Isaiah 30 (BOGWICC)

1 Yehova akuti, “Tsoka kwa ana ondipandukiraamene amachita zowakomera iwo okha osati Ine,nachita mgwirizano wawowawokoma osati motsogozedwa ndi Ine.Choncho amanka nachimwirachimwira. 2 Amapita ku Igupto kukapempha thandizokoma osandifunsa;amathawira kwa Farao kuti awateteze,ku Igupto amafuna malo opulumulira. 3 Koma chitetezo cha Farao chidzakhala manyazi anu,malo a mthunzi a ku Igupto mudzachita nawo manyazi. 4 Ngakhale kuti nduna zawo zili ku Zowani,ndipo akazembe awo afika kale ku Hanesi, 5 aliyense wa ku Yuda adzachita manyazichifukwa cha anthu opanda nawo phindu,amene sabweretsa thandizo kapena phindu,koma manyazi ndi mnyozo.” 6 Uthenga wonena za nyama za ku Negevi:Akazembe akuyenda mʼdziko lovuta ndi losautsa,mʼmene muli mikango yayimuna ndi yayikazi,mphiri ndi njoka zaululu.Iwo amasenzetsa abulu ndi ngamira chuma chawo,kupita nazo kwa mtundu wa anthuumene sungawathandize. 7 Amapita ku Igupto amene thandizo lake ndi lachabechabe.Nʼchifukwa chake dzikolo ndalitchaRahabe chirombo cholobodoka. 8 Yehova anandiwuza kuti, “Tsopano pita,ukalembe zimenezi mʼbuku iwo akuonandipo lidzakhala ngati umboni wosathamasiku a mʼtsogolo. 9 Amenewa ndi anthu owukira, onama ndiosafuna kumvera malangizo a Yehova. 10 Iwo amawuza alosi kuti,‘Musationerenso masomphenya!’Ndipo amanena kwa mneneri kuti,‘Musatinenerenso zoona,’mutiwuze zotikomera,munenere za mʼmutu mwanu. 11 Patukani pa njira ya Yehova,lekani kutsata njira ya Yehova;ndipo tisamvenso mawua Woyerayo uja wa Israeli!” 12 Nʼchifukwa chake Woyerayo wa Israeli akunena kuti,“Popeza inu mwakana uthenga uwu,mumakhulupirira zopondereza anzanundipo mumadalira kuchita zoyipa, 13 choncho tchimo linalo lidzakhala ngati mingʼalupa khoma lalitali ndi lopendamalimene linagwa mwadzidzidzi ndi mwamsangamsanga. 14 Lidzaphwanyika ngati mbiyaimene yanyenyekeratu,mwakuti pakati pake sipadzapezeka phale ngakhalelopalira moto mʼngʼanjokapena lotungira madzi mʼchitsime.” 15 Zimene Ambuye Yehova, Woyerayo wa Israeli ananena ndi izi:“Ngati mubwerera ndi kupuma mudzapulumuka,ngati mukhala chete ndi kukhulupirira mudzakhala amphamvu,koma inu munakana zimenezi. 16 Inu mukuti, ‘Ayi ife tidzathawa,tidzakwera pa akavalo aliwiro.’Zoonadi kuti mudzakwera pa akavalo aliwiro,koma okuthamangitsani adzakhalanso aliwiro. 17 Anthu 1,000 mwa inu adzathawapoona mdani mmodzi;poona adani asanu okhanonsenu mudzathawa.Otsala anuadzakhala ngati mbendera pa phiri,ndi ngati chizindikiro cha pa chulu.” 18 Komatu Yehova akufunitsitsa kuti akukomereni mtima,iye ali wokonzeka kuti akuchitireni chifundo.Pakuti Yehova ndi Mulungu wachilungamo.Ndi odala onse amene amakhulupirira Iye! 19 Inu anthu a ku Ziyoni, amene mukhala mu Yerusalemu simudzaliranso. Mulungu adzakukomerani mtima pamene adzamva kulira kwanu kopempha thandizo! Ndipo akadzamva, adzakuyankhani. 20 Ngakhale Ambuye adzakulowetseni mʼmasautso, aphunzitsi anu sadzakhala kakasi; inu mudzawaona ndi maso anuwo. 21 Ngati mudzapatukira kumanja kapena kumanzere, mudzamva mawu kumbuyo kwanu woti, “Njira ndi iyi; yendani mʼmenemo.” 22 Pamenepo mudzawononga mafano anu okutidwa ndi siliva ndiponso zifanizo zanu zokutidwa ndi golide; mudzawataya ngati zinthu zonyansa ndipo mudzati, “Zichoke zonsezi!” 23 Yehova adzakugwetseraninso mvula pa mbewu zanu zimene mukadzale mʼnthaka, ndipo chakudya chimene mudzakolole chidzakhala chabwino ndi chochuluka. Tsiku limenelo ngʼombe zanu zidzadya msipu wochuluka. 24 Ngʼombe ndi abulu amene amalima mʼmunda adzadya chakudya chamchere, chopetedwa ndi foloko ndi fosholo. 25 Pa tsiku limene adani anu adzaphedwa ndi nsanja zawo kugwa, mitsinje ya madzi idzayenda pa phiri lililonse lalikulu ndi pa phiri lililonse lalingʼono. 26 Mwezi udzawala ngati dzuwa, ndipo kuwala kwa dzuwa kudzawonjezereka kasanu nʼkawiri, ngati kuwala kwa tsiku limodzi. Yehova adzamanga mabala a anthu ake ndi kupoletsa zilonda zimene Iye anachititsa polanga anthu ake. 27 Taonani, Yehova akubwera kuchokera kutali,ndipo mkwiyo wake ndiwonyeka ndi chiweruzo chake chidzakhala chopweteka.Iye wayankhula mwaukali kwambiri,ndipo mawu ake ali ngati moto wonyeka. 28 Mpweya wake uli ngati mtsinje wosefukira,wa madzi ofika mʼkhosi.Iye adzasefa anthu a mitundu ina ndi sefa wosakaza;Iye akuyika zitsulo mʼkamwa mwa anthu a mitundu ina ngati akavalo,kuti ziwasocheretse. 29 Ndipo inu mudzayimbamokondwa monga mumachitira usiku pa chikondwerero chopatulika.Mudzasangalalangati anthu oyimba zitoliropopita ku phiri la Yehova,thanthwe la Israeli. 30 Anthu adzamva liwu la ulemerero la Yehovandipo adzaona dzanja lake likutsika pa iwondi mkwiyo woopsa, pamodzi ndi moto wonyeketsa,mphenzi, namondwe ndi matalala. 31 Asiriya adzaopa liwu la Yehova,ndipo Iye adzawakantha ndi ndodo. 32 Yehova akamadzalanga adani ake ndi ndodo,anthu ake adzakhala akuvina nyimbozoyimbira matambolini ndi azeze,Yehova ndiye ati adzamenyane ndi Asiriyawo. 33 Malo otenthera zinthu akonzedwa kale;anakonzera mfumu ya ku Asiriya.Dzenje la motolo ndi lozama ndi lalikulu,ndipo muli nkhuni zambiri;mpweya wa Yehova,wangati mtsinje wa sulufule,udzayatsa motowo pa nkhunizo.

In Other Versions

Isaiah 30 in the ANGEFD

Isaiah 30 in the ANTPNG2D

Isaiah 30 in the AS21

Isaiah 30 in the BAGH

Isaiah 30 in the BBPNG

Isaiah 30 in the BBT1E

Isaiah 30 in the BDS

Isaiah 30 in the BEV

Isaiah 30 in the BHAD

Isaiah 30 in the BIB

Isaiah 30 in the BLPT

Isaiah 30 in the BNT

Isaiah 30 in the BNTABOOT

Isaiah 30 in the BNTLV

Isaiah 30 in the BOATCB

Isaiah 30 in the BOATCB2

Isaiah 30 in the BOBCV

Isaiah 30 in the BOCNT

Isaiah 30 in the BOECS

Isaiah 30 in the BOHCB

Isaiah 30 in the BOHCV

Isaiah 30 in the BOHLNT

Isaiah 30 in the BOHNTLTAL

Isaiah 30 in the BOICB

Isaiah 30 in the BOILNTAP

Isaiah 30 in the BOITCV

Isaiah 30 in the BOKCV

Isaiah 30 in the BOKCV2

Isaiah 30 in the BOKHWOG

Isaiah 30 in the BOKSSV

Isaiah 30 in the BOLCB

Isaiah 30 in the BOLCB2

Isaiah 30 in the BOMCV

Isaiah 30 in the BONAV

Isaiah 30 in the BONCB

Isaiah 30 in the BONLT

Isaiah 30 in the BONUT2

Isaiah 30 in the BOPLNT

Isaiah 30 in the BOSCB

Isaiah 30 in the BOSNC

Isaiah 30 in the BOTLNT

Isaiah 30 in the BOVCB

Isaiah 30 in the BOYCB

Isaiah 30 in the BPBB

Isaiah 30 in the BPH

Isaiah 30 in the BSB

Isaiah 30 in the CCB

Isaiah 30 in the CUV

Isaiah 30 in the CUVS

Isaiah 30 in the DBT

Isaiah 30 in the DGDNT

Isaiah 30 in the DHNT

Isaiah 30 in the DNT

Isaiah 30 in the ELBE

Isaiah 30 in the EMTV

Isaiah 30 in the ESV

Isaiah 30 in the FBV

Isaiah 30 in the FEB

Isaiah 30 in the GGMNT

Isaiah 30 in the GNT

Isaiah 30 in the HARY

Isaiah 30 in the HNT

Isaiah 30 in the IRVA

Isaiah 30 in the IRVB

Isaiah 30 in the IRVG

Isaiah 30 in the IRVH

Isaiah 30 in the IRVK

Isaiah 30 in the IRVM

Isaiah 30 in the IRVM2

Isaiah 30 in the IRVO

Isaiah 30 in the IRVP

Isaiah 30 in the IRVT

Isaiah 30 in the IRVT2

Isaiah 30 in the IRVU

Isaiah 30 in the ISVN

Isaiah 30 in the JSNT

Isaiah 30 in the KAPI

Isaiah 30 in the KBT1ETNIK

Isaiah 30 in the KBV

Isaiah 30 in the KJV

Isaiah 30 in the KNFD

Isaiah 30 in the LBA

Isaiah 30 in the LBLA

Isaiah 30 in the LNT

Isaiah 30 in the LSV

Isaiah 30 in the MAAL

Isaiah 30 in the MBV

Isaiah 30 in the MBV2

Isaiah 30 in the MHNT

Isaiah 30 in the MKNFD

Isaiah 30 in the MNG

Isaiah 30 in the MNT

Isaiah 30 in the MNT2

Isaiah 30 in the MRS1T

Isaiah 30 in the NAA

Isaiah 30 in the NASB

Isaiah 30 in the NBLA

Isaiah 30 in the NBS

Isaiah 30 in the NBVTP

Isaiah 30 in the NET2

Isaiah 30 in the NIV11

Isaiah 30 in the NNT

Isaiah 30 in the NNT2

Isaiah 30 in the NNT3

Isaiah 30 in the PDDPT

Isaiah 30 in the PFNT

Isaiah 30 in the RMNT

Isaiah 30 in the SBIAS

Isaiah 30 in the SBIBS

Isaiah 30 in the SBIBS2

Isaiah 30 in the SBICS

Isaiah 30 in the SBIDS

Isaiah 30 in the SBIGS

Isaiah 30 in the SBIHS

Isaiah 30 in the SBIIS

Isaiah 30 in the SBIIS2

Isaiah 30 in the SBIIS3

Isaiah 30 in the SBIKS

Isaiah 30 in the SBIKS2

Isaiah 30 in the SBIMS

Isaiah 30 in the SBIOS

Isaiah 30 in the SBIPS

Isaiah 30 in the SBISS

Isaiah 30 in the SBITS

Isaiah 30 in the SBITS2

Isaiah 30 in the SBITS3

Isaiah 30 in the SBITS4

Isaiah 30 in the SBIUS

Isaiah 30 in the SBIVS

Isaiah 30 in the SBT

Isaiah 30 in the SBT1E

Isaiah 30 in the SCHL

Isaiah 30 in the SNT

Isaiah 30 in the SUSU

Isaiah 30 in the SUSU2

Isaiah 30 in the SYNO

Isaiah 30 in the TBIAOTANT

Isaiah 30 in the TBT1E

Isaiah 30 in the TBT1E2

Isaiah 30 in the TFTIP

Isaiah 30 in the TFTU

Isaiah 30 in the TGNTATF3T

Isaiah 30 in the THAI

Isaiah 30 in the TNFD

Isaiah 30 in the TNT

Isaiah 30 in the TNTIK

Isaiah 30 in the TNTIL

Isaiah 30 in the TNTIN

Isaiah 30 in the TNTIP

Isaiah 30 in the TNTIZ

Isaiah 30 in the TOMA

Isaiah 30 in the TTENT

Isaiah 30 in the UBG

Isaiah 30 in the UGV

Isaiah 30 in the UGV2

Isaiah 30 in the UGV3

Isaiah 30 in the VBL

Isaiah 30 in the VDCC

Isaiah 30 in the YALU

Isaiah 30 in the YAPE

Isaiah 30 in the YBVTP

Isaiah 30 in the ZBP