Isaiah 58 (BOGWICC)

1 “Fuwula kwambiri, usaleke.Mawu ako amveke ngati lipenga.Uwawuze anthu anga za kulakwa kwawo;uwuze nyumba ya Yakobo za machimo awo. 2 Pakuti tsiku ndi tsiku amafunafuna Ine;amaoneka ngati a chidwi chofuna kudziwa zimene ndimafuna,kukhala ngati kuti ndi dziko limene limachita zolondolandipo silinasiye zolamulira za Mulungu wake.Amandipempha kuti ndigamule mlandu wawo mwachilungamondipo amaonetsa chidwi chofuna kukhala pafupi ndi Mulungu. 3 Anthu akufunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani ife tasalakudya pamene Inu simukulabadirapo?Kodi ife tavutikiranji nʼkudzichepetsapamene Inu simunasamalepo?’ ” Yehova akuti, “Komatu tsiku lanu losala kudya, mumachita zinthu zokukondweretsani,ndipo mumazunza antchito anu onse. 4 Mumati uku mukusala kudya, uku mukukangana ndi kumenyana,mpaka kumenyana ndi nkhonya zopweteka.Kusala kudya mukuchitiramu musayembekezere kuti mawu anu amveka kumwamba. 5 Kodi kusala kudya kumene ndimakufuna Ine nʼkumeneku,kungokhala tsiku loti munthu adzichepetse basi?Kodi ndi tsiku loti munthu angowerama pansi ngati bangondi kumayala ziguduli nʼkuthirapo phulusa nʼkugonapo?Kodi ndiye mumati kusala kudya kumeneko,tsiku lokondweretsa Yehova? 6 “Kodi si uku kusala kudya kumene Ine ndimakufuna:Kumasula maunyolo ozunzizira anthundi kumasula zingwe za goli,kupereka ufulu kwa oponderezedwandi kuphwanya goli lililonse? 7 Anthu anjala kodi mwawagawira chakudya chanu?Osowa ndi ongoyendayenda,kodi mwawapatsa malo ogona?Munthu wausiwa kodi mwamupatsa chovala? 8 Mukatero chipulumutso chanu chidzabwera ngati mʼbandakucha,ndipo mabala anu adzachira msangamsanga;chilungamo chanu chidzakutsogoleranindipo ulemerero wa Yehova udzakhala chokutchinjirizani kumbuyo kwanu. 9 Mukamadzapemphera Yehova adzakuyankhani;mukadzapempha thandizo, Iye adzati: Ine ndili pano. “Ngati muleka kuzunza anzanu,ngati musiya kuloza chala ndiponso kunena zoyipa za anzanu. 10 Ndipo ngati mudyetsa anthu anjala,ndi kuthandiza anthu oponderezedwa,pamenepo kuwala kwanu kudzaonekera mu mdima,ndipo usiku wanu udzakhala ngati usana. 11 Yehova adzakutsogolerani nthawi zonse;adzakwaniritsa zosowa zanu mʼdziko longʼalukangʼaluka dzuwandipo adzalimbitsa matupi anu.Mudzakhala ngati dimba la madzi ambiri,ngati kasupe amene madzi ake saphwa. 12 Anthu ako adzamanganso nyumba zimene zakhala mabwinja nthawi yayitali,ndipo adzamanganso pa maziko akalekale;inu mudzatchedwa okonza makoma opasuka.Anthu okonza misewu ndi nyumba zake. 13 “Muzisunga osaphwanya Sabata;musamachite zimene mukufuna pa masiku anga opatulika,tsiku la Sabata lizikhala tsiku lachisangalalo.Tsiku lopatulika la Yehova muzililemekezaposayenda mʼnjira zanu,kapena kuchita zimene mukufuna ndi kuyankhula zopandapake, 14 mukatero mudzapeza chimwemwe mwa Yehova,ndipo ndidzakukwezani ndi kukupambanitsani pa dziko lonse lapansi.Mudzadyerera dziko limene ndinapatsa Yakobo kholo lanu.”Yehova wayankhula ndi pakamwa pake.

In Other Versions

Isaiah 58 in the ANGEFD

Isaiah 58 in the ANTPNG2D

Isaiah 58 in the AS21

Isaiah 58 in the BAGH

Isaiah 58 in the BBPNG

Isaiah 58 in the BBT1E

Isaiah 58 in the BDS

Isaiah 58 in the BEV

Isaiah 58 in the BHAD

Isaiah 58 in the BIB

Isaiah 58 in the BLPT

Isaiah 58 in the BNT

Isaiah 58 in the BNTABOOT

Isaiah 58 in the BNTLV

Isaiah 58 in the BOATCB

Isaiah 58 in the BOATCB2

Isaiah 58 in the BOBCV

Isaiah 58 in the BOCNT

Isaiah 58 in the BOECS

Isaiah 58 in the BOHCB

Isaiah 58 in the BOHCV

Isaiah 58 in the BOHLNT

Isaiah 58 in the BOHNTLTAL

Isaiah 58 in the BOICB

Isaiah 58 in the BOILNTAP

Isaiah 58 in the BOITCV

Isaiah 58 in the BOKCV

Isaiah 58 in the BOKCV2

Isaiah 58 in the BOKHWOG

Isaiah 58 in the BOKSSV

Isaiah 58 in the BOLCB

Isaiah 58 in the BOLCB2

Isaiah 58 in the BOMCV

Isaiah 58 in the BONAV

Isaiah 58 in the BONCB

Isaiah 58 in the BONLT

Isaiah 58 in the BONUT2

Isaiah 58 in the BOPLNT

Isaiah 58 in the BOSCB

Isaiah 58 in the BOSNC

Isaiah 58 in the BOTLNT

Isaiah 58 in the BOVCB

Isaiah 58 in the BOYCB

Isaiah 58 in the BPBB

Isaiah 58 in the BPH

Isaiah 58 in the BSB

Isaiah 58 in the CCB

Isaiah 58 in the CUV

Isaiah 58 in the CUVS

Isaiah 58 in the DBT

Isaiah 58 in the DGDNT

Isaiah 58 in the DHNT

Isaiah 58 in the DNT

Isaiah 58 in the ELBE

Isaiah 58 in the EMTV

Isaiah 58 in the ESV

Isaiah 58 in the FBV

Isaiah 58 in the FEB

Isaiah 58 in the GGMNT

Isaiah 58 in the GNT

Isaiah 58 in the HARY

Isaiah 58 in the HNT

Isaiah 58 in the IRVA

Isaiah 58 in the IRVB

Isaiah 58 in the IRVG

Isaiah 58 in the IRVH

Isaiah 58 in the IRVK

Isaiah 58 in the IRVM

Isaiah 58 in the IRVM2

Isaiah 58 in the IRVO

Isaiah 58 in the IRVP

Isaiah 58 in the IRVT

Isaiah 58 in the IRVT2

Isaiah 58 in the IRVU

Isaiah 58 in the ISVN

Isaiah 58 in the JSNT

Isaiah 58 in the KAPI

Isaiah 58 in the KBT1ETNIK

Isaiah 58 in the KBV

Isaiah 58 in the KJV

Isaiah 58 in the KNFD

Isaiah 58 in the LBA

Isaiah 58 in the LBLA

Isaiah 58 in the LNT

Isaiah 58 in the LSV

Isaiah 58 in the MAAL

Isaiah 58 in the MBV

Isaiah 58 in the MBV2

Isaiah 58 in the MHNT

Isaiah 58 in the MKNFD

Isaiah 58 in the MNG

Isaiah 58 in the MNT

Isaiah 58 in the MNT2

Isaiah 58 in the MRS1T

Isaiah 58 in the NAA

Isaiah 58 in the NASB

Isaiah 58 in the NBLA

Isaiah 58 in the NBS

Isaiah 58 in the NBVTP

Isaiah 58 in the NET2

Isaiah 58 in the NIV11

Isaiah 58 in the NNT

Isaiah 58 in the NNT2

Isaiah 58 in the NNT3

Isaiah 58 in the PDDPT

Isaiah 58 in the PFNT

Isaiah 58 in the RMNT

Isaiah 58 in the SBIAS

Isaiah 58 in the SBIBS

Isaiah 58 in the SBIBS2

Isaiah 58 in the SBICS

Isaiah 58 in the SBIDS

Isaiah 58 in the SBIGS

Isaiah 58 in the SBIHS

Isaiah 58 in the SBIIS

Isaiah 58 in the SBIIS2

Isaiah 58 in the SBIIS3

Isaiah 58 in the SBIKS

Isaiah 58 in the SBIKS2

Isaiah 58 in the SBIMS

Isaiah 58 in the SBIOS

Isaiah 58 in the SBIPS

Isaiah 58 in the SBISS

Isaiah 58 in the SBITS

Isaiah 58 in the SBITS2

Isaiah 58 in the SBITS3

Isaiah 58 in the SBITS4

Isaiah 58 in the SBIUS

Isaiah 58 in the SBIVS

Isaiah 58 in the SBT

Isaiah 58 in the SBT1E

Isaiah 58 in the SCHL

Isaiah 58 in the SNT

Isaiah 58 in the SUSU

Isaiah 58 in the SUSU2

Isaiah 58 in the SYNO

Isaiah 58 in the TBIAOTANT

Isaiah 58 in the TBT1E

Isaiah 58 in the TBT1E2

Isaiah 58 in the TFTIP

Isaiah 58 in the TFTU

Isaiah 58 in the TGNTATF3T

Isaiah 58 in the THAI

Isaiah 58 in the TNFD

Isaiah 58 in the TNT

Isaiah 58 in the TNTIK

Isaiah 58 in the TNTIL

Isaiah 58 in the TNTIN

Isaiah 58 in the TNTIP

Isaiah 58 in the TNTIZ

Isaiah 58 in the TOMA

Isaiah 58 in the TTENT

Isaiah 58 in the UBG

Isaiah 58 in the UGV

Isaiah 58 in the UGV2

Isaiah 58 in the UGV3

Isaiah 58 in the VBL

Isaiah 58 in the VDCC

Isaiah 58 in the YALU

Isaiah 58 in the YAPE

Isaiah 58 in the YBVTP

Isaiah 58 in the ZBP