Isaiah 45 (BOGWICC)
1 Yehova akuyankhula ndi wodzozedwa wakeKoresi amene anamugwira dzanja lamanjakuti agonjetse mitundu ya anthundi kuwalanda mafumu zida zawo zankhondo,ndi kutsekula zitsekokuti zipatazo zisadzatsekedwenso ndi ichi: 2 Ine ndidzayenda patsogolo pako,ndi kusalaza mapiri;ndidzaphwanya zitseko za mkuwandi kuthyola mipiringidzo ya chitsulo. 3 Ndidzakupatsa chuma chobisika mu mdima,katundu wa pamalo obisika,kotero kuti udziwe kuti Ine ndine YehovaMulungu wa Israeli, amene ndakuyitana pokutchula dzina. 4 Chifukwa cha mtumiki wanga Yakobo,chifukwa cha wosankhidwa wanga Israeli,Ine ndakuyitana pokutchula dzinandipo ndakupatsa dzina laulemungakhale iwe sukundidziwa Ine. 5 Ine ndine Yehova ndipo palibenso wina;kupatula Ine palibenso Mulungu wina.Ndidzakupatsa mphamvu,ngakhale sukundidziwa Ine, 6 kotero kuti kuchokera kummawa mpaka kumadzuloanthu adzadziwa kuti palibe wina koma Ine ndekha.Ine ndine Yehova,ndipo palibenso wina. 7 Ndimalenga kuwala ndi mdima,ndimabweretsa madalitso ndi tsoka;ndine Yehova, amene ndimachita zonsezi. 8 “Iwe thambo gwetsa mvula kuchokera kumwamba;mitambo ivumbwe mivumbi ya chilungamo.Dziko lapansi litsekuke,ndipo chipulumutso chiphuke kutichilungamo chimereponso;Ine Yehova, ndine ndalenga zimenezi. 9 “Tsoka kwa wokangana ndi mlengi wake,ngakhale kuti ali ngati phale chabe pakati pa mapale anzake.Kodi dongo lingafunse munthu wowumba kuti,‘Kodi ukuwumba chiyani?’Kodi ntchito yako inganene kuti,‘Ulibe luso?’ 10 Tsoka kwa wofunsa abambo ake kuti,‘Kodi munabereka chiyani?’Kapena amayi ake kuti,‘Kodi mufuna kubereka chiyani?’ 11 “YehovaWoyerayo wa Israeli, ndiponso Mlengi wake akunena,zokhudza zinthu zimene zikubwera ndi izi:Kodi iwe ukundifunsa za ana anga,kapena kundilamula pa zokhudza ntchito zanga? 12 Ndine amene ndinapanga dziko lapansindikulenga munthu kuti akhalemo.Ine ndi manja anga ndinayalika thambo;ndimalamulira zolengedwa zonse za mlengalenga. 13 Ndine amene ndidzawutsa Koresi kuti chilungamo changa chikwaniritsidwe:ndipo ndidzawongolera njira zake zonse.Iye adzamanganso mzinda wangandi kumasula anthu anga amene ali mu ukapolo,wopanda kupereka ndalama kapena mphotho,akutero Yehova Wamphamvuzonse.” 14 Yehova akuti,“Chuma cha ku Igupto ndi chuma cha malonda cha Kusi chidzakhala chanu.Anthu amphamvu zawo ndi athanzi a ku Sebaadzabwera kwa inundipo adzakhala anthu anu;iwo adzidzakutsatani pambuyo panuali mʼmaunyolo.Adzakugwadiranindi kukupemphani, ponena kuti,‘Ndithudi Mulungu ali ndi inu, ndipo palibenso wina;palibenso mulungu wina.’ ” 15 Zoonadi inu muli ndi Mulungu wobisikaamene ali Mulungu ndi Mpulumutsi wa Israeli. 16 Onse amene amapanga mafano adzawachititsa manyazi ndi kuwanyozetsa.Adzakhala osokonezeka maganizo. 17 Koma Yehova adzapulumutsa Israelindi chipulumutso chamuyaya;simudzachitanso manyazi kapena kunyozekampaka kalekale. 18 Yehovaanalenga zinthu zakumwamba,Iye ndiye Mulungu;amene akulenga dziko lapansi,ndi kulikhazikitsa,sanalipange kuti likhale lopanda kanthu,koma analipanga kuti anthu akhalemo.Iyeyu akunena kuti:Ine ndine Yehova,ndipo palibenso wina. 19 Ine sindinayankhule mwachinsinsi,pamalo ena a mdima;Ine sindinaziwuze zidzukulu za Yakobo kuti,“Ndifunefuneni ku malo kopanda kanthu.”Ine Yehova, ndimayankhula zoona;ndikunena zolungama. 20 Yehova akuti, “Sonkhanani pamodzi ndipo mubwere;yandikirani, inu amene munapulumuka pothawa nkhondo kwa anthu a mitundu ina.Ndinu opanda nzeru amene mumanyamula mafano a mitengo,amene mumapemphera kwa milungu imene singathe kupulumutsa. 21 Fotokozani mlandu wanu,mupatsane nzeru nonse pamodzi.Kodi ndani ananeneratu zimenezi kalekale?Ndani anazifotokozeratu zimenezi nthawi yamakedzana?Kodi si Ineyo Yehova?Ndipo palibenso Mulungu wina kupatula Ine,Mulungu wolungama ndi Wopulumutsa,palibenso wina kupatula Ine. 22 “Tembenukirani kwa Ine kuti mupulumuke,inu anthu onse a pa dziko lapansi,pakuti Ine ndine Mulungu ndipo palibenso wina. 23 Ndalumbira ndekha,pakamwa panga patulutsa mawu owona,mawu amene sadzasinthika konse akuti,bondo lililonse lidzagwada pamaso panga;anthu onse adzalumbira potchula dzina langa. 24 Iwo adzanene kwa Ine kuti,‘Chilungamo ndi mphamvu zimapezeka mwa Yehova yekha.’ ”Onse amene anamuwukira Iyeadzabwera kwa Iye ndipo adzachita manyazi. 25 Koma mwa Yehova zidzukulu zonse za Israelizidzapambana ndi kupeza ulemerero.