Jeremiah 4 (BOGWICC)

1 “Ngati mukufuna kubwerera, inu Aisraeli,bwererani kwa Ine,”akutero Yehova.“Chotsani mafano anu onyansa pamaso pangandipo musasocherenso. 2 Muzilumbira mokhulupirika ndiponso mwa chilungamokuti, ‘Pali Yehova wamoyo.’Mukatero anthu a mitundu ina yonse adzandipempha kuti ndiwadalitsendipo adzanditamanda.” 3 Zimene Yehova akunena kwa anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu ndi izi:“Limani masala anumusadzale pakati pa minga. 4 Dziperekeni nokha kwa Inekuti munditumikire ndi mtima wanu wonse,inu anthu a ku Yuda ndi ku Yerusalemu.Muzichita zimenezi kuopa kuti mkwiyo wanga ungabuke ngati moto ndi kukutenthani,chifukwa cha ntchito zanu zoyipazopopanda wina wowuzimitsa. 5 “Lengeza ku Yuda ndi kulalikira mu Yerusalemu kuti,‘Lizani lipenga mʼdziko lonse!’Ndipo fuwulani kuti,‘Sonkhanani!Tiyeni tithawire ku mizinda yotetezedwa!’ 6 Kwezani mbendera kuyangʼana ku Ziyoni!Musachedwe, thawani kuti mupulumuke!Pakuti Ine ndikubweretsa chilango kuchokera kumpoto,kudzakhala chiwonongeko choopsa.” 7 Monga mkango umatulukira mʼngaka yakemomwemonso wowononga mayikowanyamuka ndi kutuluka ku mbuto yake.Watero kuti awononge dziko lanu.Mizinda yanu idzakhala mabwinjapopanda wokhalamo. 8 Choncho valani ziguduli,lirani ndi kubuwula,pakuti mkwiyo waukulu wa Yehovasunatichokere. 9 “Pa tsiku limenelo, mfumu ndi nduna zake adzataya mtima,ansembe adzachita mantha kwambiri,ndipo aneneri adzathedwa nzeru,”akutero Yehova. 10 Ndipo ine ndinati, “Haa, Ambuye Yehova, ndithu munawanyenga anthu awa pamodzi ndi Yerusalemu pamene munanena kuti, ‘Mudzakhala pa mtendere,’ chonsecho lupanga lili pakhosi pathu.” 11 Nthawi imeneyo anthu awa ndi Yerusalemu adzawawuza kuti, “Mphepo yotentha yochokera ku magomo a mʼchipululu ikuwomba pa anthu anga, osati mphepo yopeta kapena yoyeretsa; 12 koma mphepo yamphamvu kwambiri yochokera kwa Ine. Tsono ndi Ineyo amene ndikuwaweruza.” 13 Taonani, adani akubwera ngati mitambo,magaleta awo akubwera ngati kamvuluvulu,akavalo awo ndi aliwiro kupambana chiwombankhanga.Tsoka ilo! Tawonongeka! 14 Iwe Yerusalemu, tsuka mtima wako kuchotsa zoyipa kuti upulumuke.Kodi maganizo ako oyipawo udzakhala nawo mpaka liti? 15 Pakuti amithenga akulalika mawu mʼdziko la Dani;akulengeza za masautso kuchokera ku mapiri a Efereimu. 16 Iwo akuti, “Fotokozani zimenezi kwa anthu a mitundu ina,lengezani zimenezi mu Yerusalemu kuti,‘Ankhondo akubwera kuchokera ku dziko lakutali,akufuwula ndi kudzazinga mizinda ya Yuda. 17 Azinga Yerusalemu ngati anthu olondera munda,chifukwa Yerusalemu wandiwukira,’ ”akutero Yehova. 18 “Makhalidwe anu ndi zochita zanuzakubweretserani zimenezi.Chimenechi ndiye chilango chanu.Nʼchowawa kwambiri!Nʼcholasa mpaka mu mtima!” 19 Mayo, mayo,ndikumva kupweteka!Aa, mtima wanga ukupweteka,ukugunda kuti thi, thi, thi.Sindingathe kukhala chete.Pakuti ndamva kulira kwa lipenga;ndamva mfuwu wankhondo. 20 Tsoka limatsata tsoka linzake;dziko lonse lasanduka bwinja.Mwadzidzidzi matenti athu awonongedwa,mwa kanthawi kochepa nsalu zake zotchinga zagwetsedwa. 21 Kodi ndikhale ndikuona mbendera ya nkhondo,ndi kumva kulira kwa lipenga mpaka liti? 22 Yehova akuti, “Anthu anga ndi zitsiru;iwo sandidziwa.Iwo ndi ana opanda nzeru;samvetsa chilichonse.Ali ndi luso lochita zoyipa,koma sadziwa kuchita zabwino.” 23 Ndinayangʼana dziko lapansi,ndipo linali lopanda anthu ndi lopanda kanthu;ndinayangʼana thambo,koma linalibe kuwala kulikonse. 24 Ndinayangʼana mapiri,ndipo ankagwedezeka;magomo onse ankangosunthira uku ndi uku. 25 Ndinayangʼana, ndipo sindinaone anthu;mbalame iliyonse ya mlengalenga inali itathawa. 26 Ndinayangʼana, dziko lachonde linali litasanduka chipululu;mizinda yake yonse inali itasanduka bwinjapamaso pa Yehova, chifukwa cha mkwiyo wake. 27 Yehova akuti,“Dziko lonse lidzasanduka chipululukomabe sindidzaliwononga kotheratu. 28 Chifukwa chake dziko lapansi lidzalirandipo thambo lidzachita mdima,pakuti ndayankhula ndipo sindidzafewa mtima,ndatsimikiza ndipo sindidzabwerera mʼmbuyo.” 29 Pakumva phokoso la okwera pa akavalo ndi la anthu oponya mivi,anthu a mʼmizinda adzathawa.Ena adzabisala ku nkhalango;ena adzakwera mʼmatanthwemizinda yonse nʼkuyisiya;popanda munthu wokhalamo. 30 Iwe Yerusalemu, ndiwe bwinja!Ukutanthauza chiyani kuvala zovala zofiirandi kuvalanso zokometsera zagolide?Ngakhale udzikonze maso ako powapaka zokometsera,ukungodzivuta chabe.Zibwenzi zako zikukunyoza;zikufuna kuchotsa moyo wako. 31 Ndikumva kulira ngati kwa mayi pa nthawi yake yobereka,kubuwula ngati kwa mayi amene akubereka mwana wake woyamba.Kuliraku ndi kwa anthu a mu Ziyoni, wefuwefu.Atambalitsa manja awo nʼkumati,“Kalanga ife! Tikukomoka.Moyo wathu waperekedwa kwa anthu otipha.”

In Other Versions

Jeremiah 4 in the ANGEFD

Jeremiah 4 in the ANTPNG2D

Jeremiah 4 in the AS21

Jeremiah 4 in the BAGH

Jeremiah 4 in the BBPNG

Jeremiah 4 in the BBT1E

Jeremiah 4 in the BDS

Jeremiah 4 in the BEV

Jeremiah 4 in the BHAD

Jeremiah 4 in the BIB

Jeremiah 4 in the BLPT

Jeremiah 4 in the BNT

Jeremiah 4 in the BNTABOOT

Jeremiah 4 in the BNTLV

Jeremiah 4 in the BOATCB

Jeremiah 4 in the BOATCB2

Jeremiah 4 in the BOBCV

Jeremiah 4 in the BOCNT

Jeremiah 4 in the BOECS

Jeremiah 4 in the BOHCB

Jeremiah 4 in the BOHCV

Jeremiah 4 in the BOHLNT

Jeremiah 4 in the BOHNTLTAL

Jeremiah 4 in the BOICB

Jeremiah 4 in the BOILNTAP

Jeremiah 4 in the BOITCV

Jeremiah 4 in the BOKCV

Jeremiah 4 in the BOKCV2

Jeremiah 4 in the BOKHWOG

Jeremiah 4 in the BOKSSV

Jeremiah 4 in the BOLCB

Jeremiah 4 in the BOLCB2

Jeremiah 4 in the BOMCV

Jeremiah 4 in the BONAV

Jeremiah 4 in the BONCB

Jeremiah 4 in the BONLT

Jeremiah 4 in the BONUT2

Jeremiah 4 in the BOPLNT

Jeremiah 4 in the BOSCB

Jeremiah 4 in the BOSNC

Jeremiah 4 in the BOTLNT

Jeremiah 4 in the BOVCB

Jeremiah 4 in the BOYCB

Jeremiah 4 in the BPBB

Jeremiah 4 in the BPH

Jeremiah 4 in the BSB

Jeremiah 4 in the CCB

Jeremiah 4 in the CUV

Jeremiah 4 in the CUVS

Jeremiah 4 in the DBT

Jeremiah 4 in the DGDNT

Jeremiah 4 in the DHNT

Jeremiah 4 in the DNT

Jeremiah 4 in the ELBE

Jeremiah 4 in the EMTV

Jeremiah 4 in the ESV

Jeremiah 4 in the FBV

Jeremiah 4 in the FEB

Jeremiah 4 in the GGMNT

Jeremiah 4 in the GNT

Jeremiah 4 in the HARY

Jeremiah 4 in the HNT

Jeremiah 4 in the IRVA

Jeremiah 4 in the IRVB

Jeremiah 4 in the IRVG

Jeremiah 4 in the IRVH

Jeremiah 4 in the IRVK

Jeremiah 4 in the IRVM

Jeremiah 4 in the IRVM2

Jeremiah 4 in the IRVO

Jeremiah 4 in the IRVP

Jeremiah 4 in the IRVT

Jeremiah 4 in the IRVT2

Jeremiah 4 in the IRVU

Jeremiah 4 in the ISVN

Jeremiah 4 in the JSNT

Jeremiah 4 in the KAPI

Jeremiah 4 in the KBT1ETNIK

Jeremiah 4 in the KBV

Jeremiah 4 in the KJV

Jeremiah 4 in the KNFD

Jeremiah 4 in the LBA

Jeremiah 4 in the LBLA

Jeremiah 4 in the LNT

Jeremiah 4 in the LSV

Jeremiah 4 in the MAAL

Jeremiah 4 in the MBV

Jeremiah 4 in the MBV2

Jeremiah 4 in the MHNT

Jeremiah 4 in the MKNFD

Jeremiah 4 in the MNG

Jeremiah 4 in the MNT

Jeremiah 4 in the MNT2

Jeremiah 4 in the MRS1T

Jeremiah 4 in the NAA

Jeremiah 4 in the NASB

Jeremiah 4 in the NBLA

Jeremiah 4 in the NBS

Jeremiah 4 in the NBVTP

Jeremiah 4 in the NET2

Jeremiah 4 in the NIV11

Jeremiah 4 in the NNT

Jeremiah 4 in the NNT2

Jeremiah 4 in the NNT3

Jeremiah 4 in the PDDPT

Jeremiah 4 in the PFNT

Jeremiah 4 in the RMNT

Jeremiah 4 in the SBIAS

Jeremiah 4 in the SBIBS

Jeremiah 4 in the SBIBS2

Jeremiah 4 in the SBICS

Jeremiah 4 in the SBIDS

Jeremiah 4 in the SBIGS

Jeremiah 4 in the SBIHS

Jeremiah 4 in the SBIIS

Jeremiah 4 in the SBIIS2

Jeremiah 4 in the SBIIS3

Jeremiah 4 in the SBIKS

Jeremiah 4 in the SBIKS2

Jeremiah 4 in the SBIMS

Jeremiah 4 in the SBIOS

Jeremiah 4 in the SBIPS

Jeremiah 4 in the SBISS

Jeremiah 4 in the SBITS

Jeremiah 4 in the SBITS2

Jeremiah 4 in the SBITS3

Jeremiah 4 in the SBITS4

Jeremiah 4 in the SBIUS

Jeremiah 4 in the SBIVS

Jeremiah 4 in the SBT

Jeremiah 4 in the SBT1E

Jeremiah 4 in the SCHL

Jeremiah 4 in the SNT

Jeremiah 4 in the SUSU

Jeremiah 4 in the SUSU2

Jeremiah 4 in the SYNO

Jeremiah 4 in the TBIAOTANT

Jeremiah 4 in the TBT1E

Jeremiah 4 in the TBT1E2

Jeremiah 4 in the TFTIP

Jeremiah 4 in the TFTU

Jeremiah 4 in the TGNTATF3T

Jeremiah 4 in the THAI

Jeremiah 4 in the TNFD

Jeremiah 4 in the TNT

Jeremiah 4 in the TNTIK

Jeremiah 4 in the TNTIL

Jeremiah 4 in the TNTIN

Jeremiah 4 in the TNTIP

Jeremiah 4 in the TNTIZ

Jeremiah 4 in the TOMA

Jeremiah 4 in the TTENT

Jeremiah 4 in the UBG

Jeremiah 4 in the UGV

Jeremiah 4 in the UGV2

Jeremiah 4 in the UGV3

Jeremiah 4 in the VBL

Jeremiah 4 in the VDCC

Jeremiah 4 in the YALU

Jeremiah 4 in the YAPE

Jeremiah 4 in the YBVTP

Jeremiah 4 in the ZBP