Isaiah 5 (BOGWICC)

1 Ndidzamuyimbira bwenzi langanyimbo yokamba za munda wake wa mpesa:Wokondedwa wanga anali ndi munda wamphesapa phiri la nthaka yachonde. 2 Anatipula nachotsa miyala yonsendipo anawokamo mipesa yabwino kwambiri.Anamanga nsanja yolondera pakati pa mundawondipo anasemanso mopsinyira mphesa mʼmundamo.Ndipo iye anayembekezera kuti mundawo udzabala mphesa zabwino,koma ayi, unabala mphesa zosadya. 3 “Tsopano, inu amene mumakhala mu Yerusalemu ndi inu anthu a ku Yuda,weruzani pakati pa ine ndi munda wanga wa mpesawu. 4 Kodi nʼchiyaninso china chimene ndikanachitira munda wanga wa mpesakupambana chomwe ndawuchitira kale?Pamene ndinkayembekezera kuti udzabala mphesa zabwino,bwanji unabala mphesa zosadya? 5 Tsopano ndikuwuzanichimene ndidzawuchitire munda wanga wa mpesa:ndidzachotsa mpanda wake,ndipo mundawo udzawonongeka;ndidzagwetsa khoma lake,ndipo nyama zidzapondapondamo. 6 Ndidzawusandutsa tsala,udzakhala wosatengulira ndi wosalimirandipo mudzamera mkandankhuku ndi minga ina.Ndidzalamula mitambokuti isagwetse mvula pa mundapo.” 7 Munda wamphesa wa Yehova Wamphamvuzonsendi Aisraeli,ndipo anthu a ku Yuda ndiwominda yake yomukondweretsa.Ndipo Iye ankayembekezera chiweruzo cholungama, mʼmalo mwake anaona kuphana;mʼmalo mwa chilungamo Iye anamva kulira kwa anthu ozunzika. 8 Tsoka kwa inu amene mumangokhalira kulumikiza nyumba,ndipo mumangokhalira kuwonjezera minda,mpaka mutalanda malo onsekuti muzikhalamo nokha mʼdzikomo. 9 Yehova Wamphamvuzonse wayankhula ine ndikumva kuti,“Ndithudi nyumba zambirizo zidzasanduka mabwinja,nyumba zazikulu zokongolazo zidzakhala zopanda anthu. 10 Munda wamphesa wa maekala khumi udzatulutsa vinyo wodzaza mbiya imodzi,kufesa madengu khumi a mbewu, zokolola zake zidzangodzaza dengu limodzi.” 11 Tsoka kwa iwo amene amadzuka mmamawanathamangira chakumwa choledzeretsa,amene amamwa mpaka usikukufikira ataledzera kotheratu. 12 Pa maphwando awo pamakhala azeze, apangwe,matambolini, zitoliro ndi vinyo,ndipo sasamala ntchito za Yehova,salemekeza ntchito za manja ake. 13 Motero anthu anga adzatengedwa ukapolochifukwa cha kusamvetsa zinthu;atsogoleri awo olemekezeka adzafa ndi njala,ndipo anthu wamba ochuluka adzafa ndi ludzu. 14 Nʼchifukwa chake ku manda sikukhutandipo kwayasama kwambiri kukamwa kwake;mʼmandamo mudzagweranso anthu otchuka a mu Yerusalemu pamodzi ndi anthu wamba ochuluka;adzagweramo ali wowowo, nʼkuledzera kwawoko. 15 Ndipo munthu aliyense adzatsitsidwa,anthu onse adzachepetsedwa,anthu odzikuza adzachita manyazi. 16 Koma Yehova Wamphamvuzonse adzalemekezedwa chifukwa cha chiweruzo chake cholungama.Ndipo Mulungu woyera adzadzionetsa kuti ndi woyera pochita chilungamo chake. 17 Tsono nkhosa zidzadya pamenepo ngati pabusa pawo;ana ankhosa adzadya mʼmabwinja a anthu olemera. 18 Tsoka kwa amene amadzikokera tchimo ndi zingwe zachinyengo,ndipo amadzikokera zoyipa ndi zingwe zokokera ngolo, 19 amene amanena kuti, “Yehova afulumire,agwire ntchito yake mwamsangakuti ntchitoyo tiyione.Ntchito zionekere,zimene Woyerayo wa Israeli akufuna kuchita,zichitike kuti tizione.” 20 Tsoka kwa amene zoyipa amaziyesa zabwinondipo zabwino amaziyesa zoyipa,amene mdima amawuyesa kuwalandipo kuwala amakuyesa mdima,amene zowawasa amaziyesa zotsekemerandipo zotsekemera amaziyesa zowawasa. 21 Tsoka kwa amene amadziona ngati anzerundipo amadziyesa ochenjera. 22 Tsoka kwa zidakwa zimene zimayika mtima pa vinyondipo ndi akatswiri posakaniza zakumwa, 23 amene amamasula olakwa chifukwa cha chiphuphukoma amayipitsa mlandu wa munthu wosalakwa. 24 Nʼchifukwa chake monga momwe moto umawonongera chiputundipo monga momwe udzu wowuma umapsera mʼmalawi a moto,momwemonso mizu yawo idzawolandipo maluwa awo adzafota ndi kuwuluka ngati fumbi;chifukwa akana malamulo a Yehova Wamphamvuzonse,ndipo anyoza mawu a Woyerayo wa Israeli. 25 Nʼchifukwa chake mkwiyo wa Yehova wayakira anthu ake;watambasula dzanja lake pa anthuwo ndipo akuwakanthaMapiri akugwedezeka,ndipo mitembo ya anthu yangoti mbwee mʼmisewu ngati zinyalala. Komabe ngakhale watero, mkwiyo wake sunaleke,dzanja lake likanali chitambasulire; 26 Yehova wakweza mbendera kuyitana mtundu wa anthu akutali,akuyitana anthuwo ndi likhweru kuti abwere kuchokera ku mathero a dziko lapansi.Awo akubwera,akubweradi mofulumira kwambiri! 27 Palibe ndi mmodzi yemwe amene akutopa kapena kupunthwa,palibe amene akusinza kapena kugona;palibe lamba wa mʼchiwuno amene akumasuka,palibe chingwe cha nsapato chimene chaduka. 28 Mivi yawo ndi yakuthwa,mauta awo onse ndi okoka,ziboda za akavalo awo nʼzolimba ngati mwala wansagalabwi,magaleta awo ndi aliwiro ngati kamvuluvulu. 29 Kufuwula kwawo kuli ngati kubangula kwa mkango,amabangula ngati misona ya mkango;imadzuma pamene ikugwira nyamandipo imapita nayo popanda ndi mmodzi yemwe woyipulumutsa. 30 Tsiku limenelo mitundu ya anthu idzabangulangati mkokomo wa madzi a mʼnyanja.Ndipo wina akakayangʼana dzikoloadzangoona mdima ndi zovuta;ngakhale kuwala kudzasanduka mdima chifukwa cha mitambo.

In Other Versions

Isaiah 5 in the ANGEFD

Isaiah 5 in the ANTPNG2D

Isaiah 5 in the AS21

Isaiah 5 in the BAGH

Isaiah 5 in the BBPNG

Isaiah 5 in the BBT1E

Isaiah 5 in the BDS

Isaiah 5 in the BEV

Isaiah 5 in the BHAD

Isaiah 5 in the BIB

Isaiah 5 in the BLPT

Isaiah 5 in the BNT

Isaiah 5 in the BNTABOOT

Isaiah 5 in the BNTLV

Isaiah 5 in the BOATCB

Isaiah 5 in the BOATCB2

Isaiah 5 in the BOBCV

Isaiah 5 in the BOCNT

Isaiah 5 in the BOECS

Isaiah 5 in the BOHCB

Isaiah 5 in the BOHCV

Isaiah 5 in the BOHLNT

Isaiah 5 in the BOHNTLTAL

Isaiah 5 in the BOICB

Isaiah 5 in the BOILNTAP

Isaiah 5 in the BOITCV

Isaiah 5 in the BOKCV

Isaiah 5 in the BOKCV2

Isaiah 5 in the BOKHWOG

Isaiah 5 in the BOKSSV

Isaiah 5 in the BOLCB

Isaiah 5 in the BOLCB2

Isaiah 5 in the BOMCV

Isaiah 5 in the BONAV

Isaiah 5 in the BONCB

Isaiah 5 in the BONLT

Isaiah 5 in the BONUT2

Isaiah 5 in the BOPLNT

Isaiah 5 in the BOSCB

Isaiah 5 in the BOSNC

Isaiah 5 in the BOTLNT

Isaiah 5 in the BOVCB

Isaiah 5 in the BOYCB

Isaiah 5 in the BPBB

Isaiah 5 in the BPH

Isaiah 5 in the BSB

Isaiah 5 in the CCB

Isaiah 5 in the CUV

Isaiah 5 in the CUVS

Isaiah 5 in the DBT

Isaiah 5 in the DGDNT

Isaiah 5 in the DHNT

Isaiah 5 in the DNT

Isaiah 5 in the ELBE

Isaiah 5 in the EMTV

Isaiah 5 in the ESV

Isaiah 5 in the FBV

Isaiah 5 in the FEB

Isaiah 5 in the GGMNT

Isaiah 5 in the GNT

Isaiah 5 in the HARY

Isaiah 5 in the HNT

Isaiah 5 in the IRVA

Isaiah 5 in the IRVB

Isaiah 5 in the IRVG

Isaiah 5 in the IRVH

Isaiah 5 in the IRVK

Isaiah 5 in the IRVM

Isaiah 5 in the IRVM2

Isaiah 5 in the IRVO

Isaiah 5 in the IRVP

Isaiah 5 in the IRVT

Isaiah 5 in the IRVT2

Isaiah 5 in the IRVU

Isaiah 5 in the ISVN

Isaiah 5 in the JSNT

Isaiah 5 in the KAPI

Isaiah 5 in the KBT1ETNIK

Isaiah 5 in the KBV

Isaiah 5 in the KJV

Isaiah 5 in the KNFD

Isaiah 5 in the LBA

Isaiah 5 in the LBLA

Isaiah 5 in the LNT

Isaiah 5 in the LSV

Isaiah 5 in the MAAL

Isaiah 5 in the MBV

Isaiah 5 in the MBV2

Isaiah 5 in the MHNT

Isaiah 5 in the MKNFD

Isaiah 5 in the MNG

Isaiah 5 in the MNT

Isaiah 5 in the MNT2

Isaiah 5 in the MRS1T

Isaiah 5 in the NAA

Isaiah 5 in the NASB

Isaiah 5 in the NBLA

Isaiah 5 in the NBS

Isaiah 5 in the NBVTP

Isaiah 5 in the NET2

Isaiah 5 in the NIV11

Isaiah 5 in the NNT

Isaiah 5 in the NNT2

Isaiah 5 in the NNT3

Isaiah 5 in the PDDPT

Isaiah 5 in the PFNT

Isaiah 5 in the RMNT

Isaiah 5 in the SBIAS

Isaiah 5 in the SBIBS

Isaiah 5 in the SBIBS2

Isaiah 5 in the SBICS

Isaiah 5 in the SBIDS

Isaiah 5 in the SBIGS

Isaiah 5 in the SBIHS

Isaiah 5 in the SBIIS

Isaiah 5 in the SBIIS2

Isaiah 5 in the SBIIS3

Isaiah 5 in the SBIKS

Isaiah 5 in the SBIKS2

Isaiah 5 in the SBIMS

Isaiah 5 in the SBIOS

Isaiah 5 in the SBIPS

Isaiah 5 in the SBISS

Isaiah 5 in the SBITS

Isaiah 5 in the SBITS2

Isaiah 5 in the SBITS3

Isaiah 5 in the SBITS4

Isaiah 5 in the SBIUS

Isaiah 5 in the SBIVS

Isaiah 5 in the SBT

Isaiah 5 in the SBT1E

Isaiah 5 in the SCHL

Isaiah 5 in the SNT

Isaiah 5 in the SUSU

Isaiah 5 in the SUSU2

Isaiah 5 in the SYNO

Isaiah 5 in the TBIAOTANT

Isaiah 5 in the TBT1E

Isaiah 5 in the TBT1E2

Isaiah 5 in the TFTIP

Isaiah 5 in the TFTU

Isaiah 5 in the TGNTATF3T

Isaiah 5 in the THAI

Isaiah 5 in the TNFD

Isaiah 5 in the TNT

Isaiah 5 in the TNTIK

Isaiah 5 in the TNTIL

Isaiah 5 in the TNTIN

Isaiah 5 in the TNTIP

Isaiah 5 in the TNTIZ

Isaiah 5 in the TOMA

Isaiah 5 in the TTENT

Isaiah 5 in the UBG

Isaiah 5 in the UGV

Isaiah 5 in the UGV2

Isaiah 5 in the UGV3

Isaiah 5 in the VBL

Isaiah 5 in the VDCC

Isaiah 5 in the YALU

Isaiah 5 in the YAPE

Isaiah 5 in the YBVTP

Isaiah 5 in the ZBP