James 2 (BOGWICC)

1 Abale anga, okhulupirira Yesu Khristu waulemerero, musaonetse tsankho. 2 Tangoganizirani, pakati panu patabwera munthu atavala mphete yagolide ndi zovala zapamwamba, ndipo winanso wosauka nʼkulowa atavala sanza. 3 Ngati musamala kwambiri munthu wovala bwinoyu uja, nʼkumuwuza kuti, “Khalani pa mpando wabwinowu,” koma wosauka uja nʼkumuwuza kuti, “Ima apo,” kapena “Khala pansi pafupi ndi chopondapo mapazi angawa,” 4 kodi simunachite tsankho pakati panu ndi kukhala oweruza a maganizo oyipa? 5 Tamverani abale anga okondedwa, kodi Mulungu sanasankhe amene dziko lapansi limawaona ngati amphawi kuti akhale olemera mʼchikhulupiriro ndi kulowa ufumu umene Iye analonjeza kwa amene amamukonda? 6 Koma mwakhala mukunyoza amphawi. Kodi si anthu olemerawa amene akukudyerani masuku pamutu? Si anthu amenewa amene amakukokerani ku bwalo la milandu? 7 Kodi si omwewa amene amachita chipongwe dzina la wolemekezeka, limene inu mumatchulidwa? 8 Ngati musungadi lamulo laufumu lija lopezeka mʼMalemba lakuti, “Konda mnansi wako monga iwe mwini,” ndiye kuti mukuchita bwino. 9 Koma mukamaonetsa tsankho mukuchimwa, ndipo ndinu wochimwa monga wophwanya lamulo. 10 Pakuti amene amasunga Malamulo onse, akangophwanya fundo imodzi yokha, waphwanya Malamulo onse. 11 Pakuti amene anati “Usachite chigololo” ndi yemweyonso anati “Usaphe.” Ngati suchita chigololo koma umapha, ndiwe wophwanya Malamulo. 12 Muziyankhula ndi kuchita zinthu monga anthu amene mudzaweruzidwe ndi lamulo limene limapereka ufulu, 13 chifukwa munthu woweruza mopanda chifundo, nayenso adzaweruzidwa mopanda chifundo. Chifundo chimapambana pa chiweruzo. 14 Abale anga, phindu lake nʼchiyani ngati munthu anena kuti ali ndi chikhulupiriro koma chopanda ntchito zabwino? Kodi chikhulupiriro choterechi chingamupulumutse? 15 Tangoganizirani, mʼbale kapena mlongo amene ali ndi usiwa, ndipo alibe chakudya cha tsiku ndi tsiku. 16 Ngati mmodzi wa inu amuwuza kuti, “Pita ndi mtendere, ukafundidwe ndipo ukakhute,” koma osamupatsa zimene akuzisowa, phindu lake nʼchiyani pamenepa? 17 Chomwechonso, chikhulupiriro chokha chopanda ntchito zabwino ndi chakufa. 18 Koma wina anganene kuti, “Inuyo muli ndi chikhulupiriro koma ine ndili ndi ntchito zabwino.”Onetsani chikhulupiriro chanu chopanda ntchito zabwino ndipo ineyo ndidzakuonetsani chikhulupiriro changa pochita ntchito zabwino. 19 Mumakhulupirira kuti kuli Mulungu mmodzi yekha. Mumachita bwino. Komatu ngakhale ziwanda zimakhulupirira zimenezi ndipo zimanjenjemera ndi mantha. 20 Munthu wopusa iwe, kodi ukufuna umboni woti chikhulupiriro chopanda ntchito zabwino nʼchakufa? 21 Kodi Abrahamu kholo lathu sanatengedwe kukhala wolungama chifukwa cha zimene anachita pamene anapereka mwana wake Isake pa guwa lansembe? 22 Tsono mukuona kuti chikhulupiriro chake ndi ntchito zabwino zinkachitika pamodzi, ndipo chikhulupiriro chake chinasanduka chenicheni chifukwa cha ntchito zake zabwino. 23 Ndipo Malemba akunena kuti, “Abrahamu anakhulupirira Mulungu ndipo anatengedwa kukhala wolungama,” ndipo anatchedwa bwenzi la Mulungu. 24 Tsono mukuona kuti munthu amasanduka wolungama ndi ntchito zabwino osati ndi chikhulupiriro chokha ayi. 25 Nʼchimodzimodzinso, kodi wadama uja, Rahabe, sanasanduke wolungama chifukwa cha zomwe anachita pamene anapereka malo ogona kwa azondi aja ndi kuwathawitsira mbali ina? 26 Monga thupi lopanda mzimu ndi lakufa, chomwechonso chikhulupiriro chopanda ntchito zabwino ndi chakufa.

In Other Versions

James 2 in the ANGEFD

James 2 in the ANTPNG2D

James 2 in the AS21

James 2 in the BAGH

James 2 in the BBPNG

James 2 in the BBT1E

James 2 in the BDS

James 2 in the BEV

James 2 in the BHAD

James 2 in the BIB

James 2 in the BLPT

James 2 in the BNT

James 2 in the BNTABOOT

James 2 in the BNTLV

James 2 in the BOATCB

James 2 in the BOATCB2

James 2 in the BOBCV

James 2 in the BOCNT

James 2 in the BOECS

James 2 in the BOHCB

James 2 in the BOHCV

James 2 in the BOHLNT

James 2 in the BOHNTLTAL

James 2 in the BOICB

James 2 in the BOILNTAP

James 2 in the BOITCV

James 2 in the BOKCV

James 2 in the BOKCV2

James 2 in the BOKHWOG

James 2 in the BOKSSV

James 2 in the BOLCB

James 2 in the BOLCB2

James 2 in the BOMCV

James 2 in the BONAV

James 2 in the BONCB

James 2 in the BONLT

James 2 in the BONUT2

James 2 in the BOPLNT

James 2 in the BOSCB

James 2 in the BOSNC

James 2 in the BOTLNT

James 2 in the BOVCB

James 2 in the BOYCB

James 2 in the BPBB

James 2 in the BPH

James 2 in the BSB

James 2 in the CCB

James 2 in the CUV

James 2 in the CUVS

James 2 in the DBT

James 2 in the DGDNT

James 2 in the DHNT

James 2 in the DNT

James 2 in the ELBE

James 2 in the EMTV

James 2 in the ESV

James 2 in the FBV

James 2 in the FEB

James 2 in the GGMNT

James 2 in the GNT

James 2 in the HARY

James 2 in the HNT

James 2 in the IRVA

James 2 in the IRVB

James 2 in the IRVG

James 2 in the IRVH

James 2 in the IRVK

James 2 in the IRVM

James 2 in the IRVM2

James 2 in the IRVO

James 2 in the IRVP

James 2 in the IRVT

James 2 in the IRVT2

James 2 in the IRVU

James 2 in the ISVN

James 2 in the JSNT

James 2 in the KAPI

James 2 in the KBT1ETNIK

James 2 in the KBV

James 2 in the KJV

James 2 in the KNFD

James 2 in the LBA

James 2 in the LBLA

James 2 in the LNT

James 2 in the LSV

James 2 in the MAAL

James 2 in the MBV

James 2 in the MBV2

James 2 in the MHNT

James 2 in the MKNFD

James 2 in the MNG

James 2 in the MNT

James 2 in the MNT2

James 2 in the MRS1T

James 2 in the NAA

James 2 in the NASB

James 2 in the NBLA

James 2 in the NBS

James 2 in the NBVTP

James 2 in the NET2

James 2 in the NIV11

James 2 in the NNT

James 2 in the NNT2

James 2 in the NNT3

James 2 in the PDDPT

James 2 in the PFNT

James 2 in the RMNT

James 2 in the SBIAS

James 2 in the SBIBS

James 2 in the SBIBS2

James 2 in the SBICS

James 2 in the SBIDS

James 2 in the SBIGS

James 2 in the SBIHS

James 2 in the SBIIS

James 2 in the SBIIS2

James 2 in the SBIIS3

James 2 in the SBIKS

James 2 in the SBIKS2

James 2 in the SBIMS

James 2 in the SBIOS

James 2 in the SBIPS

James 2 in the SBISS

James 2 in the SBITS

James 2 in the SBITS2

James 2 in the SBITS3

James 2 in the SBITS4

James 2 in the SBIUS

James 2 in the SBIVS

James 2 in the SBT

James 2 in the SBT1E

James 2 in the SCHL

James 2 in the SNT

James 2 in the SUSU

James 2 in the SUSU2

James 2 in the SYNO

James 2 in the TBIAOTANT

James 2 in the TBT1E

James 2 in the TBT1E2

James 2 in the TFTIP

James 2 in the TFTU

James 2 in the TGNTATF3T

James 2 in the THAI

James 2 in the TNFD

James 2 in the TNT

James 2 in the TNTIK

James 2 in the TNTIL

James 2 in the TNTIN

James 2 in the TNTIP

James 2 in the TNTIZ

James 2 in the TOMA

James 2 in the TTENT

James 2 in the UBG

James 2 in the UGV

James 2 in the UGV2

James 2 in the UGV3

James 2 in the VBL

James 2 in the VDCC

James 2 in the YALU

James 2 in the YAPE

James 2 in the YBVTP

James 2 in the ZBP