Job 39 (BOGWICC)
1 “Kodi iwe umadziwa nthawi imene mbalale yayikazi imaswera?Kodi umaonerera pamene nswala ikubala? 2 Kodi umawerenga miyezi imene zimakhala ndi bere?Kodi nthawi imene zimaswana iwe umayidziwa? 3 Zimakhala tsonga ndi kuswa ana awo;pamenepo ululu wobereka nʼkutha. 4 Ana a nyamazi amakhala ndi mphamvu ndipo amakulira mʼthengo;kenaka amachoka ndipo sabwereranso. 5 “Kodi bulu wakuthengo amamupatsa ndani ufulu wongodziyendera?Ndani amamasula zingwe zake? 6 Ine ndinamupatsa chipululu kuti chikhale mudzi wake,nthaka ya mchere kuti ikhale malo ake okhalamo 7 Iye amakhala kutali ndi phokoso la mu mzinda;ndipo samva kufuwula kwa oyendetsa nyama zakatundu. 8 Amayendayenda mʼmapiri kudya msipundipo amafunafuna msipu uliwonse wobiriwira. 9 “Kodi njati ingavomere kukutumikira?Kodi ingagone mu gome lako usiku? 10 Kodi ungathe kuyimanga ndi zingwe kuti izilima?Kodi ingasalaze nthumbira mʼmunda mwako? 11 Kodi ungadalire njatiyo chifukwa champhamvu zake?Kodi ungayilekere kuti igwire ntchito zako zolemetsa? 12 Kodi ungadalire kuti idzakubweretsera tirigu wakondi kumuyika ku malo opunthira? 13 “Nthiwatiwa imakupiza mapiko ake monyadira,koma mapikowo sangafanane ndi mapiko ndi nthenga za kakowa. 14 Nthiwatiwa imakwirira mazira ake pansindipo amafundidwa ndi nthaka, 15 nthiwatiwayo sidera nkhawa kuti mazira ake angathe kuswanyidwa,ndi kuti nyama zakuthengo zitha kuwaponda. 16 Nthiwatiwa imachitira nkhanza ana ake ngati anawo si ake;Imayiwala zoti inavutika powabala. 17 Chifukwa Mulungu anayimana nzeru,simvetsa kanthu kalikonse. 18 Komatu nthiwatiwa ikadzambatuka ndi kuyamba kuthamanga,imamusiya kutali kavalo ndi wokwerapo wake. 19 “Kodi ndiwe amene umamupatsa mphamvu kavalokapena kumuveka chenjerere mʼkhosi mwake? 20 Kodi ndiwe amene umalipatsa dzombe ulemerero wolumphira,ukali wake nʼkumachititsa mantha? 21 Iye amalumphalumpha moopseza, kukondwerera mphamvu zake,ndipo amapita ku nkhondo ndi mphamvu zake zonse. 22 Iye sachita mantha, saopa chilichonse;sabwerera mʼmbuyo akaona lupanga. 23 Zida zankhondo zimachita kwichikwichi mʼchimake pambali pakepamodzi ndi mkondo wonyezimira ndi nthungo. 24 Kavaloyo amanjenjemera ndi ukali ndi kulumphalumpha;satha kungoyima pamene wamva kulira kwa lipenga. 25 Lipenga likalira amati, ‘Twee!’Amamva fungo la nkhondo ali patali,kufuwula kwa anthu olamulira nkhondo ndi mfuwu wankhondo. 26 “Kodi kabawi amawuluka ndi nzeru zako,ndi kutambasula mapiko ake kupita kummwera? 27 Kodi umalamulira chiwombankhanga ndiwe kuti chiziwulukandi kumanga chisa chake pamwamba penipeni? 28 Chimakhala pa phiri ndipo chimakhala pamenepo usiku;chimakhala pa msonga penipeni pa mwala. 29 Chili pamenepo chimayangʼanayangʼana choti chigwire kuti chidye;maso ake amachionera patali chinthucho. 30 Ana ake amayamwa magazi,ndipo kumene kuli mitembo ndiko chimapezeka.”
In Other Versions
Job 39 in the ANGEFD
Job 39 in the ANTPNG2D
Job 39 in the AS21
Job 39 in the BAGH
Job 39 in the BBPNG
Job 39 in the BBT1E
Job 39 in the BDS
Job 39 in the BEV
Job 39 in the BHAD
Job 39 in the BIB
Job 39 in the BLPT
Job 39 in the BNT
Job 39 in the BNTABOOT
Job 39 in the BNTLV
Job 39 in the BOATCB
Job 39 in the BOATCB2
Job 39 in the BOBCV
Job 39 in the BOCNT
Job 39 in the BOECS
Job 39 in the BOHCB
Job 39 in the BOHCV
Job 39 in the BOHLNT
Job 39 in the BOHNTLTAL
Job 39 in the BOICB
Job 39 in the BOILNTAP
Job 39 in the BOITCV
Job 39 in the BOKCV
Job 39 in the BOKCV2
Job 39 in the BOKHWOG
Job 39 in the BOKSSV
Job 39 in the BOLCB
Job 39 in the BOLCB2
Job 39 in the BOMCV
Job 39 in the BONAV
Job 39 in the BONCB
Job 39 in the BONLT
Job 39 in the BONUT2
Job 39 in the BOPLNT
Job 39 in the BOSCB
Job 39 in the BOSNC
Job 39 in the BOTLNT
Job 39 in the BOVCB
Job 39 in the BOYCB
Job 39 in the BPBB
Job 39 in the BPH
Job 39 in the BSB
Job 39 in the CCB
Job 39 in the CUV
Job 39 in the CUVS
Job 39 in the DBT
Job 39 in the DGDNT
Job 39 in the DHNT
Job 39 in the DNT
Job 39 in the ELBE
Job 39 in the EMTV
Job 39 in the ESV
Job 39 in the FBV
Job 39 in the FEB
Job 39 in the GGMNT
Job 39 in the GNT
Job 39 in the HARY
Job 39 in the HNT
Job 39 in the IRVA
Job 39 in the IRVB
Job 39 in the IRVG
Job 39 in the IRVH
Job 39 in the IRVK
Job 39 in the IRVM
Job 39 in the IRVM2
Job 39 in the IRVO
Job 39 in the IRVP
Job 39 in the IRVT
Job 39 in the IRVT2
Job 39 in the IRVU
Job 39 in the ISVN
Job 39 in the JSNT
Job 39 in the KAPI
Job 39 in the KBT1ETNIK
Job 39 in the KBV
Job 39 in the KJV
Job 39 in the KNFD
Job 39 in the LBA
Job 39 in the LBLA
Job 39 in the LNT
Job 39 in the LSV
Job 39 in the MAAL
Job 39 in the MBV
Job 39 in the MBV2
Job 39 in the MHNT
Job 39 in the MKNFD
Job 39 in the MNG
Job 39 in the MNT
Job 39 in the MNT2
Job 39 in the MRS1T
Job 39 in the NAA
Job 39 in the NASB
Job 39 in the NBLA
Job 39 in the NBS
Job 39 in the NBVTP
Job 39 in the NET2
Job 39 in the NIV11
Job 39 in the NNT
Job 39 in the NNT2
Job 39 in the NNT3
Job 39 in the PDDPT
Job 39 in the PFNT
Job 39 in the RMNT
Job 39 in the SBIAS
Job 39 in the SBIBS
Job 39 in the SBIBS2
Job 39 in the SBICS
Job 39 in the SBIDS
Job 39 in the SBIGS
Job 39 in the SBIHS
Job 39 in the SBIIS
Job 39 in the SBIIS2
Job 39 in the SBIIS3
Job 39 in the SBIKS
Job 39 in the SBIKS2
Job 39 in the SBIMS
Job 39 in the SBIOS
Job 39 in the SBIPS
Job 39 in the SBISS
Job 39 in the SBITS
Job 39 in the SBITS2
Job 39 in the SBITS3
Job 39 in the SBITS4
Job 39 in the SBIUS
Job 39 in the SBIVS
Job 39 in the SBT
Job 39 in the SBT1E
Job 39 in the SCHL
Job 39 in the SNT
Job 39 in the SUSU
Job 39 in the SUSU2
Job 39 in the SYNO
Job 39 in the TBIAOTANT
Job 39 in the TBT1E
Job 39 in the TBT1E2
Job 39 in the TFTIP
Job 39 in the TFTU
Job 39 in the TGNTATF3T
Job 39 in the THAI
Job 39 in the TNFD
Job 39 in the TNT
Job 39 in the TNTIK
Job 39 in the TNTIL
Job 39 in the TNTIN
Job 39 in the TNTIP
Job 39 in the TNTIZ
Job 39 in the TOMA
Job 39 in the TTENT
Job 39 in the UBG
Job 39 in the UGV
Job 39 in the UGV2
Job 39 in the UGV3
Job 39 in the VBL
Job 39 in the VDCC
Job 39 in the YALU
Job 39 in the YAPE
Job 39 in the YBVTP
Job 39 in the ZBP