Jeremiah 23 (BOGWICC)

1 “Tsoka kwa abusa amene akuwononga ndi kubalalitsa nkhosa za pabusa panga!” akutero Yehova. 2 Nʼchifukwa chake Yehova, Mulungu wa Israeli, ponena za abusa amene akuweta anthu anga akuti, “Mwabalalitsa ndi kumwaza nkhosa zanga. Komanso simunazisamale bwino. Choncho ndidzakulangani chifukwa cha machimo anu,” akutero Yehova. 3 “Pambuyo pake Ine mwini wakene ndidzasonkhanitsa nkhosa zanga zotsala, kuzichotsa ku mayiko onse kumene ndinazibalalitsira ndi kuzibweretsanso ku msipu wawo. Kumeneko zidzaswana ndi kuchulukana. 4 Ndidzazipatsa abusa amene adzaziweta, ndipo sizidzaopanso kapena kuchita mantha, ndipo palibe imene idzasochera,” akutero Yehova. 5 Yehova akuti, “Masiku akubwera,pamene ndidzaphukitsira Davide Nthambi yowongoka.Imeneyi ndiye mfumu imene idzalamulira mwanzeru, mwachilungamo ndi mosakondera mʼdziko. 6 Pa masiku a ulamuliro wake Yuda adzapulumukandipo Israeli adzakhala pamtendere.Dzina limene adzamutcha ndi ili:Yehova ndiye Chilungamo Chathu. 7 Choncho, masiku akubwera,” akutero Yehova, “pamene anthu sadzanenanso polumbira kuti, ‘Pali Yehova wamoyo, amene anatulutsa Aisraeli ku Igupto,’ 8 koma adzanena kuti, ‘Pali Yehova wamoyo, amene anatulutsa zidzukulu za Israeli ku dziko lakumpoto ndi ku mayiko konse kumene anawabalalitsira.’ Ndipo iwo adzawabweretsa ku dziko lawolawo.” 9 Kunena za aneneri awa:Mtima wanga wasweka;mʼnkhongono mwati zii.Ndakhala ngati munthu woledzera,ngati munthu amene wasokonezeka ndi vinyo,chifukwa cha Yehovandi mawu ake opatulika. 10 Dziko ladzaza ndi anthu achigololo;lili pansi pa matemberero.Dziko lasanduka chipululu ndipo msipu wawuma.Aneneri akuchita zoyipandipo akugwiritsa ntchito mphamvu zawo molakwika. 11 “Mneneri ngakhale wansembe onse sapembedza Yehova.Amachita zoyipa ngakhale mʼnyumba yanga,”akutero Yehova. 12 “Nʼchifukwa chake njira zawo zidzakhala zoterera;adzawapirikitsira ku mdimandipo adzagwera kumeneko.Adzaona zosaonamʼnthawi ya chilango chawo,”akutero Yehova. 13 “Pakati pa aneneri a ku Samariyandinaona chonyansa ichi:Ankanenera mʼdzina la Baalandipo anasocheretsa anthu anga, Aisraeli. 14 Ndipo pakati pa aneneri a ku Yerusalemundaonapo chinthu choopsa kwambiri:amachita chigololo, amanena bodzandipo amalimbitsa mtima anthu ochita zoyipa.Choncho palibe amene amasiya zoyipa zake.Kwa Ine anthu onsewaali ngati a ku Sodomu ndi Gomora.” 15 Choncho ponena za aneneriwa Yehova Wamphamvuzonse akuti,“Ndidzawadyetsa zakudya zowawandi kuwamwetsa madzi a ndulu,chifukwa uchimo umene wafalikira mʼdziko lonsendi wochokera kwa aneneri a ku Yerusalemuwa.” 16 Koma Yehova Wamphamvuzonse akuti,“Musamvere zimene aneneri amenewa akulosera kwa inu;zomwe aloserazo nʼzachabechabe.Iwo akungoyankhula za masomphenya a mʼmitima mwawo basi,osati zochokera kwa Yehova. 17 Iwo amapita ndi kumakawuza amene amandinyoza Ine kuti,‘zinthu zidzakuyenderani bwino.’Kwa iwo amene amawumirira kutsata zofuna za mitima yawo amakawawuza kuti,‘palibe choyipa chimene chidzakugwereni.’ ” 18 Ine ndikuti, “Koma ndani wa iwo amene anakhalapo mu msonkhano wa Yehova?Ndani anaonapo kapena kumvapo mawu ake?Ndani mwa iwo analabadirako za mawu ake ndi kuwamvera? 19 Taonani ukali wa Yehovauli ngati chimphepo chamkuntho,inde ngati namondwe.Ndipo adzakantha mitu ya anthu oyipa. 20 Mkwiyo wa Yehova sudzalekampaka atachita zonse zimeneanatsimikiza mu mtima mwake.Mudzazizindikira bwino zimenezimasiku akubwerawa.” 21 Yehova anati, “Ine sindinatume aneneri amenewa,komabe iwo athamanga uku ndi uku kulalikira uthenga wawo;Ine sindinawayankhule,komabe iwo ananenera. 22 Iwo akanakhala pa msonkhano wangandiye kuti akanamayankhula mawu anga kwa anthu anga.Komanso bwenzi atawachotsa anthu anga mʼnjira zawo zoyipakuti aleke machimo awo.” 23 Yehova akuti, “Kodi ndimakhala Mulungu pokhapokha ndikakhala pafupi,ndiye sindine Mulungu? 24 Kodi wina angathe kubisalaIne osamuona?”“Kodi Ine sindili ponseponse kumwamba ndi dziko lapansi?”Akutero Yehova. 25 “Ndamva zimene aneneri akuyankhula. Iwo amalosera zabodza mʼdzina langa nʼkumati, ‘Ndalota! Ndalota!’ 26 Kodi zabodzazi zidzakhalabe mʼmitima ya aneneriwa mpaka liti? Iwotu amalosera zonyenga za mʼmitima yawo. 27 Aneneriwa amakhulupirira kuti anthu anga adzayiwala mawu anga akamamva za maloto awo amene amayankhulana ngati mmene anachitira makolo awo popembedza Baala. 28 Mneneri amene ali ndi maloto afotokoze malotowo. Koma iye amene ali ndi mawu anga alalikire mawuwo mokhulupirika. Kodi phesi lingafanane ndi chimanga? 29 Kodi suja mawu anga amatentha ngati moto? Suja mawu anga amaphwanya monga ichitira nyundo kuphwanya miyala?” Akutero Yehova. 30 Yehova akuti, “Nʼchifukwa chake, Ine ndikudana nawo aneneri amene amaberana okhaokha mawu nʼkumati mawuwo ndi a Yehova.” 31 Yehova akuti, “Inde, Ine ndikudana ndi aneneri amene amakonda kuyankhula zabodza nʼkumanena kuti, ‘Amenewa ndi mawu a Yehova.’ ” 32 Yehova akuti, “Ndithudi, Ine ndikudana ndi aneneri a maloto abodzawa. Iwo amafotokoza malotowo nʼkumasocheretsa anthu anga ndi bodza lawo losachita nalo manyazilo, chonsecho Ine sindinawatume kapena kuwalamula. Iwo sathandiza anthuwa ndi pangʼono pomwe,” akutero Yehova. 33 Yehova anawuza Yeremiya kuti, “Anthu awa, kapena mneneri, kapenanso wansembe, akakufunsa kuti, ‘Kodi uthenga wolemetsa wa Yehova ukuti chiyani?’ uwawuze kuti, ‘Inuyo ndinu katundu wolemetsa Yehova, ndipo adzakutayani.’ 34 Ngati mneneri kapena wansembe kapenanso munthu wina aliyense anena kuti, ‘Uthenga wolemetsa wa Yehova ndi uwu,’ Ine ndidzalanga munthu ameneyo pamodzi ndi banja lake. 35 Koma chimene aliyense wa inu azifunsa kwa mnzake kapena mʼbale wake ndi ichi: ‘Kodi Yehova wayankha chiyani?’ kapena ‘Yehova wayankhula chiyani?’ 36 Koma musanenenso kuti ‘nawu uthenga wolemetsa wa Yehova,’ chifukwa mawu a munthu aliyense ndiwo uthenga wa iye mwini, kotero kuti inu mumakhotetsa mawu a Mulungu wamoyo, Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wathu. 37 Tsono iwe Yeremiya udzamufunse mneneri kuti, ‘Kodi Yehova wakuyankha chiyani?’ kapena, ‘Kodi Yehova wayankhula chiyani?’ 38 Ngati mudzanena kuti, ‘Nawu uthenga wolemetsa wa Yehova,’ ndiye tsono Yehova akuti, ‘Popeza mwagwiritsa ntchito mawu akuti: Nawu uthenga wolemetsa wa Yehova, mawu amene ndinakuletsani kuti musawatchule, 39 ndiye kuti Ine ndidzakunyamulani ngati katundu nʼkukuponyani kutali. Ndidzakuchotsani pamaso panga, inuyo pamodzi ndi mzinda umene ndinakupatsani inu ndi makolo anu. 40 Ndidzakunyozani mpaka muyaya. Ndidzakuchititsani manyazi osayiwalika.’ ”

In Other Versions

Jeremiah 23 in the ANGEFD

Jeremiah 23 in the ANTPNG2D

Jeremiah 23 in the AS21

Jeremiah 23 in the BAGH

Jeremiah 23 in the BBPNG

Jeremiah 23 in the BBT1E

Jeremiah 23 in the BDS

Jeremiah 23 in the BEV

Jeremiah 23 in the BHAD

Jeremiah 23 in the BIB

Jeremiah 23 in the BLPT

Jeremiah 23 in the BNT

Jeremiah 23 in the BNTABOOT

Jeremiah 23 in the BNTLV

Jeremiah 23 in the BOATCB

Jeremiah 23 in the BOATCB2

Jeremiah 23 in the BOBCV

Jeremiah 23 in the BOCNT

Jeremiah 23 in the BOECS

Jeremiah 23 in the BOHCB

Jeremiah 23 in the BOHCV

Jeremiah 23 in the BOHLNT

Jeremiah 23 in the BOHNTLTAL

Jeremiah 23 in the BOICB

Jeremiah 23 in the BOILNTAP

Jeremiah 23 in the BOITCV

Jeremiah 23 in the BOKCV

Jeremiah 23 in the BOKCV2

Jeremiah 23 in the BOKHWOG

Jeremiah 23 in the BOKSSV

Jeremiah 23 in the BOLCB

Jeremiah 23 in the BOLCB2

Jeremiah 23 in the BOMCV

Jeremiah 23 in the BONAV

Jeremiah 23 in the BONCB

Jeremiah 23 in the BONLT

Jeremiah 23 in the BONUT2

Jeremiah 23 in the BOPLNT

Jeremiah 23 in the BOSCB

Jeremiah 23 in the BOSNC

Jeremiah 23 in the BOTLNT

Jeremiah 23 in the BOVCB

Jeremiah 23 in the BOYCB

Jeremiah 23 in the BPBB

Jeremiah 23 in the BPH

Jeremiah 23 in the BSB

Jeremiah 23 in the CCB

Jeremiah 23 in the CUV

Jeremiah 23 in the CUVS

Jeremiah 23 in the DBT

Jeremiah 23 in the DGDNT

Jeremiah 23 in the DHNT

Jeremiah 23 in the DNT

Jeremiah 23 in the ELBE

Jeremiah 23 in the EMTV

Jeremiah 23 in the ESV

Jeremiah 23 in the FBV

Jeremiah 23 in the FEB

Jeremiah 23 in the GGMNT

Jeremiah 23 in the GNT

Jeremiah 23 in the HARY

Jeremiah 23 in the HNT

Jeremiah 23 in the IRVA

Jeremiah 23 in the IRVB

Jeremiah 23 in the IRVG

Jeremiah 23 in the IRVH

Jeremiah 23 in the IRVK

Jeremiah 23 in the IRVM

Jeremiah 23 in the IRVM2

Jeremiah 23 in the IRVO

Jeremiah 23 in the IRVP

Jeremiah 23 in the IRVT

Jeremiah 23 in the IRVT2

Jeremiah 23 in the IRVU

Jeremiah 23 in the ISVN

Jeremiah 23 in the JSNT

Jeremiah 23 in the KAPI

Jeremiah 23 in the KBT1ETNIK

Jeremiah 23 in the KBV

Jeremiah 23 in the KJV

Jeremiah 23 in the KNFD

Jeremiah 23 in the LBA

Jeremiah 23 in the LBLA

Jeremiah 23 in the LNT

Jeremiah 23 in the LSV

Jeremiah 23 in the MAAL

Jeremiah 23 in the MBV

Jeremiah 23 in the MBV2

Jeremiah 23 in the MHNT

Jeremiah 23 in the MKNFD

Jeremiah 23 in the MNG

Jeremiah 23 in the MNT

Jeremiah 23 in the MNT2

Jeremiah 23 in the MRS1T

Jeremiah 23 in the NAA

Jeremiah 23 in the NASB

Jeremiah 23 in the NBLA

Jeremiah 23 in the NBS

Jeremiah 23 in the NBVTP

Jeremiah 23 in the NET2

Jeremiah 23 in the NIV11

Jeremiah 23 in the NNT

Jeremiah 23 in the NNT2

Jeremiah 23 in the NNT3

Jeremiah 23 in the PDDPT

Jeremiah 23 in the PFNT

Jeremiah 23 in the RMNT

Jeremiah 23 in the SBIAS

Jeremiah 23 in the SBIBS

Jeremiah 23 in the SBIBS2

Jeremiah 23 in the SBICS

Jeremiah 23 in the SBIDS

Jeremiah 23 in the SBIGS

Jeremiah 23 in the SBIHS

Jeremiah 23 in the SBIIS

Jeremiah 23 in the SBIIS2

Jeremiah 23 in the SBIIS3

Jeremiah 23 in the SBIKS

Jeremiah 23 in the SBIKS2

Jeremiah 23 in the SBIMS

Jeremiah 23 in the SBIOS

Jeremiah 23 in the SBIPS

Jeremiah 23 in the SBISS

Jeremiah 23 in the SBITS

Jeremiah 23 in the SBITS2

Jeremiah 23 in the SBITS3

Jeremiah 23 in the SBITS4

Jeremiah 23 in the SBIUS

Jeremiah 23 in the SBIVS

Jeremiah 23 in the SBT

Jeremiah 23 in the SBT1E

Jeremiah 23 in the SCHL

Jeremiah 23 in the SNT

Jeremiah 23 in the SUSU

Jeremiah 23 in the SUSU2

Jeremiah 23 in the SYNO

Jeremiah 23 in the TBIAOTANT

Jeremiah 23 in the TBT1E

Jeremiah 23 in the TBT1E2

Jeremiah 23 in the TFTIP

Jeremiah 23 in the TFTU

Jeremiah 23 in the TGNTATF3T

Jeremiah 23 in the THAI

Jeremiah 23 in the TNFD

Jeremiah 23 in the TNT

Jeremiah 23 in the TNTIK

Jeremiah 23 in the TNTIL

Jeremiah 23 in the TNTIN

Jeremiah 23 in the TNTIP

Jeremiah 23 in the TNTIZ

Jeremiah 23 in the TOMA

Jeremiah 23 in the TTENT

Jeremiah 23 in the UBG

Jeremiah 23 in the UGV

Jeremiah 23 in the UGV2

Jeremiah 23 in the UGV3

Jeremiah 23 in the VBL

Jeremiah 23 in the VDCC

Jeremiah 23 in the YALU

Jeremiah 23 in the YAPE

Jeremiah 23 in the YBVTP

Jeremiah 23 in the ZBP