Hebrews 6 (BOGWICC)
1 Tsono tiyeni tisangoyima pa maphunziro oyambirira enieni a Khristu koma tipitirire kuti mukule msinkhu. Tisaphunzitsenso zinthu zomwe zili ngati maziko, monga za kutembenuka mtima kusiya ntchito zosapindulitsa pa moyo wosatha, za kukhulupirira Mulungu, 2 za maubatizo, za kusanjika manja, za kuuka kwa akufa ndi za chiweruzo chotsiriza. 3 Ndipo Mulungu akalola, tidzaterodi. 4 Nʼkosatheka kuwabwezanso anthu amene nthawi ina anawunikiridwa. Iwowa analawapo mphatso yochokera kumwamba, nʼkulandira nawo Mzimu Woyera. 5 Analawa kukoma kwa mawu a Mulungu ndi mphamvu za nthawi ikubwera. 6 Popeza anabwerera mʼmbuyo, nʼkosatheka kuti atembenukenso mtima chifukwa akupachikanso Mwana wa Mulungu ndi kumunyozetsa poyera. 7 Nthaka yolandira mvula kawirikawiri nʼkubala mbewu zopindulitsa oyilima, Mulungu amayidalitsa. 8 Koma nthaka yobereka minga ndi nthula ndi yopanda phindu ndipo ili pafupi kutembereredwa. Matsiriziro ake idzatenthedwa mʼmoto. 9 Okondedwa anga, ngakhale tikuyankhula zimenezi, ife tikudziwa kuti muli nazo zinthu zabwino zomwe zimabwera pamodzi ndi chipulumutso. 10 Mulungu ndi wolungama, sangayiwale ntchito zanu ndi chikondi chanu chimene munamuonetsa pothandiza anthu ake monga mmene mukuchitirabe tsopano. 11 Ife tikufuna kuti aliyense wa inu aonetse changu chomwechi mpaka kumapeto, kuti zichitikedi zomwe mukuyembekezera. 12 Ife sitikufuna kuti inu mukhale aulesi, koma mutsatire anthu amene, pokhulupirira ndi kupirira, akulandira zimene zinalonjezedwa. 13 Pamene Mulungu ankamulonjeza Abrahamu, popeza panalibe wamkulu womuposa, amene akanamutchula ndikulumbira mwa Iye, analumbira mwa Iye yekha kuti, 14 “Ine ndidzakudalitsa ndithu, ndipo ndidzakupatsa zidzukulu zambiri.” 15 Ndipo Abrahamu atayembekezera mofatsa, analandira zimene anamulonjezazo. 16 Anthu amalumbira mʼdzina la wina amene akuwaposa, ndipo lumbiro lotere limatsimikizira zomwe zayankhulidwa ndi kuthetsa mikangano yonse. 17 Momwemonso Mulungu pofuna kutsimikizira anthu amene adzalandire lonjezo, kuti Iye sangasinthe maganizo, anatsimikiza lonjezo lakelo ndi lumbiro. 18 Mulungu anachita zinthu ziwiri, lonjezo ndi lumbiro, zimene sizingathe kusintha ndipo Mulungu sangathe kunama. Choncho Mulungu akutilimbikitsa mtima ife amene tinathawira kwa Iye kuti tichigwiritsitse chiyembekezo chimene tinalandira. 19 Chiyembekezo chimenechi tili nacho ngati nangula wa moyo wathu. Nʼchokhazikika ndi chosagwedezeka ndipo chimalowa mʼkatikati mwa malo opatulika, kuseri kwa chinsalu chotchinga. 20 Yesu anatitsogolera kupita kumeneko, nalowako mʼmalo mwathu. Iye anasanduka Mkulu wa ansembe onse wamuyaya, monga mwa dongosolo la unsembe wa Melikizedeki.
In Other Versions
Hebrews 6 in the ANGEFD
Hebrews 6 in the ANTPNG2D
Hebrews 6 in the AS21
Hebrews 6 in the BAGH
Hebrews 6 in the BBPNG
Hebrews 6 in the BBT1E
Hebrews 6 in the BDS
Hebrews 6 in the BEV
Hebrews 6 in the BHAD
Hebrews 6 in the BIB
Hebrews 6 in the BLPT
Hebrews 6 in the BNT
Hebrews 6 in the BNTABOOT
Hebrews 6 in the BNTLV
Hebrews 6 in the BOATCB
Hebrews 6 in the BOATCB2
Hebrews 6 in the BOBCV
Hebrews 6 in the BOCNT
Hebrews 6 in the BOECS
Hebrews 6 in the BOHCB
Hebrews 6 in the BOHCV
Hebrews 6 in the BOHLNT
Hebrews 6 in the BOHNTLTAL
Hebrews 6 in the BOICB
Hebrews 6 in the BOILNTAP
Hebrews 6 in the BOITCV
Hebrews 6 in the BOKCV
Hebrews 6 in the BOKCV2
Hebrews 6 in the BOKHWOG
Hebrews 6 in the BOKSSV
Hebrews 6 in the BOLCB
Hebrews 6 in the BOLCB2
Hebrews 6 in the BOMCV
Hebrews 6 in the BONAV
Hebrews 6 in the BONCB
Hebrews 6 in the BONLT
Hebrews 6 in the BONUT2
Hebrews 6 in the BOPLNT
Hebrews 6 in the BOSCB
Hebrews 6 in the BOSNC
Hebrews 6 in the BOTLNT
Hebrews 6 in the BOVCB
Hebrews 6 in the BOYCB
Hebrews 6 in the BPBB
Hebrews 6 in the BPH
Hebrews 6 in the BSB
Hebrews 6 in the CCB
Hebrews 6 in the CUV
Hebrews 6 in the CUVS
Hebrews 6 in the DBT
Hebrews 6 in the DGDNT
Hebrews 6 in the DHNT
Hebrews 6 in the DNT
Hebrews 6 in the ELBE
Hebrews 6 in the EMTV
Hebrews 6 in the ESV
Hebrews 6 in the FBV
Hebrews 6 in the FEB
Hebrews 6 in the GGMNT
Hebrews 6 in the GNT
Hebrews 6 in the HARY
Hebrews 6 in the HNT
Hebrews 6 in the IRVA
Hebrews 6 in the IRVB
Hebrews 6 in the IRVG
Hebrews 6 in the IRVH
Hebrews 6 in the IRVK
Hebrews 6 in the IRVM
Hebrews 6 in the IRVM2
Hebrews 6 in the IRVO
Hebrews 6 in the IRVP
Hebrews 6 in the IRVT
Hebrews 6 in the IRVT2
Hebrews 6 in the IRVU
Hebrews 6 in the ISVN
Hebrews 6 in the JSNT
Hebrews 6 in the KAPI
Hebrews 6 in the KBT1ETNIK
Hebrews 6 in the KBV
Hebrews 6 in the KJV
Hebrews 6 in the KNFD
Hebrews 6 in the LBA
Hebrews 6 in the LBLA
Hebrews 6 in the LNT
Hebrews 6 in the LSV
Hebrews 6 in the MAAL
Hebrews 6 in the MBV
Hebrews 6 in the MBV2
Hebrews 6 in the MHNT
Hebrews 6 in the MKNFD
Hebrews 6 in the MNG
Hebrews 6 in the MNT
Hebrews 6 in the MNT2
Hebrews 6 in the MRS1T
Hebrews 6 in the NAA
Hebrews 6 in the NASB
Hebrews 6 in the NBLA
Hebrews 6 in the NBS
Hebrews 6 in the NBVTP
Hebrews 6 in the NET2
Hebrews 6 in the NIV11
Hebrews 6 in the NNT
Hebrews 6 in the NNT2
Hebrews 6 in the NNT3
Hebrews 6 in the PDDPT
Hebrews 6 in the PFNT
Hebrews 6 in the RMNT
Hebrews 6 in the SBIAS
Hebrews 6 in the SBIBS
Hebrews 6 in the SBIBS2
Hebrews 6 in the SBICS
Hebrews 6 in the SBIDS
Hebrews 6 in the SBIGS
Hebrews 6 in the SBIHS
Hebrews 6 in the SBIIS
Hebrews 6 in the SBIIS2
Hebrews 6 in the SBIIS3
Hebrews 6 in the SBIKS
Hebrews 6 in the SBIKS2
Hebrews 6 in the SBIMS
Hebrews 6 in the SBIOS
Hebrews 6 in the SBIPS
Hebrews 6 in the SBISS
Hebrews 6 in the SBITS
Hebrews 6 in the SBITS2
Hebrews 6 in the SBITS3
Hebrews 6 in the SBITS4
Hebrews 6 in the SBIUS
Hebrews 6 in the SBIVS
Hebrews 6 in the SBT
Hebrews 6 in the SBT1E
Hebrews 6 in the SCHL
Hebrews 6 in the SNT
Hebrews 6 in the SUSU
Hebrews 6 in the SUSU2
Hebrews 6 in the SYNO
Hebrews 6 in the TBIAOTANT
Hebrews 6 in the TBT1E
Hebrews 6 in the TBT1E2
Hebrews 6 in the TFTIP
Hebrews 6 in the TFTU
Hebrews 6 in the TGNTATF3T
Hebrews 6 in the THAI
Hebrews 6 in the TNFD
Hebrews 6 in the TNT
Hebrews 6 in the TNTIK
Hebrews 6 in the TNTIL
Hebrews 6 in the TNTIN
Hebrews 6 in the TNTIP
Hebrews 6 in the TNTIZ
Hebrews 6 in the TOMA
Hebrews 6 in the TTENT
Hebrews 6 in the UBG
Hebrews 6 in the UGV
Hebrews 6 in the UGV2
Hebrews 6 in the UGV3
Hebrews 6 in the VBL
Hebrews 6 in the VDCC
Hebrews 6 in the YALU
Hebrews 6 in the YAPE
Hebrews 6 in the YBVTP
Hebrews 6 in the ZBP