

Galatians 3 in the BPBB

Galatians 3 in the BPH

Galatians 3 in the BSB

Galatians 3 in the CCB

Galatians 3 in the CUV

Galatians 3 in the CUVS

Galatians 3 in the DBT

Galatians 3 in the DGDNT

Galatians 3 in the DHNT

Galatians 3 in the DNT

Galatians 3 in the ELBE

Galatians 3 in the EMTV

Galatians 3 in the ESV

Galatians 3 in the FBV

Galatians 3 in the FEB

Galatians 3 in the GGMNT

Galatians 3 in the GNT

Galatians 3 in the HARY

Galatians 3 in the HNT

Galatians 3 in the IRVA

Galatians 3 in the IRVB

Galatians 3 in the IRVG

Galatians 3 in the IRVH

Galatians 3 in the IRVK

Galatians 3 in the IRVM

Galatians 3 in the IRVM2

Galatians 3 in the IRVO

Galatians 3 in the IRVP

Galatians 3 in the IRVT

Galatians 3 in the IRVT2

Galatians 3 in the IRVU

Galatians 3 in the ISVN

Galatians 3 in the JSNT

Galatians 3 in the KAPI

Galatians 3 in the KBT1ETNIK

Galatians 3 in the KBV

Galatians 3 in the KJV

Galatians 3 in the KNFD

Galatians 3 in the LBA

Galatians 3 in the LBLA

Galatians 3 in the LNT

Galatians 3 in the LSV

Galatians 3 in the MAAL

Galatians 3 in the MBV

Galatians 3 in the MBV2

Galatians 3 in the MHNT

Galatians 3 in the MKNFD

Galatians 3 in the MNG

Galatians 3 in the MNT

Galatians 3 in the MNT2

Galatians 3 in the MRS1T

Galatians 3 in the NAA

Galatians 3 in the NASB

Galatians 3 in the NBLA

Galatians 3 in the NBS

Galatians 3 in the NBVTP

Galatians 3 in the NET2

Galatians 3 in the NIV11

Galatians 3 in the NNT

Galatians 3 in the NNT2

Galatians 3 in the NNT3

Galatians 3 in the PDDPT

Galatians 3 in the PFNT

Galatians 3 in the RMNT

Galatians 3 in the SBIAS

Galatians 3 in the SBIBS

Galatians 3 in the SBIBS2

Galatians 3 in the SBICS

Galatians 3 in the SBIDS

Galatians 3 in the SBIGS

Galatians 3 in the SBIHS

Galatians 3 in the SBIIS

Galatians 3 in the SBIIS2

Galatians 3 in the SBIIS3

Galatians 3 in the SBIKS

Galatians 3 in the SBIKS2

Galatians 3 in the SBIMS

Galatians 3 in the SBIOS

Galatians 3 in the SBIPS

Galatians 3 in the SBISS

Galatians 3 in the SBITS

Galatians 3 in the SBITS2

Galatians 3 in the SBITS3

Galatians 3 in the SBITS4

Galatians 3 in the SBIUS

Galatians 3 in the SBIVS

Galatians 3 in the SBT

Galatians 3 in the SBT1E

Galatians 3 in the SCHL

Galatians 3 in the SNT

Galatians 3 in the SUSU

Galatians 3 in the SUSU2

Galatians 3 in the SYNO

Galatians 3 in the TBIAOTANT

Galatians 3 in the TBT1E

Galatians 3 in the TBT1E2

Galatians 3 in the TFTIP

Galatians 3 in the TFTU

Galatians 3 in the TGNTATF3T

Galatians 3 in the THAI

Galatians 3 in the TNFD

Galatians 3 in the TNT

Galatians 3 in the TNTIK

Galatians 3 in the TNTIL

Galatians 3 in the TNTIN

Galatians 3 in the TNTIP

Galatians 3 in the TNTIZ

Galatians 3 in the TOMA

Galatians 3 in the TTENT

Galatians 3 in the UBG

Galatians 3 in the UGV

Galatians 3 in the UGV2

Galatians 3 in the UGV3

Galatians 3 in the VBL

Galatians 3 in the VDCC

Galatians 3 in the YALU

Galatians 3 in the YAPE

Galatians 3 in the YBVTP

Galatians 3 in the ZBP