Jeremiah 17 (BOGWICC)

1 “Tchimo la Yuda lazokotedwa ndi cholembera cha chitsulo,lalembedwa ndi msonga ya mwala wadayimondi.Uchimowo walembedwa pa mitima yawondiponso pa nyanga za maguwa awo. 2 Ngakhale ana awo amakumbukiramaguwa awo ndi zoyimiritsa ngati zifanizo za mulungu wawo Asera,pa tsinde la mitengo ya masamba ambiri,pa mapiri aatali mʼdzikomo. 3 Chuma chanu ndiponso katundu wanu yensendidzazipereka kwa ofunkhakuti zikhale dipo lawochifukwa cha machimoochitika mʼdziko lonse. 4 Mudzataya dziko limene ndinakupatsanikuti likhale cholowa chanu.Ndidzakusandutsani akapolo otumikira adani anumʼdziko limene inu simukulidziwa,chifukwa mwabutsa mkwiyo wanga ngati moto,ndipo udzayaka mpaka muyaya.” 5 Yehova akuti,“Ndi wotembereredwa munthu amene amadalira munthu mnzake,amene amatsamira pa munthu mnzake kuti amuthandizepamene mtima wake wafulatira Yehova. 6 Munthuyo adzakhala ngati chitsamba mʼchipululu;iye sadzapeza zabwino.Adzakhala mʼchipululu mopanda madzi,mʼdziko lamchere limene munthu sangathe kukhalamo. 7 “Koma ndi wodala munthu amene amadalira Yehova,amene amatsamira pa Iye. 8 Adzakhala ngati mtengo wodzalidwa mʼmphepete mwa madziumene umatambalitsa mizu yake mʼmbali mwa mtsinje.Mtengowo suopa pamene kukutentha;masamba ake amakhala obiriwira nthawi zonse.Suchita mantha pa chaka cha chilalandipo sulephera kubereka chipatso.” 9 Mtima wa munthu ndi wonyenga kupambana zinthu zonsendipo kuyipa kwake nʼkosachizika.Ndani angathe kuwumvetsa? 10 “Ine Yehova ndimafufuza mtimandi kuyesa maganizo,ndimachitira munthu aliyense molingana ndi makhalidwe akendiponso moyenera ntchito zake.” 11 Munthu amene amapeza chuma mwachinyengoali ngati nkhwali imene imafungatira mazira amene sinayikire.Pamene ali pakatikati pa moyo wake, chumacho chidzamuthera,ndipo potsiriza adzasanduka chitsiru. 12 Nyumba yathu yopemphereramo ili ngati mpando waufumu waulemererowokhazikitsidwa pa phiri lalitali chiyambire. 13 Inu Yehova, chiyembekezo cha Israeli,onse amene amakusiyani adzachita manyazi.Iwo amene amakufulatirani mayina awo adzafafanizika ngati olembedwa pa fumbichifukwa anakana Yehova,kasupe wa madzi amoyo. 14 Inu Yehova, chiritseni, ndipo ndidzachira;pulumutseni ndipo ndidzapulumuka,chifukwa ndinu amene ndimakutamandani. 15 Anthu akumandinena kuti,“Mawu a Yehova ali kuti?Zichitiketu lero kuti tizione!” 16 Ine sindinakuwumirizeni kuti muwalange.Mukudziwa kuti ine sindilakalaka tsiku la tsoka.Zonse zimene ndinayankhula Inu mukuzidziwa. 17 Musandichititse mantha;ndinu pothawira panga pa tsiku la mavuto. 18 Ondizunza anga achite manyazi,koma musandichititse manyazi;iwo achite mantha kwambiri,koma ine mundichotsere manthawo.Tsiku la mavuto liwafikire;ndipo muwawononge kotheratu. 19 Yehova anandiwuza kuti, “Pita ukayime pa chipata chodzerapo anthu, chimene mafumu a ku Yuda amalowerapo ndi kutulukirapo. Ukayimenso pa zipata zina zonse za Yerusalemu. 20 Ukawawuze kuti, ‘Imvani mawu a Yehova, inu mafumu onse a ku Yuda ndi anthu onse a ku Yuda ndi inu nonse okhala mu Yerusalemu amene mumatulukira pa zipata izi.’ 21 Yehova akuti: samalani kuti pa tsiku la Sabata musanyamule katundu kapena kulowa naye pa zipata za Yerusalemu. 22 Musalowetse katundu mʼnyumba zanu kapena kugwira ntchito pa tsiku la Sabata, koma mulipatule tsiku la Sabatalo, monga ndinalamulira makolo anu. 23 Komatu iwo sanandimvere kapena kulabadira. Ndi mitima yawo yowumayo sanamvere kapena kulandira malangizo anga. 24 Yehova akuti, ‘Muzimvera Ine ndi kuleka kulowetsa kapena kutulutsa katundu pa zipata za mzinda pa tsiku la Sabata. Muzisunga tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika posachita ntchito iliyonse pa tsikuli. 25 Mukatero ndiye mafumu anu amene akukhala pa mpando wa Davide adzatulukira pa zipata za mzindawu pamodzi ndi nduna zawo. Iwo pamodzi ndi nduna zawo azidzalowa atakwera magaleta ndi akavalo, akuperekezedwa ndi anthu a ku Yuda ndi amene amakhala mu Yerusalemu, ndipo mu mzinda muno mudzakhala anthu mpaka muyaya. 26 Anthu adzabwera kuchokera ku mizinda ya Yuda ndi ku midzi yozungulira Yerusalemu, kuchokera ku dziko la Benjamini ndi ku mapiri a kumadzulo, kuchokera ku dziko la mapiri ndi ku Negevi. Adzabwera ndi nsembe zopsereza, nsembe zaufa ndi za chakudya, nsembe za lubani ndi zopereka zachiyamiko ku nyumba ya Yehova. 27 Koma ngati simundimvera; mukapanda kusunga tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika ndi kumanyamula katundu nʼkumalowa naye pa zipata za Yerusalemu pa tsikuli, Ine ndidzabutsa moto pa zipata za Yerusalemu. Moto umenewo udzanyeketsa nyumba zaufumu za ku Yerusalemu ndipo moto wake sudzazima.’ ”

In Other Versions

Jeremiah 17 in the ANGEFD

Jeremiah 17 in the ANTPNG2D

Jeremiah 17 in the AS21

Jeremiah 17 in the BAGH

Jeremiah 17 in the BBPNG

Jeremiah 17 in the BBT1E

Jeremiah 17 in the BDS

Jeremiah 17 in the BEV

Jeremiah 17 in the BHAD

Jeremiah 17 in the BIB

Jeremiah 17 in the BLPT

Jeremiah 17 in the BNT

Jeremiah 17 in the BNTABOOT

Jeremiah 17 in the BNTLV

Jeremiah 17 in the BOATCB

Jeremiah 17 in the BOATCB2

Jeremiah 17 in the BOBCV

Jeremiah 17 in the BOCNT

Jeremiah 17 in the BOECS

Jeremiah 17 in the BOHCB

Jeremiah 17 in the BOHCV

Jeremiah 17 in the BOHLNT

Jeremiah 17 in the BOHNTLTAL

Jeremiah 17 in the BOICB

Jeremiah 17 in the BOILNTAP

Jeremiah 17 in the BOITCV

Jeremiah 17 in the BOKCV

Jeremiah 17 in the BOKCV2

Jeremiah 17 in the BOKHWOG

Jeremiah 17 in the BOKSSV

Jeremiah 17 in the BOLCB

Jeremiah 17 in the BOLCB2

Jeremiah 17 in the BOMCV

Jeremiah 17 in the BONAV

Jeremiah 17 in the BONCB

Jeremiah 17 in the BONLT

Jeremiah 17 in the BONUT2

Jeremiah 17 in the BOPLNT

Jeremiah 17 in the BOSCB

Jeremiah 17 in the BOSNC

Jeremiah 17 in the BOTLNT

Jeremiah 17 in the BOVCB

Jeremiah 17 in the BOYCB

Jeremiah 17 in the BPBB

Jeremiah 17 in the BPH

Jeremiah 17 in the BSB

Jeremiah 17 in the CCB

Jeremiah 17 in the CUV

Jeremiah 17 in the CUVS

Jeremiah 17 in the DBT

Jeremiah 17 in the DGDNT

Jeremiah 17 in the DHNT

Jeremiah 17 in the DNT

Jeremiah 17 in the ELBE

Jeremiah 17 in the EMTV

Jeremiah 17 in the ESV

Jeremiah 17 in the FBV

Jeremiah 17 in the FEB

Jeremiah 17 in the GGMNT

Jeremiah 17 in the GNT

Jeremiah 17 in the HARY

Jeremiah 17 in the HNT

Jeremiah 17 in the IRVA

Jeremiah 17 in the IRVB

Jeremiah 17 in the IRVG

Jeremiah 17 in the IRVH

Jeremiah 17 in the IRVK

Jeremiah 17 in the IRVM

Jeremiah 17 in the IRVM2

Jeremiah 17 in the IRVO

Jeremiah 17 in the IRVP

Jeremiah 17 in the IRVT

Jeremiah 17 in the IRVT2

Jeremiah 17 in the IRVU

Jeremiah 17 in the ISVN

Jeremiah 17 in the JSNT

Jeremiah 17 in the KAPI

Jeremiah 17 in the KBT1ETNIK

Jeremiah 17 in the KBV

Jeremiah 17 in the KJV

Jeremiah 17 in the KNFD

Jeremiah 17 in the LBA

Jeremiah 17 in the LBLA

Jeremiah 17 in the LNT

Jeremiah 17 in the LSV

Jeremiah 17 in the MAAL

Jeremiah 17 in the MBV

Jeremiah 17 in the MBV2

Jeremiah 17 in the MHNT

Jeremiah 17 in the MKNFD

Jeremiah 17 in the MNG

Jeremiah 17 in the MNT

Jeremiah 17 in the MNT2

Jeremiah 17 in the MRS1T

Jeremiah 17 in the NAA

Jeremiah 17 in the NASB

Jeremiah 17 in the NBLA

Jeremiah 17 in the NBS

Jeremiah 17 in the NBVTP

Jeremiah 17 in the NET2

Jeremiah 17 in the NIV11

Jeremiah 17 in the NNT

Jeremiah 17 in the NNT2

Jeremiah 17 in the NNT3

Jeremiah 17 in the PDDPT

Jeremiah 17 in the PFNT

Jeremiah 17 in the RMNT

Jeremiah 17 in the SBIAS

Jeremiah 17 in the SBIBS

Jeremiah 17 in the SBIBS2

Jeremiah 17 in the SBICS

Jeremiah 17 in the SBIDS

Jeremiah 17 in the SBIGS

Jeremiah 17 in the SBIHS

Jeremiah 17 in the SBIIS

Jeremiah 17 in the SBIIS2

Jeremiah 17 in the SBIIS3

Jeremiah 17 in the SBIKS

Jeremiah 17 in the SBIKS2

Jeremiah 17 in the SBIMS

Jeremiah 17 in the SBIOS

Jeremiah 17 in the SBIPS

Jeremiah 17 in the SBISS

Jeremiah 17 in the SBITS

Jeremiah 17 in the SBITS2

Jeremiah 17 in the SBITS3

Jeremiah 17 in the SBITS4

Jeremiah 17 in the SBIUS

Jeremiah 17 in the SBIVS

Jeremiah 17 in the SBT

Jeremiah 17 in the SBT1E

Jeremiah 17 in the SCHL

Jeremiah 17 in the SNT

Jeremiah 17 in the SUSU

Jeremiah 17 in the SUSU2

Jeremiah 17 in the SYNO

Jeremiah 17 in the TBIAOTANT

Jeremiah 17 in the TBT1E

Jeremiah 17 in the TBT1E2

Jeremiah 17 in the TFTIP

Jeremiah 17 in the TFTU

Jeremiah 17 in the TGNTATF3T

Jeremiah 17 in the THAI

Jeremiah 17 in the TNFD

Jeremiah 17 in the TNT

Jeremiah 17 in the TNTIK

Jeremiah 17 in the TNTIL

Jeremiah 17 in the TNTIN

Jeremiah 17 in the TNTIP

Jeremiah 17 in the TNTIZ

Jeremiah 17 in the TOMA

Jeremiah 17 in the TTENT

Jeremiah 17 in the UBG

Jeremiah 17 in the UGV

Jeremiah 17 in the UGV2

Jeremiah 17 in the UGV3

Jeremiah 17 in the VBL

Jeremiah 17 in the VDCC

Jeremiah 17 in the YALU

Jeremiah 17 in the YAPE

Jeremiah 17 in the YBVTP

Jeremiah 17 in the ZBP